Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Joseph F. Rutherford ndi abale ena paulendo wawo wa ku Europe

1920​—Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

1920​—Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

CHA kumayambiriro kwa m’ma 1920, anthu a Yehova analimbikitsidwa kuti akonzekere ntchito imene inali pafupi kuyambika. Choncho mu 1920 anasankha lemba la chaka lakuti “AMBUYE ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga.”—Sal. 118:14 King James Version.

Yehova anapatsa mphamvu anthu amene ankafunitsitsa kugwira ntchito yolalikirayi. M’chaka chimenechi chiwerengero cha akopotala kapena kuti apainiya chinawonjezeka kuchoka pa 225 kufika pa 350. Kwa nthawi yoyamba ofalitsa oposa 8,000 anatumiza malipoti awo a utumiki kulikulu. Apatu Yehova anawadalitsa kwambiri.

ANASONYEZA KUDZIPEREKA NDI MTIMA WONSE

Pa 21 March, 1920, Joseph F. Rutherford yemwe ankatsogolera Ophunzira Baibulo pa nthawiyo, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali Ndi Moyo Sadzafa.” Ophunzira Baibulo anayesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti aitanire anthu ambiri kuti akamvetsere nkhaniyi. Anachita lendi holo inayake yaikulu New York City ndipo anagawa timapepala toitanira anthu tokwana 320,000.

Chilengezo cha munyuzi choitanira anthu kunkhani yakuti “Anthu Mamiliyoni Amene Ali Ndi Moyo Sadzafa”

Anthu anabwera ambiri kuposa amene ankawayembekezera. Anthu oposa 5,000 anadzadza muholoyi ndipo ena 7,000 anabwezedwa. Nsanja ya olonda inafotokoza kuti, “umenewu unali msonkhano wapadera kwambiri kuposa misonkhano yonse imene Ophunzira Baibulo a Padziko Lonse anachita.”

Ophunzira Baibulo anadziwika kwambiri chifukwa cholalikira uthenga wakuti “anthu mamiliyoni ambiri amene ali ndi moyo sadzafa.” Pa nthawiyo iwo sankamvetsa kuti uthenga wa Ufumu uyenera kulalikidwa padziko lonse. Komabe anasonyeza kudzipereka pa ntchitoyi. Ida Olmstead, yemwe anayamba kusonkhana ndi Ophunzira Baibulowa mu 1902 ananena kuti, “Tinkadziwa kuti anthu onse akuyembekezera madalitso aakulu ndipo tinayesetsa kuuza ena uthenga wabwinowu mu utumiki.”

TINAYAMBA KUSINDIKIZA TOKHA MABUKU ATHU

Pofuna kuti tikhale ndi chakudya chauzimu chokwanira, abale a ku Beteli anayamba kusindikiza okha mabuku athu ena. Iwo anagula mashini osindikizira ndi kukawaika m’nyumba ina yomwe anapanga lendi ku 35 Myrtle Avenue, Brooklyn ku New York, pafupi ndi ku Beteli.

Leo Pelle ndi Walter Kessler anayamba utumiki wa pa Beteli mu January 1920. Walter anati: “Titangofika amene ankayang’anira ntchito yosindikiza mabuku anatiyang’ana ndipo anati ‘kwangotsala ola limodzi ndi hafu kuti tikapume.’ Choncho anatiuza kuti tikanyamule makatoni a mabuku kuchoka nawo m’zipinda zapansi kupita nawo m’zipinda zam’mwamba.”

Leo anakumbukira zimene zinachitika tsiku lotsatira ndipo anati: “Ntchito yathu inali yotsuka makoma a zipinda zina za nyumbayi. Ndinali ndisanatsukepo makoma akuda ngati amenewa. Koma popeza inali ntchito ya Ambuye tinaigwirabe mosangalala.”

Mashini osindikizira amene ankawagwiritsa ntchito posindikiza Nsanja ya Olonda

Patangodutsa milungu yochepa chabe, Ophunzira Baibulo odziperekawa anayamba kusindikiza magazini a Nsanja ya Olonda. Anasindikiza magazini okwana 60,000 a Nsanja ya Olonda ya February 1, 1920. Pa nthawiyi abale anaikanso mashini ena osindikizira m’chipinda china. Ndipo anayambanso kusindikiza magazini yotchedwa The Golden Age ndipo yoyamba inali ya April 14, 1920. Zinali zoonekeratu kuti Yehova ankadalitsa ntchito ya atumiki odziperekawa.

