Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 35

Muziona Kuti Achikulire Okhulupirika Ndi Amtengo Wapatali

Muziona Kuti Achikulire Okhulupirika Ndi Amtengo Wapatali

“Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero.”​—MIY. 16:31.

NYIMBO NA. 138 Imvi Ndi Chisoti cha Ulemerero

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) Mogwirizana ndi Miyambo 16:31, kodi tiziwaona bwanji achikulire okhulupirika? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

 ANTHU akapita kukaona malo kupaki ina ya ku Arkansas ku America, amatha kuona dayamondi yemwe amangooneka ngati miyala wamba. Miyala yamtengo wapataliyi imakhala kuti sinakonzedwe kuti igwiritsidwe ntchito kupangira zinthu zosiyanasiyana. Choncho anthu ambiri amene amaona miyalayi, saizindikira ndipo amangoidutsa.

2 Mofanana ndi dayamondi ameneyu, abale ndi alongo athu achikulire okhulupirika ndi chuma chamtengo wapatali. Mawu a Mulungu amayerekezera imvi zawo ndi chisoti chachifumu. (Werengani Miyambo 16:31; 20:29) Komabe mwina nthawi zina sitingazindikire chuma chimenechi. Achinyamata amene amazindikira kuti achikulire ndi ofunika, angapeze zinthu zamtengo wapatali kwambiri kuposa chuma chenicheni. Munkhaniyi, tipeza mayankho a mafunso atatu awa: N’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti achikulire okhulupirika ndi chuma chamtengo wapatali? Kodi achikulire amenewa ndi ofunika bwanji m’gulu la Yehova? Kodi tingatani kuti chitsanzo chawo chizitithandiza kwambiri?

CHIFUKWA CHAKE YEHOVA AMAONA KUTI ACHIKULIRE OKHULUPIRIKA NDI CHUMA CHAMTENGO WAPATALI

Achikulire okhulupirika ndi amtengo wapatali kwa Yehova Mulungu komanso kwa anthu ake (Onani ndime 3)

3. Mogwirizana ndi Salimo 92:12-15, n’chifukwa chiyani achikulire okhulupirika ali amtengo wapatali kwa Yehova?

3 Achikulire okhulupirika ndi amtengo wapatali kwa Yehova Mulungu. Iye amaona zimene zili mumtima mwawo komanso amadziwa makhalidwe awo abwino. Yehova amasangalala achikulirewa akamathandiza achinyamata ndi nzeru zimene apeza pa zaka zambiri zimene akhala akumutumikira mokhulupirika. (Yobu 12:12; Miy. 1:1-4) Iye amayamikiranso kupirira kwawo. (Mal. 3:16) Abale ndi alongo amenewa akhala akukumana ndi mavuto osiyanasiyana koma sanasiye kutumikira Yehova. Panopa chiyembekezo chawo ndi champhamvu kwambiri kuposa pa nthawi imene anayamba kuphunzira choonadi. Ndipo Yehova amawakonda chifukwa akupitirizabe kulalikira za dzina lake ‘ngakhale achita imvi,’ kapena kuti ndi achikulire.​—Werengani Salimo 92:12-15.

4. Kodi ndi mfundo ziti zimene zingalimbikitse abale ndi alongo athu achikulire?

4 Ngati mukukalamba, dziwani kuti Yehova amakumbukira zimene mwachita m’mbuyomu. (Aheb. 6:10) Atate wathu wakumwamba amasangalala kuti mwakhala mukugwira nawo ntchito yolalikira mwakhama. Mwapirira mayesero osiyanasiyana ngakhalenso ovuta kwambiri. Mwakhala mukutsatira mokhulupirika mfundo zolungama za m’Baibulo, kutumikira pa maudindo akuluakulu, kuphunzitsa ena ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi kusintha kumene kwakhala kukuchitika m’gulu la Yehova. Mwakhalanso mukuthandiza komanso kulimbikitsa anthu amene akuchita utumiki wa nthawi zonse. Yehova Mulungu amakukondani kwambiri chifukwa chokhalabe okhulupirika. Iye amalonjeza kuti “sadzasiya anthu ake okhulupirika.” (Sal. 37:28) Akukutsimikizirani kuti: “Munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.” (Yes. 46:4) Choncho musamaganize kuti popeza tsopano mwakalamba, si inunso ofunika m’gulu la Yehova. Ndinu ofunika kwambiri.

ACHIKULIRE NDI OFUNIKA KWAMBIRI M’GULU LA YEHOVA

5. Kodi achikulire ayenera kukumbukira chiyani?

5 Achikulire angathandize kwambiri m’gulu la Yehova. Ngakhale kuti iwo sangakhalenso ndi mphamvu ngati kale, amadziwa zambiri zimene akhala akuphunzira pa moyo wawo. Yehova angawagwiritse ntchito m’njira zosiyanasiyana, monga mmene tionere m’zitsanzo zotsatirazi za atumiki akale komanso amasiku ano.

6-7. Tchulani zitsanzo za m’Baibulo za achikulire omwe anadalitsidwa chifukwa chotumikira Yehova mokhulupirika.

6 M’Baibulo muli zitsanzo zabwino za anthu okhulupirika omwe anapitiriza kutumikira Yehova mwakhama ngakhale kuti anali okalamba. Mwachitsanzo, Mose anali ndi zaka pafupifupi 80 pamene anakhala mneneri wa Yehova komanso mtsogoleri wa Aisiraeli. Ngakhale kuti Danieli anali ndi zaka za m’ma 90, Yehova anapitiriza kumugwiritsa ntchito ngati mneneri wake. Ndipo nayenso mtumwi Yohane ayenera kuti anali ndi zaka za m’ma 90 pamene anauziridwa kuti alembe buku la Chivumbulutso.

7 Atumiki ambiri okhulupirika sanali otchuka ndiponso mwina anthu ambiri sankawadziwa. Koma Yehova ankawadziwa ndipo anawapatsa mphoto chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Mwachitsanzo, Simiyoni yemwe anali “wolungama ndi woopa Mulungu,” satchulidwa kawirikawiri m’Baibulo. Koma Yehova ankamudziwa ndipo anamupatsa mwayi woona Yesu ali wakhanda komanso wolosera zokhudza mwanayu ndi mayi ake. (Luka 2:22, 25-35) Taganiziranso za mneneri wamkazi Anna, yemwenso anali wamasiye. Iye anali ndi zaka 84 koma “sanali kusowa pakachisi.” Popeza ankapezeka pakachisi nthawi zonse, nayenso anapatsidwa mwayi woona Yesu ali wakhanda. Simiyoni komanso Anna, anali amtengo wapatali kwa Yehova.​—Luka 2:36-38.

Mlongo Didur, yemwe tsopano ali ndi zaka za m’ma 80 akupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika (Onani ndime 8)

8-9. Kodi alongo amasiye amathandiza bwanji gulu la Yehova?

8 Masiku ano, pali achikulire ambiri okhulupirika omwe amapereka chitsanzo chabwino kwa achinyamata. Taganizirani chitsanzo cha Mlongo Lois Didur. Iye anali ndi zaka 21 zokha pamene anayamba kutumikira ngati mpainiya wapadera ku Canada. Kenako iye ndi mwamuna wake John anachita utumiki woyang’anira dera kwa zaka zambiri. Kenako anakatumikira ku Beteli ya ku Canada kwa zaka zoposa 20. Ali ndi zaka 58, Lois ndi mwamuna wake anapemphedwa kuti akatumikire ku Ukraine. Kodi iwo akanatani? Kodi akanaganiza kuti akula moti sangakatumikire m’dziko lina? Iwo anavomera ndipo John ankatumikira m’Komiti ya Nthambi kumeneko. Patatha zaka 7, John anamwalira ndipo Lois anasankha kupitirizabe kutumikira komweko. Panopa ali ndi zaka 81, ndipo akupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika komanso abale ndi alongo ku Beteli ya ku Ukraine amamukonda kwambiri.

9 Mwina anthu ambiri samaona zimene akazi amasiye ngati Lois akuchita kusiyana ndi mmene zinaliri amuna awo ali moyo. Komabe kukhala amasiye sikuchititsa kuti asakhale amtengo wapatali. Yehova amayamikira kwambiri alongo amenewa omwe anathandiza amuna awo kwa zaka zambiri ndipo panopa akupitirizabe kumutumikira mokhulupirika. (1 Tim. 5:3) Iwo amalimbikitsanso kwambiri achinyamata.

10. Kodi Tony anapereka chitsanzo chabwino chiti?

10 Achikulire okhulupirika omwe sangathe kuchoka panyumba, nawonso ndi amtengo wapatali. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Tony panopa amakhala kunyumba zosamalira okalamba. Iye anabatizidwa ku Pennsylvania, U.S.A., mu August 1942 ali ndi zaka 20. Pasanapite nthawi atabatizidwa, anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali ndipo anakakhala m’ndende zaka ziwiri ndi hafu. Iye ndi mkazi wake Hilda anathandiza ana awo awiri kuphunzira choonadi. Kwa zaka zambiri Tony wakhala akutumikira m’mipingo itatu monga woyang’anira wotsogolera (yemwe panopa amadziwika kuti wogwirizanitsa ntchito za akulu) komanso woyang’anira msonkhano. Iye ankachititsa misonkhano komanso maphunziro a Baibulo kundende ina. Panopa Tony ali ndi zaka 98 koma akupitirizabe kutumikira Yehova mwakhama. Iye akupitirizabe kuchita zonse zimene angathe potumikira Yehova limodzi ndi abale ndi alongo amumpingo wake.

11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza achikulire omwe sangathe kuchoka panyumba?

11 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza achikulire omwe sangathe kuchoka panyumba? Ngati n’kotheka, akulu angathandize achikulirewa kuti azichita misonkhano komanso kulalikira. Tingasonyezenso kuti timawaganizira ngati titamapita kukawaona kapena kucheza nawo pa vidiyokomferensi. Timafunikanso kusonyeza chidwi kwa achikulire amene amakhala kunyumba zosamalira okalamba zomwe zili kutali ndi mpingo wakwawo. Koma ngati sitingasamale tikhoza kumawaiwala. Ena mwa achikulirewa zimawavuta kapenanso sakonda kuti azingolankhula zokhudza iwowo. Koma tingapindule kwambiri ngati titawachititsa kuti akhale omasuka, n’kumamvetsera akamatifotokozera zinthu zosangalatsa zimene akumana nazo m’gulu la Yehova.

12. Kodi mumpingo wathu tikhoza kupezamo abale ndi alongo otani?

12 Tikhoza kudabwa kuona kuti mumpingo mwathu tilinso ndi zitsanzo zabwino za achikulire okhulupirika. Mlongo wina dzina lake Harriette, anatumikira Yehova kwa zaka zambiri mumpingo wakwawo ku New Jersey, U.S.A. Kenako anasamuka n’kumakakhala ndi mwana wake wamkazi. Abale amumpingo wake watsopanowu ankapeza nthawi yocheza naye kuti amudziwe bwino, ndipo anaona kuti ndi wamtengo wapatali. Mlongoyu anawalimbikitsa powafotokozera zinthu zosiyanasiyana zimene ankakumana nazo mu utumiki atangophunzira kumene choonadi cha m’ma 1920. Pa nthawiyo, iye ankatenga nswachi nthawi iliyonse akamapita kolalikira kuopera kuti mwina angakagwidwe n’kutsekeredwa m’ndende. Ndipotu anamangidwa kawiri mu 1933, moti ulendo uliwonse anakhala m’ndende kwa mlungu umodzi. Pa nthawi ngati imeneyi, mwamuna wake yemwe sanali wa Mboni ankamuthandiza kusamalira ana awo atatu aang’ono. Kunena zoona, achikulire okhulupirika monga Harriette amafunika kuti tiziwalemekeza.

13. Kodi taphunzira kuti achikulire ndi ofunika bwanji m’gulu la Yehova?

13 Abale ndi alongo athu achikulire ndi ofunika kwambiri kwa Yehova komanso gulu lake. Iwo aona mmene Yehova wawadalitsira komanso mmene wakhala akudalitsira gulu lake m’njira zosiyanasiyana. Aphunziranso mfundo zofunika kuchokera pa zinthu zimene akhala akulakwitsa. Muziona kuti iwo ndi “chitsime cha nzeru” ndipo muziphunzirapo kanthu pa zimene zakhala zikuwachitikira. (Miy. 18:4) Mukamapeza nthawi yocheza nawo, mukhoza kulimbitsa chikhulupiriro chanu komanso mungaphunzire zinthu zambiri.

ZIMENE TINGACHITE KUTI CHITSANZO CHA ACHIKULIRE CHIZITITHANDIZA KWAMBIRI

Mofanana ndi Elisa, yemwe anapindula chifukwa chokhala limodzi ndi Eliya, abale ndi alongo angapindulenso akamamvetsera zimene achikulire omwe atumikira Yehova kwa nthawi yaitali akufotokoza (Onani ndime 14-15)

14. Kodi lemba la Deuteronomo 32:7 limalimbikitsa achinyamata kuchita chiyani?

14 Muziyesetsa kuyamba ndinu kucheza ndi achikulire. (Werengani Deuteronomo 32:7.) N’zoona kuti mwina panopa maso awo saona bwino, amayenda pang’onopang’ono komanso mawu awo samveka kwambiri. Koma iwo amafunitsitsa atamachita zambiri ndipo apanga “mbiri yabwino” pamaso pa Yehova. (Mlal. 7:1) Muzikumbukira chifukwa chake Yehova amawaona kuti ndi amtengo wapatali. Pitirizani kuwalemekeza. Muzikhala ngati Elisa, yemwe anafunitsitsa kukhalabe ndi Eliya pa tsiku lawo lomaliza kuchitira zinthu limodzi. Katatu konse Elisa ananena kuti “sindikusiyani.”​—2 Maf. 2:2, 4, 6.

15. Kodi ndi mafunso ati omwe tingafunse achikulire?

15 Tingasonyeze chidwi kwa achikulire powafunsa mafunso mwaulemu. (Miy. 1:5; 20:5; 1 Tim. 5:1, 2) Mungawafunse mafunso ngati akuti: “Kodi muli wachinyamata, n’chiyani chinakutsimikizirani kuti mwapeza choonadi?” “Kodi zinthu zimene zakuchitikirani pa moyo wanu zakuthandizani bwanji kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?” “Kodi mwapeza kuti chinsinsi chokhalira osangalala potumikira Yehova ndi chiyani?” (1 Tim. 6:6-8) Ndiyeno muzimvetsera akamakufotokozerani.

16. Kodi wachikulire akamacheza ndi wachinyamata, onse amapindula bwanji?

16 Achikulire akamacheza ndi achinyamata, onse amalimbikitsana. (Aroma 1:12) Achinyamatanu, zimenezi zidzakuthandizani kutsimikiza kuti Yehova amasamalira atumiki ake okhulupirika, ndipo wachikulireyo adzaona kuti mumamukonda. Iye adzasangalala kukufotokozerani mmene Yehova wamudalitsira.

17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti achikulire okhulupirika amakongola kwambiri zaka zikamapita?

17 Kukongola kumatha munthu akamakalamba. Koma kwa anthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika, kukongola kwawo kumawonjezereka zaka zikamapita. (1 Ates. 1:2, 3) N’chifukwa chiyani zili choncho? Zili choncho chifukwa kwa zaka zambiri, iwo alola kuti mzimu wa Mulungu uziwaphunzitsa komanso kuwathandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. Tikamayesetsa kuwadziwa bwino abale ndi alongo athu achikulire, kuwalemekeza komanso kuphunzira kuchokera kwa iwo, m’pamenenso timawaona kuti ndi chuma chamtengo wapatali.

18. Kodi tikambirana chiyani munkhani yotsatira?

18 Mpingo umakhala wolimba kwambiri achinyamata akamaona kuti achikulire ndi ofunika komanso achikulirewo akamaona kuti achinyamata ndi ofunika. Munkhani yotsatira tikambirana mmene achikulire angasonyezere kuti amaona kuti achinyamata ndi ofunika mumpingo.

NYIMBO NA. 144 Yang’ananibe Pamphoto

^ ndime 5 Achikulire okhulupirika ali ngati chuma chamtengo wapatali. Nkhaniyi itilimbikitsa kuti tiziwayamikira kwambiri komanso tikambirana zimene tingachite kuti tizipindula kwambiri ndi nzeru zawo ndiponso zimene amadziwa. Ithandizanso achikulire kuona kuti gulu la Yehova limawaona kukhala ofunika kwambiri.