Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziyendera Maganizo a Yehova

Tiziyendera Maganizo a Yehova

“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.”​—AROMA 12:2.

NYIMBO: 56, 123

1, 2. Kodi munthu akamakula mwauzimu amayamba kuchita zinthu ziti? Perekani chitsanzo.

TIYEREKEZE kuti mwana wapatsidwa mphatso ndiye makolo ake akumuuza kuti: “Nena kuti zikomo.” Mwanayo akunenadi kuti zikomo koma osati mochokera mumtima. Koma pamene akukula, akumvetsa maganizo a makolo ake ndipo amayamikira zimene ena amuchitira. Ndipo akapatsidwa chinthu amathokoza ndi mtima wonse. Apa tingati makolowo amuthandiza kuti aziyendera maganizo awo oyamikira.

2 N’chimodzimodzi ndi zimene zimachitika tikayamba kuphunzira choonadi. Timaphunzira ubwino womvera malamulo akuluakulu a Yehova. Koma tikamakula mwauzimu, timayamba kudziwa maganizo a Yehova, zimene amakonda, zimene amadana nazo komanso mmene amaonera zinthu zosiyanasiyana. Ndiye tikayamba kuona zinthu mmene iye amaonera n’kumachita zinthu mogwirizana ndi maganizo ake zimakhala kuti tayamba kuyendera maganizo a Yehova.

3. N’chifukwa chiyani zimativuta kutengera maganizo a Yehova?

3 Kutengera maganizo a Yehova kumakhala kosangalatsa koma si kophweka. Popeza si ife angwiro, nthawi zina zimativuta. Mwachitsanzo, tikhoza kuvutika kumvetsa maganizo a Yehova pa nkhani ya makhalidwe abwino, chuma, ntchito yolalikira, kugwiritsa ntchito magazi ndi nkhani zina. Ndiye kodi zikatero tiyenera kuchita chiyani? Kodi tingatani kuti tipitirize kuyendera maganizo a Yehova? Nanga kodi kuyendera maganizo a Yehova kungatithandize bwanji posankha zochita panopa komanso m’tsogolo?

TIYENERA KUTENGERA MAGANIZO A YEHOVA

4. Kodi tingatani kuti ‘tisinthe maganizo athu’?

4 Werengani Aroma 12:2. Palembali mtumwi Paulo anafotokoza zimene tingachite kuti titengere maganizo a Yehova. Munkhani yapita ija tinakambirana zimene zingatithandize kuti ‘tisamatengere nzeru za nthawi ino.’ Tinaona kuti tiyenera kupewa zinthu zimene zingasokoneze maganizo ndi mtima wathu. Komatu Paulo ananenanso kuti tiyenera ‘kusintha maganizo athu.’ Kuti tisinthe maganizo athu, tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu n’cholinga choti tizindikire maganizo a Yehova, tiwaganizire kwambiri ndipo tiyambe kuwatengera.

5. Kodi kungowerenga nkhani kumasiyana bwanji ndi kuiphunzira?

5 Kuphunzira kumatanthauza zambiri osati kungowerenga nkhani kapena kungopeza mayankho a mafunso. Tikamaphunzira tiyenera kudzifunsa kuti, Kodi nkhaniyi ikundiuza chiyani za makhalidwe a Yehova, njira zake komanso maganizo ake? Tizidzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani Mulungu amatilamula kuti tizichita zakutizakuti n’kumatiletsa kuchita zakutizakuti? Ndi bwinonso kuganizira zimene tiyenera kusintha pa moyo wathu komanso kaganizidwe kathu. N’zoona kuti sitingachite zonsezi pa nkhani iliyonse imene tikuphunzira. Koma tiyenera kupatula nthawi, mwina hafu ya nthawi yonse imene tikufuna kuphunzirayo, kuti tiganizire mwakuya zimene tawerengazo.​—Sal. 119:97; 1 Tim. 4:15.

6. Kodi chimachitika n’chiyani tikamasinkhasinkha maganizo a Yehova?

6 Tikamasinkhasinkha Mawu a Mulungu zinthu zina zodabwitsa zimachitika. Timayamba kupeza umboni wotsimikizira kuti maganizo a Yehova pa nkhani iliyonse amakhala olondola. Timayamba kuona zinthu mmene Yehova amazionera n’kumagwirizana ndi maganizo ake. Ndiyeno kaganizidwe kathu kamasintha moti pang’ono ndi pang’ono timayamba kukhala ndi maganizo a Yehova.

ZIMENE TIMAGANIZA N’ZIMENE TIMACHITA

7, 8. (a) Kodi maganizo a Yehova pa nkhani ya chuma ndi otani? (Onani zithunzi zoyambirira.) (b) Ngati timayendera maganizo ake, kodi tiziona kuti chofunika kwambiri n’chiyani?

7 Tizikumbukira kuti maganizo athu amakhudza kwambiri zimene timachita. (Maliko 7:21-23; Yak. 2:17) Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo kuti timvetse mfundoyi. Choyamba, mabuku a Uthenga Wabwino amatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani ya chuma. Yehova anasankha banja losauka kuti lilere Mwana wake. (Lev. 12:8; Luka 2:24) Yesu atabadwa, Mariya anamugoneka “modyeramo ziweto, chifukwa anasowa malo m’nyumba ya alendo.” (Luka 2:7) Yehova akanafuna akanatha kupeza malo abwino oti Mwana wake abadwiremo. Koma anaona kuti chofunika kwambiri ndi banja lokonda zinthu zauzimu limene lingasamalire bwino Mwanayo.

8 Nkhani ya kubadwa kwa Yesu ikutithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani ya chuma. Makolo ambiri amayesetsa kwambiri kuti ana awo adzakhale ndi chuma ndipo nthawi zina saganizira n’komwe za moyo wawo wauzimu. Koma Yehova amaona kuti zinthu zauzimu ndi zofunika kuposa chilichonse. Kodi inuyo mumayendera maganizo a Yehova pa nkhani imeneyi? Nanga zochita zanu zimasonyeza chiyani?​—Werengani Aheberi 13:5.

9, 10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi maganizo a Yehova pa nkhani yokhumudwitsa ena?

9 Chitsanzo china ndi maganizo a Yehova pa nkhani yokhumudwitsa anthu ena. Yesu anati: “Aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana tokhulupirirati, zingakhale bwino kwambiri kuti amumangirire chimwala champhero m’khosi mwake, ngati chimene bulu amayendetsa, ndi kumuponya m’nyanja.” (Maliko 9:42) Mawu amenewatu ndi amphamvu. Popeza Yesu anatengera Yehova ndendende, n’zosachita kufunsa kuti Yehova amanyansidwa kwambiri ndi anthu amene amakhumudwitsa otsatira a Yesu.​—Yoh. 14:9.

10 Kodi ifeyo timayenderanso maganizo a Yehova ndi Yesu pa nkhani imeneyi? Nanga zochita zathu zimasonyeza chiyani? Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti timakonda kuvala kapena kudzikongoletsa m’njira imene ikhoza kukhumudwitsa anthu ena mumpingo, kapena kuchititsa ena kuganizira zachiwerewere. Kodi tidzalolera kusiya n’cholinga choti tisakhumudwitse abale athu?​—1 Tim. 2:9, 10.

11, 12. Kodi kukhala ndi maganizo a Yehova pa nkhani ya zinthu zoipa komanso kukhala odziletsa kungatithandize bwanji kuti tipewe zoipa?

11 Chitsanzo chachitatu ndi nkhani yodana ndi zinthu zopanda chilungamo. (Yes. 61:8) Yehova amadziwa kuti uchimo umene tinatengera umachititsa kuti nthawi zina tizikhala ndi maganizo olakwika. Koma amatiuza kuti nafenso tizidana ndi zinthu zopanda chilungamo. (Werengani Salimo 97:10.) Kuganizira chifukwa chake Yehova amadana ndi zoipa kungatithandize kuti tikhale ndi maganizo ake pa nkhani imeneyi ndipo zingatilimbikitse kuti tizidana kwambiri ndi zoipazo.

12 Munthu akakhala ndi maganizo a Yehova pa nkhani imeneyi, akhoza kudziwa kuti kuchita zinazake n’kulakwa ngakhale kuti zinthuzo sizinatchulidwe mwachindunji m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, masiku ano anthu akumakonda kavinidwe kena kofananako ndi kugonana. Ena amaganiza kuti kavinidwe kameneka si koipa ngati kugonana kwenikweni. * Koma kodi zimenezi zimasonyeza kuti munthu ali ndi maganizo a Mulungu, amene amadana ndi zoipa zilizonse? Tiyeni tizipeweratu zoipa pokhala odziletsa ndipo tizidana kwambiri ndi zinthu zimene Yehova amadana nazo.​—Aroma 12:9.

TIZIGANIZIRIRATU ZIMENE TINGASANKHE M’TSOGOLO

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuoneratu maganizo a Yehova pa zinthu zimene tingadzakumane nazo m’tsogolo?

13 Tikamaphunzira tingachite bwino kuona maganizo a Yehova pa zinthu zimene zingadzatichitikire m’tsogolo. Tikamatero sitingasowe chochita ngati titakumana ndi vuto lina lofunika kuti tisankhe zochita pompopompo. (Miy. 22:3) Tiyeni tikambirane zitsanzo zina za m’Baibulo pa nkhaniyi.

14. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yosefe anachita akunyengereredwa ndi mkazi wa Potifara?

14 Chitsanzo choyamba ndi cha Yosefe yemwe anakana kugonana ndi mkazi wa Potifara. Zimene Yosefe anachita zimasonyeza kuti anaganiziratu maganizo a Yehova pa nkhani ya kukhulupirika m’banja. (Werengani Genesis 39:8, 9.) Pamene anamuyankha kuti: “Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?” anasonyeza kuti ankayendera maganizo a Yehova. Nanga bwanji ifeyo? Kodi tingatani ngati munthu wina kuntchito wayamba kutikopa? Nanga tingatani ngati munthu watitumizira zinthu zolaula pa foni? * Zinthu ngati zimenezi sizingakhale zovuta ngati tikudziwiratu maganizo a Yehova pa nkhanizi ndipo tinasankhiratu zochita.

15. Kodi tingatsanzire bwanji Aheberi atatu pa nkhani yokhalabe okhulupirika kwa Yehova?

15 Chitsanzo chachiwiri ndi cha Sadirake, Mesake ndi Abedinego. Zimene anachita komanso kulankhula atauzidwa kuti alambire fano la Mfumu Nebukadinezara zimasonyeza kuti ankadziwiratu zoyenera kuchita kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova. (Eks. 20:4, 5; Dan. 3:4-6, 12, 16-18) Ndiye tiyerekeze kuti bwana wanu akukuuzani kuti musonkhe nawo ndalama zinazake zodzagwiritsa ntchito pa chikondwerero chinachake chokhudza kulambira konyenga. Kodi mungatani? M’malo modikira kuti zidzakuchitikireni kenako muziganiza zochita, ndi bwino kuoneratu panopa maganizo a Yehova pa nkhani ngati zimenezi. Ndiyeno zikadzakuchitikirani mudzakhala ngati Aheberi atatu aja ndipo simudzasowa zochita kapena zolankhula.

Kodi munafufuza m’mabuku anthu, kulemberatu zimene mungafune komanso kukambirana ndi dokotala wanu? (Onani ndime 16)

16. Kodi kudziwiratu maganizo a Yehova kungatithandize bwanji kuti tisadzapanikizike tikadwala?

16 Kudziwiratu zochita kuti tikhale okhulupirika n’kofunikanso pa nkhani zachipatala. N’zoona kuti tonse tinatsimikiza mumtima mwathu kuti sitingalandire magazi kapena zigawo zikuluzikulu za magazi. Koma pali njira zina zimene madokotala amagwiritsira ntchito magazi zomwe aliyense ayenera kusankha yekha mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo zimene zimasonyeza maganizo a Yehova. (Mac. 15:28, 29) Nthawi yabwino kusankha zochita pa nkhani zimenezi ndi inoyo osati pamene tagonekedwa m’chipatala, tikumva ululu ndipo anthu akutipanikiza kuti tisankhe msangamsanga. Ndi bwino panopa kufufuza m’mabuku athu, kulemberatu bwinobwino zimene tingakonde komanso kulankhulana ndi dokotala wathu. *

17-19. N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana panopa? Perekani chitsanzo cha zinthu zimene tiyenera kukonzekereratu.

17 Chitsanzo chomaliza ndi cha Yesu pa nthawi imene Petulo anamuuza kuti ‘adzikomere mtima.’ Yesu ayenera kuti anali ataganizira kwambiri cholinga cha Yehova pa nkhani ya moyo wake komanso malemba okhudza moyo ndiponso imfa yake. Zimenezi zinamuthandiza kuti akhalebe wokhulupirika kwa Mulungu n’kupereka moyo wake nsembe.​—Werengani Mateyu 16:21-23.

18 Masiku ano, Yehova amafuna kuti anthu ake akhale naye pa ubwenzi wabwino komanso azigwira mwakhama ntchito yolalikira. (Mat. 6:33; 28:19, 20; Yak. 4:8) Mofanana ndi zimene zinachitikira Yesu, anthu ena omwe mwina angakhale ndi zolinga zabwino angatilimbikitse kuti tisiye kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, kodi tingatani ngati bwana wathu akufuna kutikweza udindo komanso kutiwonjezera malipiro, koma zimenezo zichititsa kuti tiziphonya zinthu zina zauzimu? Nanga ngati muli pasukulu, kodi mungatani ena atakupatsani mwayi woti muchoke kunyumba n’kukachita maphunziro owonjezera? Kodi mungafunike kupemphera, kufufuza m’mabuku athu, kukambirana ndi achibale komanso akulu kenako n’kusankha zochita? Koma kodi sizingakhale zothandiza kuoneratu maganizo a Yehova pa nkhani zimenezi panopa n’cholinga choti tiziyendera maganizo akewo? Tikatero sitingasowe chochita ngati zoterezi zitadzatichitikira ndipo sitingazionenso ngati mayesero. Zimakhala ngati uli kale ndi zolinga zako zauzimu, watsimikiza kale mumtima ndipo kwatsala n’kungochita zimene wasankha kalezo.

19 Mukhoza kuganizira zinthu zosiyanasiyana zimene zingakuchitikireni mwadzidzidzi. N’zoona kuti sitingakonzekereretu chilichonse chimene tingakumane nacho. Koma ngati timasinkhasinkha zinthu ngati zimenezi pa nthawi imene tikuphunzira patokha n’kudziwa maganizo a Yehova, zimakhala zosavuta kuzikumbukira komanso kuzitsatira pa nthawi imene takumana ndi mayesero. Choncho tiyeni tiziyesetsa kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana ndipo tiziyendera maganizo akewo. Tiziganiziranso mmene maganizo a Yehova angatithandizire posankha zoti tichite panopa komanso zoti tidzachite m’tsogolo.

TIKAMAYENDERA MAGANIZO A YEHOVA ZINTHU ZIDZATIYENDERA BWINO

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ufulu wathu m’dziko latsopano udzakhala ndi malire? (b) Kodi tingalawe bwanji chisangalalo cha m’dziko latsopano panopa?

20 Tonsefe tikuyembekezera mwachidwi dziko latsopano. Ambirife tikuyembekezera moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dziko lonse, anthu sadzakumananso ndi mavuto amene akutizunza masiku anowa. Koma ngakhale pa nthawi imeneyo anthu adzakhala ndi ufulu wosankha zochita. Anthu azidzasankha zinthu malinga ndi zimene amakonda.

21 Koma ufulu wosankhawo udzakhala ndi malire ake. Pa nkhani yoti ichi n’chabwino ichi n’choipa, anthu ofatsa m’dzikolo azidzayendera malamulo ndi maganizo a Yehova. Zimenezi zidzakhala zosangalatsa chifukwa tonse tizidzakhala mwachimwemwe komanso mwamtendere. (Sal. 37:11) Koma ngakhale panopa tikhoza kulawa chisangalalo chimenechi ngati titayambiratu kuyendera maganizo a Yehova.

^ ndime 12 Kavinidwe kamene tikunena apa ndi koti wovinayo savala kwenikweni ndipo amakhalira kasitomala pantchafu n’kumamunyekulira. Koma malinga ndi zimene zachitika, zinthu ngati zimenezi zikhoza kukhala dama ndipo pangafunike komiti yoweruza. Mkhristu amene wachita zimenezi afunika kupempha thandizo kwa akulu.​—Yak. 5:14, 15.

^ ndime 14 Masiku ano anthu ambiri amakonda kutumizirana mauthenga, zithunzi, kapena mavidiyo olaula. Malinga ndi zinthu zimene anthu akutumizirana, akhoza kukumana ndi komiti yoweruza. Nthawi zina, ana amene amatumizirana zinthu zoterezi amatha kuimbidwa mlandu ndi boma. Kuti mumve zambiri, pitani pawebusaiti ya jw.org pa nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa​—Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Mameseji ndi Zinthu Zina Zolaula?” (Onani pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA.) Mutha kuonanso nkhani yakuti “Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula” mu Galamukani! ya November 2013, tsamba 4-5.

^ ndime 16 Mabuku athu akhala akufotokoza mfundo zambiri zothandiza pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo, mungaone buku lakuti Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?, patsamba 246-249.