“Inali ntchito ya Ambuye, choncho tinaigwira mosangalala”

“TIZIKHALA MWAMTENDERE”

Anthu okhulupirika a Yehova anayambanso kugwira ntchito mwakhama komanso mogwirizana. Komabe Ophunzira Baibulo ena anachoka m’gulu la Mulungu pa nthawi yovuta kuyambira chaka cha 1917 mpaka 1919. Kodi gulu linachita chiyani pofuna kuwathandiza?

Nsanja ya Olonda ya April 1, 1920, inali ndi nkhani yakuti “Tizikhala Mwamtendere.” Nkhaniyi inalimbikitsa anthu mwachikondi kuti: “Tikukhulupirira kuti . . . aliyense amene ali ndi mzimu wa Ambuye, . . . ndiwokonzeka kuiwala zinthu zakale, . . . n’kukhala limodzi ndi ena mogwirizana komanso kugwirizana ndi anthu a Mulungu n’kumagwira ntchito yake.”

Anthu ambiri anamvera malangizo a chikondi amenewa. Banja lina linalemba kuti: “Zaka za m’mbuyomu tinkalakwitsa kwambiri kumangokhala, pamene anzathu ankagwira ntchito yolalikira. . . . Tikukhulupirira kuti sitidzalolanso kusocheretsedwa.” Anthu amene anabwererawa anali ndi ntchito yambiri yoti aigwire.

KUGAWIRA BUKU LA “ZG”

Pa 21 June 1920, Ophunzira Baibulo anayamba ntchito yapadera yogawira buku la “ZG” lomwe linali buku la The Finished Mystery * koma lachikuto chofewa. Ambiri mwa mabukuwa anasungidwa pamene boma linaletsa kuti bukuli lisafalitsidwenso mu 1918.

Ofalitsa onse osati apainiya okha, anapemphedwa kuti agwire nawo ntchito yogawira mabukuwa. Anawapempha kuti: “Aliyense yemwe ndi wobatizidwa mumpingo uliwonse, amene angathe kugwira nawo ntchito imeneyi achite zimenezo mofunitsitsa. Panopa aliyense akhale ndi cholinga chakuti: ‘Ndikufunitsitsa ndigawire buku limeneli basi.” Edmund Hooper ananena kuti, kwa anthu ambiri ntchito yapaderayi inawapatsa mwayi wolalikira kunyumba ndi nyumba kwa nthawi yoyamba. Ananenanso kuti, “Tinayamba kumvetsa kuti tili ndi ntchito yayikulu kwambiri yoti tigwire kuposa mmene tinkaganizira.”

ANAYAMBIRANSO KUGWIRA NTCHITO YOLALIKIRA KU EUROPE

Popeza kuti pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse zinali zovuta kuti Ophunzira Baibulo azilankhulana ndi anzawo a m’mayiko ena, M’bale Rutherford ankafuna kuwalimbikitsa abalewa komanso kuwathandiza kuti ayambirenso ntchito yolalikira. Choncho pa 12 August 1920, M’bale Rutherford ndi anzake ena 4 anayamba ulendo wopita ku England ndi mayiko ena ambiri.

M’bale Rutherford ali ku Egypt

M’bale Rutherford atafika ku England, Ophunzira Baibulo anapanga misonkhano yachigawo itatu ndi misonkhano 12 ing’onoing’ono. Anthu pafupifupi 50,000 anafika pamisonkhanoyi. Pofotokoza mwachidule za ulendowu, Nsanja ya Olonda inanena kuti: “Abale analimbikitsidwa kwambiri. Iwo ankacheza komanso kugwira ntchito limodzi. Zimenezi zinawathandiza kuti akhale osangalala. Ku Paris, M’bale Rutherford anakambanso nkhani yakuti, “Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali Ndi Moyo Sadzafa.” Pamene nkhaniyi inkayamba, holo imene anachitira msonkhanowu inali itadzaza kwambiri. Anthu okwana 300 anapempha kuti akufuna kudziwa zambiri.

