Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Kodi lemba la Mlaliki 5:8 limanena za olamulira a anthu, kapena za Yehova?

Lembali ndi lochititsa chidwi chifukwa limati: “Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zachiwawa ndi zopanda chilungamo zikuchitika m’chigawo cha dziko, usadabwe nazo. Pakuti wamkulu kuposa amene akuchita zimenezoyo akuona, ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo.”​—Mlal. 5:8.

Popanda kuganizira mmene Yehova amaonera zinthu, tingaone ngati vesili likungonena zimene olamulira maboma a anthu amachita. Koma tikaliganizira kwambiri, tingaone kuti likunenanso za Yehova, zomwe zingatitonthoze ndi kutilimbikitsa.

Lemba la Mlaliki 5:8 limanena za olamulira amene amapondereza osauka komanso kuwachitira zopanda chilungamo. Wolamulira ayenera kukumbukira kuti pali munthu winanso amene amamuyang’anira, yemwe ndi waudindo waukulu kuposa iyeyo. Ndiponso pamwamba pa munthu waudindo waukuluyu, pangakhale enanso a maudindo aakulu kwambiri. Chomvetsa chisoni n’chakuti m’maboma a anthu, olamulira onsewa amakhala achinyengo ndipo anthu amavutika ndi katangale komanso zinthu zopanda chilungamo.

Ngakhale zili choncho, sitiyenera kutaya mtima chifukwa tikudziwa kuti Yehova, amaona zimene anthu a maudindo aakulu m’maboma a anthu amachita. Choncho tingapemphe Yehova kuti atithandize komanso tingathe kumutulira nkhawa zathu. (Sal. 55:22; Afil. 4:6, 7) Timadziwa kuti “maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”​—2 Mbiri 16:9.

Choncho lemba la Mlaliki 5:8 limatikumbutsa zomwe zimachitikadi m’maboma a anthu, kuti nthawi zonse munthu waudindo waukulu, amakhalanso ndi wina waudindo waukulu kuposa iyeyo. Chofunika kwambiri n’chakuti vesili lingatithandize kuganizira mfundo yakuti Yehova ndi amene ali wamkulu kwambiri, iye ndi Wolamulira Wamkulu. Panopa Yehova akulamulira kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Yehova yemwe ndi Wamphamvuyonse amaona zinthu zonse komanso munthu aliyense ndipo iye komanso Mwana wake ndi achilungamo.