Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 43

Yehova Akutsogolera Gulu Lake

Yehova Akutsogolera Gulu Lake

“‘Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,’ watero Yehova wa makamu.”​—ZEK. 4:6.

NYIMBO NA. 40 Kodi Ndife a Ndani?

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Akhristu obatizidwa ayenera kupitiriza kuchita chiyani?

KODI ndinu obatizidwa? Ngati ndi choncho munasonyeza poyera kuti mumakhulupirira Yehova komanso kuti mukufunitsitsa kumutumikira limodzi ndi gulu lake. * Komabe muyenera kupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chanu mwa Yehova. Muyeneranso kupitiriza kukhulupirira kuti Yehova akugwiritsa ntchito gulu lake masiku ano.

2-3. Kodi Yehova amatsogolera bwanji gulu lake masiku ano? Perekani zitsanzo.

2 Masiku ano Yehova amatsogolera gulu lake m’njira imene imasonyeza makhalidwe ake, cholinga chake komanso mfundo zake. Tiyeni tikambirane makhalidwe atatu a Yehova amene timawaona m’gulu lake.

3 Choyamba, “Mulungu alibe tsankho.” (Mac. 10:34) Chikondi ndi chimene chinapangitsa Yehova kuti apereke mwana wake kuti akhale “dipo . . . m’malo mwa onse.” (1 Tim. 2:6; Yoh. 3:16) Yehova amagwiritsa ntchito anthu ake polalikira uthenga wabwino kwa anthu onse amene angamvetsere. Zimenezi zimathandiza anthu ambiri kuti apindule ndi dipo la Yesu n’kudzapulumuka. Chachiwiri, Yehova ndi Mulungu wadongosolo komanso wamtendere. (1 Akor. 14:33, 40) Choncho tingayembekezere kuti anthu amene amamutumikira azimutumikira mwadongosolo komanso mwamtendere. Chachitatu, Yehova ndi “Mlangizi Wamkulu.” (Yes. 30:20, 21) N’chifukwa chake gulu lake limayesetsa kuphunzitsa Mawu ake mumpingo komanso mu utumiki. Kodi Akhristu a mumpingo woyambirira anatsanzira bwanji makhalidwe a Yehova atatu amenewa? Nanga anthu a Yehova masiku ano amasonyeza bwanji makhalidwewa? Kodi mzimu woyera ungakuthandizeni bwanji pamene mukutumikira limodzi ndi gulu la Yehova masiku ano?

MULUNGU ALIBE TSANKHO

4. Mogwirizana ndi Machitidwe 1:8, kodi Yesu analamula otsatira ake kuchita chiyani, nanga ankayembekezera kulandira thandizo lotani?

4 Munthawi ya atumwi. Uthenga umene Yesu ankalalikira unkapereka chiyembekezo kwa anthu onse. (Luka 4:43) Iye analamula otsatira ake kuti apitirize kugwira ntchito imene anayambitsa yochitira umboni “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Werengani Machitidwe 1:8.) N’zoona kuti iwo sakanakwanitsa kugwira ntchito imeneyi ndi mphamvu zawo zokha. Ankafunika mzimu woyera kapena kuti “mthandizi” amene Yesu anawalonjeza.​—Yoh. 14:26; Zek. 4:6.

5-6. Kodi mzimu woyera unathandiza bwanji otsatira a Yesu?

5 Otsatira a Yesu analandira mzimu woyera pa Pentekosite mu 33 C.E. Mzimuwo unawathandiza ndipo nthawi yomweyo anayamba kugwira ntchito yolalikira. M’kanthawi kochepa anthu ambiri anamva uthenga wabwino. (Mac. 2:41; 4:4) Pamene anthu anayamba kuwazunza ophunzirawo sanachite mantha n’kusiya kulalikira, m’malo mwake anapempha Mulungu kuti awathandize. Iwo anapemphera kuti: “Lolani kuti akapolo anu apitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.” Kenako iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo “anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.”​—Mac. 4:18-20, 29, 31.

