NKHANI YOPHUNZIRA 12
NYIMBO NA. 77 Kuwala M’dziko Lamdima
Musakhale Mumdima, Koma Khalanibe M’kuwala
“Poyamba munali ngati mdima, koma pano muli ngati kuwala.”—AEF. 5:8.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona zimene tiphunzire pa mawu akuti mdima ndi kuwala otchulidwa mu Aefeso chaputala 5.
1-2. (a) Kodi zinthu zinali bwanji pamene kalata yopita kwa Aefeso inkalembedwa? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
MTUMWI Paulo ali pa ukaidi wosachoka pakhomo ku Roma, ankafuna kulimbikitsa Akhristu anzake. Iye sakanatha kuwayendera, choncho anawalembera makalata. Imodzi mwa makalatawa inali yopita kwa Akhristu a ku Efeso, ndipo inalembedwa cha 60 kapena 61 C.E.—Aef. 1:1; 4:1.
2 Zaka pafupifupi 10 m’mbuyomo, Paulo ankaphunzitsa komanso kulalikira uthenga wabwino ku Efeso. (Mac. 19:1, 8-10; 20:20, 21) Iye ankakonda kwambiri abale akewo ndipo ankafunitsitsa kuwathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova. Koma n’chifukwa chiyani iye analembera Akhristu odzozedwa zokhudza kuwala ndi mdima? Nanga Akhristu onse angaphunzire chiyani pa malangizo amenewa? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa.
KUCHOKA MUMDIMA KUPITA M’KUWALA
3. Kodi Paulo anagwiritsa ntchito mawu ati m’kalata imene analembera Akhristu a ku Efeso?
3 Paulo analembera Akhristu a ku Efeso kuti: “Poyamba munali ngati mdima, koma pano muli ngati kuwala.” (Aef. 5:8) Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti mdima ndi kuwala pofuna kusiyanitsa zinthu ziwiri. N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti poyamba Aefeso ‘anali mumdima’?
4. Kodi Akhristu a ku Efeso anali mumdima pa nkhani ya kulambira m’njira yotani?
4 Mdima pa nkhani ya kulambira. Akhristu a ku Efeso amene Paulo anawalembera kalata, asanaphunzire choonadi ankakhulupirira zinthu zabodza komanso ankachita zamizimu. Mumzinda wa Efeso munali kachisi wa Atemi yemwe anthu kalelo ankaona kuti anali chimodzi mwa zinthu 7 zodabwitsa padziko lonse. Anthu amene ankalambira kukachisiyu ankagwiritsa ntchito kwambiri mafano. Kupanga ndiponso kugulitsa tiakachisi ta mulungu wamkazi Atemi inali bizinesi ya ndalama zambiri. (Mac. 19:23-27) Kuwonjezera pamenepo, anthu ambiri mumzinda wa Efeso ankachita zamatsenga.—Mac. 19:19.
5. Kodi anthu a ku Efeso anali mumdima wa makhalidwe m’njira iti?
5 Mdima wa makhalidwe. Anthu ambiri mumzinda wa Efeso anali achiwerewere komanso a khalidwe lopanda manyazi. Nthabwala zotukwana zinkanenedwa m’mabwalo amasewera ngakhalenso pamiyambo yachipembedzo. (Aef. 5:3) ‘Sankathanso kuzindikira makhalidwe abwino’ kutanthauza kuti “sankamvanso kupweteka kulikonse.” (Aef. 4:17-19) Asanaphunzire zolondola pa nkhani ya zoyenera ndi zosayenera, chikumbumtima cha Akhristu a ku Efeso sichinkawavutitsa ndipo sankaganiza n’komwe kuti Yehova angawaimbe mlandu chifukwa cha zochita zawo. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti iwo anali “mumdima wa maganizo ndipo anali otalikirana ndi moyo umene umachokera kwa Mulungu.”
6. N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti Akhristu a ku Efeso tsopano “anali ngati kuwala”?
6 Koma anthu ena a ku Efeso sanakhalebe mumdima. Ponena za iwo Paulo analemba kuti “pano muli ngati kuwala popeza ndinu ogwirizana ndi Ambuye.” (Aef. 5:8) Iwo anali ataona kuwala kwa choonadi cha m’Malemba. (Sal. 119:105) Anali atasiya miyambo ya chipembedzo chabodza komanso makhalidwe oipa. Iwo anayamba kutsanzira Mulungu ndipo ankachita zonse zimene angathe kuti azimulambira komanso kumusangalatsa.—Aef. 5:1.
7. Kodi ifeyo tikufanana bwanji ndi Akhristu ambiri a ku Efeso?
7 Ifenso tisanaphunzire choonadi tinali mumdima pa nkhani ya kulambira komanso makhalidwe. Ena ankachita maholide a chipembedzo chabodza pomwe ena anali achiwerewere. Koma titaphunzira mfundo za Yehova pa nkhani ya zoyenera ndi zolakwika, tinasintha. Tinayamba kusintha moyo wathu kuti ugwirizane ndi mfundo zake zolungama ndipo tsopano tikupeza madalitso ambiri. (Yes. 48:17) Komabe panopa pali mavuto amene tikukumana nawo. Tiyenera kutalikirana ndi mdima womwe tinausiya n’kupitiriza “kuyenda ngati ana a kuwala.” Kodi tingachite bwanji zimenezi?
MUSAKHALE MUMDIMA
8. Mogwirizana ndi Aefeso 5:3-5, kodi Akhristu a ku Efeso ankafunika kupewa chiyani?
8 Werengani Aefeso 5:3-5. Kuti atalikirane ndi mdima wa makhalidwe oipa, Akhristu a ku Efeso anafunika kupitiriza kupewa miyambo imene sisangalatsa Yehova. Sikuti ankangofunika kupewa chiwerewere, koma ankafunikanso kupewa nthabwala zotukwana. Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Efeso kuti ayenera kupewa zimenezi kuti adzalowe “mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.”
9. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa chilichonse chomwe chingachititse kuti tichite chiwerewere?
9 Ifenso tiyenera kukhala osamala kuti tisamachite zinthu zomwe ndi “ntchito zosapindulitsa zamumdima.” (Aef. 5:11) Zimene zachitikirapo anthu ena zikusonyeza kuti munthu amene amakonda kuona, kumvetsera kapena kulankhula za zinthu zodetsa kapena zachiwerewere, zimakhala zosavuta kuti achite zinthu zoipa. (Gen. 3:6; Yak. 1:14, 15) M’dziko lina, gulu la abale angapo linkacheza pamalo ochezera a pa intaneti. Poyamba ambiri mwa abalewa ankakambirana zokhudza Yehova komanso choonadi. Koma pang’ono ndi pang’ono, iwo anayamba kukambirana zinthu zimene Yehova sasangalala nazo. Anayamba kukambirana zokhudza chiwerewere. Pambuyo pake, ambiri mwa abalewa anavomereza kuti nkhani zimene ankakambiranazo zinachititsa kuti achite zachiwerewere.
10. Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira iti pofuna kutipusitsa? (Aefeso 5:6)
10 Dziko la Satanali limafuna kutipusitsa kuti tizikhulupirira kuti zimene Yehova amaona kuti ndi zoipa komanso zodetsa ndi zabwinobwino. (2 Pet. 2:19) Sitiyenera kudabwa ndi zimenezi. Njira imodzi yomwe Mdyerekezi wakhala akugwiritsa ntchito ndi kusokoneza anthu akuti asamathe kuzindikira choyenera ndi chosayenera. (Yes. 5:20; 2 Akor. 4:4) Mpake kuti mafilimu ambiri, mapulogalamu a pa TV komanso pa intaneti amalimbikitsa mfundo zosemphana ndi mfundo zolungama za Yehova. Satana amafuna kutichititsa kuti tiziganiza kuti makhalidwe oipa komanso achiwerewere omwe ndi ofala m’dzikoli ndi ovomerezeka, osangalatsa komanso osaopsa.—Werengani Aefeso 5:6.
11. Kodi zimene zinachitikira Angela zikusonyeza bwanji kufunika kotsatira malangizo anzeru opezeka pa Aefeso 5:7? (Onaninso chithunzi.)
