Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 36

Muziona Kuti Achinyamata Ndi Amtengo Wapatali

Muziona Kuti Achinyamata Ndi Amtengo Wapatali

“Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo.”​—MIY. 20:29.

NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi cholinga chiti chimene tingadziikire tikamakalamba?

 TIKAMAKALAMBA mwina tingamade nkhawa kuti Yehova sangatigwiritsenso ntchito ngati kale. N’zoona kuti mphamvu zathu zingachepe koma tikhoza kugwiritsa ntchito nzeru ndi zimene tikudziwa pothandiza achinyamata kuti azichita zambiri potumikira Yehova komanso kutumikira m’maudindo osiyanasiyana. Mkulu wina yemwe watumikira kwa zaka zambiri anafotokoza kuti, “Nditayamba kuona kuti ndikulephera kuchita zinthu zina chifukwa cha uchikulire, ndinasangalala kuti panali achinyamata oyenerera amene akanatha kupitiriza utumiki umene ndinkachita.”

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Munkhani yapita ija, tinaona mmene achinyamata angapindulire chifukwa chocheza ndi achikulire. Munkhaniyi tiona mmene makhalidwe monga kudzichepetsa, kuzindikira zimene tingakwanitse kuchita, mtima woyamikira komanso kuwolowa manja angathandizire achikulire kuti azigwira ntchito limodzi ndi achinyamata zomwe zimachititsa kuti zinthu ziziyenda bwino mumpingo.

MUZIKHALA ODZICHEPETSA

3. Kodi lemba la Afilipi 2:3, 4, likusonyeza kuti munthu wodzichepetsa amatani, nanga zimenezi zingathandize bwanji Mkhristu?

3 Achikulire ayenera kukhala odzichepetsa kuti azithandiza achinyamata. Munthu wodzichepetsa amaona ena kukhala omuposa. (Werengani Afilipi 2:3, 4.) Achikulire omwe ndi odzichepetsa amazindikira kuti pali njira zosiyanasiyana zochitira zinthu, zimene sizisemphana ndi mfundo za m’Malemba komanso zomwe zingakhale zothandiza. Choncho sayembekezera kuti aliyense azichita zinthu ngati mmene iwowo ankachitira kale. (Mlal. 7:10) Ngakhale kuti amadziwa zinthu zambiri zimene angathandize nazo achinyamata, amazindikira kuti “zochitika za padzikoli zikusintha.” Iwo angafunike kuphunzira njira zatsopano zochitira zinthu.​—1 Akor. 7:31.

Achikulire amafunitsitsa kuuza ena zimene akudziwa (Onani ndime 4-5) *

4. Kodi oyang’anira madera amasonyeza bwanji mtima umene Alevi anali nawo?

4 Akhristu odzichepetsa akamakula amazindikira kuti sangamachite zambiri ngati mmene ankachitira kale. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zimachitikira oyang’anira madera. Iwo akafika zaka 70, amapemphedwa kuti ayambe utumiki wina. Zimenezi zingakhale zovuta. Iwo amakhala kuti ankasangalala kutumikira abale awo. Umenewu ndi utumiki umene ankaukonda ndipo mumtima mwawo amalakalaka atapitiriza kuuchita. Koma amamvetsa kuti zingakhale bwino achinyamata atapitiriza ntchitoyi. Akamachita zimenezi amasonyeza mtima umene Alevi ku Isiraeli anali nawo, omwe akafika zaka 50 ankafunika kusiya kutumikira pachihema. Sikuti chimwemwe cha Alevi achikulirewa chinkadalira utumiki umene ankachita. Ankachita zonse zimene angathe pa utumiki umene wapezeka komanso kuthandiza achinyamata. (Num. 8:25, 26) Masiku anonso abale amene anali oyang’anira madera ngakhale kuti sayenderanso mipingo, amathandiza komanso kulimbikitsa abale ndi alongo mumpingo umene akusonkhana.

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Dan ndi Katie?

5 Taganizirani chitsanzo cha Dan yemwe anatumikira ngati woyang’anira dera kwa zaka 23. Atakwanitsa zaka 70, iye ndi mkazi wake Katie anauzidwa kuti azichita upainiya wapadera. Ndiye kodi amatani kuti azisangalala ndi utumiki wawo watsopanowu? Dan anafotokoza kuti panopa amatanganidwa kwambiri kuposa kale. Iye amakhala ndi zochita zambiri mumpingo, amathandiza abale kuti ayenerere kukhala atumiki othandiza komanso amaphunzitsa ena kuti azilalikira m’malo opezeka anthu ambiri ndiponso kundende. Achikulirenu, kaya mukuchita utumiki wa nthawi zonse kapena ayi mukhoza kuchita zambiri pothandiza ena. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzisangalala ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu panopa, muzikhala ndi zolinga zatsopano komanso muziganizira kwambiri zimene mungakwanitse kuchita, osati zimene simungakwanitse.

MUZIZINDIKIRA ZIMENE MUNGAKWANITSE KUCHITA

6. N’chifukwa chiyani ndi nzeru kuzindikira zimene tingakwanitse kuchita? Perekani chitsanzo.

6 Mukamazindikira zimene mungakwanitse kuchita mumasonyeza kuti ndinu odzichepetsa. (Miy. 11:2) Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamayembekezere kuchita zambiri kuposa zimene simungakwanitse, muzikhalabe osangalala komanso muzichita khama. Tingayerekezere zimenezi ndi munthu amene akuyendetsa galimoto pamalo okwera. Woyendetsa galimotoyo amafunika kuika giya yochepa yomwe imakhala yamphamvu, n’cholinga choti ipitirizebe kukwera mtundawo. N’zoona kuti galimotoyo imayenda pang’onopang’ono komabe ulendowo umapitirira. Mofanana ndi zimenezi, munthu amene amazindikira zimene sangakwanitse kuchita, amadziwa nthawi imene ayenera “kubweza magiya” n’cholinga choti apitirize kutumikira Yehova komanso kuthandiza ena.​—Afil. 4:5

7. Kodi Barizilai anasonyeza bwanji kuti ankazindikira zimene sangakwanitse?

7 Taganizirani chitsanzo cha Barizilai yemwe anali ndi zaka 80 pamene Mfumu Davide inamuitana kuti azikakhala kunyumba yachifumu. Barizilai anakana mwayi umene mfumu inamupatsa. Poganizira zimene sakanachita chifukwa chakuti anali wachikulire, iye anapempha kuti Chimamu yemwe anali wachinyamata apite m’malomwake. (2 Sam. 19:35-37) Mofanana ndi Barizilai, abale achikulire amasangalala kupereka mwayi wa utumiki kwa achinyamata.

Mfumu Davide inavomereza zimene Mulungu anasankha zoti mwana wake ndi amene adzamange kachisi (Onani ndime 8)

8. Kodi Mfumu Davide anasonyeza bwanji kuti ankadziwa malire ake ochitira zinthu pankhani yomanga kachisi?

8 Mfumu Davide inasonyezanso chitsanzo chabwino pankhani yozindikira malire a zimene ankayenera kuchita. Iye ankafunitsitsa kumanga nyumba ya Yehova. Koma atauzidwa kuti mwayi umenewu udzaperekedwa kwa Solomo yemwe anali wachinyamata, Davide anavomereza zimene Yehova anasankha ndipo anachita zonse zimene akanatha pothandiza kukonzekera ntchitoyo. (1 Mbiri 17:4; 22:5) Davide sankaona kuti iye ndi amene angagwire bwino ntchitoyo chifukwa chakuti Solomo anali “wamng’ono ndi wosakhwima.” (1 Mbiri 29:1) Iye ankadziwa kuti ntchitoyo ingayende bwino ngati Yehova akuidalitsa, osati chifukwa cha kudziwa zinthu kapena msinkhu wa amene ankatsogolera. Mofanana ndi Davide, masiku ano achikulire amapitirizabe kuchita khama ngakhale pamene utumiki wawo wasintha. Ndipo amadziwa kuti Yehova adzadalitsa achinyamata amene akugwira ntchito imene iwowo ankagwira.

9. Kodi m’bale wina wa m’Komiti ya Nthambi anasonyeza bwanji kuti ankazindikira zimene sangakwanitse kuchita?

9 M’bale wina dzina lake Shigeo ndi chitsanzo cha masiku ano pankhani yozindikira zimene sitingakwanitse kuchita. Mu 1976, ali ndi zaka 30, iye anavomerezedwa kuti azitumikira mu Komiti ya Nthambi. Mu 2004 anakhala wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi. Patapita nthawi iye anazindikira kuti mphamvu zake zikuchepa ndipo sankakwanitsa kuchita bwinobwino zinthu zina. Atapemphera komanso kuganizira nkhaniyi, anaona ubwino wopereka udindo wake kwa achinyamata. Ngakhale kuti panopa Shigeo si wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi, iye akupitirizabe kutumikira ndi abale ena a m’komitiyi. Monga mmene taonera pa chitsanzo cha Barizilai, Mfumu Davide ndi Shigeo, munthu wodzichepetsa komanso yemwe amazindikira zimene angakwanitse, amaganizira kwambiri mphamvu zimene achinyamata ali nazo osati luso lawo. Iye amaona kuti achinyamatawo ndi antchito anzake osati anthu opikisana nawo.​—Miy. 20:29.