6 Ophunzira a Yesu anakumananso ndi mavuto ena. Mwachitsanzo, iwo anali ndi mipukutu yochepa. Komanso analibe zinthu zina ndi mabuku owathandiza kumvetsa Baibulo ngati zilili masiku ano. Ophunzirawo ankafunika kulalikira kwa anthu ambiri amene ankalankhula zinenero zosiyanasiyana. Ngakhale kuti panali mavuto amenewa iwo anachita zinthu zosayembekezereka, m’zaka zochepa anali atalalikira uthenga wabwino “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.”​—Akol. 1:6, 23.

7. Zaka zoposa 100 zapitazo, kodi atumiki a Yehova anadziwa bwanji zimene Mulungu ankafuna kuti achite, nanga anachita chiyani?

7 M’masiku athu ano. Yehova akupitirizabe kutsogolera komanso kupereka mphamvu kwa anthu ake. Njira yaikulu imene amagwiritsa ntchito potsogolera anthu ndi Baibulo, lomwe linauziridwa ndi mzimu woyera. M’Baibulo timapezamo nkhani yonena za utumiki wa Yesu komanso lamulo limene anapereka kwa otsatira ake, loti apitirize kugwira ntchito imene anayambitsa. (Mat. 28:19, 20) M’mbuyomu magazini ya July 1881, inanena kuti: “Yehova sanatisankhe kapena kutidzoza n’cholinga choti anthu ena azitilemekeza kapena kuti tikhale olemera. Koma anafuna kuti tizigwiritsa ntchito chilichonse chimene tingakhale nacho polalikira uthenga wabwino.” Kabuku kamutu wakuti Kwa Amene Anapatsidwa Ntchitoyi komwe kanatulutsidwa mu 1919, kananena kuti: “Ntchitoyi ikuoneka kuti ndi yayikulu kwambiri, komabe mwiniwake ndi Ambuye ndipo atithandiza kuti tiikwanitse.” Mofanana ndi Akhristu oyambirira, abalewa anali olimba mtima ndipo ankagwira ntchito mwakhama chifukwa ankakhulupirira kuti mzimu woyera uwathandiza kuti alalikire kwa anthu amitundu yonse. Masiku anonso timakhulupirira kuti mzimu woyera umatithandiza.

Gulu la Yehova likugwiritsa ntchito zinthu zabwino kwambiri pofalitsa uthenga wabwino (Onani ndime 8-9)

8-9. Kodi gulu la Yehova lakhala likugwiritsa ntchito njira ziti polalikira uthenga wabwino?

8 Gulu la Yehova lakhala likugwiritsa ntchito zinthu zabwino kwambiri polalikira uthenga wabwino. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo mabuku, “Sewero la Pakanema,” magalamafoni, magalimoto okhala ndi zokuzira mawu, mawailesi ndiponso chaposachedwapa gululi layamba kugwiritsa ntchito makompyuta komanso intaneti. Gulu la Mulungu lakhalanso likumasulira mabuku ndi zinthu zina m’zilankhulo zambiri kuposa kale. N’chifukwa chiyani gululi lakhala likuchita zonsezi? Gululi lakhala likuchita zimenezi n’cholinga choti anthu amitundu yonse amve uthenga wabwino m’chilankhulo chawo. Yehova ndi Mulungu wopanda tsankho iye ananeneratu kuti uthenga wabwino udzalalikidwa ku “fuko lililonse chinenero chilichonse ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6, 7) Iye amafuna kuti munthu aliyense akhale ndi mwayi womva uthenga wa Ufumu.

9 Nanga bwanji za anthu amene sitingathe kuwalalikira kunyumba zawo mwina chifukwa chakuti amakhala kunyumba zokhala ndi alonda komanso mipanda? Pofuna kuthandiza anthu amenewa, gulu la Yehova linayamba kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira m’malo opezeka anthu ambiri. Mwachitsanzo, mu 2001 Bungwe Lolamulira linavomereza kuti abale a ku France ayambe kugwiritsa ntchito timashelefu ndi matebulo polalikira. Ndipo kenako abale am’mayiko ena anayambanso kugwiritsa ntchito njira imeneyi. Zotsatira zake zinali zabwino kwambiri. Mu 2011 ku New York City anayamba kugwiritsa ntchito njira yatsopano polalikira m’madera amene kumapezeka anthu ambiri. M’chaka choyamba anagawira mabuku okwana 102,129 komanso magazini okwana 68, 911. Ndipo anthu okwana 4,701 anapempha kuti aziphunzira Baibulo. Apa n’zoonekeratu kuti Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera pothandiza pa ntchitoyi. Choncho Bungwe Lolamulira linavomereza kuti abale padziko lonse, azigwiritsa ntchito timashelefu ndi matebulo polalikira.

10. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizitha kulalikira komanso kuphunzitsa bwino?

10 Zimene mungachite. Pamisonkhano yathu Yehova amatiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito yolalikira. Choncho tiyenera kumagwiritsa ntchito zimene amatiphunzitsazo. Nthawi zonse muzilalikira limodzi ndi kagulu kanu ka utumiki. Abale ndi alongo a n’kagulu kanu angakuthandizeni kuti muzilalikira komanso kuphunzitsa bwino. Ndiponso angakulimbikitseni ndi chitsanzo chawo chabwino. Muzilalikirabe ngakhale mukumane ndi mavuto. Monga mmene lemba limene pachokera nkhaniyi likunenera, timatha kuchita chifuniro cha Mulungu osati chifukwa cha mphamvu zathu koma chifukwa chakuti Yehova amatithandiza ndi mzimu wake woyera. (Zek. 4:6) Sitikukayikira kuti Mulungu angatipatse mphamvu chifukwa tikugwira ntchito yake.

YEHOVA NDI MULUNGU WADONGOSOLO KOMANSO WAMTENDERE

11. Kodi bungwe lolamulira la munthawi ya atumwi linachita bwanji zinthu mogwirizana kuti anthu a Mulungu azichita zinthu mwadongosolo?

11 M’nthawi ya atumwi. Bungwe Lolamulira ku Yerusalemu, linkagwira ntchito mogwirizana kuti anthu a Mulungu azichita zinthu mwadongosolo komanso azikhala mwamtendere. (Mac. 2:42) Mwachitsanzo pamene nkhani ya mdulidwe inabuka cha m’ma 49 C.E. abale a m’bungwe lolamulira motsogoleredwa ndi mzimu woyera anakambirana nkhaniyi. Nkhaniyi ikanapanda kuthetsedwa, abale akanakhala ogawanika ndipo zimenezi zikanachititsa kuti ntchito yolalikira isamayende bwino. Komanso ngakhale kuti atumwi ndi akuluwo anali a mtundu wa Chiyuda sanalole kusokonezedwa ndi miyambo yachiyuda kapena anthu amene ankalimbikitsa miyamboyi. M’malo mwake iwo anadalira Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera kuti uwatsogolere posankha zochita. (Mac. 15:1, 2, 5-20, 28) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Yehova anadalitsa zimene anasankha, mpingo unapitiriza kukhala mwamtendere komanso mogwirizana ndipo ntchito yolalikira inapitiriza kuyenda bwino.​—Mac. 15:30, 31; 16:4, 5.

12. N’chiyani chikusonyeza kuti masiku ano m’gulu la Yehova anthu amachita zinthu mwadongosolo komanso amakhala mwamtendere?

12 M’masiku athu ano. Gulu la Yehova lathandiza anthu a Mulungu kuti apitirize kuchita zinthu mwadongosolo komanso kuti azikhala mwamtendere. M’mbuyomu mu 1895, magazini ya Nsanja ya Olonda yomwe pa nthawiyo inkatchedwa kuti Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence ya November 15, inali ndi nkhani ya mutu wakuti “Muzichita Zinthu Moyenera ndi Mwadongosolo,” wochokera pa 1 Akorinto 14:40. Nkhaniyo inati: “Atumwi analembera Mipingo zinthu zambiri pa nkhani yochita zinthu mwadongosolo. . . m’pofunika kupitiriza kutsatira mosamala ‘zinthu zimene zinalembedwa kalekale kuti zitilangize.’” (Aroma 15:4) Masiku anonso, gulu la Yehova limathandiza Akhristu m’mipingo yonse kuti azichita zinthu mwadongosolo komanso kuti azikhala mwamtendere ngati mmene Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankachitira. Mwachitsanzo ngati mukupita kukasonkhana kumpingo wina kaya wa dziko lina kapena m’dziko lanu lomwelo, mumadziwa mmene Phunziro la Nsanja ya Olonda likachitidwire komanso mutu umene mukaphunzire. Choncho mukafika kumisonkhanoko simuchitanso chilendo. Ndi mzimu wa Mulungu wokha umene umachititsa kuti atumiki a Mulungu azitumikira mogwirizana padziko lonse.​—Zef. 3:9.

13. Poganizira lemba la Yakobo 3:17, kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa?

13 Zimene mungachite. Yehova amafuna kuti ‘tizisunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa.’ (Aef. 4:1-3) Choncho dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimalimbikitsa mgwirizano ndi mtendere mumpingo? Kodi ndimamvera amene amatitsogolera? Ngati ndili ndi udindo mumpingo, kodi anthu ena amatha kundidalira? Kodi ndimasunga nthawi komanso ndine wokonzeka kuthandiza ndi kutumikira ena?’ (Werengani Yakobo 3:17.) Ngati mukuona kuti pali zina zimene mukufunika kusintha, muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni ndi mzimu wake woyera. Mukamalola kuti mzimu woyera ukuthandizeni kusintha makhalidwe komanso zochita zanu, abale ndi alongo angayambe kukukondani komanso kuyamikira zimene mumachita mumpingo.

YEHOVA AMATIPHUNZITSA KOMANSO AMATIPATSA ZOFUNIKA

14. Mogwirizana ndi Akolose 1:9,10, kodi Yehova anaphunzitsa bwanji anthu ake munthawi ya atumwi?

14 M’nthawi ya atumwi. Yehova amakonda kuphunzitsa anthu ake. (Sal. 32:8) Iye amafuna kuti anthuwo amudziwe, kumukonda komanso kuti adzakhale ndi moyo wosatha monga ana ake okondedwa. Zimenezi sizingatheke ngati Yehova sangaphunzitse anthu akewo. (Yoh. 17:3) Yehova anagwiritsa ntchito mpingo wa Akhristu oyambirira pophunzitsa anthu ake. (Werengani Akolose 1:9, 10.) Mzimu woyera omwe ndi “mthandizi” umene Yesu analonjeza unathandiza kwambiri ophunzira. (Yoh. 14:16) Unawathandiza kuti azimvetsa bwino kwambiri Mawu a Mulungu. Unawathandizanso kuti azikumbukira zonse zimene Yesu ananena komanso kuchita zimene kenako zinalembedwa m’Mauthenga abwino. Zimene ankaphunzirazo zinathandiza Akhristuwo kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba, azikonda Mulungu ndi Mwana wake komanso kuti azikondana.

15. Kodi masiku ano Yehova akukwaniritsa bwanji lonjezo lake lopezeka pa Yesaya 2:2, 3?

15 M’masiku athu ano. Yehova ananeneratu kuti “m’masiku otsiriza,” anthu amitundu yonse adzakhamukira kuphiri lake lophiphiritsira kuti akawaphunzitse njira zake. (Werengani Yesaya 2:2, 3.) Ulosi umenewu ukukwaniritsidwa masiku ano. Kulambira koona kwakwezedwa pamwamba kwambiri kuposa kulambira kulikonse konyenga. Ndipotu Yehova akuthandiza anthu ake kudziwa zinthu zambiri za m’Baibulo. (Yes. 25:6) Iye amagwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kutipatsa chakudya chauzimu chochuluka. Mwachitsanzo amatipatsa chakudyachi kudzera m’mabuku, nkhani zimene timamvetsera, mavidiyo komanso makatuni amene timaonera. (Mat. 24:45) Timamva ngati mmene anamvera mnzake wa Yobu dzina lake Elihu. Iye anati: “Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana naye?”​—Yobu 36:22.

