Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 43

Nzeru Yeniyeni Ikufuula

Nzeru Yeniyeni Ikufuula

“Nzeru yeniyeni imangokhalira kufuula mumsewu. Imangokhalira kutulutsa mawu ake m’mabwalo a mzinda.”​—MIY. 1:20.

NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi anthu ambiri masiku ano amatani nzeru ikamawafuulira? (Miyambo 1:20, 21)

 M’MAYIKO ambiri, si zachilendo kuona olalikira za Ufumu osangalala ali m’misewu yomwe mumadutsa anthu ambiri akugawa magazini ndi mabuku. N’kutheka kuti munachitapo ulaliki wosangalatsawu. Ngati ndi choncho muyenera kuti munaganizirapo mawu opezeka m’buku la Miyambo onena za nzeru yomwe ikufuulira anthu kuti adzamvetsere malangizo ake. (Werengani Miyambo 1:20, 21.) M’Baibulo komanso m’mabuku athu mumapezeka “nzeru yeniyeni” yochokera kwa Yehova. Imeneyi ndi nzeru yomwe anthu amafunikira kuti ayambe kuyenda pamsewu wopita kumoyo. Timasangalala munthu akalandira mabuku athu. Komabe si onse amene amachita zimenezi. Ena samafuna kudziwa zimene Baibulo limanena. Ena amatiseka. Amaganiza kuti Baibulo ndi lachikale. Ndiye palinso ena omwe amatsutsa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya makhalidwe abwino, n’kumanena kuti amene amalitsatira ndi okhwimitsa zinthu komanso amadziona kuti ndi olungama kwambiri. Komabe mwachikondi Yehova akupitirizabe kuthandiza anthu onse kuti apeze nzeru yeniyeni. Motani?

2. Kodi tingapeze bwanji nzeru yeniyeni masiku ano, koma anthu ambiri amasankha kuchita chiyani?

2 Njira imodzi imene Yehova amaperekera nzeru ndi kudzera m’Mawu ake Baibulo. Pafupifupi wina aliyense akhoza kulipeza bukuli. Nanga bwanji za mabuku athu? Popeza kuti Yehova akutidalitsa, mabukuwa akupezeka mu zilankhulo zoposa 1,000. Anthu omwe amamvetsera, kapena kuti kuwerenga komanso kugwiritsa ntchito zimene akuphunzirazo, zinthu zimawayendera bwino. Komabe anthu ambiri amasankha kuti asamamvetsere mawu a nzeru yeniyeni. Akafuna kusankha zochita amakonda kuyendera maganizo awo kapena kumvetsera zimene anthu ena awauza. Mwinanso angamatinyoze chifukwa choti tikutsatira mfundo za m’Baibulo. Nkhaniyi ifotokoza chifukwa chake anthu amachita zimenezi. Koma choyamba tiyeni tione mmene tingapezere nzeru yochokera kwa Yehova.

KUDZIWA YEHOVA KUNGATITHANDIZE KUPEZA NZERU

3. Kodi nzeru yeniyeni imaphatikizapo chiyani?

3 Nzeru ingatanthauze luso lotha kugwiritsa ntchito zimene munthu akudziwa kuti asankhe bwino zochita. Komabe nzeru yeniyeni imaphatikizapo zambiri. Baibulo limati: “Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru. Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.” (Miy. 9:10) Choncho tikafuna kusankha zochita pa nkhani yofunika kwambiri tiyenera kudziwa mmene Yehova amaganizira pa nkhaniyo, komwe ndi “kudziwa Woyera Koposa.” Tingachite zimenezo pofufuza m’Baibulo komanso m’mabuku athu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tili ndi nzeru yeniyeni.​—Miy. 2:5-7.

4. N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene angatipatse nzeru yeniyeni?

4 Yehova yekha ndi amene angatipatse nzeru yeniyeni. (Aroma 16:27) N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, iye pokhala Mlengi amadziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene analenga. (Sal. 104:24) Chachiwiri, chilichonse chimene iye amachita chimasonyeza kuti iye ndi wanzeru. (Aroma 11:33) Chachitatu, onse amene amagwiritsa ntchito malangizo anzeru a Yehova zinthu zimawayendera bwino. (Miy. 2:10-12) Choncho kuti tipeze nzeru yeniyeni tiyenera kulola kuti mfundo za choonadi zimenezi zizititsogolera tikamasankha zochita komanso tikamachita zimene tasankhazo.

5. Kodi zotsatirapo zake zimakhala zotani ngati anthu sakuvomereza kuti Yehova ndi Mwiniwake wa nzeru yeniyeni?

5 Anthu ambiri omwe timakumana nawo tikamalalikira amavomereza kuti chilengedwechi ndi chogometsa koma safuna kuvomereza kuti kunja kuno kuli Mlengi. M’malomwake amati zinthu zinachita kusintha. Enanso omwe timakumana nawo amati amakhulupirira Mulungu koma amaona kuti mfundo za m’Baibulo n’zachikale ndipo amasankha kuyendera maganizo awo. Ndiye kodi zotsatirapo zake zimakhala zotani? Kodi m’dzikoli zinthu zikuyenda bwino chifukwa chakuti anthu akumadalira nzeru zawo osati za Mulungu? Kodi anthu apeza chimwemwe chenicheni komanso chiyembekezo chotsimikizika cha m’tsogolo? Zimene timaona zimatsimikizira mfundo ya choonadi yakuti: “Palibe nzeru kapena kuzindikira kulikonse, kapena malangizo alionse otsutsana ndi Yehova.” (Miy. 21:30) Zimenezitu ndi zomwe zimatichititsa kupempha Yehova kuti azitipatsa nzeru yeniyeni. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ambiri sachita zimenezi. Chifukwa chiyani?

CHIFUKWA CHAKE ANTHU AMAKANA NZERU YENIYENI

6. Mogwirizana ndi Miyambo 1:22-25, kodi ndi anthu ati omwe safuna kupeza nzeru?

6 Anthu ambiri safuna kumvetsera nzeru yeniyeni “ikamafuula mumsewu.” Baibulo limasonyeza kuti pali magulu atatu a anthu amene safuna kupeza nzeru: “osadziwa,” “onyoza,” ndi “opusa.” (Werengani Miyambo 1:22-25.) Tsopano tiyeni tione zimene zimachititsa anthu amenewa kukana nzeru yochokera kwa Mulungu komanso zimene tingachite kuti tisakhale ngati iwowo.

7. N’chifukwa chiyani ena amasankha kukhala “osadziwa”?

7 Anthu “osadziwa” ndi amene amangokhulupirira zilizonse zimene amva ndiponso amapusitsidwa mosavuta. (Miy. 14:15) Nthawi zambiri tikamalalikira timakumana ndi anthu ngati amenewa. Mwachitsanzo, taganizirani za anthu mamiliyoni omwe amapusitsidwa ndi atsogoleri achipembedzo komanso andale. Anthu ena amakhumudwa akadziwa kuti apusitsidwa ndi atsogoleri ngati amenewa. Koma anthu otchulidwa pa Miyambo 1:22, amasankha kukhala osadziwa chifukwa chakuti n’zimene amafuna. (Yer. 5:31) Iwo amasangalala kumangotsatira zimene akufuna ndipo safuna kudziwa zimene Baibulo limanena kapena kutsatira malamulo ake. Ambiri ali ngati mayi wina wa ku Quebec, ku Canada yemwe ndi wodzipereka kwambiri pa nkhani ya chipembedzo. Iye anauza wa Mboni wina kuti: “Ngati wansembe wathu amatisocheretsa, vuto ndi iyeyo osati ifeyo.” Ife sitikufuna kukhala ngati anthu amenewa omwe amasankha kukhala osadziwa.​—Miy. 1:32; 27:12.