11 Satana amafuna kuti tizigwirizana ndi anthu amene angachititse kuti tisamamvere mfundo za Yehova. N’chifukwa chake Paulo anauza Akhristu a ku Efeso kuti: “Musamachite zimene iwo amachita” kutanthauza anthu amene amachita zimene Mulungu amadana nazo. (Aef. 5:7) Tizikumbukira kuti anthu amene timagwirizana nawo si amene timacheza nawo pamasom’pamaso okha. Anthuwa akuphatikizapo amene timacheza nawo pa intaneti, zinthu zimene m’nthawi ya Akhristu akale a ku Efeso kunalibe. Angela, a amene amakhala ku Asia, anaona kuti kucheza ndi anthu pa intaneti ndi koopsa. Iye anati: “Pang’ono ndi pang’ono, msampha umenewu ukhoza kusokoneza maganizo a munthu. Ndinafika pomaganiza kuti palibe vuto kucheza ndi anthu amene salemekeza mfundo za m’Baibulo. Patapita nthawi ndinayamba kuganiza kuti palibe vuto kuchita zinthu zimene sizisangalatsa Yehova.” Koma mwamwayi, akulu achikondi anathandiza Angela kuti asinthe. Iye anati: “Panopa ndimaganizira kwambiri za Yehova ndi mfundo zake osati mfundo za pa intaneti.”
12. N’chiyani chingatithandize kuti tiziyendera mfundo za Yehova pa nkhani ya zoyenera ndi zosayenera?
12 Tiyenera kupewa maganizo a m’dzikoli akuti khalidwe lachiwerewere si lolakwika. Ifeyo timadziwa kuti maganizo amenewa ndi olakwika. (Aef. 4:19, 20) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayesetsa kupewa kucheza mosayenera ndi anzanga a kuntchito, kusukulu kapena anthu ena amene salemekeza mfundo zolungama za Yehova? Kodi ndimalolera kutsatira mfundo za Yehova ngakhale ena azindiona kuti ndine wovuta?’ Mogwirizana ndi 2 Timoteyo 2:20-22, tiyenera kukhalanso osamala pamene tikusankha anzathu mumpingo. Tizikumbukira kuti ena sangatithandize kukhalabe okhulupirika potumikira Yehova.
MUZIYENDA “NGATI ANA A KUWALA”
13. Kodi ‘kupitiriza kuyenda ngati ana a kuwala’ kumatanthauza chiyani? (Aefeso 5:7-9)
13 Sikuti Paulo anangolimbikitsa Akhristu a ku Efeso kuti azipewa mdima, koma anawalimbikitsanso kuti ‘apitirize kuyenda ngati ana a kuwala.’ (Werengani Aefeso 5:7-9.) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Iye ankatanthauza kuti nthawi zonse tiyenera kumachita zinthu ngati Akhristu oona. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kuwerenga ndiponso kuphunzira mwakhama Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo. N’zofunika kuti tiziganizira kwambiri chitsanzo cha Yesu Khristu yemwe ndi “kuwala kwa dziko” komanso zimene anaphunzitsa.—Yoh. 8:12; Miy. 6:23.
14. Kodi mzimu woyera ungatithandize bwanji?
14 Timafunikanso mzimu woyera wa Mulungu kuti tipitirize kuchita zinthu ngati “ana a kuwala.” Chifukwa chiyani? Chifukwa si zophweka kupitiriza kukhala oyera m’dziko la makhalidwe oipali. (1 Ates. 4:3-5, 7, 8) Mzimu woyera ungatithandize kupewa maganizo a m’dzikoli kuphatikizapo nzeru za anthu komanso mfundo zimene zimasemphana ndi maganizo a Mulungu. Ungatithandizenso kuti tizichita ‘chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama.’—Aef. 5:9.
15. Kodi tingalandire mzimu woyera m’njira ziti? (Aefeso 5:19, 20)
15 Njira imodzi imene tingalandirire mzimu woyera ndi kuupempha. Yesu ananena kuti Yehova “adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akumupempha.” (Luka 11:13) Komanso tikamatamanda Yehova pamisonkhano ndi Akhristu anzathu timalandira mzimu woyera. (Werengani Aefeso 5:19, 20.) Mzimu woyera umatithandiza kuti tizichita zinthu zimene zimasangalatsa Mulungu.
16. N’chiyani chingatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru? (Aefeso 5:10, 17)
16 Tikafuna kusankha zochita pankhani zikuluzikulu, tiyenera “kuzindikira chifuniro cha Yehova” n’kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo. (Werengani Aefeso 5:10, 17.) Tikapeza mfundo za m’Baibulo zogwirizana ndi mmene zinthu zilili kwa ifeyo timakhala kuti tapeza maganizo a Yehova pa nkhaniyo. Ndiyeno tikamagwiritsa ntchito mfundozo, timasankha zochita mwanzeru.
17. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru? (Aefeso 5:15, 16) (Onaninso chithunzi.)
17 Paulo analangizanso Akhristu a ku Efeso kuti azigwiritsa ntchito nthawi mwanzeru. (Werengani Aefeso 5:15, 16.) Satana, yemwe ndi mdani wathu “woipayo,” amafuna kuti tizitanganidwa ndi zinthu zam’dzikoli n’cholinga choti tisakhale ndi nthawi yotumikira Mulungu. N’zosavuta kuti Mkhristu aziika patsogolo chuma, maphunziro kapena ntchito m’malo motumikira Yehova. (1 Yoh. 5:19) Zikatero, munthuyo amakhala kuti wayamba kuganiza ngati anthu a m’dzikoli. N’zoona kuti zinthu zimenezi pazokha si zolakwika koma siziyenera kukhala pamalo oyamba. Kuti tiziyenda “ngati ana a kuwala,” tiyenera ‘kumagwiritsa ntchito bwino nthawi yathu’ n’kumaganizira zinthu zofunika kwambiri.
18. Kodi Donald anachita chiyani kuti azigwiritsa ntchito bwino nthawi yake?
18 Muzifufuza mipata yomwe ingakuthandizeni kuti muzitumikira Yehova mokwanira. Izi ndi zimene Donald yemwe amakhala ku South Africa, anachita. Iye anati: “Ndinaona mmene zinthu zinalili pa moyo wanga ndipo ndinapempha Yehova kuti andithandize kuti ndizichita zambiri mu utumiki. Ndinamupempha kuti andithandize kupeza ntchito yomwe ingandipatse mpata woti ndizipeza nthawi yambiri yolalikira. Yehova anandithandizadi kupeza ntchitoyo. Choncho ine ndi mkazi wanga tinayamba utumiki wa nthawi zonse.”
19. Kodi tingatani kuti tipitirize kuyenda “ngati ana a kuwala”?
19 Kalata imene Paulo analembera Akhristu a ku Efeso iyenera kuti inawathandiza kuti apitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova. Ndipo malangizo a m’kalatayo angatithandizenso ifeyo masiku ano. Monga mmene taonera, malangizowo angatithandize kuti tizisankha mwanzeru zosangalatsa komanso anthu ocheza nawo. Kalatayi ingatilimbikitse kuti tipitirize kukhala m’kuwala kwa choonadi pophunzira Baibulo nthawi zonse. Ikusonyezanso kufunika kwa mzimu woyera womwe ungatithandize kukhala ndi makhalidwe abwino. Kugwiritsa ntchito zimene Paulo analemba kungatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru ndiponso zogwirizana ndi maganizo a Yehova. Tikamachita zimenezi tidzapewa mdima wa m’dzikoli ndipo tidzakhalabe m’kuwala.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
-
Kodi mawu akuti “mdima” ndi “kuwala” otchulidwa pa Aefeso 5:8, amatanthauza chiyani?
-
Kodi tingatani kuti tisakhale ‘mumdima’?
-
Kodi tingatani kuti tipitirize “kuyenda ngati ana a kuwala”?
NYIMBO NA. 95 Kuwala Kukuwonjezerekabe
a Mayina ena asinthidwa.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pachithunzipa pakuoneka kalata yakale imene Paulo analembera Akhristu a ku Efeso.