Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 41

Mungapeze Chimwemwe Chenicheni

Mungapeze Chimwemwe Chenicheni

“Wodala ndi aliyense woopa Yehova, amene amayenda m’njira za Mulungu.”​—SAL. 128:1.

NYIMBO NA. 110 “Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ‘chosowa chathu chauzimu’ ndi chiti, nanga chimagwirizana bwanji ndi kukhala osangalala?

 CHIMWEMWE chenicheni sichimangotanthauza kusangalala kwakanthawi, koma chimakhalapo nthawi zonse. N’chifukwa chiyani tikutero? Yesu anafotokoza pa ulaliki wake wapaphiri kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Yesu ankadziwa kuti anthu analengedwa kuti azifunitsitsa kudziwa ndi kulambira Mlengi wawo Yehova. Chimenechi ndiye ‘chosowa chathu chauzimu.’ Popeza kuti Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe,” anthu amene amamulambira angathenso kukhala osangalala.​—1 Tim. 1:11.

“Odala ndi anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo.”​—Mat. 5:10 (Onani ndime 2-3) *

2-3. (a) Mogwirizana ndi mawu a Yesu, kodi ndi enanso ati omwe angakhale osangalala? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zingakhale zofunika?

2 Kodi timafunikira kuti zinthu zizitiyendera bwino kuti tikhale osangalala? Ayi. Mu ulaliki wake, Yesu ananena chinthu china chochititsa chidwi. Iye ananena kuti, anthu amene “akumva chisoni,” kaya chifukwa cha zoipa zomwe anachita kapena chifukwa cha mavuto omwe akukumana nawo, angathe kukhala osangalala. Iye ananenanso zomwezi ponena za “anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo” kapenanso amene ‘akunyozedwa’ chifukwa chokhala otsatira a Khristu. (Mat. 5:4, 10, 11) Koma kodi zingatheke bwanji kuti munthu azisangalala pamene akukumana ndi zimenezi?

3 Yesu anaphunzitsa kuti sikuti chimwemwe chenicheni chimabwera zinthu zikamatiyendera bwino pa moyo. M’malomwake, chimapezeka tikamazindikira zosowa zathu zauzimu komanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Yak. 4:8) Ndiye kodi tingachite bwanji zimenezi? Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zimene tiyenera kuchita kuti tipeze chimwemwe chenicheni.

TIZIWERENGA KOMANSO KUPHUNZIRA BAIBULO

4. Kodi ndi chinthu choyamba chiti chimene munthu ayenera kuchita kuti apeze chimwemwe chenicheni? (Salimo 1:1-3)

4 1: Kuti tikhaledi osangalala tiyenera kumadya chakudya chauzimu. Zinyama komanso anthu amafunika chakudya kuti akhale ndi moyo. Koma anthu okha ndi amene amafunikira chakudya chauzimu. Ndipo chakudya chauzimu n’chofunikadi. N’chifukwa chake Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:4) Choncho tisamalole kuti tsiku lizidutsa tisanawerenge Mawu amtengo wapatali a Mulungu. Wolemba masalimo ananena kuti, ‘Wodala ndi munthu amene amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amachiwerenga usana ndi usiku.’​—Werengani Salimo 1:1-3.

5-6. (a) Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera m’Baibulo? (b) Kodi kuwerenga Baibulo kungatithandize m’njira ziti?

5 M’Baibulo, Yehova anatipatsa malangizo amene angatithandize kukhala ndi moyo wosangalala. Timaphunziramo za cholinga chimene anatilengera, zimene tingachite kuti tikhale naye pa ubwenzi komanso azitikhululukira machimo athu. Timaphunziramonso za chiyembekezo chosangalatsa ndi malonjezo a m’tsogolo. (Yer. 29:11) Mfundo za choonadi zimene timaphunzira m’Baibulozi zimachititsa mitima yathu kukhala yosangalala.

6 Monga tikudziwira, m’Baibulo mulinso malangizo omwe amatithandiza pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Tikamatsatira malangizo amenewa tingathe kukhala osangalala. Mukakhumudwa chifukwa cha mavuto amene mukukumana nawo, muzipeza nthawi yambiri yowerenga komanso kuganizira mozama Mawu a Yehova. Yesu anati: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”​—Luka 11:28.

7. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzisangalala mukamawerenga Mawu a Mulungu?

7 Mukamawerenga Mawu a Mulungu, muzipeza nthawi yoganizira kuti muzisangalala ndi zimene mukuwerengazo. Mwachitsanzo, kodi zinthu ngati izi zinakuchitikiraponi? Munthu wina wakuphikirani chakudya chimene mumachikonda. Koma mwina chifukwa choti mulibe nthawi yokwanira kapena mwasokonezedwa chifukwa choganizira zinthu zina, mwangodya chakudyacho mofulumira osamvetsera kukoma kwake bwinobwino. Pamene mwamaliza kudya, mukuzindikira kuti mumadya mofulumira kwambiri ndipo mukulakalaka mukanachidya pang’onopang’ono kuti muchimve kukoma. Kodi munayamba mwawerengapo Baibulo mofulumira choncho, moti munalephera kumvetsa uthenga wake? Muzikhala ndi nthawi yokwanira kuti muzisangalala mukamawerenga Mawu a Mulungu. Muziyerekezera kuti mukuona zimene zikuchitikazo m’maganizo mwanu, kumva phokoso komanso zimene anthu akulankhula ndipo muziganizira zimene mwawerengazo. Zimenezi zingachititse kuti muzisangalala kwambiri.

8. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amakwaniritsa bwanji udindo wake? (Onaninso mawu a m’munsi)

8 Yesu anasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera ndipo timadyetsedwa bwino mwauzimu. * (Mat. 24:45) Malemba ouziridwa ndi mbali yaikulu ya chakudya chauzimu chomwe kapoloyu amatipatsa. (1 Ates. 2:13) Chakudya chauzimuchi chimatithandiza kudziwa maganizo a Yehova omwe amapezeka m’Baibulo. N’chifukwa chake timawerenga magazini a Nsanja ya Olonda, Galamukani! komanso nkhani za pa jw.org. Timakonzekeranso misonkhano yamkati komanso kumapeto kwa mlungu. Ndiponso mwezi uliwonse timaonera pulogalamu ya JW Broadcasting® ngati ilipo m’chilankhulo chathu. Tikamadya mokwanira chakudya chauzimu, zimatithandiza kuchita chinthu chachiwiri chomwe chingatithandize kupeza chimwemwe chenicheni.

TIZITSATIRA MFUNDO ZA YEHOVA

9. Kodi ndi chinthu chachiwiri chiti chomwe chingatithandize kuti tipeze chimwemwe chenicheni?

9 2: Kuti tipeze chimwemwe chenicheni tiyenera kumatsatira mfundo za Yehova. Wolemba masalimo anati: “Wodala ndi aliyense woopa Yehova, amene amayenda m’njira za Mulungu.” (Sal. 128:1) Kuopa Yehova kumatanthauza kumulemekeza kwambiri komanso kupewa kuchita chilichonse chomwe sichingamusangalatse. (Miy. 16:6) Choncho timayesetsa kuti tizitsatira mfundo za Mulungu zokhudza chabwino ndi choipa monga mmene Baibulo limafotokozera. (2 Akor. 7:1) Tidzakhala osangalala tikamachita zimene Yehova amakonda komanso kupewa zimene amadana nazo.​—Sal. 37:27; 97:10; Aroma 12:9.

10. Mogwirizana ndi Aroma 12:2, kodi udindo wathu ndi wotani?

10 Werengani Aroma 12:2. Munthu angathe kudziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu zonena kuti ichi n’chabwino kapena choipa koma ayeneranso kuvomereza mfundo za Mulungu payekha. Mwachitsanzo, munthu angathe kudziwa kuti boma lili ndi ufulu woletsa munthu woyendetsa galimoto kupitirira liwiro linalake. Koma mwina munthuyo sangavomereze malamulowo payekha. Zotsatira zake n’zakuti akhoza kumathamangitsa kwambiri galimoto. Choncho zochita zathu zimasonyeza ngati timavomereza kuti kutsatira mfundo za Yehova n’kothandiza kwambiri. (Miy. 12:28) Davide ankaonanso choncho chifukwa ponena za Yehova, iye anati: “Mudzandidziwitsa njira ya moyo. Chifukwa cha nkhope yanu, munthu adzakondwera mokwanira. Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka muyaya.”​—Sal. 16:11.

11-12. (a) Kodi tiyenera kukhala osamala ndi chiyani tikamada nkhawa kapena tikafooka? (b) Kodi malangizo a pa Afilipi 4:8, angatithandize bwanji tikamasankha zosangalatsa?

11 Tikamada nkhawa kapena tikafooka, tingamafune kuchita zinthu zina zomwe zingatithandize kuti tisiye kuda nkhawa. Zimenezitu n’zomveka. Komabe tiyenera kukhala osamala kuti tisachite zinthu zimene Yehova amadana nazo.​—Aef. 5:10-12, 15-17.

12 M’kalata imene analembera Akhristu a ku Filipi, mtumwi Paulo anawalimbikitsa kupitiriza kuganizira zinthu zimene ndi “zolungama, . . . zoyera, . . . zachikondi, [komanso] khalidwe labwino lililonse.” (Werengani Afilipi 4:8.) Ngakhale kuti Paulo sankanena mwachindunji zokhudza zinthu zosangalatsa, zimene ananenazi ziyenera kutithandiza kuganizira zosangalatsa zimene timasankha. Tayesani izi: Paliponse pamene pali mawu akuti “zilizonse” mulembali, yesani kuikapo mawu akuti “nyimbo,” “mafilimu,” “mabuku,” kapena “magemu.” Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudziwa zosangalatsa zomwe zingakhale zovomerezeka kapena zosavomerezeka kwa Mulungu. Timafuna kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi mfundo zapamwamba za Yehova. (Sal. 119:1-3) Zimenezi zingatithandize kukhala ndi chikumbumtima chabwino ndipo tingathe kuchita chinthu chachitatu chomwe chingatithandize kukhala osangalala.​—Mac. 23:1.

TIZIIKA KULAMBIRA YEHOVA PAMALO OYAMBA

13. Kodi ndi chinthu chachitatu chiti chomwe chingatithandize kupeza chimwemwe chenicheni? (Yoh. 4:23, 24)

13 3: Tizionetsetsa kuti kulambira Yehova kuzikhala pamalo oyamba pa moyo wathu. Monga Mlengi wathu, Yehova ndi woyenera kuti tizimulambira. (Chiv. 4:11; 14:6, 7) Choncho tizionetsetsa kuti chinthu chofunika kwambiri chizikhala kumulambira m’njira imene iye amaivomereza, yomwe ndi kumulambira “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.” (Werengani Yohane 4:23, 24.) Timafuna kuti mzimu wake uzititsogolera pomulambira n’cholinga choti tizichita zinthu mogwirizana ndi mfundo za choonadi zopezeka m’Mawu ake. Kulambira kwathu kuyenera kukhala pamalo oyamba ngakhale zitakhala kuti tili m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Panopa abale ndi alongo athu oposa 100 ali m’ndende, chabe chifukwa chokhala a Mboni za Yehova.  * Ngakhale zili choncho, iwo amasangalala kuchita zonse zomwe angathe kuti azipemphera, kuphunzira komanso kuuza ena zokhudza Mulungu ndi Ufumu wake. Tikamanyozedwa kapena kuzunzidwa, tingakhalebe osangalala podziwa kuti Yehova ali nafe ndipo adzatipatsa mphoto.​—Yak. 1:12; 1 Pet. 4:14.

CHITSANZO CHA WACHINYAMATA WINA

14. Kodi n’chiyani chinachitikira m’bale wina wachinyamata ku Tajikistan, nanga n’chifukwa chiyani?

14 Zimene zinachitikira anthu ena, zimatsimikizira kuti mfundo zitatu takambiranazi zimathandizadi kupeza chimwemwe chenicheni posatengera mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Taganizirani zimene zinachitikira wachinyamata wina wazaka 19, dzina lake Jovidon Bobojonov wa ku Tajikistan. Pa 4 October 2019, iye anagwidwa n’kukatsekeredwa m’ndende kwa miyezi ingapo chifukwa chokana kulowa usilikali ndipo ankachitiridwa nkhanza ngati chigawenga. Zopanda chilungamo zomwe zinamuchitikirazi zinaulutsidwa m’mawailesi komanso m’manyuzipepala m’mayiko ambiri. Malipoti anasonyeza kuti iye anamenyedwa pokakamizidwa kuti alumbire kuti adzakhala wokhulupirika ku malamulo ausilikali ndiponso kuvala yunifolomu. Pambuyo pake anaweruzidwa kuti ndi wolakwa ndipo anamutsekera m’ndende mpaka pamene pulezidenti wa dzikolo anamukhululukira n’kulamula kuti atulutsidwe. Pa nthawi yonse imene ankakumana ndi zimenezi, Jovidon anapitirizabe kukhala wokhulupirika komanso wosangalala. N’chiyani chinamuthandiza? Iye nthawi zonse ankazindikira zosowa zake zauzimu.

Jovidon ankadya chakudya chauzimu, kutsatira mfundo za Mulungu komanso kuika kulambira Yehova pamalo oyamba pa moyo wake (Onani ndime 15-17)

15. Kodi Jovidon ankatani kuti adye chakudya chauzimu ali m’ndende?

15 Ali m’ndende Jovidon ankadya chakudya chauzimu ngakhale kuti analibe Baibulo kapena mabuku ena. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Abale ndi alongo akamakamupatsira zakudya, ankalemba lemba la tsiku pazikwama zomwe ankanyamuliramo zakudyazo. Choncho ankakwanitsa kuwerenga Baibulo komanso kuganizira mfundo zake tsiku lililonse. Atatulutsidwa m’ndendemo, iye analangiza onse omwe sanakumanepo ndi mayesero aakulu kuti: “N’zofunika kwambiri kuti panopa muzigwiritsa ntchito mokwanira ufulu umene muli nawo kuti muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova powerenga Mawu ake komanso mabuku athu.”

16. Kodi Jovidon ankaganizira kwambiri za chiyani?

16 M’bale wathuyu ankatsatira mfundo za Yehova. M’malo momaganizira komanso kuchita zinthu zoipa, iye ankaganizira kwambiri za Yehova komanso zimene amaona kuti n’zoyenera. Jovidon ankachita chidwi ndi zinthu zokongola zimene Mulungu analenga. M’mawa uliwonse kukacha ankamva kulira kwa mbalame. Usiku ankaona mwezi komanso nyenyezi. Iye anati: “Mphatso zochokera kwa Yehovazi zinkandilimbikitsa ndipo zinkandithandiza kukhala wosangalala.” Tikamayamikira chakudya chauzimu komanso zinthu zina zonse zimene Yehova amatipatsa, timakhala ndi chimwemwe mumtima ndipo chimwemwe chimenecho chimatithandiza kuti tizipirira kwambiri.

17. Kodi mawu a pa 1 Petulo 1:6, 7, angathandize bwanji munthu yemwe wakumana ndi zomwe Jovidon anakumana nazo?

17 Jovidon ankaikanso kulambira Yehova pamalo oyamba. Ankadziwa kufunika kokhalabe wokhulupirika kwa Mulungu woona. Yesu anati: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Luka 4:8) Asilikali komanso akuluakulu awo ankafuna kuti Jovidon asiye chipembedzo chake. Koma iye ankapemphera kuchokera pansi pa mtima tsiku lililonse, usana ndi usiku womwe, kumupempha Yehova kuti amuthandize kuti asagonje ndiponso akhalebe wokhulupirika. Ngakhale kuti anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, Jovidon anakwanitsa kukhalabe wokhulupirika. Panopa amasangalala kwambiri kuposa mmene ankasangalalira asanagwidwe, kumangidwa komanso kutsekeredwa m’ndende chifukwa amaona kuti ali ndi chikhulupiriro chomwe chinayesedwa.​—Werengani 1 Petulo 1:6, 7.

18. Kodi tingatani kuti tipitirize kukhala osangalala?

18 Yehova amadziwa zimene timafunikira kuti tikhale wosangalala. Ngati mutatsatira zinthu zitatu takambiranazi, zomwe zimathandiza kuti munthu apezedi chimwemwe chenicheni, mudzapitirizabe kukhala osangalala ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto aakulu. Ndipo inunso mudzafika ponena kuti: “Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”​—Sal. 144:15.

NYIMBO NA. 89 Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso

^ Kwa ambiri, kupeza chimwemwe chenicheni n’kovuta chifukwa amachifunafuna m’njira yolakwika pochita zosangalatsa, kufunafuna chuma, kutchuka kapena udindo. Koma Yesu ali padzikoli anauza anthu zimene angachite kuti apeze chimwemwe chenicheni. Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zomwe zingatithandize kuti tipeze chimwemwe chenicheni.

^ Onani nkhani yakuti, “Kodi Mukulandira ‘Chakudya pa Nthawi Yoyenera’?” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2014.

^ Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani zakuti, “Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira,” pa jw.org.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pachithunzichi, abale ndi alongo abwera kudzalimbikitsa m’bale yemwe wamangidwa ndipo akupita naye kukhothi.