Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 41

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1

“Zikuonekeratu kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu yolembedwa ndi ifeyo kudzera mu utumiki wathu.”​—2 AKOR. 3:3.

NYIMBO NA. 78 “Kuphunzitsa Mawu a Mulungu”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Anthu onse mumpingo amasangalala kwambiri akaona wophunzira Baibulo amene amamukonda akubatizidwa. (Onani ndime 1)

1. Kodi lemba la 2 Akorinto 3:1-3, limatithandiza bwanji kuti tiziyamikira mwayi umene tili nawo wophunzira Baibulo ndi anthu mpaka kufika pobatizidwa? (Onani chithunzi chapachikuto.)

KODI mumamva bwanji mukaona wophunzira Baibulo wa m’gawo la mpingo wanu akubatizidwa? Kunena zoona, mumasangalala kwambiri. (Mat. 28:19) Ndipo zikakhala kuti ndi inuyo amene mumaphunzira naye Baibulo mumasangalaladi kwambiri. (1 Ates. 2:19, 20) Ophunzira Baibulo amene angobatizidwa kumene amakhala ngati ‘makalata ochitira umboni,’ osati kwa anthu amene amaphunzira nawo okha komanso kwa mpingo wonse.​—Werengani. 2 Akorinto 3:1-3.

2. (a) Kodi ndi funso lofunika liti limene tiyenera kuliganizira, nanga n’chifukwa chiyani? (b) Kodi phunziro la Baibulo n’chiyani? (Onani mawu a m’munsi.)

2 N’zosangalatsa kuona kuti m’zaka 4 zapitazi, mwezi uliwonse timachititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 10,000,000 * padziko lonse ndipo m’zaka zimenezi anthu oposa 280,000 ankabatizidwa chaka chilichonse kukhala a Mboni za Yehova komanso ophunzira a Yesu Khristu. Ndiye kodi tingatani kuti tithandize anthu mamiliyoni amenewa omwe timaphunzira nawo Baibulo kuti abatizidwe? Yehova moleza mtima akuperekabe mwayi kwa anthu kuti akhale ophunzira a Khristu. Panopa nthawi yatha, choncho tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tithandize anthu amenewa kuti abatizidwe mwamsanga.​—1 Akor. 7:29a; 1 Pet. 4:7.

3. Kodi tikambirana chiyani pa nkhani yochititsa maphunziro a Baibulo?

3 Popeza ntchito yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ndi yofunika kwambiri panopa, Bungwe Lolamulira linafunsa maofesi a nthambi kuti afotokoze zimene tingachite kuti tizithandiza anthu ambiri amene timaphunzira nawo Baibulo kuti abatizidwe. Munkhaniyi komanso yotsatira, tiona zimene tingaphunzire kuchokera kwa apainiya, amishonale komanso oyang’anira madera amene akhala akugwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali. * (Miy. 11:14; 15:22) Iwo akufotokoza zimene mphunzitsi komanso wophunzira ayenera kuchita kuti phunziro la Baibulo likhale lothandiza kwa wophunzirayo. Munkhaniyi, tikambirana zinthu 5 zimene wophunzira aliyense ayenera kuchita kuti asinthe n’kufika pobatizidwa.

MUZIPHUNZIRA NAWO MLUNGU ULIWONSE

Mungapemphe wophunzira wanu kuti ngati n’kotheka muziphunzira Baibulo mutakhala pansi (Onani ndime 4-6)

4. Kodi tiyenera kudziwa chiyani pa nkhani ya maphunziro a Baibulo achidule?

4 Abale ndi alongo ambiri amachititsa maphunziro a Baibulo choimirira pakhomo la munthu. Ngakhale kuti imeneyi ndi njira yabwino yothandiza munthu kuti ayambe kukonda zimene akuphunzira m’Baibulo, nthawi zambiri timangophunzira mwachidule ndi munthuyo ndiponso mwina zingakhale zovuta kuti tiziphunzira naye mlungu uliwonse. Pofuna kuthandiza anthu oterewa, abale ndi alongo ena amafunsa anthuwo kuti awapatse nambala yafoni n’cholinga choti akambirane mfundo inayake ya m’Baibulo lisanafike tsiku loti akumanenso. Iwo amachita zimenezi kwa miyezi ndithu asanayambe kuphunzira ndi munthuyo mokwanira. Komabe, kodi wophunzira wotereyu angafike podzipereka ndi kubatizidwa ngati sakupeza nthawi yokwanira yophunzira Mawu a Mulungu? Ayi.

5. Mogwirizana ndi Luka 14:27-33, kodi Yesu anafotokoza malangizo otani amene tingagwiritse ntchito pothandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo?

5 Pa nthawi ina Yesu anafotokoza fanizo losonyeza zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale wophunzira wake. Iye anafotokoza za munthu amene akufuna kumanga nsanja komanso za mfumu imene ikufuna kupita kunkhondo. Yesu ananena kuti munthuyo amafunika kuyamba “wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge” kuti aone ngati angamalize kumanga nsanjayo. Komanso mfumuyo iyenera kuyamba “yakhala pansi ndi kuganiza mofatsa” kuti ione ngati asilikali ake ali okonzeka kumenya nkhondoyo. (Werengani Luka 14:27-33.) Mofanana ndi zimenezi, Yesu ankadziwa kuti munthu amene akufuna kukhala wophunzira wake amafunika kufufuza mosamala kuti adziwe zimene wotsatira wa Yesu amayenera kuchita. Choncho tiyenera kumalimbikitsa anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti azipeza nthawi yoti tiziphunzira nawo mlungu uliwonse. Ndiye kodi tingachite bwanji zimenezi?

6. Kodi tingachite chiyani kuti tiziphunzira mokwanira ndi anthu amene timaphunzira nawo Baibulo?

6 Mungayambe ndi kuwonjezera nthawi imene mumaphunzira choimirira ndi anthu pamakomo awo. Mwina m’malo mongokambirana nawo vesi limodzi, mungathe kukambirana nawo mavesi awiri paulendo uliwonse. Anthuwo akazolowera kuphunzira kwa nthawi yotalikirapo, mungawapemphe ngati mungapitirize kuphunzirako mutakhala pansi pamalo enaake. Zimene angayankhe zingakuthandizeni kudziwa ngati amaona kuti kuphunzira Baibuloko n’kofunika. Ndiyeno kuti aphunzire mwachangu, mungawapemphe ngati angakonde kuti muziphunzira naye kawiri pamlungu. Komabe pali zinanso zimene mungachite kuposa kungophunzira nawo kamodzi kapena kawiri pamlungu.

MUZIKONZEKERA MUSANAPITE KUKAPHUNZIRA NDI MUNTHU

Muzikonzekera bwino musanakaphunzire ndi wophunzira wanu ndipo muzimusonyeza mmene angakonzekerere (Onani ndime 7-9)

7. Kodi mphunzitsi angakonzekere bwanji asanapite kukachititsa phunziro la Baibulo lililonse?

7 Monga mphunzitsi, muyenera kukonzekera bwino musanapite kukaphunzira ndi munthu Baibulo. Mungayambe ndi kuwerenga ndime zimene mwakonza kuti mukaphunzire komanso kuwerenga malemba amene ali mundimezo. Muyeneranso kumvetsa bwino mfundo zazikulu za nkhaniyo. Muziganizira mutu wa nkhaniyo, timitu ting’onoting’ono, mafunso, malemba ofunika kuwerenga, zithunzi komanso mavidiyo amene akufotokoza bwino nkhaniyo. Kenako muziganiziranso wophunzira Baibulo wanuyo, n’kuona mmene mungamufotokozere mfundozo mosavuta ndi momveka bwino kuti athe kuzimvetsa komanso kuzigwiritsa ntchito pa moyo wake.​—Neh. 8:8; Miy. 15:28a.

8. Kodi mawu a mtumwi Paulo a pa Akolose 1:9, 10, akutiphunzitsa chiyani pa nkhani yopempherera amene timaphunzira nawo Baibulo?

8 Mukamakonzekera muzipemphera kwa Yehova ndipo m’pempherolo muzitchula wophunzira wanuyo komanso zosowa zake. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuti muziphunzitsa mfundo za m’Baibulo m’njira yakuti zimufike munthuyo pamtima. (Werengani Akolose 1:9, 10.) Muzidzifunsa kuti muone ngati pali zinazake zimene zingakhale zovuta kuti wophunzirayo azimvetse kapena kuzivomereza. Muzikumbukira kuti cholinga chanu n’choti mumuthandize mpaka afike pobatizidwa.

9. Kodi mphunzitsi angathandize bwanji wophunzira wake kukonzekera? Fotokozani.

9 Tikukhulupirira kuti kuphunzira Baibulo ndi munthu nthawi zonse, kungamuthandize kuti aziyamikira zimene Yehova ndi Yesu anachita ndipo angafune kuti aphunzire zambiri. (Mat. 5:3, 6) Kuti apindule mokwanira, wophunzira ayenera kumaikirapo mtima pa zimene akuphunzira. Kuti zimenezi zitheke muzimufotokozera kufunika koti azikonzekera phunziro lililonse. Angakonzekere powerenga ndime zimene tidzaphunzire naye n’kumaganizira mmene angagwiritsire ntchito mfundozo pa moyo wake. Ndiye kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuti azikonzekera? Mungakonzekere naye limodzi kuti mumusonyeze mmene angamakonzekerere. * Muzimufotokozera mmene angapezere mayankho a mafunso mosavuta ndiponso muzimusonyeza mmene angadulire mzere kunsi kwa mawu amene angamuthandize kukumbukira mayankhowo. Mukatero, muzimupempha kuti ayankhe m’mawu akeake. Akachita zimenezi, mungadziwe kuti akumvetsa zimene akuphunzira. Koma pali zinanso zimene muyenera kulimbikitsa wophunzira wanu kuti azichita.

MUZIWAPHUNZITSA KUTI AZILANKHULANA NDI YEHOVA TSIKU LILILONSE

Muziphunzitsa wophunzira wanu mmene angalankhulire ndi Yehova (Onani ndime 10-11)

10. N’chifukwa chiyani kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku n’kofunika, nanga ophunzira angatani kuti azipindula kwambiri akamawerenga Baibulo?

10 Kuwonjezera pa kuphunzira Baibulo ndi mphunzitsi wawo mlungu uliwonse, ophunzira Baibulo angamapindulenso ngati atamachita zinthu zina paokha tsiku lililonse. Ayenera kumalankhulana ndi Yehova. Kodi angachite bwanji zimenezi? Angachite zimenezi akamamvetsera komanso kulankhula ndi Yehova. Angamvetsere kwa Mulungu, akamawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. (Yos. 1:8; Sal. 1:1-3) Mungawasonyeze mmene angagwiritsire ntchito “Ndandanda Yowerengera Baibulo” yomwe ikupezeka pa jw.org. * Kuti muwathandize kuti azipindula kwambiri ndi kuwerenga Baibulo, muziwalimbikitsa kuti aziganizira mozama zimene akuphunzira ponena za Yehova komanso mmene angazigwiritsire ntchito pa moyo wawo.​—Mac. 17:11; Yak. 1:25.

11. Kodi wophunzira wathu angaphunzire bwanji kupemphera, nanga n’chifukwa chiyani n’kofunika kuti azipemphera pafupipafupi?

11 Muzilimbikitsa wophunzira wanu kuti azilankhula ndi Yehova popemphera tsiku lililonse. Muzipemphera mochokera pansi pamtima ndi wophunzira wanu musanayambe komanso mukamaliza kuphunzira ndipo muzimutchula m’mapempherowo. Wophunzirayo angaphunzire kupemphera kuchokera mumtima akamamvetsera mmene inuyo mumapempherera ndipo nayenso akhoza kumapemphera kwa Yehova Mulungu m’dzina la Yesu Khristu. (Mat. 6:9; Yoh. 15:16) Wophunzira Baibulo akamawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, komwe ndi (kumvetsera kwa Yehova) komanso kupemphera komwe ndi (kulankhula ndi Yehova) adzakhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Mulungu. (Yak. 4:8) Iye akamachita zimenezi tsiku lililonse zingamuthandize kuti adzipereke kwa Yehova ndi kubatizidwa. Koma kodi chinanso n’chiyani chomwe chingamuthandize?

MUZIWATHANDIZA KUTI AKHALE PA UBWENZI NDI YEHOVA

12. Kodi mphunzitsi angathandize bwanji wophunzira wake kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova?

12 Tiziyesetsa kuti zimene wophunzira wathu akuphunzira m’Baibulo zizimufika pamtima. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa zimene akuphunzirazo zikamamufika pamtima angamazigwiritse ntchito pa moyo wake. Yesu ankaphunzitsa anthu zinthu zambiri ndipo anthuwo ankakonda kumvetsera zimene ankawaphunzitsa. Koma anthu ankamutsatira chifukwa zomwe ankaphunzitsa zinkawafikanso pamtima. (Luka 24:15, 27, 32) Wophunzira wanu ayenera kumaona kuti Yehova ndi weniweni ndipo angathe kukhala naye pa ubwenzi. Azimuona ngati Atate wake, Mulungu wake komanso mnzake. (Sal. 25:4, 5) Kuti zimenezi zitheke, tikamaphunzira naye tizimuthandiza kudziwa makhalidwe abwino a Mulungu wathu. (Eks. 34:5, 6; 1 Pet. 5:6, 7) Kaya tikuphunzira mutu wanji, tizionetsetsa kuti tikuthandiza wophunzirayo kudziwa bwino makhalidwe a Yehova. Muzimuthandiza kudziwa kuti Yehova ali ndi makhalidwe abwino monga chikondi, kukoma mtima komanso chifundo. Yesu ananena kuti “lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba” ndi loti “uzikonda Yehova Mulungu wako.” (Mat. 22:37, 38) Choncho muziyesetsa kuthandiza wophunzira wanu kuti azikonda kwambiri Yehova.

13. Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kudziwa makhalidwe abwino a Yehova?

13 Nthawi zonse mukamakambirana ndi wophunzira wanu, muzimufotokozera zimene zimakuchititsani kuti muzikonda Yehova. Zimenezi zingamuthandize kuzindikira kuti nayenso akufunika kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. (Sal. 73:28) Mwachitsanzo, kodi pali chiganizo chinachake m’buku limene mukuphunzira kapena lemba lomwe limafotokoza khalidwe linalake la Yehova monga chikondi, nzeru, chilungamo kapena mphamvu, limene limakusangalatsani kwambiri? Muzimufotokozera zimenezo wophunzirayo ndipo muzimuuza kuti chimenechi ndi chimodzi mwa zifukwa zimene zimakuchititsani kuti muzikonda Atate anu akumwamba. Koma pali chinanso chimene wophunzira Baibulo aliyense ayenera kuchita kuti afike pobatizidwa.

MUZIWALIMBIKITSA KUTI AZIFIKA KUMISONKHANO

Muzilimbikitsa wophunzira wanu kuyamba kufika kumisonkhano mukangoyamba kuphunzira naye (Onani ndime 14-15)

14. Kodi lemba la Aheberi 10:24, 25 limatiuza chiyani pa nkhani ya misonkhano, zomwe zingathandize wophunzira Baibulo kuti afike pobatizidwa?

14 Tonsefe timafuna ophunzira athu atabatizidwa. Kuti zimenezi zitheke tiziwalimbikitsa kuti azifika pamisonkhano yampingo nthawi zonse. Abale ndi alongo amene agwira ntchito yophunzitsa ena kwa nthawi yaitali amanena kuti ophunzira amene amafika pamisonkhano akangoyamba kuphunzira ndi omwe amabatizidwa mwamsanga. (Sal. 111:1) Abale ndi alongo ena amafotokozera ophunzira awo kuti akapita kumisonkhano, angakamve zinthu zambiri zimene sangaziphunzire paphunziro la Baibulo. Werengani Aheberi 10:24, 25 ndi wophunzira wanu ndipo mufotokozereni kufunika koti azifika pamisonkhano. Muonetseni vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? * Muzithandiza wophunzira wanu kuti aziona kuti kufika pamisonkhano mlungu uliwonse ndi kofunika kwambiri pa moyo wake.

