Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyenda Mwanzeru M’dzikoli

Kuyenda Mwanzeru M’dzikoli

Kuyenda Mwanzeru M’dzikoli

“Muyendere munzeru ndi iwo akunja.”​—AKOLOSE 4:5.

1. Kodi Akristu oyambirira anayang’anizana ndi chiyani, ndipo ndiuphungu wotani umene Paulo anaupereka ku mpingo wa ku Kolose?

AKRISTU oyambirira okhala m’mizinda ya dziko la Roma nthaŵi zonse anayang’anizana ndi kulambira mafano, zosangulutsa zachisembwere, ndi madzoma achikunja ndi miyambo. Mosakaikira awo okhala m’Kolose, mzinda wa kumadzulo chapakati pa Asia Minor, anayang’anizana ndi kulambira kwa mulungu wachikazi ndi kukhulupirira mizimu kwa nzika za Frugiya, nthanthi zachikunja za Agiriki amene anadzakhala m’dzikolo, ndi chipembedzo Chachiyuda cha dziko la Ayuda. Mtumwi Paulo analangiza mpingo Wachikristu ‘kuyenda mwanzeru’ kulinga kwa “akunja” oterowo.​—Akolose 4:5.

2. Kodi nchifuwa ninji Mboni za Yehova lerolino zifunikira kuyenda mwanzeru kulinga kwa akunja?

2 Lerolino, Mboni za Yehova zikuyang’anizana ndi machitachita olakwa ofananawo, ndipo ngakhale oipirapo. Motero, nazonso zimafunikira kuchita mwanzeru kulinga kwa anthu akunja kwa mpingo wowona Wachikristu. Anthu ambiri m’zipembedzo ndi m’ndale ndiponso m’zofalitsira nkhani amazitsutsa. Ena a ameneŵa, mwakuukira mwachindunji, kapena kaŵirikaŵiri mwamawu oneneza, amayesa kuipitsa mbiri ya Mboni za Yehova ndi kudzutsa malingaliro olakwa ponena za izo. Monga momwe Akristu oyambirira analingaliridwa molakwa kukhala “mpatuko” wa anthu otengeka maganizo kapena ngakhale aupandu, Mboni za Yehova lerolino kaŵirikaŵiri zili mkhole wa kulingaliridwa molakwa ndi kusamvetsetsedwa bwino.​—Machitidwe 24:14; 1 Petro 4:4.

Kugonjetsa Kulingaliridwa Molakwa

3, 4. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu owona sadzakondedwa konse ndi dziko, koma kodi nchiyani chimene tiyenera kuyesa kuchita? (b) Kodi wolemba wina analembanji ponena za Mboni za Yehova zomangidwa mumsasa wachibalo wa Nazi?

3 Akristu owona samayembekezera kukondedwa ndi dziko, limene, malinga nkunena kwa mtumwi Yohane, “ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Komabe, Baibulo limalimbikitsa Akristu kuyesayesa kukopera anthu kwa Yehova ndi kulambiridwa kwake koyera. Timachita zimenezo mwakupereka umboni mwachindunji ndi mwa makhalidwe athu abwino. Mtumwi Petro analemba kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m’mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuwona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.”​—1 Petro 2:12.

4 M’buku lake lakuti Forgive​—But Do Not Forget, wolemba Sylvia Salvesen ananena za Mboni zachikazi zimene zinali andende anzake mumsasa wachibalo wa Nazi kuti: “Aŵiri aja, Käthe ndi Margarethe, ndi ena ambiri, anandithandiza kwambiri, osati kokha mwachikhulupiriro chawo komanso m’kuchita zinthu. Iwo anatipezera nsalu zoyera zomangira zilonda zathu . . . Kunena mwachidule tinawona kuti tinali pakati pa anthu amene anatifunira zabwino, ndipo amene anasonyeza ubwenzi wawo mwa zochita zawo.” Ndiumboni wabwino chotani nanga wochokera kwa “akunja”!

5, 6. (a) Kodi ndintchito yotani imene Kristu akuichita panthaŵi ino, ndipo kodi nchiyani chimene sitiyenera kuiŵala? (b) Kodi mkhalidwe wa maganizo athu uyenera kukhala wotani kulinga kwa anthu adziko, ndipo chifukwa ninji?