Chikwangwani choitanira anthu kunkhani imene inakambidwa mu Royal Albert Hall ku London

Milungu yotsatira abale ena anakafika ku Athens, Cairo komanso ku Jerusalem. Pofuna kuthandiza anthu achidwi m’madera amenewa, M’bale Rutherford anakhazikitsa malo olandirira mabuku m’tauni ya Ramallah kufupi ndi ku Jerusalem. Kenako anabwerera ku Europe ndipo anakhazikitsa ofesi ya nthambi ya Central Europe n’kukonza zoti mabuku azisindikizidwa kumeneko.

ANAPANGITSA KUTI ZINTHU ZOPANDA CHILUNGAMO ZIDZIWIKE

Mu September 1920, Ophunzira Baibulo anatulutsa magazini ya The Golden Age ya nambala 27. Magazini yapaderayi inafotokoza mmene Ophunzira Baibulo ankazunzidwira mu 1918. Mashini osindikizira omwe tawatchula koyambirira aja ankagwira ntchito usana ndi usiku kuti asindikize magazini oposa 4 miliyoni.

Chithunzi cha Mlongo Martin chimene chinali ndi apolisi

Anthu amene anawerenga magaziniyi anamva zokhudza zinthu zopanda chilungamo zimene zinachitikira Mlongo Emma Martin. Mlongo Martin anali mpainiya ku San Bernardino, California. Pa 17 March 1918, mlongoyu pamodzi ndi abale ena atatu, M’bale E. Hamma, E.J. Sonnenburg ndi E. A. Stevens anali pamsonkhano.

Munthu wina amene anabwera pamsonkhanopo, sanabwere n’cholinga choti adzamvetsere mfundo za m’Baibulo. Pambuyo pake munthuyo ananena kuti “Ndinapita kumsonkhanoko . . . nditachita kutumidwa ndi loya waboma. Anandituma kumsonkhanowu kuti ndikapeze umboni.” Munthuyu anapezadi “umboni” umene ankafunawo chifukwa analandira buku la The Finished Mystery. Patadutsa masiku ochepa Mlongo Martin ndi abale atatu aja anamangidwa ndipo anaimbidwa mlandu chifukwa ankagawira buku loletsedwa.

Mlongo Martin ndi abale aja anapezeka olakwa ndipo anagamulidwa kuti akakhale mundende zaka zitatu. Pa 17 May 1920 abalewa analibenso mwayi woti angachite apilo choncho anayamba kugwira ukayidi. Koma pasanapite nthawi zinthu zinasintha.

Pa 20 June 1920, M’bale Rutherford anafotokoza zimene zinachitikira abalewa pamsonkhano wina womwe unachitikira ku San Francisco. Anthu amene anapezeka pamsonkhanowu anakhudzidwa kwambiri ndi zimene zinachitikira abalewa, choncho anatumiza telegalamu kwa pulezidenti wa dziko la United States. Mutelegalamuyo analembamo kuti: “Tikuona kuti kumangidwa kwa . . . Mayi Martin . . . chifukwa chophwanya lamulo limeneli sikunachitike mwachilungamo . . . Tikuona kuti zimene apolisi anachita pogwiritsa ntchito mphamvu zawo . . . kuti amange Mayi Martin . . . ndikuwatsekera m’ndende . . . zinali zosayenera.”

Tsiku lotsatira pulezidenti Woodrow Wilson anathetsa mlandu wa Mlongo Martin, M’bale Hamm, M’bale Sonnenburg komanso M’bale Stevens ndipo abalewa anatulutsidwa m’ndende.

Pofika kumapeto kwa chaka cha 1920, Ophunzira Baibulo anaona kuti panali zinthu zambiri zosangalatsa zimene zinachitika. Kulikulu ntchito inapitiriza kuwonjezeka, ndipo kuposa kale lonse Ophunzira Baibulo anapitiriza kulalikira mwakhama kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto onse a anthu. (Mat. 24:14) Chaka chotsatira cha 1921, chinali chaka chimene tinagwiranso kwambiri ntchito yolalikira choonadi cha Ufumu.

^ ndime 18 The Finished Mystery linali voliyumu ya nambala 7 ya buku lakuti Studies in the Scriptures. Buku lachikuto chofewa lomwe linkatchedwa kuti “ZG” linasindikizidwa ngati Nsanja ya Olonda ya March 1, 1918. Chilembo cha “Z” chinkaimira Zion’s Watch Tower ndipo chilembo cha “G” chomwe ndi cha nambala 7 mu afabeti, chinkaimira voliyumu nambala 7.