Beeriseba—Kumene Chitsime Chinatanthauza Moyo
Malo a ku Dziko Lolonjezedwa
Beeriseba—Kumene Chitsime Chinatanthauza Moyo
“KUYAMBIRA ku Dani mpaka ku Beeriseba.” Ameneŵa ali mawu ozoloŵereka kwa oŵerenga Baibulo. Amafotokoza Israyeli yense, kuchokera ku Dani, pafupi ndi malire akumpoto, mpaka ku Beeriseba, kummwera kwake. Mtendere wa ulamuliro wa Solomo unafotokozedwa motere: “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.”—1 Mafumu 4:25; Oweruza 20:1.
Komabe, kusiyana kwa Dani ndi Beeriseba sikunali mtunda wotalikirana wokha. Mwachitsanzo, Dani anali ndi mvula yokwanira; madzi anatumphuka kuchokera pansi ndi kupanga amodzi a magwero a mtsinje wa Yordano, monga tikuwonera pachithunzithunzi kulamanja. Beeriseba anali wosiyana chotani nanga, popeza kuti anali kuchigawo chouma, pakati pa gombe la nyanja ndi mphepete mwa kumadzulo kwa Nyanja Yakufa.
Mvula ya chaka ndi chaka inali ya mlingo wa mamilimita 150 kukafika ku 200 okha m’dera la Beeriseba. Podziŵa zimenezo, onani chithunzithunzicho cha chitunda pamwambapa, kapena chikweza cha Beeriseba. * Kubiriŵira kumene mukuwonako kumasonyeza kuti chithunzithunzichi chinajambulidwa pambuyo pa mvula yochepayo ya nyengo yachisanu, pamene kwanthaŵi yaifupi minda ya m’Beeriseba imakhala yobiriŵira. Zidikha zapafupipo zinali—ndipo zidakali—zabwino kubzalamo dzinthu.
Popeza kuti maloŵa anali ouma, nkhani za m’Baibulo zonena za Beeriseba zimagogomezera zitsime ndi umwini wa zitsimezo. Mzindawo unali pafupi ndi misewu kapena njira za aulendo zimene zinadutsa chipululu chouma kumunsi chakummwera. Yerekezerani, aulendo akudutsa kapena kuima panopa akufuna madzi awo ndi a nyama zawo. Madzi amenewo sanatumphuke kuchokera pansi, monga momwe anachitira ku Dani, koma anatungidwa pazitsime. Kwenikweni, liwu Lachihebri lakuti beʼerʹ linatanthauza mchera kapena dzenje lokumbidwa kutungamo madzi apansi. Dzina lakuti Beeriseba limatanthauza “Chitsime cha Lumbiro” kapena, “Chitsime cha Asanu ndi Aŵiri.”
Abrahamu ndi banja lake anakhala kwanthaŵi yaitali mkati ndi kunja kwa Beeriseba, ndipo iwo anadziŵa kufunika kwa zitsime. Pamene Hagara mdzakazi wa Sara anathaŵira m’chipululu, ayenera kuti anakonzekera kukapeza madzi pazitsime kapena kwa anthu Achibedouin amene anazigwiritsira ntchito—monga ngati mkazi Wachibedouin patsamba lotsatira, pamwamba, akutunga madzi pachitsime m’ndomo ya Sinai. Pambuyo Genesis 21:19.
pake pamene Abrahamu anakakamizika kuthamangitsa Hagara ndi mwana wake wovutayo, iye mokoma mtima anawapatsa madzi. Kodi iwo anatani pamene madziwo anatha? “Ndipo Mulungu anamtsegula m’maso mwake, ndipo anawona chitsime cha madzi; namuka nadzaza mchenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.”—Kodi Abrahamu anawapeza kuti madzi amene anadzaza nawo thumba la madzi la Hagara? Mwinamwake pachitsime chimene iye adaakumba, pafupi ndi pamene adawoka mtengo wabwemba. (Genesis 21:25-33) Kunganenedwe kuti asayansi tsopano akuwona chimene Abrahamu anasankhira mtengo wabwemba, chifukwa chakuti mtengowu uli ndi timasamba tating’onoting’ono timene sitimatulutsa kwambiri madzi amtengowo, chotero umakhalabe wobiriŵira mosasamala kanthu za kuuma kwa maloŵa. Onani chithunzithunzi pansipo.
Kukumba chitsime kwa Abrahamu kunatchulidwa chifukwa cha mkangano umene anakhala nawo ndi mfumu Yachifilisti. Chitsime chinali chuma chifukwa cha kuvuta kwa madzi ndi ntchito yaikulu yoloŵetsedwamo pokumba chitsime chakuya. Kwenikweni, kalelo kunali kuswa lamulo la umwini wa chinthu cha munthu ngati wina anatunga pachitsime popanda chilolezo.—Yerekezerani ndi Numeri 20:17, 19.
Ngati mungafike ku chitunda cha Beeriseba, mukhoza kusuzumira pansi pa chitsime chakuyacho kumunsi chakummwera koma kummaŵa kwake. Palibe amene adziŵa pamene chinakumbidwa kupyola nthanthwe lolimba ndi mbali yake yapamwamba (yowoneka pansipo) ndiyeno kuchirikizidwa ndi miyala. Ofukula za m’mabwinja amakono anachifukula kuya pansi mamita 30 popanda kufika pansi pake. Mmodzi wa iwo ananena kuti: “Nkosavuta kuganiza kuti chitsimechi chinali . . . ‘Chitsime cha Lumbiro’ pamene Abrahamu ndi Abimeleki anapanganira pangano lawo.”—Biblical Archaeology Review.
Mwachiwonekere, Beeriseba anakula pambuyo pake m’nyengo za m’Baibulo, nakhala mzinda wolimba ndi chipata chachikulu. Koma mfungulo ya kukhalapo kwake ndi chitukuko inali madzi ofunikawo a chitsime chake chakuya.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Onani mawonekedwe aakulu a chitunda cha Beeriseba pa Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1993.
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.