5 Tingachite zochuluka kuti tichotse kulingaliridwa molakwa mwanjira yanzeru yakudzisungira kwathu kulinga kwa akunja. Zowona, tikukhala m’nthaŵi pamene Mfumu yathu yolamulira, Kristu Yesu, ikulekanitsa anthu a mitundu, “monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” (Mateyu 25:32) Koma tisaiŵale konse kuti Kristu ali Woweruza; ali iye amene amagamula kuti “nkhosa” ndani ndipo “mbuzi” ndani.​—Yohane 5:22.

6 Zimenezi ziyenera kusonkhezera mkhalidwe wathu wamaganizo kulinga kwa awo amene sali mbali ya gulu la Yehova. Tingawalingalire kukhala anthu akudziko, koma iwo ali mbali ya dziko la mtundu wa anthu limene “Mulungu anakonda . . . kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ndibwino kwambiri kulingalira anthuwo monga oyembekezeredwa kukhala nkhosa mmalo mwakudzigangira ife eni ndi kugamula kuti ali mbuzi. Ena amene kale anali otsutsa chowonadi mwachiwawa tsopano ali Mboni zodzipereka. Ndipo ambiri a iwo poyamba anakopeka ndi machitidwe a kukoma mtima, asanavomereze ulaliki uliwonse wachindunji. Mwachitsanzo, onani chithunzithunzi patsamba 18.

Achangu, Osati Oumiriza

7. Kodi papa anapereka chisulizo chotani, koma ndifunso lotani limene tingafunse?

7 Papa John Paul II anasuliza mipatuko yonse, ndipo makamaka Mboni za Yehova, pamene anati: “Changu choumiriza chimene ena akufunafuna nacho owatsatira, akumapita kunyumba ndi nyumba, kapena kuimitsa oyenda m’makwalala ndi pamphambano zanjira, chili mpatuko wachinyengo wa changu chonamizira chautumwi ndi chaumishonale.” Tikhoza kufunsa kuti, Ngati changu chathu chili “changu chonamizira chautumwi ndi chaumishonale,” kodi changu chenicheni chakulalikira chingapezeke kuti? Kunena zowona, sichingapezeke pakati pa Akatolika, osatinso pakati pa Aprotestanti kapena ziŵalo za matchalitchi a Orthodox.

8. Kodi tiyenera kuchita motani umboni wa kunyumba ndi nyumba, tikumayembekezera zotulukapo zotani?

8 Komabe, kuti titsimikiziritse bodza la chinenezo chakuti ndife oumiriza polalikira, nthaŵi zonse tiyenera kukhala okoma mtima, aulemu, ndi ofatsa pamene tifikira anthu. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Awonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.” (Yakobo 3:13) Mtumwi Paulo akutilangiza ‘kusakhala andewu.’ (Tito 3:2) Mwachitsanzo, mmalo mwakutsutsa poyera zikhulupiriro za munthu amene tikumlalikira, bwanji osasonyeza chikondwerero chowona mtima cha kufuna kumva malingaliro ake? Ndiyeno uzani munthuyo mbiri yabwino ya m’Baibulo. Mwakukhala ndi kafikidwe kabwino ndi kusonyeza ulemu kwa anthu a zikhulupiriro zina, tidzawathandiza kukhala ndi mkhalidwe wamaganizo wabwinopo wakuti amvetsere ndipo mwinamwake angawone phindu la uthenga wa Baibulo. Chotsatirapo chingakhale chakuti ena akafikira pa ‘kulemekeza Mulungu.’​—1 Petro 2:12.

9. Kodi tingagwiritsire ntchito motani uphungu umene Paulo anapereka (a) pa Akolose 4:5? (b) pa Akolose 4:6?

9 Mtumwi Paulo anapereka uphungu wakuti: “Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthaŵi ingatayike.” (Akolose 4:5) Pofotokoza mawu otsatirapo ameneŵa, J. B. Lightfoot analemba kuti: “Kusaphonya mpata uliwonse, wa kunena ndi kuchita chimene chingapititse patsogolo chifuniro cha Mulungu.” (Kanyenye ngwathu.) Inde, tiyenera kukhala okonzeka ndi mawu ndi zochita pamwaŵi uliwonse. Nzeru yoteroyo imaloŵetsamonso kusankha nthaŵi yoyenera patsiku la kufikira anthu. Ngati uthenga wathu ukanidwa, kodi nchifukwa chakuti anthu sakuuyamikira, kapena kodi nchifukwa chakuti tinawafikira panthaŵi yowonekera kukhala yosayenera? Paulo analembanso kuti: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.” (Akolose 4:6) Zimenezi zimafunikiritsa kulingalira pasadakhale ndi chikondi chenicheni kwa mnansi. Tiyeni nthaŵi zonse tipereke uthenga wa Ufumu mwachisomo.

Aulemu ndi “Okonzeka pa Ntchito Iliyonse Yabwino”

10. (a) Kodi ndiuphungu wotani umene mtumwi Paulo anapatsa Akristu okhala m’Krete? (b) Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zachitira bwino koposa m’kutsatira uphungu wa Paulo?

10 Sitingalolere molakwa pa malamulo amkhalidwe a Baibulo. Kumbali ina, sitiyenera kumakangana mosafunikira pamafunso amene saloŵetsamo umphumphu Wachikristu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Uwakumbutse iwo [Akristu m’Krete] agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino; asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale aulere, nawonetsere chifatso chonse pa anthu onse.” (Tito 3:1, 2) Katswiri wa Baibulo E. F. Scott analemba ponena za ndime imeneyi kuti: “Akristu sanangofunikira kumvera aulamuliro, koma anayenera kukhala okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino. Izi . . . zitanthauza kuti, pamene kunali kofunika, Akristu anayenera kukhala pakati pa oyambirira kusonyeza mzimu wakuthandiza anthu. Sipakakhala kubuka kwakaŵirikaŵiri kwa moto, miliri, masoka a mtundu uliwonse, ngati nzika zabwino zonse zinali ndi chifuno cha kuthandiza mnansi wawo.” Kuzungulira dziko lonse pachitika masoka ambiri ndipo Mboni za Yehova zakhala pakati pa oyamba kuchita ntchito yakuthandiza. Izo zathandiza osati abale awo okha komanso akunja.

11, 12. (a) Kodi Akristu ayenera kuchita motani kulinga kwa aulamuliro? (b) Kodi kugonjera aulamuliro kumaphatikizapo chiyani ponena za kumanga Nyumba Zaufumu?

11 Ndime imodzimodziyo ya m’kalata ya Paulo kwa Tito imagogomezeranso kufunika kwa kukhala ndi maganizo aulemu kulinga kwa olamulira. Akristu achichepere makamaka, amene chifukwa cha kaimidwe kawo kauchete amawonekera pamaso pa oweruza ayenera kukhala osamala kwambiri kuyenda mwanzeru kulinga kwa akunja. Iwo akhoza kuthandiza kwambiri kuwongolera kapena kuipitsa mbiri ya anthu a Yehova mwa mawonekedwe awo, mkhalidwe wawo, ndi mmene amalankhulira kwa aulamuliro oterowo. Ayenera ‘kupereka ulemu kwa eni ake a ulemu,’ ndi kuchita chodzikanira ndi ulemu waukulu.​—Aroma 13:1-7; 1 Petro 2:17; 3:15.

12 “Aulamuliro” amaphatikizapo akuluakulu a boma a m’dzikolo. Tsopano pokhala kuti Nyumba Zaufumu zowonjezereka zikumangidwa, kuchita ndi akuluakulu a boma kuli kosapeŵeka. Kaŵirikaŵiri, akulu amayang’anizana ndi kulingaliridwa molakwa. Koma kwadziŵika kuti kumene oimira mpingo akhazikitsa unansi wabwino ndi akuluakulu aboma ndi kugwirizana ndi bungwe losamalira mzinda, kulingaliridwa molakwa kumeneku kungathetsedwe. Kaŵirikaŵiri umboni wabwino umaperekedwa kwa anthu amene kale anadziŵa zochepa chabe kapena sanadziŵe kalikonse ponena za Mboni za Yehova ndi uthenga wawo.