8. N’chiyani chingatithandize kuti tikhale odziwa zinthu?

8 Potifunira zabwino, Baibulo limatilimbikitsa kuti tisapitirize kukhala osadziwa zinthu koma kuti ‘pa luntha la kuzindikira tikhale aakulu msinkhu.’ (1 Akor. 14:20) Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu kumatithandiza kukhala odziwa zinthu. Pang’ono ndi pang’ono timadzionera tokha mmene mfundozi zimatithandizira kupewa mavuto komanso kusankha zochita mwanzeru. Tingachite bwino kudzifufuza mmene tikuchitira pa nkhaniyi. Ngati takhala tikuphunzira Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano kwa kanthawi, tingadzifunse chifukwa chake sitinadzipereke komanso kubatizidwa mpaka pano. Ngati tinabatizidwa, kodi tikupita patsogolo pa nkhani yophunzitsa komanso kulalikira uthenga wabwino? Kodi zosankha zathu zimasonyeza kuti tikutsogoleredwa ndi mfundo za m’Baibulo? Kodi timasonyeza makhalidwe abwino tikamachita zinthu ndi ena? Ngati taona kuti pali zimene tifunika kukonza, tiyenera kumvetsera zikumbutso za Yehova zomwe “zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.”​—Sal. 19:7.

9. Kodi anthu “onyoza” amasonyeza bwanji kuti safuna kupeza nzeru?

9 Gulu lachiwiri la anthu omwe amakana nzeru za Mulungu ndi “onyoza.” Nthawi zina timakumana ndi anthu ngati amenewa tikamalalikira. Iwo amasangalala kuchitira chipongwe ena. (Sal. 123:4) Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza padzakhala anthu ambiri onyoza. (2 Pet. 3:3, 4) Mofanana ndi akamwini a Loti, yemwe anali wolungama, anthu ena masiku ano safuna kumvetsera machenjezo ochokera kwa Mulungu. (Gen. 19:14) Ambiri amaseka anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo. Onyozawa amatsatira “zilakolako zawo pa zinthu zonyoza Mulungu.” (Yuda 7, 17, 18) Zimene Baibulo limafotokoza zokhudza anthu onyoza zimagwirizana ndi zimene ampatuko komanso anthu ena okana Yehova amachita.

10. Mogwirizana ndi Salimo 1:1, kodi tingatani kuti tisakhale onyoza?

10 Kodi tingatani kuti tisakhale m’gulu la anthu onyoza? Njira imodzi ndi kupewa kugwirizana ndi anthu omwe amangokhalira kudandaula zilizonse. (Werengani Salimo 1:1.) Zimenezi zikutanthauza kuti sitikuyenera kumvetsera kapena kuwerenga chilichonse chochokera kwa ampatuko. Timazindikira kuti ngati sitingasamale, tikhoza kuyamba kumangodandaula zilizonse komanso kumakayikira Yehova ndi malangizo amene amatipatsa kudzera m’gulu lake. Kuti zimenezi zisatichitikire tiyenera kumadzifunsa kuti: ‘Kodi nthawi zambiri ndimakonda kudandaula tikalandira malangizo kapena mfundo zina zikafotokozedwa mwatsopano? Kodi ndimakonda kupezera zifukwa amene akutsogolera?’ Tikasiya kuchita zimenezi mwamsanga Yehova adzasangalala nafe.​—Miy. 3:34, 35.

11. Kodi “anthu opusa” amaziona bwanji mfundo za Yehova za makhalidwe abwino?

11 Gulu lachitatu la anthu omwe amakana nzeru za Mulungu ndi “anthu opusa.” Iwo ndi opusa chifukwa amakana kutsatira malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino. M’malomwake amangochita zimene akuona kuti n’zabwino kwa iwowo. (Miy. 12:15) Anthu amenewa amakhala akukana Yehova yemwe ndi Mwiniwake wa nzeru. (Sal. 53:1) Tikakumana nawo pamene tikulalikira nthawi zambiri amatitsutsa mwamphamvu chifukwa chakuti timalemekeza mfundo za m’Baibulo. Koma iwo sangatithandize kukhala ndi moyo wabwino. Baibulo limati: “Kwa munthu wopusa, nzeru zenizeni n’chinthu chapatali. Iye satsegula pakamwa pake pachipata cha mzinda.” (Miy. 24:7) Anthu opusa sangatipatse malangizo aliwonse anzeru. Mpake kuti Yehova amatichenjeza kuti, “choka pamaso pa munthu wopusa.”​—Miy. 14:7.

12. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisakhale opusa?

12 Mosiyana ndi anthu amene amadana ndi malamulo a Mulungu, ifeyo timakonda malamulo ake kuphatikizaponso mfundo zake za makhalidwe abwino. Tikhoza kumakonda kwambiri mfundozi tikayerekezera zotsatirapo za kumvera ndi kusamvera. Taganizirani mavuto osiyanasiyana, omwe anthu amadzibweretsera chifukwa chochita zinthu mopusa pokana malangizo anzeru a Yehova. Ndiyeno ganizirani mmene zinthu zikukuyenderani bwino pa moyo wanu chifukwa chakuti mumamvera Mulungu.​—Sal. 32:8, 10.

13. Kodi Yehova amatikakamiza kuti tizimvera malangizo ake anzeru?

13 Yehova amapereka malangizo anzeru kwa wina aliyense koma sakakamiza anthu kuti awatsatire. Komabe amafotokoza zimene zimachitikira anthu amene samvera malangizo ake anzeru. (Miy. 1:29-32) Amene amasankha kusamvera Yehova adzakolola “zipatso za njira yawo.” N’kupita kwa nthawi zochita zawo zidzawabweretsera mavuto okhaokha ndipo pamapeto pake adzawonongedwa. Koma amene amamvetsera malangizo anzeru a Yehova komanso kuwagwiritsa ntchito, amalonjezedwa kuti: “Munthu wondimvera adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”​—Miy. 1:33.

NZERU ZENIZENI ZIMATIPINDULITSA

Kuyankha pamisonkhano kumatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova (Onani ndime 15)

14-15. Kodi tikuphunzira chiyani pa Miyambo 4:23?

14 Nthawi zonse tikamagwiritsa ntchito nzeru za Mulungu, zinthu zimatiyendera bwino. Monga mmene taonera, Yehova amapereka malangizo ake anzeru kwa aliyense. Mwachitsanzo, m’buku la Miyambo, Yehova amatipatsa malangizo othandiza omwe tingawagwiritse ntchito nthawi ina iliyonse. Tiyeni tione zitsanzo 4 za malangizo anzeruwa.

15 Tiziteteza mtima wathu wophiphiritsa. Baibulo limati: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miy. 4:23) Taganizirani zimene timafunika kuchita kuti titeteze mtima wathu. Timafunika kudya zakudya zopatsa thanzi, kuchita masewero olimbitsa thupi komanso kupewa zizolowezi zoipa. Timachitanso zofanana ndi zimenezi kuti titeteze mtima wathu wophiphiritsa. Tsiku lililonse timadya kapena kuti timawerenga Mawu a Mulungu, timakonzekera, kupezeka komanso kuyankha pamisonkhano. Kugwira ntchito yolalikira nthawi zonse kumatithandiza kuti tizikhala maso. Komanso timapewa makhalidwe oipa posachita chilichonse chomwe chingasokoneze maganizo athu monga ngati zosangalatsa zosayenera komanso kugwirizana ndi anthu oipa.

Kuona ndalama moyenera kumatithandiza kukhala okhutira ndi zomwe tili nazo (Onani ndime 16)

16. N’chifukwa chiyani mfundo za pa Miyambo 23:4, 5, zili zothandiza kwambiri masiku ano?

16 Tizikhutira ndi zimene tili nazo. Baibulo limapereka malangizo awa: “Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma. . . . Kodi maso ako amayang’anitsitsa chuma, pomwe icho sichichedwa kuchoka? Chifukwa ndithu chimadzipangira mapiko ngati a chiwombankhanga n’kuulukira kumwamba.” (Miy. 23:4, 5) Ndalama komanso katundu ndi zosakhalitsa. Koma masiku ano anthu olemera ndi osauka omwe amadera nkhawa kwambiri za mmene angapezere ndalama. Nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti azichita zinthu zimene zingawononge mbiri yawo, ubwenzi wawo ndi anthu ena ngakhalenso thanzi lawo. (Miy. 28:20; 1 Tim. 6:9, 10) Koma nzeru zimatithandiza kuti tisamadere nkhawa kwambiri zokhudza ndalama. Choncho sitikhala adyera ndipo timakhala okhutira komanso osangalala ndi zimene tili nazo.​—Mlal. 7:12.

