Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 44

Kodi Ana Anu Akadzakula Azidzatumikira Mulungu?

Kodi Ana Anu Akadzakula Azidzatumikira Mulungu?

“Yesu anali kukulabe m’nzeru ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.”​—LUKA 2: 52.

NYIMBO NA. 134 Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi chinthu chanzeru chimene aliyense angasankhe kuchita ndi chiyani?

NTHAWI zambiri, zimene makolo amasankha kuchita zimakhudza ana awo kwa nthawi yayitali. Ngati makolo sangasankhe zinthu mwanzeru, zingabweretse mavuto kwa ana awo. Koma akasankha zinthu mwanzeru amathandiza anawo kuti akhale ndi moyo wabwino komanso osangalala. Komabe anawo paokha ayeneranso kusankha zinthu mwanzeru. Chinthu chanzeru chimene aliyense angasankhe ndi kutumikira Atate wathu wachikondi Yehova.​—Sal. 73:28.

2. Kodi Yesu komanso makolo ake anasankha bwanji zinthu mwanzeru?

2 Makolo a Yesu ankathandiza ana awo kutumikira Yehova ndipo zimene ankasankha zinasonyeza kuti ankaona kuti kutumikira Yehova ndi kofunika kwambiri pa moyo wawo. (Luka 2:40, 41, 52) Yesu nayenso ankasankha zinthu mwanzeru ndipo zimenezi zinkamuthandiza kuti azichita zimene Yehova amafuna. (Mat. 4:1-10) Yesu atakula anali munthu wokoma mtima, wokhulupirika komanso wolimba mtima. Makolo onse amene amakonda Yehova angasangalale kukhala ndi mwana ngati ameneyu.

3. Kodi munkhaniyi tiyankha mafunso ati?

3 Munkhaniyi tikambirana mafunso awa: Kodi Yehova anasankha zinthu zabwino ziti zokhudza Yesu? Kodi makolo a Chikhristu angaphunzire chiyani pa zimene makolo a Yesu anasankha? Nanga kodi Akhristu achinyamata angaphunzire chiyani pa zimene Yesu anasankha?

KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI KWA YEHOVA?

4. Kodi Yehova anasankha zinthu zabwino zotani zokhudza Mwana wake?

4 Yehova anasankhira Yesu makolo abwino kwambiri. (Mat. 1:18-23; Luka 1:26-38) Mawu a Mariya ochokera pansi pamtima amene amapezeka m’Baibulo, amasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yehova komanso Mawu ake. (Luka 1:46-55) Komanso zimene Yosefe ankachita pomvera malangizo a Yehova, zimasonyeza kuti ankakonda Mulungu ndipo ankafunitsitsa kumusangalatsa.​—Mat. 1:24.

5-6. Kodi Yehova analola kuti Mwana wake akumane ndi zinthu zotani?

5 Kumbukirani kuti Yehova sanamusankhire Yesu makolo olemera. Nsembe imene Yosefe ndi Mariya anapereka Yesu atabadwa imasonyeza kuti anali osauka. (Luka 2:24) N’kutheka kuti Yosefe ankagwirira ntchito ya ukalipentala pafupi ndi nyumba yake ku Nazareti. Banjali liyenera kuti linalibe ndalama komanso zinthu zambiri makamaka chifukwa chakuti linali banja lalikulu, lokhala ndi ana 7 kapena kuposa.​—Mat. 13:55, 56.

6 Yehova ankateteza Yesu pa zinthu zina koma sanamuteteze pa mavuto onse amene anakumana nawo. (Mat. 2:13-15) Mwachitsanzo, Yesu anali ndi achibale ake ena omwe poyamba sankamukhulupirira. Zinalitu zokhumudwitsa kwambiri kwa Yesu kuti achibale ake ena sankavomereza kuti iye anali Mesiya. (Maliko 3:21; Yoh. 7:5) Zikuonekanso kuti Yosefe anamwalira Yesu adakali wamng’ono ndipo zimenezi zinali zopweteka kwambiri kwa iye. Kumwalira kwa Yosefe kunachititsa kuti Yesu yemwe anali mwana wamkulu m’banjalo, ayambe kugwira ntchito imene bambo ake ankagwira. (Maliko 6:3) Pamene Yesu ankakula anaphunzira zimene angachite kuti azisamalira banja lawo. Iye ankafunika kugwira ntchito mwakhama kuti azipeza ndalama komanso zinthu zina zofunika. Choncho ankadziwa bwino mmene munthu amatopera pambuyo pogwira ntchito tsiku lonse.

Makolo muzithandiza ana anu kukonzekera mavuto amene angakumane nawo. Mungachite zimenezi powaphunzitsa kuti azidalira malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu (Onani ndime 7) *

7. (a) Kodi ndi mafunso ati amene angathandize anthu okwatirana kulera bwino ana awo? (b) Kodi lemba la Miyambo 2:1-6 lingathandize bwanji makolo pamene akuphunzitsa ana awo?

7 Ngati muli pabanja ndipo mumafuna mutakhala ndi ana mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndife anthu odzichepetsa komanso timakonda Yehova ndi Mawu ake? Kodi Yehova angatisankhe kuti tikhale makolo a ana omwe amawaona kuti ndi amtengo wapatali?’ (Sal. 127:3, 4) Ngati ndinu kholo mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaphunzitsa ana anga kuti aziona kufunika kogwira ntchito mwakhama?’ (Mlal. 3:12, 13) Kodi ndimayesetsa kuteteza ana anga ku zinthu zoopsa zimene angakumane nazo m’dziko la Satanali?’ (Miy. 22:3) Simungathe kuteteza ana anu ku mavuto onse amene angakumane nawo. Zimenezo n’zosatheka. Koma mungawathandize kukonzekera mavuto amene angakumane nawo popitiriza kuwaphunzitsa mwachikondi kuti azidalira malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. (Werengani Miyambo 2:1-6.) Mwachitsanzo, ngati wachibale wanu wina wasiya kutumikira Yehova, muzithandiza ana anu pogwiritsira ntchito Baibulo kuti adziwe kufunika kopitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova. (Sal. 31:23) Kapena ngati munthu wina amene mumamukonda wamwalira muzisonyeza ana anu mavesi a m’Baibulo amene angawathandize kupirira chisoni chimene ali nacho komanso kuti akhale ndi mtendere.​—2 Akor. 1:3, 4; 2 Tim. 3:16.

KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI KWA YOSEFE NDI MARIYA?

8. Kodi Yosefe ndi Mariya anatsatira malangizo ati opezeka pa Deuteronomo 6:6, 7?

8 Yosefe ndi Mariya anathandiza Yesu kuti akule ndi makhalidwe abwino amene Mulungu amasangalala nawo chifukwa ankatsatira malangizo amene Yehova anapereka kwa makolo. (Werengani Deuteronomo 6:6, 7.) Makolo a Yesu ankakonda kwambiri Yehova ndipo cholinga chawo chachikulu chinali chothandiza ana awo kuti azikondanso Yehova.

9. Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene Yosefe ndi Mariya anasankha?

9 Yosefe ndi Mariya anasankha kuti nthawi zonse azilambira Mulungu limodzi ndi ana awo. N’chifukwa chake mlungu uliwonse ankakasonkhana ku sunagoge ku Nazareti komanso chaka chilichonse ankapita kumwambo wa Pasika ku Yerusalemu. (Luka 2:41; 4:16) Pa maulendo opita ku Yerusalemuwa iwo ankapezerapo mwayi wophunzitsa Yesu ndi abale ake zinthu zimene zinachitikira anthu a Yehova m’mbuyomu. Komanso mwina ankaima kuti aone malo ena amene amatchulidwa m’Malemba. Pamene banja lawo linkakula sizinali zophweka kuti Yosefe ndi Mariya apitirize kuchita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse. Koma Mulungu anawadalitsa kwambiri chifukwa chopitiriza kuchita zimenezi. Banjali linapitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova chifukwa chakuti linkaika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba.

10. Kodi makolo a Chikhristu angaphunzire chiyani kuchokera kwa Yosefe ndi Mariya?

10 Kodi makolo oopa Mulungu angaphunzire chiyani kuchokera kwa Yosefe ndi Mariya? Chofunika kwambiri ndi choti ana anu aziona kuti mumakonda kwambiri Yehova kudzera mu zolankhula komanso zochita zanu. Muzikumbukira kuti mphatso yayikulu imene mungapatse ana anu ndi kuwathandiza kuti azikonda kwambiri Yehova. Ndipo chinthu chamtengo wapatali chimene mungawachitire ndi kuwaphunzitsa kuti nthawi zonse azipemphera, aziphunzira Mawu a Mulungu, azisonkhana komanso azilalikira. (1 Tim. 6:6) N’zoona kuti mumafunika kupezera ana anu zinthu zofunika pa moyo. (1 Tim. 5:8) Komabe muzikumbukira kuti ndalama kapena katundu sizingathandize ana anu kuti adzapulumuke dziko la Satanali likamadzawonongedwa. Kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi komwe kungawathandize kuti adzalowe m’dziko latsopano la Mulungu.​—Ezek. 7:19; 1 Tim. 4:8.

N’zosangalatsa kuti makolo a Chikhristu amasankha zochita zimene zimathandiza kuti mabanja awo akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu (Onani ndime 11) *

11. (a) Kodi malangizo a pa 1 Timoteyo 6:17-19, angathandize bwanji makolo kusankha bwino zochita pamene akulera ana awo? (b) Kodi banja lanu lingakhale ndi zolinga zotani, nanga mungapeze madalitso otani? (Onani bokosi lakuti “ Kodi Muyenera Kukhala ndi Zolinga Zotani?”)

11 N’zosangalatsa kuona kuti makolo ambiri a Chikhristu amayesetsa kuthandiza ana awo akuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Iwo nthawi zonse amalambira Mulungu limodzi ndi ana awo. Amapita kumisonkhano yonse yampingo, misonkhano ikuluikulu komanso amalalikira uthenga wabwino. Mabanja ena amapita kukalalikira m’magawo amene salalikidwa kawirikawiri. Enanso amapita kukaona malo ku Beteli kapenanso kugwira nawo ntchito zomangamanga zimene zikuchitika m’gulu la Yehova. Mabanja amene amasankha kuchita zimenezi amafunika kugwiritsa ntchito ndalama zawo komanso amakumana ndi mavuto ena. Koma Yehova amawadalitsa kwambiri chifukwa chochita zimenezi. (Werengani 1 Timoteyo 6:17-19.) Ana a m’mabanja amenewa akakula amapitirizabe kutsatira zimene makolo awo anawaphunzitsa ndipo sasiya kutumikira Yehova komanso sanong’oneza bondo. *​—Miy. 10:22.

KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI KWA YESU

12. Kodi Yesu pamene ankakula ankafunika kuchita chiyani?

12 Nthawi zonse Atate ake a Yesu amasankha bwino zochita komanso pamene anali padziko lapansi makolo ake ankasankha zinthu mwanzeru. Komabe Yesu atakula ankafunika kusankha yekha zochita. (Agal. 6:5) Mofanana ndi tonsefe, Yesu nayenso anali ndi ufulu wosankha zochita. Iye akanatha kusankha kuti azingochita zofuna zake osati zimene Mulungu amafuna. Koma m’malomwake, anasankha kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Yoh. 8:29) Kodi chitsanzo cha Yesu chingathandize bwanji achinyamata masiku ano?

Achinyamata musamakane malangizo a makolo anu (Onani ndime 13) *

13. Kodi Yesu ali wamng’ono anasankha kuchita chiyani?

13 Yesu ali mwana anasankha kuti azimvera makolo ake. Iye sanakane kumvera makolo ake poganiza kuti ankadziwa zinthu zambiri kuposa iwowo. M’malomwake, “anapitiriza kuwamvera.” (Luka 2:51) Yesu anali ndi udindo waukulu chifukwa anali mwana woyamba ndipo ankayesetsa kukwaniritsa udindo wakewo. Iye anayesetsa kuphunzira ntchito ya ukalipentala kuchokera kwa Yosefe bambo ake n’cholinga choti azipeza ndalama zothandizira banja lawo.

14. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu ankaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama?

14 Makolo ake a Yesu ayenera kuti anamufotokozera zodabwitsa zimene zinachitika kuti abadwe komanso zimene angelo ananena zokhudza iyeyo. (Luka 2:8-19, 25-38) Komabe Yesu sankangodalira zimene makolo ake ankamuuza koma nayenso ankaphunzira Malemba payekha. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu ankaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama? Tikudziwa zimenezi chifukwa iye ali mnyamata, aphunzitsi ku Yerusalemu “anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.” (Luka 2:46, 47) Ndipo ali ndi zaka 12 zokha, Yesu anali atasonyeza kale kuti Yehova ndi Atate ake.​—Luka 2:42, 43, 49.

15. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anasankha kuchita zimene Yehova amafuna?

15 Yesu atadziwa zimene Yehova ankafuna kuti achite, anasankha kuchita zimenezo. (Yoh. 6:38) Iye ankadziwa kuti anthu ambiri adzadana naye ndipo zimenezi zinkamuvutitsa maganizo, komabe anasankha kumvera Yehova. Pamene Yesu anabatizidwa mu 29 C.E, ankaona kuti chofunika kwambiri pa moyo wake n’kuchita zimene Yehova amafuna. (Aheb. 10:5-7) Ndipo ngakhale pamene ankafa pamtengo wozunzikirapo, Yesu sanasiye kuchita zimene Atate ake amafuna.​—Yoh. 19:30.

16. Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Yesu?

16 Muzimvera makolo anu. Mofanana ndi Yosefe ndi Mariya, makolo anu si angwiro. Komabe Yehova wapereka udindo kwa makolo anuwo kuti azikutetezani, kukuphunzitsani komanso kukutsogolerani. Choncho mukamamvera malangizo awo komanso kuwalemekeza, zinthu ‘zidzakuyenderani bwino.’​—Aef. 6:1-4.

17. Mogwirizana ndi Yoswa 24:15, kodi achinyamata paokha ayenera kusankha kuchita chiyani?

17 Musankhe amene mukufuna kumutumikira. Muyenera kumudziwa bwino Yehova, zimene amafuna komanso mmene mungachitire zimene amafunazo pa moyo wanu. (Aroma 12:2) Mukatero ndi pamene mungathe kusankha kutumikira Yehova, chomwe ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanu. (Werengani Yoswa 24:15; Mlal. 12:1) Mukamawerenga komanso kuphunzira Baibulo nthawi zonse, mudzapitiriza kukonda kwambiri Yehova komanso chikhulupiriro chanu chidzalimba.

18. Kodi achinyamata ayenera kusankha kuchita chiyani, nanga zotsatira zake zingakhale zotani?

18 Sankhani kuti zimene Yehova amafuna zikhale pamalo oyamba m’moyo wanu. Dziko la Satanali limalonjeza kuti achinyamata akamagwiritsa ntchito luso lawo pochita zinthu zodzipindulitsa okha angakhale osangalala. Koma zoona n’zakuti anthu amene amangokhalira kufunafuna chuma amadzibweretsera “zopweteka zambiri pathupi lawo.” (1 Tim. 6:9, 10) Komabe mukamvera Yehova komanso kusankha kuti zimene amafuna zikhale pamalo oyamba m’moyo wanu, zinthu zidzakuyenderani bwino ndipo ‘mudzachita zinthu mwanzeru.’​—Yos. 1:8.

KODI MUSANKHA KUCHITA CHIYANI?

19. Kodi makolo ayenera kukumbukira chiyani?

19 Makolo, yesetsani kuthandiza ana anu kuti azitumikira Yehova. Muzimudalira ndipo iye adzakuthandizani kuti muzisankha zochita mwanzeru. (Miy. 3:5, 6) Muzikumbukira kuti ana anu amatengera kwambiri zimene mumachita kuposa zimene mumalankhula. Choncho muzisankha zinthu zimene zingathandize kuti ana anu azisangalatsa Yehova.

20. Kodi achinyamata angapeze madalitso otani akasankha kutumikira Yehova?

20 Achinyamata, makolo anu angakuthandizeni kuti muzisankha zochita mwanzeru pa moyo wanu. Koma ndi udindo wanu kusankha kusangalatsa Mulungu. Choncho muzitsanzira Yesu ndipo musankhe kutumikira Atate anu akumwamba womwe ndi achikondi. Mukatero mudzakhala ndi moyo wopindulitsa komanso wosangalatsa panopa. (1 Tim. 4:16) Ndipo m’tsogolo mudzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

NYIMBO NA. 133 Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata

^ ndime 5 Makolo a Chikhristu amafuna kuti ana awo akadzakula azidzasangalala kutumikira Yehova. Kodi makolo angasankhe kuchita chiyani kuti athandize ana awo kutumikira Yehova? Nanga achinyamata angachite chiyani kuti zinthu ziwayendere bwino pa moyo wawo? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa.

^ ndime 11 Onani bokosi lakuti “Makolo Anga ndi Anthu Abwino Kwambiri” mu Galamukani! ya October 2011 tsamba 20, komanso nkhani yakuti “Kalata Yapadera Yopita Kwa Makolo Awo” mu Galamukani! ya March 8, 1999 tsamba 25.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mariya anathandiza Yesu ali wamng’ono kuti azikonda kwambiri Yehova. Masiku anonso amayi angathandize ana awo kuti azikonda Yehova.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Yosefe ankakonda kupita kusunagoge ndi banja lake lonse. Masiku anonso abambo aziona kuti n’kofunika kupita kumisonkhano ndi banja lawo lonse.

^ ndime 69 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Yesu anaphunzira ntchito kuchokera kwa bambo ake. Masiku anonso achinyamata angaphunzire ntchito kuchokera kwa bambo awo.