‘Ngati Kutheka, Khalani ndi Mtendere ndi Onse’

13, 14. Kodi ndiuphungu wotani umene Paulo anapereka kwa Akristu a ku Roma, ndipo kodi tingaugwiritsire ntchito motani m’maunansi athu ndi akunja?

13 Paulo anapereka uphungu wotsatirawu kwa Akristu okhala m’Roma wachikunja: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW]. Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake. Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.”​—Aroma 12:17-21.

14 Muunansi wathu ndi akunja, ifeyo monga Akristu owona mosapeŵeka timakumana ndi otsutsa. M’ndime yapitayi, Paulo akusonyeza kuti njira yanzeru ndiyo kuyesayesa kugonjetsa chitsutsocho mwa machitidwe okoma mtima. Mofanana ndi makala amoto, machitidwe okoma mtima ameneŵa angasungunule chidanicho ndi kufeŵetsa maganizo a wotsutsayo kulinga kwa anthu a Yehova, mwinamwake ngakhale kudzutsa chikondwerero mwa iye cha mbiri yabwino. Pamene zimenezi zichitika, choipa chimalakidwa ndi chabwino.

15. Kodi nliti makamaka pamene Akristu ayenera kukhala osamala kuyenda mwanzeru kulinga kwa akunja?

15 Kuyenda mwanzeru kulinga kwa akunja kuli kofunika makamaka m’mabanja amene mmodzi wa muukwati sanalandirebe chowonadi. Kusunga malamulo amkhalidwe a Baibulo kumapanga amuna abwino, akazi abwino, atate abwino, amayi abwino, ndi ana omvera kwambiri ndi amene amayesayesa zolimba m’maphunziro akusukulu. Wosakhulupirira ayenera kuwona chiyambukiro chabwino cha malamulo amkhalidwe a Baibulo pa wokhulupirira. Motero, ena akhoza ‘kukodwa popanda mawu mwa mayendedwe’ a ziŵalo za banja zodzipereka.​—1 Petro 3:1, 2.

“Tichitire Onse Chokoma”

16, 17. (a) Kodi Mulungu amakondweretsedwa ndi nsembe zotani? (b) Kodi ndimotani mmene ‘tingachitire chokoma’ kwa abale athu ndiponso kwa akunja?

16 Chokoma chachikulu koposa chimene tingachitire mnansi wathu ndicho kumbweretsera uthenga wa moyo ndi kumphunzitsa za kuyanjanitsidwa ndi Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu. (Aroma 5:8-11) Motero mtumwi Paulo akutiuza kuti: “Potero mwa iye [Kristu] tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo [imene imalengeza poyera, NW] za dzina lake.” (Ahebri 13:15) Paulo akuwonjezera kuti: “Koma musaiŵale kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” (Ahebri 13:16) Kuwonjezera pa kuchitira umboni kwathu kwapoyera, sitiyenera kuiŵala ‘kuchita chokoma.’ Kuli mbali yofunika kwambiri ya nsembe zimene Mulungu amakondweretsedwa nazo.

17 Mwachibadwa, timachita zokoma kwa abale athu auzimu, amene angakhale ndi kusoŵa mwamalingaliro, mwauzimu, ndi mwakuthupi, kapena m’zachuma. Paulo anasonyeza zimenezi pamene analemba kuti: “Monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pabanja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10; Yakobo 2:15, 16) Komabe, sitiyenera kuiŵala mawuwo, “Tichitire onse chokoma.” Mchitidwe wokoma mtima kwa wachibale, mnansi, kapena mnzathu wapantchito kungathandize kwambiri kuchotsa malingaliro olakwa ndi kutsegulira mtima wa munthuyo chowonadi.

18. (a) Kodi ndimaupandu otani amene tiyenera kupeŵa? (b) Kodi tingagwiritsire ntchito motani ubwino wathu Wachikristu monga chochirikizira ntchito yathu ya umboni wapoyera?

18 Kuti tichite zimenezi, sikuti tifunikira kupanga ubwenzi wapafupi ndi akunja. Mayanjano oterowo ngaupandu kwambiri. (1 Akorinto 15:33) Ndipo tilibe cholinga chakukhala mabwenzi a dziko. (Yakobo 4:4) Koma ubwino wathu Wachikristu ungachirikize kulalikira kwathu. M’maiko ena, kukukhala kovutirapo kulankhula kwa anthu panyumba zawo. Nyumba zina nzotetezeredwa ndi zipangizo zimene zimatiletsa kukambitsirana ndi okhalamo. M’maiko otukuka, mafoni amakhala njira yabwino yolalikira nayo. M’maiko ambiri umboni wa m’khwalala ukhoza kuchitidwa. Komabe, m’maiko onse, kukhala waubwenzi, waulemu, wokoma mtima, ndi wothandiza kwa ena kumatsegula mipata ya kuchotsa kulingaliridwa molakwa ndi kupereka umboni.

Kutontholetsa Otsutsa

19. (a) Popeza kuti cholinga chathu sindicho kukondweretsa anthu, kodi tiyenera kuyembekezeranji? (b) Kodi tiyenera kuyesetsa motani kutsanzira Danieli ndi kugwiritsira ntchito uphungu wa Petro?

19 Mboni za Yehova sizili zokondweretsa anthu kapena zowopa anthu. (Miyambo 29:25; Aefeso 6:6) Izo zimazindikira bwino lomwe kuti mosasamala kanthu za kuyesayesa kwawo kukhala za chitsanzo chabwino m’kukhoma misonkho ndi kukhala nzika zabwino, otsutsa adzafalitsabe mabodza ovulaza ndi kuzineneza zoipa. (1 Petro 3:16) Podziŵa zimenezi, izo zimayesayesa kutsanzira Danieli, amene adani ake anati ponena za iye: “Sitidzamtola chifukwa chilichonse Danieli amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.” (Danieli 6:5) Sitidzalolera molakwa konse malamulo amkhalidwe a Baibulo kuti tikondweretse anthu. Kumbali ina, sitikufunafuna kufera chikhulupiriro. Tikuyesayesa kukhala mwamtendere ndi kulabadira uphungu wa mtumwi wakuti: “Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa.”​—1 Petro 2:15.

20. (a) Kodi tili okhutiritsidwa za chiyani, ndipo nchilimbikitso chotani chimene Yesu anatipatsa? (b) Kodi tingayende motani mwanzeru kulinga kwa akunja?

20 Tili okhutiritsidwa kuti kaimidwe kathu kakukhala olekana ndi dziko kali kogwirizana kotheratu ndi Baibulo. Kamachirikizidwa ndi mbiri yakale ya Akristu a m’zaka za zana loyamba. Timalimbikitsidwa ndi mawu a Yesu akuti: “M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi ine.” (Yohane 16:33) Sitichita mantha. “Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino? Komatu ngatinso mukamva zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, odala, inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhaŵa; koma mumpatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:13-15) Pamene tikuchita mwanjirayi, tidzapitirizabe kuyenda mwanzeru kulinga kwa akunja.

Kubwereza

◻ Kodi nchifukwa ninji Mboni zimafunikira kuyenda mwanzeru kulinga kwa akunja?

◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu owona sangayembekezere konse kukondedwa ndi dziko, koma kodi iwo ayenera kuyesa kuchitanji?

◻ Kodi tiyenera kukhala ndi mkhalidwe wamaganizo wotani kulinga kwa anthu a dziko, ndipo chifukwa ninji?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera ‘kuchitira chokoma’ osati abale athu okha komanso akunja?

◻ Kodi kuyenda kwathu mwanzeru kulinga kwa akunja kungatithandize motani m’ntchito yathu yolalikira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kumanzere: Akristu owona m’Falansa akuthandiza anansi awo pambuyo pa kusefukira kwa madzi

[Chithunzi patsamba 20]

Machitidwe Achikristu okoma mtima angathandize kwambiri kuthetsa kulingaliridwa molakwa

[Chithunzi patsamba 23]

Akristu ayenera ‘kukhala okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino’