Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani lemba la 2 Samueli 21:7-9, limanena kuti Davide ‘anamvera chisoni Mefiboseti’ koma kenako anapereka Mefiboseti kuti aphedwe?

Anthu ena omwe amangowerenga nkhani imeneyi mofulumira amadabwa nazo zimenezi. Komatu panali anthu awiri omwe anali ndi dzina lakuti Mefiboseti, ndipo tingaphunzirepo mfundo zina tikaganizira zomwe zinachitika.

Mfumu Sauli ya ku Isiraeli, inali ndi ana aamuna 7 ndi aakazi awiri. Mwana woyamba anali Yonatani. Kenako mfumuyi inaberekanso mwana wina wamwamuna dzina lake Mefiboseti, yemwe mayi ake anali mkazi wake wamng’ono, Rizipa. N’zochititsa chidwi kuti nayenso Yonatani anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Mefiboseti. Choncho Mfumu Sauli anali ndi mwana wotchedwa Mefiboseti ndi mdzukulu yemwenso anali ndi dzina lomweli.

Panthawi ina Mfumu Sauli anaukira Agibeoni omwe ankakhala pakati pa Aisiraeli ndipo ankafuna kuwapha onse. Ndipotu Agibeoni ena anali ataphedwa kale. Zimenezitu sizinali zoyenera. Chifukwa chiyani? Chifukwa m’nthawi ya Yoswa, akuluakulu a Isiraeli anachita pangano la mtendere ndi Agibeoniwo.​—Yos. 9:3-27.

Pangano limeneli linali likugwirabe ntchito munthawi ya Mfumu Sauli. Koma mosemphana ndi panganolo, mfumuyo inkafuna kupha Agibeoni onse. Zimenezi zinachititsa kuti ‘Sauli pamodzi ndi nyumba yake, akhale ndi mlandu wa magazi.’ (2 Sam. 21:1) Kenako Davide anakhala mfumu. Agibeoni omwe anapulumuka anamuuza zimene zinachitikazi. Davide anawafunsa zimene angachite kuti akonze zoipa zimene Sauli anachita, n’cholinga choti Yehova apitirize kudalitsa dziko lawo. M’malo monena kuti awapatse ndalama, Agibeoniwo anapempha kuti aphe ana 7 a munthu yemwe ‘anawakonzera chiwembu.’ (Num. 35:30, 31) Ndipo Davide anavomereza zimene anapemphazo.​—2 Sam. 21:2-6.

Panthawiyo, Sauli ndi Yonatani anali ataphedwa kunkhondo koma mwana wa Yonatani Mefiboseti anali adakali ndi moyo. Iye anali wolumala chifukwa cha ngozi yomwe inachitika ali mwana ndipo n’zodziwikiratu kuti sanatenge nawo mbali pa zoipa zomwe agogo ake anachitira Agibeoni. Davide anachita pangano ndi Yonatani yemwe anali mnzake ndipo panganolo likanathandiza ana a Yonatani kuphatikizapo Mefiboseti. (1 Sam. 18:1; 20:42) Baibulo limati: “Mfumu [Davide] inamvera chisoni Mefiboseti mwana wamwamuna wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha lumbiro limene Davideyo ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pakati pawo pamaso pa Yehova.”​—2 Sam. 21:7.

Ngakhale zinali choncho, Davide analemekezabe zimene Agibeoni anapempha. Iye anawapatsa zidzukulu 5 za Sauli komanso ana ake awiri, omwe mmodzi wa iwo anali Mefiboseti. (2 Sam. 21:8, 9) Zimene Davide anachita zinachotsa mlandu wa magazi m’dzikolo.

Sikuti nkhaniyi yangokhala mbiri chabe. Lamulo la Mulungu linkanena momveka bwino kuti: “Ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo” awo. (Deut. 24:16) Yehova sakanavomereza zomwe zinachitikira ana awiri a Sauli komanso zidzukulu zake 5 zikanakhala kuti iwo sanali olakwa. Lamulo lija linkapitiriza kuti: “Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.” Zikuoneka kuti anthu 7 a m’banja la Sauli omwe anaphedwawa, anatenga nawo mbali pa chiwembu chomwe Sauliyo anakonzera Agibeoni. Choncho anthu 7 amenewa anaphedwa chifukwa cha machimo awo.

Nkhaniyi ikusonyeza kuti munthu sangadzikhululukire pa zoipa zomwe wachita poganiza kapena kunena kuti anangotsatira malangizo omwe anapatsidwa. Mwambi wina wanzeru umanena kuti: “Salaza njira ya phazi lako, ndipo njira zako zonse zikhazikike.”​—Miy. 4:24-27; Aef. 5:15.