15. Kodi tingalimbikitse bwanji wophunzira kuti azifika pamisonkhano nthawi zonse?

15 Kodi muyenera kuchita chiyani ngati wophunzira wanu sanayambe wafika pamisonkhano yathu kapena amafika mwa apo ndi apo? Mungachite bwino kumufotokozera zinthu zosangalatsa zimene mwaphunzira kumisonkhano yaposachedwapa. Zimenezi zingamuthandize kuti ayambe kufika pamisonkhano kusiyana ndi kungomuitanira kuti abwere kumisonkhano. Mungachite bwino kumupatsa Nsanja ya Olonda kapena Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu zimene zikuphunziridwa pamisonkhano. Muzimusonyeza zimene tikaphunzire mlungu wotsatira ndipo muzimufunsa kuti anene mbali zimene akuona kuti ndi zosangalatsa kwambiri. Zimene wophunzirayo angamve ndi kuona akafika koyamba pamisonkhano yathu zidzakhala zabwino kwambiri kuposa zimene anamva ndi kuona kumisonkhano ya zipembedzo zina. (1 Akor. 14:24, 25) Komanso adzakumana ndi abale ndi alongo achitsanzo chabwino chimene ayenera kutsanzira ndiponso omwe angamuthandize kuti afike pobatizidwa.

16. Kodi tingatani kuti tizithandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti afike pobatizidwa, nanga tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

16 Kodi tingatani kuti tizithandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti afike pobatizidwa? Tingathandize wophunzira aliyense kuti aziona kufunika kophunzira, pomulimbikitsa kuti tiziphunzira naye mlungu uliwonse komanso kuti azikonzekera phunziro lililonse. Tiyeneranso kumulimbikitsa kuti azilankhulana ndi Yehova tsiku lililonse komanso kuti akhale naye pa ubwenzi. Tizilimbikitsanso ophunzira kuti azipezeka pamisonkhano yampingo. (Onani bokosi lakuti  “Zimene Ophunzira Angachite Kuti Abatizidwe.”) Komabe, munkhani yotsatira tidzakambirana zinthu zinanso 5 zimene mphunzitsi angachite pothandiza wophunzira wake kuti afike pobatizidwa.

NYIMBO NA. 76 Kodi Mumamva Bwanji?

^ ndime 5 Kuphunzitsa kumatanthauza kuthandiza munthu kuti ayambe “kuganiza komanso kuchita zinthu m’njira yatsopano kapena kuti mosiyana ndi mmene amachitira poyamba.” Lemba lathu lachaka cha 2020, la Mateyu 28:19, limatikumbutsa kufunika kophunzira Baibulo ndi anthu n’kuwathandiza kuti afike pobatizidwa n’kukhala ophunzira a Yesu Khristu. Munkhaniyi komanso yotsatira, tikambirana zimene tingachite kuti tizigwira bwino ntchito yofunika kwambiri imeneyi.

^ ndime 2 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Ngati nthawi ndi nthawi mumakambirana ndi munthu mfundo za m’Baibulo pogwiritsa ntchito buku linalake, ndiye kuti mukuchititsa phunziro la Baibulo. Muyenera kuwerengera phunzirolo ngati mwaphunzira maulendo awiri kuchokera pamene munamusonyeza mmene timaphunzirira ndiponso ngati mukuona kuti phunzirolo likhoza kupitirira.

^ ndime 3 Munkhanizi mulinso mfundo zothandiza zochokera munkhani zakuti “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo,” zimene zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 2004 mpaka May 2005.

^ ndime 9 Onerani vidiyo ya 4 minitsi yakuti Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azikonzekera. Pa JW Library®, pitani pamene alemba kuti MEDIA > OUR MEETINGS AND MINISTRY > IMPROVING OUR SKILLS.

^ ndime 10 Pitani pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ZOKUTHANDIZANI POPHUNZIRA BAIBULO.

^ ndime 14 Pa JW Library®, pitani pamene alemba kuti MEDIA > OUR MEETINGS AND MINISTRY > TOOLS FOR THE MINISTRY.