Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Masiku Ano Sitimenya Nkhondo Ngati Mmene Ankachitira Aisiraeli?

N’chifukwa Chiyani Masiku Ano Sitimenya Nkhondo Ngati Mmene Ankachitira Aisiraeli?

PA NTHAWI ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, mkulu wina wa asilikali a Nazi anauza gulu lina la a Mboni za Yehova mokalipa kuti, “Ngati aliyense wa inu akane kukamenya nawo nkhondo yolimbana ndi France kapena England, ndiye kuti nonsenu muphedwa.” Ngakhale kuti asilikali a Nazi anali pomwepo ali ndi zida zoopsa, palibe ngakhale mmodzi wa abale athuwo amene anavomera kumenya nkhondoyo. Kumenekutu kunali kulimba mtima kwakukulu, ndipo ichi ndi chitsanzo chabwino chosonyeza mmene a Mboni za Yehovafe timaonera nkhani yomenya nkhondo. Timakana kulowerera m’mikangano ya mayiko ngakhale pamene taopsezedwa kuti tiphedwa.

Komabe si anthu onse omwe amati ndi Akhristu amene amaona choncho. Ambiri amakhulupirira kuti Mkhristu angathe kumenya nkhondo kuti ateteze dziko lake, ndipo amafunika kutero. Iwo angamanene kuti: ‘Aisiraeli anali anthu a Mulungu ndipo ankamenya nkhondo, ndiye n’chifukwa chiyani Akhristu masiku ano sayenera kutero?’ Inuyo mungayankhe bwanji funsoli? Mungafunike kufotokoza kuti mmene zinaliri ndi Aisiraeli n’zosiyana kwambiri ndi mmene zilili ndi anthu a Mulungu masiku ano. Tiyeni tikambirane zinthu 5 zosonyeza kusiyana kumeneku.

1. ANTHU ONSE A MULUNGU ANALI M’DZIKO LIMODZI

Kale Yehova anasankha mtundu wa Isiraeli kuti ukhale anthu ake. Iye ankawaona monga ‘chuma chake chapadera pakati pa anthu ena onse.’ (Eks. 19:5) Mulungu anawapatsanso dziko lawolawo. Choncho Mulungu akalamula Aisiraeli kuti akamenye nkhondo ndi mitundu ina, iwo sankapha olambira anzawo. *

Masiku ano anthu olambira Yehova amachokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” (Chiv. 7:9) Choncho ngati anthu a Mulungu angamamenye nawo nkhondo, angathe kumamenyana ngakhale kuphana ndi olambira anzawo.

2. YEHOVA ANKALAMULA AISIRAELI KUTI AKAMENYE NKHONDO

Kale Yehova ndi amene ankasankha nthawi komanso chifukwa chake Aisiraeli ankafunika kukamenya nkhondo. Mwachitsanzo, popereka chiweruzo kwa Akanani, omwe ankadziwika chifukwa cha kulambira mafano, kuchita zachiwerewere zonyansa kwambiri komanso kupereka nsembe ana, Mulungu analamula Aisiraeli kuti akamenyane nawo. Yehova analamula Aisiraeli kuchita zimenezi n’cholinga choti Aisiraeliwo asakatengere makhalidwe oipawa akakalowa m’dziko limene anawalonjeza. (Lev. 18:24, 25) Atalowa m’Dziko Lolonjezedwa, nthawi zina Mulungu ankalola Aisiraeli kumenya nkhondo pofuna kuwateteza kwa adani awo, omwe ankawapondereza. (2 Sam. 5:17-25) Komabe palibe nthawi imene Yehova analola Aisiraeli kukamenya nkhondo mongoganiza okha. Iwo akapita kunkhondo popanda kuloledwa ndi Yehova, nthawi zambiri zinthu sizinkawayendera bwino.​—Num. 14:41-45; 2 Mbiri 35:20-24.

Masiku ano Yehova sauza anthu kuti azimenya nkhondo. Mayiko amamenyana pofuna kulimbikitsa zofuna za anthu osati za Mulungu. Iwo angamenye nkhondo chifukwa chofuna malo ambiri, ndalama zambiri, kusiyana pa nkhani zandale kapenanso chifukwa chosiyana mfundo zimene amayendera. Nanga bwanji za anthu amene amanena kuti amamenya nkhondo m’dzina la Mulungu kuti ateteze chipembedzo chawo kapena kupha adani a Mulungu? Yehova adzateteza anthu ake komanso kuwononga adani ake m’tsogolo pa nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Pa nkhondoyi, Mulungu adzagwiritsa ntchito gulu lake lankhondo lakumwamba osati anthu ake.​—Chiv. 19:11-15.

3. AISIRAELI SANKAPHA ANTHU OMWE ASONYEZA CHIKHULUPIRIRO

Kodi pa nkhondo za masiku ano anthu okhulupirika amapulumutsidwa ngati mmene Rahabi ndi a m’banja lake anapulumutsidwira pa nkhondo ya Yehova ku Yeriko?

Kale asilikali a Chiisiraeli nthawi zambiri ankachitira chifundo anthu omwe asonyeza kuti akhulupirira Mulungu ndipo ankapha anthu okhawo amene Yehova wawaweruza kuti ndi oyenera kuphedwa. Taonani zitsanzo ziwiri izi: Ngakhale kuti Yehova analamula kuti mzinda wa Yeriko uwonongedwe, Aisiraeli sanaphe Rahabi ndi banja lake chifukwa chakuti iye anasonyeza chikhulupiriro. (Yos. 2:9-16; 6:16, 17) Patapita nthawi, mzinda wonse wa Gibeoni sunawonongedwe chifukwa choti Agibeoniwo anasonyeza kuti ankaopa Mulungu.​—Yos. 9:3-9, 17-19.