Kuganiza kaye tisanalankhule kungatithandize kuti tisakhumudwitse ena (Onani ndime 17)

17. Kodi tingakhale bwanji ndi “lilime la anthu anzeru,” ngati mmene lafotokozera lemba la Miyambo 12:18?

17 Tiziganiza kaye tisanalankhule. Ngati sitingasamale, zimene tingalankhule zingakhumudwitse kwambiri anthu ena. Baibulo limati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.” (Miy. 12:18) Timapitiriza kugwirizana ndi anthu ena tikamapewa kulankhula miseche pa zimene amalakwitsa. (Miy. 20:19) Kuti zolankhula zathu zizisangalatsa ena osati kuwakhumudwitsa, tiyenera kudzadza mumtima mwathu ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu. (Luka 6:45) Tikamaganizira kwambiri zimene Baibulo limanena, mawu athu angakhale ngati “chitsime cha nzeru” ndipo angatsitsimule anthu ena.​—Miy. 18:4.

Kutsatira malangizo omwe gulu limatipatsa kungatithandize kuti tizichita bwino utumiki wathu (Onani ndime 18)

18. Kodi kugwiritsa ntchito mfundo ya pa Miyambo 24:6, kungatithandize bwanji kuti zinthu zitiyendere bwino mu utumiki?

18 Tizitsatira malangizo. Pofuna kuti zinthu zitiyendere bwino Baibulo limatilangiza kuti: “Iweyo udzatha kumenya nkhondo yako potsatira malangizo anzeru, ndipo pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.” (Miy. 24:6) Taganizirani mmene kutsatira mfundo imeneyi kungathandizire kuti zinthu zitiyendere bwino pa ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa. M’malo momagwira ntchitoyi m’njira yathuyathu, timatsatira malangizo omwe timapatsidwa. Timalandira malangizo anzeru kumisonkhano yathu, komwe aphungu anzeru amakamba nkhani za m’Baibulo komanso kuchita zitsanzo zotithandiza. Kuwonjezera pamenepo gulu la Yehova limatipatsa zinthu monga mavidiyo ndi mabuku zomwe zimathandiza anthu kumvetsa Baibulo. Kodi mukuphunzira kugwiritsa ntchito bwino zinthu zimenezi?

19. Kodi mumaona bwanji nzeru zimene Yehova amapereka? (Miyambo 3:13-18)

19 Werengani Miyambo 3:13-18. Timayamikira chifukwa cha malangizo abwino kwambiri amene timawapeza m’Mawu a Mulungu. Kodi zinthu zikanakhala bwanji pa moyo wathu pakanapanda malangizowa? Munkhaniyi taona nzeru zothandiza zopezeka m’buku la Miyambo. Komabe m’Baibulo lonse muli malangizo othandiza ochokera kwa Yehova. Tiyeni nthawi zonse tizigwiritsa ntchito nzeru zimene Yehova amatipatsa. Anthu ambiri m’dzikoli amaona kuti nzeruzi ndi zosafunika, koma ifeyo timatsimikiza kuti onse ozigwiritsa ntchito, “adzatchedwa odala.”

NYIMBO NA. 36 Timateteza Mtima Wathu

^ Nzeru zimene Yehova amapereka n’zapamwamba kwambiri kuposa chilichonse chimene dzikoli lingatipatse. Munkhaniyi tiona mawu ochititsa chidwi amene agwiritsidwa ntchito m’buku la Miyambo onena za nzeru yomwe ikufuula m’mabwalo a mzinda. Tikambirana mmene tingapezere nzeru yeniyeni, chifukwa chake ena amakana kumvetsera nzeru yochokera kwa Mulungu komanso mmene timapindulira tikaitsatira.