“Ndidzayenda M’choonadi Chanu”
“Inu Yehova, ndilangizeni za njira yanu. Ndidzayenda m’choonadi chanu.”—SAL. 86:11.
1-3. (a) Kodi tiyenera kuchiona bwanji choonadi cha m’Baibulo? Perekani chitsanzo. (Onani zithunzi zoyambirira.) (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?
MASIKU ano anthu ambiri amakonda kubweza zinthu zimene anagula. Zikuoneka kuti m’mayiko ena, anthu amatha kubweza zinthu pafupifupi 9 pa zinthu 100 zilizonse zimene agula. Ndipo pa zinthu 100 zilizonse zogulidwa kudzera pa intaneti, zinthu zoposa 30 zimatha kubwezedwa. Anthu ogula zinthuwo amazibweza chifukwa mwina apeza kuti sizikugwira ntchito mmene ankaganizira, ndi zoonongeka kapena sizinawasangalatse. Zikatero amatha kupempha kuti awapatse zina kapena angowabwezera ndalama zawo.
2 Ngakhale kuti zimatheka kubweza zinthu zimene tinagula n’kuwauza kuti atibwezere ndalama zathu, sitingakonde kubweza kapena ‘kugulitsa’ “choonadi” cha m’Baibulo chomwe ‘tinagula.’ (Werengani Miyambo 23:23; 1 Tim. 2:4) Monga tinaonera munkhani yapita ija, tinadziwa choonadi pogwiritsa ntchito nthawi yathu yambiri kuti tichiphunzire. Tinagulanso choonadi mwina pololera kusiya ntchito yapamwamba, posintha anthu ocheza nawo komanso maganizo ndi khalidwe lathu. Kapenanso tinasiya miyambo ndi zikhalidwe zosemphana ndi Malemba. Koma zimene tinalolera kusiya kuti tigule choonadi ndi zochepa poyerekezera ndi madalitso amene tinalandira.
Mat. 13:45, 46) Ifenso titadziwa choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu komanso mfundo zina zomwe tinaziphunzira m’Mawu a Mulungu, tinaona kuti ndi zamtengo wapatali. Tinalolera kusintha zinthu zambiri mwamsanga kuti tikhale m’choonadi. Ndiye tikamachiona kuti ndi chamtengo wapatali, ‘sitingachigulitse.’ Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu a Mulungu ena asiya kuona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali ndipo afika pochigulitsa. Ifeyo tisalole kuti zimenezi zitichitikire. Kuti tisonyeze kuti timaona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali komanso kuti sitingachigulitse, tiyenera kumvera malangizo a m’Baibulo akuti tipitirizebe “kuyenda m’choonadi.” (Werengani 3 Yohane 2-4.) Kuti tiziyendabe m’choonadi, tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene timaphunzira komanso kuika zinthu zokhudza choonadi pamalo oyamba. Munkhaniyi tikambirana mafunso awa: N’chifukwa chiyani ena “angagulitse” choonadi, nanga angachite bwanji zimenezi? Kodi tingatani kuti tisachite zinthu zomvetsa chisonizi? Kodi tingatani kuti tikhale ndi mtima wofuna kupitirizabe “kuyenda m’choonadi”?
3 Timaona kuti choonadi cha m’Baibulo ndi chamtengo wapatali ndipo zimenezi zimafanana ndi munthu amene Yesu anamutchula m’fanizo lake. Pofuna kusonyeza kuti choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu ndi chofunika kwambiri kwa anthu amene achipeza, Yesu anafotokoza zimene munthu wina wamalonda anachita atapeza ngale yabwino imene ankaifufuza. Ngaleyo inali yamtengo wapatali moti anapita “mwamsanga” n’kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo kuti akagule ngaleyo. (N’CHIFUKWA CHIYANI ENA ‘AMAGULITSA’ CHOONADI NDIPO ‘AMACHIGULITSA’ BWANJI?
4. N’chifukwa chiyani anthu ena ‘anagulitsa’ choonadi mu nthawi ya Yesu?
4 Mu nthawi ya Yesu, anthu ena amene poyamba anamvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa sanapitirize kuyenda m’choonadi. Mwachitsanzo, chigulu cha anthu chitadyetsedwa mozizwitsa ndi Yesu, chinamutsatira kumbali ina ya nyanja ya Galileya. Ali kumeneko, Yesu ananena zinthu zimene zinawadabwitsa kwambiri. Iye anati: “Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, mulibe moyo mwa inu.” M’malo momupempha Yesu kuti awafotokozere zimene ankatanthauza, iwo anakhumudwa ndipo anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndani angamvetsere zimenezi?” Pa chifukwa chimenechi, “ophunzira ake ambiri anamusiya ndi kubwerera ku zinthu zakumbuyo, ndipo sanayendenso naye.”—Yohane 6:53-66.
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena masiku ano sapitiriza kuyenda m’choonadi? (b) Kodi zingatheke bwanji kuti munthu asiye choonadi pang’onopang’ono?
5 N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu ena sapitirizanso kuyenda m’choonadi. Ena anakhumudwa chifukwa chakuti kafotokozedwe ka malemba ena a m’Baibulo kanasinthidwa kapena chifukwa cha zimene m’bale waudindo ananena kapena kuchita. Ena anakhumudwa chifukwa cha malangizo ochokera m’Malemba omwe anapatsidwa kapena analolera kusiya choonadi chifukwa chosemphana maganizo ndi Mkhristu mnzawo. Ndipo ena anasiya kuyenda m’choonadi chifukwa chogwirizana ndi ampatuko kapena anthu otsutsa omwe amapotoza mfundo za choonadi. Zimenezi zinapangitsa kuti ena ‘achoke’ mwadala kwa Yehova komanso mumpingo. (Aheb. 3:12-14) Anthu otere zinthu zikanawayendera bwino kwambiri akanasungabe chikhulupiriro chawo komanso kukhulupirira Yesu ngati mmene mtumwi Petulo anachitira. Yesu atafunsa atumwi ngati nawonso ankafuna kumusiya, nthawi yomweyo Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.”—Yohane 6:67-69.
6 Ena anasiya choonadi pang’onopang’ono mwinanso asakuzindikira. Munthu amene Aheb. 2:1) Mosiyana ndi munthu amene amachoka m’choonadi mwadala, munthu amene amatengeka pang’onopang’ono amachita zimenezi mosazindikira. Koma munthu akayamba kuchita zimenezi ubwenzi wake ndi Yehova umayamba kusokonekera ndipo akapanda kusamala ukhoza kutheratu. Ndiye tingatani kuti zinthu zoopsa zimenezi zisatichitikire?
amasiya choonadi pang’onopang’ono amafanana ndi bwato limene likutengeka pang’onopang’ono kupita pakatikati pa mtsinje. Baibulo limati anthu otere ‘amatengeka pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro. (KODI TINGATANI KUTI TISAGULITSE CHOONADI?
7. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kupewa kugulitsa choonadi?
7 Kuti tipitirizebe kuyenda m’choonadi, tiyenera kukhulupirira komanso kumvera mawu onse a Yehova. Tiyenera kuona kuti choonadi ndi chofunika kwambiri pa moyo wathu komanso kumachita zinthu zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mfumu Davide anapemphera kwa Yehova kuti: “Ndidzayenda m’choonadi chanu.” (Sal. 86:11) Apa tingati Davide anatsimikiza mtima kuyenda m’choonadi. Ifenso tiyenera kutsimikiza mumtima mwathu kuti tidzapitirizabe kuyenda m’choonadi cha Mulungu. Ngati titapanda kuchita zimenezi, tikhoza kuyamba kuganizira zinthu zomwe tinasiya kuti tipeze choonadi mwinanso kuyamba kulakalaka kuti tiyambirenso kuchita zinthu zomwe tinazisiyazo. Koma tiyenera kupitiriza kutsatira mfundo zonse za choonadi. Si bwino kusankha mfundo zina za choonadi zoti tizizitsatira n’kusiya zina. Paja Baibulo limati tiyenera kuyenda “m’choonadi chonse.” (Yoh. 16:13) Tiyeni tikambirane zinthu 5 zimene tinapereka kuti tigule choonadi. Zimenezi zitithandiza kuti tipewe mtima wolakalaka kuti tiyambirenso kuchita zinthu zomwe tinasiyazo.—Mat. 6:19.
8. Kodi kusagwiritsa ntchito bwino nthawi kungachititse bwanji Mkhristu kuchoka pang’onopang’ono m’choonadi? Perekani chitsanzo.
8 Nthawi yathu. Kuti tipewe kusiya choonadi pang’onopang’ono tiyenera kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu. Kupanda kusamala, nthawi yathu ikhoza kumangothera pa intaneti, pa TV kapena pa zosangalatsa zina. Zinthu zimene tatchulazi pazokha si zolakwika, koma vuto limakhalapo ngati zikutilepheretsa kupezanso nthawi yokwanira yophunzira patokha kapena yochita zinthu zina zokhudza kulambira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Emma. * Kuyambira ali wamng’ono, Emma ankakonda kukwera mahatchi. Akangopeza mpata ankapita kukakwera hatchi. Patapita nthawi, anayamba kuda nkhawa atazindikira kuti ankathera nthawi yochuluka pokwera mahatchiwo. Choncho anasintha zinthu kuti asamaike masewerawo pamalo oyamba. Analimbikitsidwanso ndi nkhani ya Cory Wells yemwe anali katswiri pa nkhani yochita masewera okwera hatchi. * Panopa Emma amasangalala kukhala ndi nthawi yambiri yochita zinthu zauzimu komanso yocheza ndi abale ake ndiponso Akhristu anzake. Ubwenzi wake ndi Yehova walimba kwambiri ndipo ali ndi mtendere mumtima podziwa kuti akugwiritsa ntchito nthawi yake mwanzeru.
9. Kodi kukonda chuma kungachititse bwanji anthu ena kuti asiye kuchita zinthu zokhudza kulambira?
9 Chuma. Kuti tipitirize kuyenda m’choonadi tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chuma. Titaphunzira choonadi tinaona kuti zinthu zauzimu ziyenera kukhala pamalo oyamba. Tinkaona kuti ndi bwino kulolera kuti tisakhale ndi zinthu zina n’cholinga choti tiziyendabe m’choonadi. Koma nthawi ikamadutsa tikhoza kumaona anzathu akugula zipangizo zamakono kapena akupeza ndalama zambiri. 2 Tim. 4:10) Kodi n’chifukwa chiyani Dema anachita zimenezi? Kaya ankakonda kwambiri zinthu zakuthupi kuposa zauzimu, kapena ankaona kuti akumanidwa zinthu zina akamayenda ndi Paulo, Baibulo silinena. Koma mfundo ndi yakuti si bwino kulola mtima wolakalaka chuma kutichititsa kusiya kukonda choonadi.
Ndiye mwina tingayambe kuganiza kuti tikumanidwa zambiri. Kenako tingayambe mtima wosakhutira ndi zinthu zofunika zomwe tili nazo moti tingalolere kusiya zinthu zokhudza kulambira n’cholinga choti tipeze ndalama kapena zinthu zinazake. Zoterezi zinachitikiranso Mkhristu wina dzina lake Dema. Mtima wokonda “zinthu za m’nthawi ino” unamuchititsa kuti asiye kutumikira limodzi ndi Paulo. (10. Kodi tiyenera kupewa chiyani kuti tipitirize kuyenda m’choonadi?
10 Anzathu. Kuti tipitirize kuyenda m’choonadi tiyenera kupewa kumangotengera zochita za anzathu. Titangophunzira kumene choonadi, kachezedwe kathu ndi anzathu komanso achibale omwe si Mboni kanasintha. Anzathu ena anazivomereza mosavuta koma ena ankatitsutsa kwambiri. (1 Pet. 4:4) N’zoona kuti timafuna kugwirizana ndi achibale athu komanso kuwakomera mtima. Koma si bwino kulolera kuphwanya mfundo za choonadi pongofuna kuwasangalatsa. Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tizigwirizana nawo. Koma malinga ndi zimene lemba la 1 Akorinto 15:33 limanena, tiyenera kugwirizana kwambiri ndi anthu amene amakonda Yehova.
11. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisakopeke ndi makhalidwe oipa?
11 Maganizo ndiponso makhalidwe amene sasangalatsa Mulungu. Anthu onse amene akuyenda m’choonadi ayenera kukhala oyera. (Yes. 35:8; werengani 1 Petulo 1:14-16.) Pamene tinkaphunzira choonadi, tonsefe tinasintha zinthu zina kuti tiziyendera mfundo za m’Baibulo. Ena anafunika kusintha kwambiri kuti zimenezi zitheke. Kaya tinasintha zambiri kapena zochepa, si bwino kugulitsa choonadi pochisinthanitsa ndi makhalidwe onyansa a m’dzikoli. Ndiye kodi tingatani kuti tisakopeke ndi makhalidwe oipa? Ndi bwino kuganizira mtengo umene Yehova analipira potithandiza kuti tikhale oyera. Pajatu anatigula ndi magazi amtengo wapatali a Mwana wake Yesu Khristu. (1 Pet. 1:18, 19) Ndiye kuti tikhalebe oyera pamaso pa Yehova, tiyenera kukumbukira nthawi zonse zoti tinagulidwa ndi nsembe ya dipo la Yesu.
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi maganizo a Yehova pa nkhani ya maholide? (b) Kodi tikambirana chiyani tsopano?
12 Miyambo ndi zikhalidwe zosemphana ndi Malemba. Achibale athu, anzathu akuntchito kapena akusukulu angafune kuti tichite nawo miyambo ina. Kodi tingapewe bwanji kuchita nawo miyambo ndi zikhalidwe zimene Mulungu amadana nazo? Chimene chingatithandize ndi kukumbukira mmene Yehova amaonera zinthuzo. Ndi bwino kuonanso nkhani za m’mabuku athu zofotokoza mmene maholide osiyanasiyana anayambira. Kukumbukira zifukwa za m’Malemba zimene zingatithandize kuti tizipewa maholidewa kumatithandiza kutsimikiza mumtima mwathu kuti tikuchita zinthu ‘zovomerezeka kwa Ambuye.’ (Aef. 5:10) Kukhulupirira Yehova ndiponso Mawu ake kumatithandiza kuti tisamaope anthu.—Miy. 29:25.
13 Nkhani yoyenda m’choonadi ilibe malire chifukwa tikuyembekezera kuchita zimenezi mpaka kalekale. Ndiye kodi tingatani kuti titsimikize mumtima mwathu zoyendabe m’choonadi? Tiyeni tikambirane njira zitatu.
ZIMENE TINGACHITE KUTI TISASIYE KUYENDA M’CHOONADI
14. (a) Kodi kupitiriza kugula choonadi kungatithandize bwanji kukhala osamala kuti tisachigulitse? (b) Kodi nzeru, malangizo komanso kumvetsa zinthu zingatithandize bwanji?
14 Choyamba, tiyenera kupitiriza kuphunzira mfundo zamtengo wapatali za m’Baibulo Miyambo 23:23 limanenanso kuti tiyenera kugula “nzeru, malangizo ndi kumvetsa zinthu.” Malinga ndi lembali, kungodziwa zinthu si kokwanira. Tiyenera kutsatira mfundo za choonadi pa moyo wathu. Kumvetsa zinthu n’kumene kungatithandize kuona kuti mfundo zonse zimene Yehova amatiuza n’zogwirizana. Pomwe nzeru zingatithandize kuchita zinthu zoyenera mogwirizana ndi zimene tikudziwa. Nthawi zina, mfundo za choonadi zimakhala malangizo otiuza zimene tiyenera kusintha. Tikalandira malangizo oterewa tiyenera kuwatsatira mwamsanga chifukwa ndi amtengo wapatali kuposa siliva.—Miy. 8:10.
komanso kuzisinkhasinkha. Tikamapeza nthawi yophunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu timakhala tikugula choonadi. Zimenezi zimathandiza kuti tiziyamikira kwambiri choonadicho komanso tikhale osamala kuti tisachigulitse. Koma kuwonjezera pa kugula choonadi, lemba la15. Kodi lamba wa choonadi amatiteteza bwanji?
15 Chachiwiri, tiyenera kutsimikiza mumtima mwathu kuti tizitsatira mfundo za choonadi tsiku lililonse. Choonadi chiyenera kukhala ngati lamba amene tamanga m’chiuno mwathu. (Aef. 6:14) Kale, lamba wa msilikali ankateteza chiuno ndi ziwalo zina zamkati. Koma kuti lambayo amuteteze bwino ankafunika kumumanga mwamphamvu. Tikutero chifukwa lamba wokhwepa sankathandiza msilikali. Ndiye kodi lamba wa choonadi amatiteteza bwanji? Tikamangirira mwamphamvu choonadi ngati lamba, chimatiteteza kuti tipewe maganizo olakwika ndipo chimatithandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Tikamayesedwa kapena kuzunzidwa, mfundo za m’Baibulo zimatithandiza kuti tichite zinthu zoyenera. Msilikali sankapita kunkhondo opanda lamba. Nafenso sitiyenera kuyerekeza ngakhale pang’ono kukhwepetsa kapena kumasuliratu lamba wathu wa choonadi. Koma tizimangirira mwamphamvu lambayu poyesetsa kutsatira mfundo za choonadi pa moyo wathu. Ntchito ina ya lamba wa msilikali inali yoti azikolekapo lupanga. Mfundo imeneyi ikutifikitsa pa njira yachitatu imene ingatithandize kuti tisasiye kuyenda m’choonadi.
16. Kodi kuphunzitsa ena choonadi kungatithandize bwanji kuti tiziyendabe m’choonadi?
16 Chachitatu, tiyenera kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira. Tikamachita zimenezi timakhala ngati tikugwira mwamphamvu lupanga la mzimu lomwe ndi “mawu a Mulungu.” (Aef. 6:17) Tonsefe tikhoza kuwonjezera luso lathu ‘pophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.’ (2 Tim. 2:15) Tikamagwiritsa ntchito Baibulo pothandiza anthu kugula choonadi n’kusiya zikhulupiriro zabodza, timakhala tikukhomerezanso mawu a Mulungu m’maganizo ndi m’mitima yathu. Tikamachita zimenezi sitidzasiya kuyenda m’choonadi.
17. N’chifukwa chiyani inuyo mumaona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali?
17 Choonadi ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova watipatsa. Chimatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova womwe ndi wamtengo wapatali kwambiri. Koma zimene Yehova wakhala akutiphunzitsazi n’zochepa tikaziyerekezera ndi zimene adzatiphunzitse tikadzalandira moyo wosatha. Choncho tiziyamikira choonadi ngati ngale yamtengo wapatali. Tiyeni tipitirize ‘kugula choonadi ndipo tisachigulitse.’ Tikatero tidzafanana ndi Davide, amene analonjeza Yehova kuti: “Ndidzayenda m’choonadi chanu.”—Sal. 86:11.
^ ndime 8 Dzina lasinthidwa.
^ ndime 8 Pitani pa JW Broadcasting pamene alemba kuti ZOCHITIKA PA MOYO WA ANTHU ENA > MFUNDO ZA M’BAIBULO ZIMASINTHA ANTHU.