Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Timafunikira Gulu Lolinganizidwa la Yehova

Timafunikira Gulu Lolinganizidwa la Yehova

Timafunikira Gulu Lolinganizidwa la Yehova

KODI munamvapo wina akuti, “Ndimakhulupirira mwa Mulungu koma osati mugulu la chipembedzo?” Malingaliro ofananawo amanenedwa kaŵirikaŵiri ndi anthu omwe poyamba anali akhama kupita ku tchalitchi koma analefulidwa chifukwa cha kulephera kwa chipembedzo chawo kukwaniritsa zofunika zawo zauzimu. Ngakhale anakhumudwitsidwa ndi magulu achipembedzo alionsewo, ambiri amaumirirabe kuti amafuna kulambira Mulungu. Komabe, iwo amakhulupirira kuti ndi bwino kumulambira, m’njira yawoyawo kusiyana ndi kumulambira mogwirizana ndi tchalitchi kapena gulu linalake.

Kodi Baibulo limanenanji? Kodi Mulungu amafuna kuti Akristu azigwirizana ndi gulu?

Akristu Oyambirira Anapindula mwa Kupanga Gulu Lolinganizidwa

Pa Pentekoste wa 33 C.E., Yehova anatsanulira mzimu wake woyera, osati pa okhulupirira ena oŵerengeka, koma pa gulu la amuna ndi akazi amene anali pamodzi “pa malo amodzi,” amene anali m’chipinda chapamwamba mu mzinda wa Yerusalemu. (Machitidwe 2:1) Panthaŵiyo, mpingo wachikristu, umene unadzakhala gulu lolinganizidwa la padziko lonse, unapangidwa. Ichi chinaoneka kukhala dalitso lalikulu kwa ophunzira oyambirira amenewo. Chifukwa chiyani? Choyamba anapatsidwa ntchito yofunikira​—ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu imene pamapeto pake idzakhala itachitidwa “padziko lonse lapansi.” (Mateyu 24:14) Mu mpingowo, otembenuka achatsopano ankatha kuphunzira kulalikira kuchokera kwa okhulupirira anzawo amene anali ozoloŵera kale kulalikirako.

Posakhalitsa uthenga wa Ufumu unafalikira kunja kwa Yerusalemu. Pakati pa 62 ndi 64 C.E., mtumwi Petro analemba kalata yoyamba kwa Akristu omwe ‘anabalalikira ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya,’ madera onseŵa ali m’dziko limene lero likutchedwa Turkey. (1 Petro 1:1) Kunalinso okhulupirira ku Palestina, Lebano, Suriya, Kupro, Girisi, Krete ndi ku Italiya. Ngati momwe Paulo analembera kwa Akolose mu 60-61 C.E., uthenga wabwino unali ‘utalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’​—Akolose 1:23.

Ubwino wina wachiŵiri wosonkhana ndi gulu unali chilimbikitso chimene Akristu anali kupatsana. Mwa kugwirizana ndi mpingo, Akristu ankamva nkhani zosonkhezera, kuphunzira Malemba Opatulika limodzi, kuuzana zokumana nazo zolimbikitsa, ndi kupemphera pamodzi ndi okhulupirira anzawo. (1 Akorinto, chaputala 14) Ndipo amuna ofikapo anali ‘kuweta gulu la Mulungu.’​—1 Petro 5:2.

Ngati anthu a mu mpingowo, Akristu analinso kudziŵana ndiponso anali kukondana. M’malo modzimva kukhala otsenderezedwa chifukwa cha kugwirizana ndi mpingo, Akristu oyambirira anali kumangiriridwa komanso kulimbikitsidwa nawo.​—Machitidwe 2:42; 14:27; 1 Akorinto 14:26; Akolose 4:15, 16.

Chifukwa china chomwe mpingo wogwirizanitsidwa wapadziko lonse, kapena gulu lolinganizidwa, unali kufunikira chinali kuchirikiza umodzi. Akristu anaphunzira ‘kunena chimodzimodzi.’ (1 Akorinto 1:10) Izi zinali zofunika. Anthu a mu mpingowo anali ophunzira mosiyanasiyana ndiponso anali osiyanasiyana pa chikhalidwe. Ankalankhula zinenero zosiyanasiyana, ndipo nawonso sanali ndi maumunthu ofanana. (Machitidwe 2:1-11) Nthaŵi zina, panalidi kusiyana kwenikweni pa kalingaliridwe kawo. Komabe, Akristu anathandizidwa kuthetsa kusiyanaku mu mpingo.​—Machitidwe 15:1, 2; Afilipi 4:2, 3.

Mafunso ovuta omwe sakanathetsedwa ndi akulu pampingo anali kuwatumiza kwa oyang’anira oyendayenda ofikapo, monga ngati Paulo. Nkhani zofunika kwambiri za chiphunzitso ankazipereka ku bungwe lolamulira lokhala mu Yerusalemu. Bungwe lolamulira poyamba linapangidwa ndi atumwi a Yesu Kristu okha koma pambuyo pake linafutukulidwa n’kuphatikizapo akulu a mpingo wa mu Yerusalemu. Mpingo uliwonse unkazindikira udindo wopatsidwa ndi Mulungu wa bungwe lolamulira ndi oliimira polinganiza utumiki, kusankha amuna pa maudindo autumiki, ndi kusankha chochita pa nkhani zachiphunzitso. Pamene nkhani inathetsedwa ndi bungwe lolamulira, mipingo inkavomereza chosankhacho ndipo “anakondwera chifukwa cha chisangalatso chake.”​—Machitidwe 15:1, 2, 28, 30, 31.

Inde, Yehova anagwiritsa ntchito gulu lolinganizidwa mu zaka za zana loyamba. Koma bwanji lerolino?

Timafunikira Gulu Lolinganizidwa Lerolino

Mofanana ndi anzawo a mu zaka za zana loyamba, Mboni za Yehova lerolino siziona mopepuka ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Imodzi mwa njira zimene zimachitira ntchitoyi ndi kugaŵira mabaibulo komanso zothandizira kuphunzira Baibulo, zomwe zimafuna gulu lolinganizidwa.

Zofalitsa zachikristu ziyenera kukonzedwa bwino, kupendedwa mosamalitsa kuti zili zolondola, kuzisindikiza, ndiyeno n’kutumizidwa ku mipingo. Pambuyo pake Akristu paokha ayenera kudzipereka kuti akapereke mabukuwo kwa anthu ofuna kuwaŵerenga. Uthenga wa Ufumu wafikira anthu mamiliyoni mu njirayi. Ofalitsa a uthenga wabwino amayesetsa kuchita ntchito yawo yolalikira mwadongosolo, kuonetsetsa kuti sakungogwira ntchito mbali imodzi ya gawo lawo pamene akunyalanyaza mbali zina. Zonsezi zimafuna gulu lolinganizidwa.

Popeza “Mulungu alibe tsankhu,” mabaibulo ndi mabuku ozikidwa pa Baibulo ayenera kutembenuzidwa. (Machitidwe 10:34) Tsopano magazini ino ili mu zinenero 132, ndipo inzake, Galamukani! ikufalitsidwa mu zinenero 83. Zimenezi zimafuna magulu olinganizidwa bwino otembenuza padziko lonse lapansi.

Anthu a mu mpingo amalandira chilimbikitso pamene amafika pa misonkhano yachikristu ya mpingo ndiponso ikuluikulu. Kumeneko amamva nkhani za Baibulo zosonkhezera, amaphunzira Malemba pamodzi, amauzana zokumana nazo zolimbikitsa, ndiponso kupemphera limodzi ndi olambira nawo anzawo. Ndipo monga abale awo a mu zaka za zana loyamba, amasangalala ndi kuchezera kolimbitsa chikhulupiriro kwa oyang’anira oyendayenda achikondi. Choncho Akristu lerolino amapanga “gulu limodzi, mbusa mmodzi.”

Indetu, Mboni za Yehova ndi zopanda ungwiro, mofanana ndi mmene anzawo oyambirira analili. Komabe zimayesetsa kugwira ntchito pamodzi. Ndiye zotsatira zake n’zakuti ntchito yolalikira Ufumu ikukwaniritsidwa kuzungulira dziko lonse lapansi.​—Machitidwe 15:36-40; Aefeso 4:13.

[Chithunzi patsamba 31]

Akristu lerolino amapanga “gulu limodzi, mbusa mmodzi”