Masiku ano mayiko akamamenyana, amapha ngakhale anthu amene amakhulupirira Mulungu. Ndipo nthawi zina anthu wamba omwe ndi osalakwa amaphedwa.

4. AISIRAELI ANKAFUNIKA KUTSATIRA MALANGIZO A MULUNGU POMENYA NKHONDO

Kale Yehova ankafuna kuti asilikali a Chiisiraeli azimenya nkhondo potsatira malangizo ake. Mwachitsanzo, nthawi zina Mulungu ankauza anthu ake kuti azilengeza kumzinda omwe akufuna kumenyana nawo “mfundo za mtendere.” (Deut. 20:10) Yehova ankayembekezeranso kuti iwo azikhala ndi makhalidwe abwino komanso misasa yawo izikhala yaukhondo. (Deut. 23:9-14) Pamene asilikali a mitundu yozungulira nthawi zambiri ankagwiririra azimayi a madera amene agonjetsa, Yehova sankalola Aisiraeli kuti azichita zimenezi. Ndipotu Mwisiraeli akanatha kukwatira mkazi wogwidwa pa nkhondo pambuyo poti patha mwezi kuchokera pamene agonjetsa mzinda.​—Deut. 21:10-13.

Masiku ano mayiko ambiri amasainirana malamulo omwe amayenera kutsatira pomenya nkhondo. Ngakhale kuti malamulowa cholinga chake chimakhala kuteteza anthu wamba, n’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri satsatiridwa.

5. MULUNGU ANKAMENYERA NKHONDO ANTHU AKE

Kodi masiku ano Mulungu amamenyera nkhondo dziko linalake ngati mmene anachitira ndi Aisiraeli ku Yeriko?

Kale Yehova ankamenyera nkhondo Aisiraeli, ndipo nthawi zambiri ankawathandiza kupambana modabwitsa. Mwachitsanzo, kodi Yehova anathandiza bwanji Aisiraeli kugonjetsa mzinda wa Yeriko? Potsatira malangizo a Yehova, Aisiraeli “anayamba kufuula mwamphamvu mfuu yankhondo, ndipo mpanda wa mzindawo unayamba kugwa mpaka pansi,” zimene zinathandiza kuti augonjetse mosavuta. (Yos. 6:20) Nanga zinakhala bwanji kuti apambane pa nkhondo yolimbana ndi Aamori? “Yehova anawagwetsera miyala ikuluikulu ya matalala kuchokera kumwamba . . . Amene anaphedwa ndi matalalawo anali ambiri kuposa amene ana a Isiraeli anapha ndi lupanga.”​—Yos. 10:6-11.

Masiku ano Yehova samenyera nkhondo dziko lililonse. Ufumu wake, womwe Yesu Khristu ndiye Mfumu yake, “suli mbali ya dziko lino.” (Yoh. 18:36) M’malomwake, Satana ndi amene ali wolamulira maboma onse a anthu. Nkhondo zankhanza zimene mayiko amamenya, zimasonyeza kuti iye ndi woipa kwambiri.​—Luka 4:5, 6; 1 Yoh. 5:19.

AKHRISTU OONA NDI ANTHU OKONDA MTENDERE

Monga mmene taonera, masiku ano pali kusiyana kwakukulu pakati pa Akhristu ndi Aisiraeli. Komabe izi si zifukwa zokhazo zimene zimachititsa kuti tisamamenye nkhondo. Palinso zifukwa zina. Mwachitsanzo, Mulungu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza anthu ophunzitsidwa ndi iye “sadzaphunziranso nkhondo,” ngakhalenso kumenya nawo nkhondozo. (Yes. 2:2-4) Kuwonjezera pamenepo, Khristu ananena kuti ophunzira ake sadzakhala “mbali ya dzikoli.” Choncho iwo samalowerera mikangano ya mayiko.​—Yoh. 15:19.

Khristu analamulanso otsatira ake kuchita zoposa zimenezi. Anawalangiza kupewa zimene zingawachititse kusunga chakukhosi, kukwiya kapena kumenya nkhondo. (Mat. 5:21, 22) Kuwonjezera pamenepo anawalangizanso kuti azikhala ‘anthu obweretsa mtendere’ ndipo azikonda adani awo.​—Mat. 5:9, 44.

Nanga bwanji ifeyo patokha? N’zoonekeratu kuti sitingafune kumenya nawo nkhondo. Koma kodi n’kutheka kuti mumtima mwathu timasungira ena zifukwa, zomwe zingachititse kuti mumpingo mukhale mikangano kapena kugawikana? Tiyeni tipitirize kuchita khama kuti tizichotsa maganizo ngati amenewa m’mitima mwathu.​—Yak. 4:1, 11.

M’malo molowerera mikangano ya mayiko, timalimbikitsa mtendere ndiponso chikondi pakati pathu. (Yoh. 13:34, 35) Tiyeni tikhale otsimikiza kuti tipitirizebe kusalowerera ndale kapena nkhondo pamene tikuyembekezera tsiku limene Yehova adzathetse nkhondo mpaka kalekale.​—Sal. 46:9.

^ Nthawi zina mafuko a Aisiraeli ankamenyana okhaokha, ngakhale kuti nkhondo zimenezi sizinkasangalatsa Yehova. (1 Maf. 12:24) Komabe nthawi zina ankalola kuti zimenezi zichitike chifukwa choti mafuko ena sanamumvere kapena achita machimo aakulu.​—Ower. 20:3-35; 2 Mbiri 13:3-18; 25:14-22; 28:1-8.