MUZIKHALA NDI MTIMA WOYAMIKIRA

10. Kodi achikulire ayenera kuona bwanji achinyamata mumpingo?

10 Achikulire amaona kuti achinyamata ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo amayamikira zimene amachita. Mphamvu zawo zikamachepa, iwo amasangalala kuona kuti achinyamata amene ali ndi mphamvu ndi ofunitsitsa kugwira ntchito zosiyanasiyana mumpingo.

11. Kodi lemba la Rute 4:13-16, limasonyeza bwanji kuti achikulire angapindule kwambiri ngati atalola kuti achinyamata awathandize?

11 Naomi wotchulidwa m’Baibulo ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha wachikulire amene analola kuti athandizidwe ndi wachinyamata. Poyamba Naomi analimbikitsa mpongozi wake Rute kuti abwerere kwawo. Komabe Rute atalimbikira kuti apita nawo ku Betelehemu, iye analola kuti mpongozi wakeyo azikamuthandiza. (Rute 1:7, 8, 18) Zimenezo zinali zothandiza kwambiri kwa azimayi awiriwa. (Werengani Rute 4:13-16.) Kudzichepetsa kungathandize achikulire kuti azitsanzira Naomi.

12. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti anali woyamikira?

12 Mtumwi Paulo ankayamikira kwambiri abale akamuthandiza. Mwachitsanzo, iye anayamikira abale a ku Filipi atamutumizira mphatso zosiyanasiyana. (Afil. 4:16) Anayamikiranso zimene Timoteyo ankachita pomuthandiza. (Afil. 2:19-22) Pamene ankatumizidwa ku Roma monga mkaidi, iye anayamikiranso Mulungu chifukwa cha abale amene anabwera kudzamulimbikitsa. (Mac. 28:15) Paulo anali munthu wamphamvu amene anayenda mitunda italiitali pokalalikira komanso kulimbikitsa mipingo. Komabe iye anali wodzichepetsa ndipo ankalola kuti abale ndi alongo azimuthandiza.

13. Kodi achikulire angasonyeze bwanji kuti amayamikira achinyamata?

13 Achikulirenu, mungasonyeze kuti mumayamikira achinyamata mumpingo mwanu m’njira zosiyanasiyana. Ngati akufuna kukuthandizani pankhani ya mayendedwe, kukagula zinthu kapena kuchita zinthu zina zofunika, muzilola kuti akuthandizeni. Muziona kuti zimene akuchita pokuthandizani ndi umboni wakuti Yehova amakukondani. Mukhoza kudabwa kuona kuti mwayamba kugwirizana nawo kwambiri. Muzithandiza anzanu achinyamata kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo muziwauza mmene mukusangalalira chifukwa choona kuti akuchita zambiri pothandiza mumpingo. Muzikhala ofunitsitsa kucheza nawo komanso kuwafotokozera zimene mwakumana nazo pa moyo wanu. Mukamachita zimenezi ‘mungasonyeze kuyamikira’ Yehova chifukwa cha achinyamata amene iye wawakokera mumpingo.​—Akol. 3:15; Yoh. 6:44; 1 Ates. 5:18.

MUZIKHALA OWOLOWA MANJA

14. Kodi Mfumu Davide inasonyeza bwanji kuwolowa manja?

14 Achikulire angaphunzirenso khalidwe lina lofunika kwambiri pachitsanzo cha Mfumu Davide, lomwe ndi kuwolowa manja. Iye anapereka zinthu zake zochuluka zothandiza pantchito yomanga kachisi. (1 Mbiri 22:11-16; 29:3, 4) Davide anachita zimenezi ngakhale kuti kachisiyo anadzatchulidwa kuti kachisi wa Solomo. Ngati tilibenso mphamvu moti sitingagwire nawo ntchito ya zomangamanga, tingathandize pa ntchitoyi popereka ndalama zathu mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Tingathandizenso achinyamata ndi luso lathu limene tapeza pa zaka zimene takhala tikutumikira.

15. Kodi ndi mphatso yamtengo wapatali iti imene Paulo anapatsa Timoteyo?

15 Pa nkhani ya kuwolowa manja, taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye anapempha Timoteyo kuti aziyenda naye pa maulendo a umishonale ndipo molowa manja anaphunzitsa wachinyamatayu zimene angachite kuti azilalikira komanso kuphunzitsa bwino. (Mac. 16:1-3) Zimenezi zinathandiza kuti Timoteyo azilalikira komanso kuphunzitsa mwaluso uthenga wabwino. (1 Akor. 4:17) Pamapeto pake nayenso Timoteyo ankaphunzitsa ena zimene anaphunzira kwa Paulo.

16. N’chifukwa chiyani Shigeo ankaphunzitsa anthu ena?

16 Achikulire masiku ano saopa kuti azioneka ngati osafunika, akaphunzitsa achinyamata ntchito imene iwowo ankagwira mumpingo. Mwachitsanzo, Shigeo yemwe tamutchula kale uja, kwa zaka zingapo anakhala akuphunzitsa abale achinyamata omwe ankatumikira nawo m’Komiti ya Nthambi. Iye anachita zimenezi n’cholinga chofuna kupititsa patsogolo ntchito za Ufumu m’dziko limene akutumikira. M’kupita kwa nthawi panapezeka m’bale woyenerera yemwe analowa m’malo mwake n’kupitiriza kutumikira monga wogwirizanitsa. Shigeo akupitirizabe kuphunzitsa achinyamata zomwe waphunzira pa zaka 45 zimene wakhala akutumikira m’Komiti ya Nthambi. Abale ngati amenewa amathandiza kwambiri anthu a Mulungu.

17. Mogwirizana Luka 6:38, kodi achikulire angapatse ena chiyani?

17 Abale ndi alongo achikulirenu mumapereka umboni wakuti kutumikira Yehova mokhulupirika komanso ndi mtima wosagawanika ndi kwabwino kwambiri. Chitsanzo chanu chimasonyeza kuti kuphunzira mfundo za m’Baibulo komanso kumazigwiritsa ntchito pa moyo wathu n’kothandiza kwambiri. Mumadziwa mmene zinthu zinkachitikira kalelo koma mumazindikiranso kuti n’kofunika kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi mmene zilili masiku ano. Inunso achikulire amene mwangobatizidwa kumene mungathandize ena. Mungawafotokozere mmene kudziwa Yehova kumakuthandizirani kukhala osangalala panopa ngakhale kuti ndinu achikulire. Achinyamata angasangalale kumva zimene mwakumana nazo pa moyo wanu komanso zimene mwakhala mukuphunzira. ‘Mukakhala opatsa’ kapena kuti kugawirako ena zimene zili munkhokwe yanu ya zinthu zimene mukudziwa, Yehova adzakudalitsani kwambiri.​—Werengani Luka 6:38.

18. Kodi achikulire ndi achinyamata amathandizana bwanji?

18 Ngati achikulirenu mutamachita zinthu limodzi ndi achinyamata, nonse mukhoza kumathandizana. (Aroma 1:12) Aliyense amakhala kuti ali ndi chinthu china chake chamtengo wapatali chimene wina alibe. Achikulire amadziwa zinthu zambiri komanso amakhala ndi nzeru zimene apeza pa nthawi imene akhala ndi moyo, pomwe achinyamata amakhala ndi mphamvu. Achinyamata ndi achikulire akamagwirizana n’kumachitira zinthu limodzi, amapereka ulemerero kwa Atate wathu wachikondi komanso amathandiza kwambiri mumpingo.

NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana

^ ndime 5 M’mipingo yathu muli achinyamata ambiri omwe akuyesetsa kuthandiza gulu la Yehova. Posatengera chikhalidwe chawo komanso kumene anakulira, achikulire angathandize achinyamatawa kugwiritsa ntchito mphamvu zawo zonse kutumikira Yehova.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Woyang’anira dera atakwanitsa zaka 70, iye ndi mkazi wake anapatsidwa utumiki watsopano. Zomwe anaphunzira pazaka zambiri zimene akhala akutumikira zimawathandiza kuphunzitsa ena mumpingo umene akutumikira panopa.