ZOTI NDIPHUNZIRE
Kupirira Zinthu Zopanda Chilungamo
Werengani Genesis 37:23-28; 39:17-23 kuti muone zinthu zopanda chilungamo zimene Yosefe anapirira.
Ganizirani nkhani yonse. N’chifukwa chiyani Yosefe anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo? (Gen. 37:3-11; 39:1, 6-10) Kodi Yosefe anapirira kwa nthawi yaitali bwanji? (Gen. 37:2; 41:46) Kodi pa nthawiyo ndi zinthu ziti zimene Yehova anamuchitira Yosefe, nanga ndi zinthu ziti zimene sanamuchitire?—Gen. 39:2, 21; w23.01 17 ¶13.
Fufuzani mozama. Baibulo silifotokoza ngati Yosefe anali ndi mwayi wofotokoza mbali yake pa zinthu zabodza zimene mkazi wa Potifara ankamuneneza. Kodi malemba otsatirawa angatithandize bwanji kudziwa chifukwa chimene mwina chinachititsa kuti Yosefe asayankhepo? Nanga angatithandize bwanji kudziwa chifukwa chake sitiyenera kuyembekezera kuti mfundo zonse zifotokozedwe? (Miy. 20:2; Yoh. 21:25; Mac. 21:37) Kodi ndi makhalidwe ati amene anathandiza Yosefe kuti apirire zinthu zopanda chilungamo?—Mika 7:7; Luka 14:11; Yak. 1:2, 3.
Onani zimene mukuphunzirapo. Dzifunseni kuti:
-
‘Kodi ndingachitiridwe zinthu zopanda chilungamo ziti chifukwa chokhala wotsatira wa Yesu?’ (Luka 21:12, 16, 17; Aheb. 10:33, 34.)
-
‘Kodi ndingakonzekere bwanji kuti ndidzapirire zinthu zopanda chilungamo?’ (Sal. 62:7, 8; 105:17-19; w19.07 2-7.)