Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Gula Choonadi Ndipo Usachigulitse”

“Gula Choonadi Ndipo Usachigulitse”

“Gula choonadi ndipo usachigulitse. Gula nzeru, malangizo ndi kumvetsa zinthu.”​MIY. 23:23.

NYIMBO: 94, 96

1, 2. (a) Kodi chinthu chamtengo wapatali kwambiri pa moyo wathu n’chiyani? (b) Tchulani mfundo za choonadi zimene taphunzitsidwa ndipo fotokozani chifukwa chake timaziyamikira. (Onani zithunzi zoyambirira.)

KODI chinthu chamtengo wapatali kwambiri kwa inuyo ndi chiyani? Kodi mungalolere kuchisinthanitsa ndi chinthu chotchipa? Mafunso amenewa si ovuta kwa atumiki a Yehova okhulupirika. Chinthu chamtengo wapatali kwambiri kwa ife ndi ubwenzi wathu ndi Yehova ndipo sitingausinthanitse ndi chilichonse. Timayamikiranso kwambiri choonadi cha m’Baibulo chimene chatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba.​—Akol. 1:9, 10.

2 Tangoganizirani mfundo zambirimbiri zimene Yehova watiphunzitsa kuchokera m’Baibulo. Iye watiuza za dzina lake, tanthauzo la dzinali komanso makhalidwe ake abwino. Iye watiphunzitsanso zoti anatisonyeza chikondi chosaneneka potumiza Mwana wake kuti akhale dipo lotiwombola. Yehova watiuzanso za Ufumu wa Mesiya, zoti odzozedwa adzapita kumwamba ndiponso zoti a “nkhosa zina” adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi. (Yoh. 10:16) Amatiphunzitsanso kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Timayamikira kwambiri zonse zimene watiphunzitsazi chifukwa zimatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino. Zimatithandizanso kuti tiziona kuti moyo wathu uli ndi cholinga.

3. Kodi kugula choonadi sikutanthauza chiyani?

3 Yehova ndi Mulungu wopereka mosaumira. Iye amapereka zinthu zabwino kwa anthu ofuna choonadi. Iye anapereka moyo wa Mwana wake wapadera ngati mphatso yaulere. Apa n’zodziwikiratu kuti Yehova sangafune kuti tigule choonadi ndi ndalama. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika pamene Simoni ankapereka ndalama kwa mtumwi Petulo kuti amupatse mphamvu yopereka mzimu woyera. Mtumwi Petulo anamudzudzula pomuuza kuti: “Siliva wakoyo awonongeke nawe limodzi, chifukwa ukuganiza kuti mphatso yaulere ya Mulungu ungaipeze ndi ndalama.” (Mac. 8:18-20) Ndiye kodi mawu oti “gula choonadi” amatanthauza chiyani?

KODI ‘KUGULA’ CHOONADI KUMATANTHAUZA CHIYANI?

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Werengani Miyambo 23:23. Munthu sangapeze choonadi cha m’Mawu a Mulungu popanda kuchita khama. Munthu ayenera kulolera kuti asakhale ndi zinthu zina n’cholinga choti apeze choonadichi. Paja wolemba buku la Miyambo ananena kuti tiyenera ‘kugula’ kapena kupeza choonadi n’kumayesetsa kuti ‘tisachigulitse’ kapena kulola kuti chitayike. Choncho tiyeni tikambirane tanthauzo la ‘kugula’ choonadi komanso zinthu zimene tingalolere kuchita kuti tigule choonadicho. Kuchita zimenezi kutithandiza kuti tiziyamikira kwambiri choonadi komanso tizisamala kuti ‘tisachigulitse.’ Tionanso kuti ndi nzeru ndithu kusiya zinthu zina kuti tigule choonadi.

5, 6. (a) Kodi tingagule bwanji choonadi popanda kupereka ndalama? Perekani chitsanzo. (b) Kodi choonadi chimatithandiza bwanji?

5 Munthu amafunika kuchita zinazake kuti apeze chinthu ngakhale chinthucho chitakhala chaulere. Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “gula” pa Miyambo 23:23 angamasuliridwenso kuti “peza.” Mawu onsewa amatanthauza kuchita zinazake, kapena kusiya zinazake kuti upeze chinthu chamtengo wapatali. Kuti timvetse mfundoyi, taganizirani za chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti kumsika winawake alengeza kuti kuli nthochi zaulere. Kodi nthochizo zingafike m’nyumba mwathu popanda kuchita chilichonse? Ayi. Tingafunike kupita kumsikako kuti tikazitenge. Kodi pamenepa tingati nthochizo ndi zaulere? Inde n’zaulere koma tifunika kuchita zinazake komanso kupeza nthawi yokazitengera kumsikako. Ndi mmene zililinso ndi kugula choonadi. N’zoona kuti ndi chaulere koma timafunika kuchita zinthu zina kuti tichipeze.

6 Werengani Yesaya 55:1-3. Mawu amene Yehova anauzira Yesaya amatithandizanso kumvetsa tanthauzo la kugula choonadi. Pamavesi amenewa, Yehova anayerekezera mawu ake ndi madzi, mkaka ndi vinyo. Mofanana ndi madzi ozizira bwino, mfundo za choonadi zimatitsitsimula. Ndipo mofanana ndi mkaka umene umatipatsa mphamvu komanso kuthandiza ana kuti akule, mawu a Mulungu amatithandiza kuti tipeze mphamvu komanso tikule mwauzimu. Koma mawu a Yehova alinso ngati vinyo. N’chifukwa chiyani tikutero? Baibulo limasonyeza kuti vinyo amathandiza kuti munthu asangalale. (Sal. 104:15) Choncho pouza anthu ake kuti ‘agule vinyo,’ Yehova akungotsimikizira anthu ake kuti akamatsatira mawu ake adzakhala osangalala. (Sal. 19:8) Kunena zoona, mfundo za m’mavesi amene takambiranawa zikutithandiza kudziwa ubwino wophunzira komanso kutsatira mfundo za choonadi za mawu a Mulungu. Koma zimene munthu amachita kuti apeze choonadicho zili ngati ndalama zimene amapereka kuti achigule. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu 5 zimene tingalolere kuchita kuti tigule choonadi.

KODI MUNACHITA ZINTHU ZITI KUTI MUGULE CHOONADI?

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupeza nthawi kuti tigule choonadi? (b) Kodi mtsikana wina anachita zotani kuti apeze choonadi, nanga zotsatira zake zinali zotani?

7 Nthawi yathu. Pamafunika nthawi kuti munthu apeze choonadi. Mwachitsanzo, munthu ayenera kupeza nthawi yoti amve uthenga wa Ufumu, awerenge Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo, aziphunzira payekha, azikonzekera misonkhano komanso azipezeka pamisonkhanopo. Kuti zimenezi zitheke, munthu amafunika ‘kugula’ nthawi kapena kugwiritsa ntchito nthawi imene akanachitira zinthu zina zosafunika kwenikweni. (Werengani Aefeso 5:15, 16 ndi mawu ake am’munsi.) Kodi pamafunika nthawi yaitali bwanji kuti munthu aphunzire mfundo zoyambirira za m’Baibulo? Zimadalira mmene zinthu zilili pa moyo wa munthuyo. Palibe malire ophunzirira nzeru za Yehova, njira zake komanso ntchito zake. (Aroma 11:33) Magazini yoyambirira ya Nsanja ya Olonda inayerekezera kupeza choonadi ndi kupeza kaduwa kokongola. Magaziniyo inati: “Zikanakhala kuti kaduwa kamodziko n’kokwanira si bwenzi pali enanso. Choncho tisamangokhutira ndi mfundo imodzi yokha ya choonadi. Nthawi zonse tizifufuza mfundo zina.” Ndiye ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi maluwa a choonadi amene ineyo ndapeza ndi ochuluka bwanji?’ Ngakhale titalandira moyo wamuyaya padzakhalabe mfundo zambiri zokhudza Yehova zimene tingaphunzire. Chofunika panopa ndi kugwiritsa ntchito mwanzeru nthawi yathu kuti tiziphunzira mfundo zambiri za choonadi. Tiyeni tikambirane chitsanzo cha munthu wina amene ankafunitsitsa kupeza choonadi.

8 Mariko * ndi mtsikana wa ku Japan amene anapita kumzinda wa New York m’dziko la United States kukaphunzira. Pa nthawiyo n’kuti ali m’gulu linalake lachipembedzo limene linayamba ku Japan chakumapeto kwa zaka za m’ma 1950. Ndiye mlongo wina amene ankachita upainiya anakumana naye mu utumiki. Atayamba kuphunzira naye Baibulo anasangalala kwambiri moti anapempha kuti aziphunzira kawiri pa mlungu. Ngakhale kuti mtsikanayu ankatanganidwa ndi sukulu komanso ankagwira ntchito yaganyu, anayamba kupezeka pamisonkhano ya mpingo. Iye anasiya kupezekapezeka m’malo osiyanasiyana amene ankacheza n’cholinga choti azipeza nthawi yophunzira choonadi. Zimene ankachitazi zinathandiza kuti akule msanga mwauzimu. Chaka chisanathe n’komwe anabatizidwa. Ndipo patangopita miyezi 6, anayamba upainiya m’chaka cha 2006. Panopa akuchitabe upainiya.

9, 10. (a) Kodi munthu akagula choonadi amaona bwanji chuma? (b) Kodi mtsikana wina analolera kusiya chiyani, nanga panopa amamva bwanji?

9 Chuma. Kuti munthu agule choonadi mwina angafunike kusiya ntchito yapamwamba. Paja Yesu ataitana Petulo ndi Andireya kuti akhale “asodzi a anthu,” nthawi yomweyo “anasiya maukonde awo.” (Mat. 4:18-20) Sikuti aliyense amene amaphunzira choonadi masiku ano amafunika kusiya ntchito yake. Paja anthufe timakhalanso ndi maudindo ena. (1 Tim. 5:8) Koma mfundo ndi yakuti munthu amene akuphunzira choonadi amafunika kusintha maganizo ake pa nkhani ya chuma komanso zimene amaziona kuti n’zofunika kwambiri. Yesu anasonyeza bwino mfundo imeneyi pamene ananena kuti: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi. . . . Koma unjikani chuma chanu kumwamba.” (Mat. 6:19, 20) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene anachita mtsikana wina.

10 Maria ankasewera gofu kuyambira ali wamng’ono, asanayambe n’komwe sukulu. Ankasewerabe mpaka pamene anapita kusekondale, moti anapeza mwayi wolipiriridwa kuyunivesite. Iye ankakonda kwambiri masewerawa moti ankafuna kuti adzakhale katswiri kwambiri. Kenako Maria anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kukonda kwambiri zimene ankaphunzira. Iye ankasangalala kwambiri chifukwa choonadi chinamuthandiza kusintha zinthu zambiri. Iye anati: “Ndikamayesetsa kwambiri kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wanga m’pamene ndinkakhalanso wosangalala kwambiri.” Kenako anazindikira kuti n’zosatheka kuti akule mwauzimu uku akusakasaka chuma. (Mat. 6:24) Choncho analolera kusiya mtima wofuna kukhala katswiri wa gofu zomwe zikanathandiza kuti apeze ndalama zambiri komanso kukhala wotchuka. Iye anagula choonadi ndipo panopa akuchita upainiya. Mariya akuona kuti anasankha bwino kwambiri moti anati panopa “moyo wake ndi wabwino kwambiri.”

11. Kodi chingachitike n’chiyani ndi anzathu tikagula choonadi?

11 Anzathu. Tikayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu, kachezedwe kathu ndi achibale komanso anthu ena kamasintha. Zili choncho chifukwa cha mfundo ina imene Yesu ananena m’pemphero yakuti: “Ayeretseni ndi choonadi. Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yoh. 17:17) Mawu oti “ayeretseni” angatanthauzenso kuti “apatuleni kuti akhale apadera.” Tikayamba kuphunzira choonadi, timakhala osiyana ndi dzikoli chifukwa sititsatira zimene anthu ake amachita. Timasinthanso mfundo zimene timayendera choncho anthu sationa mmene ankationera. Moyo wathu umayendera mfundo za choonadi cha m’Baibulo. Ngakhale kuti sitifuna kuyambitsa mikangano, anzathu komanso achibale athu ena angayambe kutisala kapena kutitsutsa. Koma ife sitidabwa nazo zimenezi chifukwa Yesu ananeneratu kuti: “Adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.” (Mat. 10:36) Anatitsimikiziranso kuti tikagula choonadi madalitso ake amakhala ambiri kuposa chilichonse chimene tingasiye.​—Werengani Maliko 10:28-30.

12. Kodi n’chiyani chinachitikira Myuda wina ataphunzira choonadi?

12 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Aaron, yemwe ndi Myuda. Kuyambira ali wamng’ono, ankaphunzitsidwa kuti dzina la Mulungu si loyenera kulitchula. Koma Aaron ankafuna kuphunzira choonadi. Iye atakumana ndi a Mboni anasangalala kumva kuti tikaika zilembo zina pa zilembo zoimira dzina la Mulungu tikhoza kulitchula kuti “Yehova.” Chifukwa chosangalala anathamanga kupita kusunagoge kukauza aphunzitsi akumeneko zomwe anamvazi. Koma anadabwa ndi zimene arabiwo anachita. M’malo mosangalala, anamulavulira n’kumuthamangitsa. Achibale ake sanasangalale nayenso. Koma iye sanabwerere m’mbuyo moti ankalalikira za Yehova molimba mtima kwa moyo wake wonse. Mofanana ndi Aaron, tikamatsatira mfundo za choonadi, timalolera kuti chilichonse chichitike, kaya kunyozedwa kapena kudedwa ndi anzathu kapena achibale athu.

13, 14. Kodi munthu amafunika kusintha maganizo ndi makhalidwe ati kuti agule choonadi? Perekani chitsanzo.

13 Maganizo ndiponso makhalidwe amene sasangalatsa Mulungu. Kuti tiphunzire choonadi n’kumatsatira mfundo za m’Baibulo, tiyenera kulolera kusintha maganizo ndi makhalidwe athu. Ponena za kusintha kumeneku, Petulo analemba kuti: “Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. Koma . . . khalani oyera m’makhalidwe anu onse.” (1 Pet. 1:14, 15) Anthu ambiri a ku Korinto anali ndi makhalidwe oipa choncho munthu anafunika kusintha kwambiri moyo wake kuti agule choonadi. (1 Akor. 6:9-11) Masiku anonso, anthu ambiri amene akuphunzira choonadi amasintha makhalidwe awo. Paja Petulo anakumbutsanso Akhristu a nthawi yake kuti: “Nthawi imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”​—1 Pet. 4:3.

14 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Devynn ndi Jasmine. Anthuwa ankakhalira limodzi ndipo onse anali zidakwa. Devynn ankadziwa bwino ntchito yowerengera ndalama za bizinezi koma uchidakwa wakewu unachititsa kuti azisowa ntchito. Pomwe Jasmine anali wolusa komanso wokonda chiwawa. Tsiku lina, Jasmine ankapita kwawo ataledzera ndipo anakumana ndi amishonale a Mboni awiri. Amishonalewo anakonza zoti ayambe kuphunzira naye Baibulo kunyumba kwa Devynn. Tsiku limene anagwirizana litafika anapita koma anapeza onse ataledzera. Iwo ankaganiza kuti amishonalewo alibe nawo ntchito ndipo sangapite kunyumba kwawo kuti azikaphunzira. Koma mlungu wotsatira zinthu zinasintha kwambiri. Phunziro litangoyambika anthu awiriwa ankaphunzira Baibulo mwakhama ndipo ankayesetsa kutsatira zimene ankaphunzira. Miyezi itatu isanathe, anaganiza zosiya kumwa ndipo patapita nthawi anakalembetsa ukwati wawo. Anthu ambiri a m’mudzi umene ankakhala anaona kuti asintha kwambiri moti ena anayambanso kuphunzira Baibulo.

15. Kodi chinthu chovuta kwambiri kusintha tikamaphunzira choonadi n’chiyani? Perekani chifukwa.

15 Miyambo ndi zikhalidwe zosemphana ndi Malemba. Zimakhala zovuta kwambiri kuti munthu amene akuphunzira choonadi asiye miyambo ndi zikhalidwe zimene anazolowera. Ena amamvetsa bwinobwino zifukwa za m’Malemba zosiyira zinthuzi koma zimawavutabe chifukwa choopa achibale kapena anzawo. Nkhaniyi imavuta kwambiri ngati miyambo yake ndi yokhudza kulemekeza achibale amene anamwalira. (Deut. 14:1) Koma chitsanzo cha anthu ena pa nkhani yolimba mtima chingatithandize kuti nafenso tisinthe. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene Akhristu ena anachita ku Efeso mu nthawi ya atumwi.

16. Kodi anthu ena ku Efeso anatani kuti agule choonadi?

16 Anthu a ku Efeso ankachita kwambiri zamatsenga. Kodi Akhristu amene anali atangophunzira kumene choonadi anatani kuti asiye zamatsengazo? Baibulo limanena kuti: “Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana 50,000. Choncho mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndi kugonjetsa zopinga zambiri.” (Mac. 19:19, 20) Akhristu okhulupirikawa atachita zimenezi anadalitsidwa kwambiri.

17. (a) Kodi anthu amalolera kuchita chiyani kuti agule choonadi? (b) Kodi tidzakambirana mafunso ati munkhani yotsatira?

17 Kodi inuyo munalolera kuchita chiyani kuti mugule choonadi? Tonsefe timagwiritsa ntchito nthawi yathu kuti tifufuze maluwa a choonadi. Ena amagula choonadi pololera kusiya ntchito kapena chuma pomwe ena amalolera kutsutsidwa ndi anzawo. Ambiri amasintha maganizo ndi makhalidwe awo komanso amasiya miyambo ndi zikhalidwe zimene anazolowera. Kaya chimene tasiya n’chiyani, madalitso amene tingapeze chifukwa chophunzira choonadi ndi ambiri kuposa zomwe tasiyazo. Timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova womwe ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Tikaganizira madalitso amene timapeza chifukwa chogula choonadi, timadabwa tikamva kuti anthu ena amafuna kuchigulitsa. Koma kodi munthu angagulitse bwanji choonadi, nanga ife tingapewe bwanji kuchita zimenezi? Munkhani yotsatira tidzakambirana mayankho a mafunso amenewa.

^ ndime 8 Mayina ena asinthidwa munkhaniyi.