Muzikhulupirira kwambiri choonadi ndipo muzigwiritsa ntchito mfundo zake pamoyo wanu (Onani ndime 16) *

16. Kodi tingatani kuti tizipindula ndi malangizo amene Yehova amatipatsa?

16 Zimene mungachite. Mzimu wa Mulungu udzakuthandizani kuti muzigwiritsa ntchito zimene mwawerenga komanso kuphunzira m’Mawu a Mulungu. Muzipemphera ngati wolemba masalimo amene ananena kuti: “Inu Yehova, ndilangizeni za njira yanu. Ndidzayenda m’choonadi chanu. Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” (Sal. 86:11) Choncho muyenera kupitiriza kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo ndi mabuku ena amene gulu la Yehova limatipatsa. Pochita zimenezi cholinga chanu sichiyenera kukhala kungofuna kudziwa zambiri. M’malo mwake chiyenera kukhala chakuti muzikhulupirira kwambiri choonadi komanso kugwiritsa ntchito mfundo zake pa moyo wanu. Mzimu wa Yehova ungakuthandizeni kuchita zimenezi. Muyeneranso kumalimbikitsa abale ndi alongo anu. (Aheb. 10:24, 25) Zimenezi n’zofunika chifukwa amenewa ndi anthu a m’banja lanu lauzimu. Muzipemphera kuti Mulungu akupatseni mzimu woyera umene ungakuthandizeni kuti muziyankha mochokera pansi pamtima mukakhala pamisonkhano komanso ngati muli ndi nkhani muziyesetsa kuikonzekera bwino. Mukamachita zimenezi mumamusonyeza Yehova ndi Mwana wake kuti mumakonda “nkhosa” zawo zamtengo wapatali.​—Yoh. 21:15-17.

17. Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu wokhulupirika ku gulu la Yehova?

17 Posachedwapa gulu limene lidzatsale padziko lapansi ndi limodzi lokha lomwe Yehova amalitsogolera ndi mzimu wake. Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tizigwirizana ndi gulu la Yehova. Muzisonyeza kuti mumakonda anthu ngati mmene Mulungu amachitira polalikira uthenga wabwino kwa anthu onse amene mungakumane nawo. Tizilimbikitsa mgwirizano mumpingo ngati mmene iye amachitira pochita zinthu mwadongosolo komanso pokonda mtendere. Muzimvetsera Mlangizi Wamkulu poyesetsa kudya chakudya chonse chauzimu chimene amatipatsa. Mukatero simudzachita mantha pamene dziko la Satanali lizidzawonongedwa. M’malomwake mudzakhala olimba mtima, n’kukhalabe ndi anthu amene akutumikira limodzi ndi gulu la Yehova mokhulupirika.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

^ ndime 5 Kodi mumakhulupirira kuti Yehova akutsogolera gulu lake masiku ano? Munkhaniyi tiona zimene Yehova anachita potsogolera mpingo wa Chikhristu woyambirira komanso zimene akuchita masiku ano potsogolera anthu ake.

^ ndime 1 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Gulu la Yehova lili ndi mbali ziwiri, mbali yakumwamba ndi mbali yapadziko lapansi. Munkhaniyi mawu akuti “gulu” akunena za mbali yapadziko lapansi.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo yemwe ndi mpainiya waonera mavidiyo amene akusonyeza anthu ena omwe akutumikira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri. Zimenezi zamulimbikitsa kuti atengere chitsanzo chawo. Kenako nayenso wakwanitsa cholinga chake chomwe ndikukatumikira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri.