“Dikirani”
“Dikirani”
“Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.”—MATEYU 24:42.
1. Kodi atumiki a Yehova amene am’tumikira kwanthaŵi yaitali amamva bwanji za zaka zawo zambirimbirizo za muutumiki wodzipatulira? Tchulani chitsanzo.
ATUMIKI ochuluka a Yehova amene am’tumikira kwa nthaŵi yaitali, anaphunzira choonadi adakali anyamata ndi atsikana. Mofanana ndi wamalonda uja amene anapeza ngale yamtengo wapatali kwambiri nagulitsa zonse anali nazo kuti agule ngaleyo, ophunzira Baibulo achidwi amenewo anadzipereka okha ndipo anapatulira miyoyo yawo kwa Yehova. (Mateyu 13:45, 46; Marko 8:34) Kodi amamva bwanji akamaganiza zoti adikira kwa nthaŵi yaitali kuposa mmene ankaganizira kuti aone zifuno za Mulungu zikukwaniritsidwa padziko lapansi? Sakudandaula! Iwo amavomerezana ndi Mbale A. H. Macmillan, amene patapita zaka pafupifupi 60 ali muutumiki wodzipatulira kwa Mulungu, anati: “Tsopano ndine wotsimikiza mtima kwambiri kuposa ndi kale lonse kuti chikhulupiriro changachi ndichigwiritsitsabe. Chandipangitsa kusangalala ndi moyo. Chikundithandizabe kudikira zam’tsogolo mosaopa kalikonse.”
2. (a) Kodi ndi uphungu wa panthaŵi yake wotani umene Yesu anapatsa otsatira ake? (b) Kodi tidzakambirana mafunso otani m’nkhani ino?
2 Nanga inuyo? Popanda kuganizira za msinkhu wanu, talingalirani mawu a Yesu akuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” (Mateyu 24:42) Mawu ochepa amenewo ali ndi choonadi chofunika zedi. Sitikudziŵa tsiku limene Ambuye adzafika kudzaweruza dongosolo loipali, ndiponso sitikufunikira kudziŵa. Koma moyo wathu uyenera kukhala woti akadzafika, tisadzadandaule. Pamenepa, kodi tikupezamo zitsanzo zotani m’Baibulo zimene zidzatithandiza kudikirabe? Kodi Yesu anasonyeza motani kufunika kwa kudikirako? Ndipo tili ndi umboni wanji lerolino wosonyeza kuti tilidi m’masiku otsiriza a dziko losaopa Mulunguli?
Chitsanzo Chochenjeza
3. Kodi anthu ambiri lerolino amafanana motani ndi anthu a m’tsiku la Nowa?
3 Anthu lerolino amafanana kwambiri ndi amuna ndi akazi a m’tsiku la Nowa. Dziko lapansi panthaŵi imeneyo linadzaza ndi chiwawa, ndipo malingaliro onse a m’mitima ya anthu anali ‘oipabe okhaokha.’ (Genesis 6:5) Ambiri anali otanganitsidwa ndi zochita zatsiku ndi tsiku za m’moyo. Koma asanadzetse Chigumula chachikulucho, Yehova anapatsa anthu mpata woti alape. Anatuma Nowa kuti alalikire, ndipo Nowa anamvera, natumikira monga “mlaliki wa chilungamo” mwina kwa zaka 40 kapena 50 kapena kuposapo. (2 Petro 2:5) Komabe, anthu ananyalanyaza uthenga wochenjeza wa Nowa. Sanadikire. Chotero pomalizira pake, Nowayo ndi banja lake ndi okhawo amene anapulumuka chiweruzo chimene Yehova anapereka.—Mateyu 24:37-39.
4. Kodi tinganene kuti ulaliki wa Nowa unali ndi phindu m’lingaliro lotani, ndipo n’chifukwa chiyani tinganenenso zomwezo pantchito yanu yolalikira?
4 Kodi utumiki wa Nowa unali ndi phindu? Musaweruze mwa kungoona chiŵerengero chochepacho cha anthu amene anamvera. Ndithudi, kulalikira kwa Nowa kunakwaniritsa cholinga chake mosasamala kanthu kuti ochuluka sanamvere. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kunapatsa anthu mpata wokwanira wosankha kutumikira Yehova kapena ayi. Nanga bwanji za gawo lanu lolalikiramo? Ngakhale kuti si ambiri amene akulabadira, mukukhozabe kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mwa kulalikira, mukulengeza chenjezo la Mulungu, chotero mukukwaniritsa ntchito imene Yesu anapatsa otsatira ake.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Kunyalanyaza Aneneri a Mulungu
5. (a) Kodi mikhalidwe inali yotani m’Yuda m’tsiku la Habakuku, ndipo kodi anthu anauona motani uthenga wake waulosi? (b) Kodi anthu a m’Yuda anachitira motani nkhanza aneneri a Yehova?
5 Zaka mazana ambiri pambuyo pa Chigumula, ufumu wa Yuda unaloŵa m’mavuto aakulu. Kulambira mafano, chisalungamo, kuponderezana, ngakhalenso mbanda zinali zofala. Yehova anadzutsa Habakuku kuti achenjeze anthu kuti ngati salapa, iwo adzaona tsoka ndipo adzagwera m’manja mwa Akasidi, kapena kuti Ababulo. (Habakuku 1:5-7) Koma anthu anakana kumva. Mwina ankaganiza kuti: ‘Ha, zaka zoposa zana limodzi zapitazo, mneneri Yesaya nayenso anaperekanso chenjezo lofananalo, koma palibe chimene chachitikapo, n’chimodzi chomwe!’ (Yesaya 39:6, 7) Akuluakulu ambiri a m’dziko la Yuda sanali chabe opanda chidwi ndi uthengawo komanso ankachitira nkhanza amithengawo. Nthaŵi inayake, anayesa kupha mneneri Yeremiya, ndipo akanamuphadi chikhala kuti Ahikamu sanaloŵererepo. Atakwiya chifukwa cha uthenga winanso waulosi, Mfumu Yehoyakimu anapha mneneri Uriya.—Yeremiya 26:21-24.
6. Kodi Yehova anam’limbikitsa motani Habakuku?
6 Uthenga wa Habakuku nawonso unali wosapita m’mbali ndipo unalinso wonyansa kwa anthuwo mofanana ndi wa Yeremiya, amene Mulungu anamuuzira kulosera kuti Yuda adzakhala wabwinja zaka 70. (Yeremiya 25:8-11) Chotero, titha kumvetsa nkhaŵa ya Habakuku pamene anafuula kuti: “Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva inu? Ndifuulira kwa inu za chiwawa, koma simupulumutsa.” (Habakuku 1:2) Yehova anayankha Habakuku mokoma mtima ndi mawu olimbitsa chikhulupiriroŵa akuti: “Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:3) Chotero Yehova anali ndi “nyengo yoikidwiratu” yodzathetsa kusalungama ndi kuponderezana. Ngati nyengoyo ikanaoneka kuti ikuchedwa, Habakuku sanayenere kutaya mtima, ndipo sanayenerenso kugwa ulesi. M’malo mwake, anayenera ‘kulindirira,’ kuchita changu tsiku lililonse. Tsiku la Yehova linali kudzafika mosazengereza!
7. N’chifukwa chiyani Yerusalemu anayenera kuwonongedwanso m’zaka za zana loyamba C.E.?
7 Patapita zaka 20 kuchokera pamene Yehova anayankhula ndi Habakuku, Yerusalemu, likulu la Yuda, Luka 21:20, 21.
linawonongedwa. Kenako linadzamangidwanso, ndipo zolakwa zambiri zomwe zinasoŵetsa mtendere Habakuku zinawongoleredwa. Komabe, m’zaka za zana loyamba C.E., mzindawo unaikidwanso chizindikiro kuti uyenera kuwonongedwa chifukwa cha kusakhulupirika kwa okhalamo ake. Mwachifundo, Yehova analinganiza kuti anthu owongoka mtima adzapulumuke. Nthaŵi ino, sanagwiritse ntchito mneneri winanso kusiyapo Yesu Kristu kuti apereke uthengawo. Mu 33 C.E., Yesu anauza otsatira ake kuti: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri.”—8. (a) Kodi Akristu ena ayenera kuti anachitanji m’kupita kwa nthaŵi pambuyo pa imfa ya Yesu? (b) Kodi mawu a Yesu olosera za Yerusalemu anakwaniritsidwa motani?
8 Pamene zaka zinali kupita, Akristu ena m’Yerusalemu ayenera kuti anasinkhasinkha za nthaŵi imene ulosi wa Yesu udzakwaniritsidwa. Eetu, tangoganizirani kudzimana kumene mosakayikira ena a iwo anali atapanga. Mwina anali atanyalanyaza malonda opezetsa phindu kwambiri pofunitsitsa kukhalabe akudikira. M’kupita kwa nthaŵi, kodi iwo anatopa? Kodi anafika poganiza kuti akungotaya nthaŵi, kulingalira kuti mawu a Yesu anali kunena za mbadwo wam’tsogolo, osati mbadwo wawo? Mu 66 C.E., ulosi wa Yesu unayamba kukwaniritsidwa pamene magulu ankhondo a Roma anazinga Yerusalemu. Awo amene anali kudikira anazindikira chizindikirocho, ndipo anathaŵamo mumzindawo ndi kupulumuka pamene Yerusalemu anawonongedwa.
Kusonyeza Kufunika kwa Kudikira
9, 10. (a) Kodi mungalongosole motani mwachidule fanizo la Yesu la akapolo amene anali kudikira mbuye wawo kuti abwereko ku ukwati wake? (b) N’chifukwa chiyani kudikira mbuye wawo kuyenera kuti kunali kovuta kwa akapolowo? (c) N’chifukwa chiyani kuleza mtima kunali kopindulitsa kwa akapolowo?
9 Pogogomeza kufunika kwa kudikira, Yesu anayerekeza ophunzira ake ndi akapolo amene akudikira ambuye wawo kuti abwereko ku ukwati wawo. Iwo ankadziŵa kuti adzabwerako usiku winawake—koma panthaŵi yanji? Pa ulonda woyamba wausiku? Pa ulonda wachiŵiri? Wachitatu? Sanali kudziŵa. Yesu anati: “[Mbuyeyo] akadza ulonda wachiŵiri, kapena wachitatu, nakawapeza [akudikira], odala ameneŵa.” (Luka 12:35-38) Tangolingalirani mmene akapoloŵa anakhalira chire. Mitima yawo inali kugunda akangomva kuti tswele! Akangoona ngati kuti kukubwera munthu iwo anali kungoti: ‘Kodi ameneyu si mbuye wathu?
10 Kodi bwanji mbuyeyo akanabwera usiku pa ulonda wachiŵiri, umene unali kuyamba 9 koloko mpaka pakati pa usiku? Kodi akapolo onse, ngakhalenso awo amene analimbikira kugwira ntchito kuyambira m’maŵa, akanakhala okonzeka kum’lonjera, kapena kodi ena akanakhala atagona? Nanga bwanji mbuyeyo akanabwerako pa ulonda wachitatu usiku, nthaŵi yoyambira pakati pa usiku kufika cha m’ma 3 koloko m’maŵa? Kodi akapolo ena akanataya mtima, n’kuyambanso kudandaula chifukwa choona ngati kuti mbuye wawo wachedwa? * Okhawo amene mbuyeyo akanapeza akum’dikira pamene akufika ndi amene anali kudzatchedwa odala. Kwa iwo mawu a pa Miyambo 13:12 adzagwiradi ntchito. Mawuwo amati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.”
11. Kodi pemphero lingatithandize motani kudikira?
11 Pamene nthaŵi idzakhala ikuoneka ngati ikuchedwa, kodi n’chiyani chikanathandiza otsatira a Yesu kukhalabe akudikira? Pamene anali m’munda wa Getsemane kutangotsala pang’ono kuti amangidwe, Yesu anauza atatu mwa atumwi ake kuti: “Khalani maso ndipo pempherani kosaleka, kuti musaloŵe m’chiyeso.” (Mateyu 26:41, NW) Patapita zaka zingapo, Petro, amene analipo pachochitikacho, anapatsa Akristu anzake uphungu umodzimodziwo. Analemba kuti: “Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m’mapemphero.” (1 Petro 4:7) Ndithudi, mapemphero ochokera pansi pa mtima ayenera kukhala mbali yachikhalire ya zochita zathu zachikristu. Inde, nthaŵi zonse tifunikira kupempha Yehova kuti atithandize kudikira.—Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17.
12. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kuyerekezera kopanda maziko ndi kudikira?
12 Onanitu kuti Petro ananenanso kuti: “Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi.” Pafupi motani? Anthu sangathe kudziŵa tsiku ndi ola lake lenileni. (Mateyu 24:36) Koma pali kusiyana pakati pa kuyerekezera kopanda maziko, kumene Baibulo siliyanja, ndi kudikira chimaliziro, kumene Baibulo limalimbikitsa. (Yerekezani ndi 2 Timoteo 4:3, 4; Tito 3:9.) Kodi njira imodzi imene tingakhalire tikudikira mapeto ndi yotani? Ndiyo mwa kutsatira mosamala umboni wosonyeza kuti chimaliziro chilidi pafupi. Tiyeni tsopano tipende maumboni asanu ndi umodzi osonyeza kuti tilidi m’masiku otsiriza a dongosolo losadziŵa Mulunguli.
Maumboni Asanu ndi Umodzi Okhutiritsa
13. Kodi ulosi wa Paulo wolembedwa pa 2 Timoteo chaputala 3 umakutsimikizirani motani kuti tikukhaladi mu “masiku otsiriza”?
13 Umboni woyamba, tikuona bwino lomwe kukwaniritsidwa kwa ulosi wa mtumwi Paulo wonena za “masiku otsiriza.” Paulo analemba kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe achipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule. Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.” (2 Timoteo 3:1-5, 13) Kodi sitikuona kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu m’tsiku lathu? Okhawo amene mwadala sakufuna kuona zenizenizi ndi amene angakane! *
14. Kodi mawu a pa Chivumbulutso 12:9 onena za Mdyerekezi akukwaniritsidwa motani lerolino, ndipo n’chiyani chidzam’chitikira posachedwapa?
14 Wachiŵiri, tikuona zotsatira za kuchotsedwa kwa Satana ndi ziŵanda zake kumwamba, kukwaniritsa Chivumbulutso 12:9. Pamenepo, timaŵerenga kuti: “Chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.” Zimenezi zinayambitsa tsoka lalikulu padziko lapansi. Ndithudi, anthu aona masoka ambiri, makamaka chiyambire 1914. Koma ulosi wa m’Chivumbulutso ukuwonjezapo mfundo yakuti pamene Mdyerekezi akuponyedwa padziko lapansi, iye akudziŵa kuti “kam’tsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Panthaŵi imeneyi, Satana akumenya nkhondo ndi otsalira odzozedwa a Kristu. (Chivumbulutso 12:17) Taonadi zotsatira za nkhondo yake pa anthuŵa m’nthaŵi yathu. * Komabe, posachedwapa, Satana adzatsekeredwa m’phompho kuti “asanyengenso amitundu.”—Chivumbulutso 20:1-3.
15. Kodi Chivumbulutso 17:9-11 chikusonyeza umboni wotani wakuti tikukhala m’nthaŵi ya chimaliziro?
15 Wachitatu, tikukhala m’nthaŵi ya “mfumu” yachisanu ndi chitatu komanso yomaliza yotchulidwa mu ulosi wolembedwa pa Chivumbulutso 17:9-11 (Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono). Pamenepa mtumwi Yohane anatchulapo mafumu asanu ndi aŵiri, oimira maulamuliro asanu ndi aŵiri amphamvu padziko lonse—Igupto, Asuri, Babulo, Amedi ndi Aperisi, Girisi, Roma, ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Anaonanso “mfumu yachisanu ndi chitatu” yomwe ili “imodzi ya mafumu asanu ndi aŵiri aja.” Mfumu yachisanu ndi chitatu imeneyi, mfumu yomaliza imene Yohane anaona, tsopano imaimira bungwe la United Nations. Yohane ananena kuti mfumu yachisanu ndi chitatu imeneyi “ipita kukawonongeka,” ndipo pambuyo pake sipakutchulidwa mafumu ena alionse a padziko lapansi. *
16. Kodi zochitika zokwaniritsa loto la Nebukadinezara la fano zikusonyeza motani kuti tili m’masiku otsiriza?
Danieli 2:36-43) Mbali zinayi zachitsulo za fanolo zikuimira maulamuliro osiyanasiyana amphamvu padziko lonse, kuyambira kumutu (Ufumu wa Babulo) mpaka kumapazi ndi zala zakumiyendo (maboma amene akulamulira lerolino). Maulamuliro onse amphamvu padziko lonse ophiphiritsidwa m’fanolo anaonekera kale. Tikukhala m’nthaŵi yophiphiritsidwa ndi mapazi a fanolo. Sipakutchulidwa kuti padzakhalanso maulamuliro amphamvu ena. *
16 Umboni wachinayi, tikukhala m’nthaŵi yophiphiritsidwa ndi mapazi a fano la m’loto la Nebukadinezara. Mneneri Danieli anamasulira loto lodabwitsa limeneli la fano lalikulu la munthu. (17. Kodi ntchito yathu yolalikira Ufumu ikupereka motani umboni winanso wakuti tili m’masiku otsiriza?
17 Umboni wachisanu ndi wakuti, tikuona ntchito yolalikira ikuchitika padziko lonse, zimene Yesu ananena kuti zidzachitika dongosolo loipa lilipoli litangotsala pang’ono kutha. Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Lero, ulosi umenewo ukukwaniritsidwa pamlingo waukulu kuposa kale lonse. Zoonadi, padakali madera ena amene sanalandirebe uthengawo, ndipo mwina panthaŵi yoikika ya Yehova, khomo lalikulu la kuntchito yaikulu lidzatseguka. (1 Akorinto 16:9) Komabe, Baibulo silinanenepo kuti Yehova adzadikira mpaka munthu wina aliyense padziko lapansi atalalikidwa mwachindunji. M’malo mwake, uthenga wabwino uyenera kulalikidwa kufikira Yehova atakhutira. Ndiyeno chidzafika chimaliziro.—Yerekezani ndi Mateyu 10:23.
18. Mwachionekere, kodi zinthu zidzakhala motani kwa odzozedwa ena pamene chisautso chachikulu chidzayamba, ndipo tikudziŵa motani?
18 Wachisanu ndi chimodzi, chiŵerengero cha otsatira a Kristu odzozedwadi chikuchepa, ngakhale kuti mwachionekere ena adzakhalabe padziko lapansi pompano pamene chisautso chachikulu chidzayamba. Otsalira ochuluka ndi achikulire, ndipo m’kupita kwa zaka chiŵerengero cha awo amene ali odzozedwadi chakhala chikuchepa. Komabe, ponena za chisautso chachikulu, Yesu anati: “Akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.” (Mateyu 24:21, 22) Chotero, zikuoneka kuti ena mwa “osankhidwawo” a Kristu adzakhala adakali padziko lapansi pompano mmene chisautso chachikulu chizidzayamba. *
Kodi Kutsogoloku Kuli Chiyani?
19, 20. N’chifukwa chiyani inoyi ndiyo nthaŵi yomwe tikufunikira kwambiri kukhala maso ndi kudikira kuposa kale lonse?
19 Kodi kutsogoloku tidzaona zotani? Kudzachitikabe zinthu zochititsa chidwi. Paulo anachenjeza kuti “tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.” Ponena za anthu ooneka ngati odziŵa bwino zochitika za anthu, iye anati: “Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera.” Chotero, Paulo analimbikitsa oŵerenga ake kuti: “Tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.” (1 Atesalonika 5:2, 3, 6) Indedi, awo amene akuyang’ana ku mabungwe a anthu kuti ndiwo adzadzetsa mtendere ndi chisungiko akunyalanyaza choonadi. Anthu oterowo ali mtulo tofa nato!
20 Chiwonongeko cha dongosolo lino la zinthu chidzabwera modzidzimutsa zedi. Chotero, dikirani tsiku la Yehova. Mulungu iyemwini anauza Habakuku kuti: ‘Silidzazengereza’! Ndithudi, inoyi ndiyo nthaŵi imene tikufunikira kwambiri kudikira kuposa kale lonse.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Mbuyeyo sanapangane ndi akapolo akewo za nthaŵi yeniyeni imene adzabwerako. Chotero, sanafunikire kulongosola zochita zake zonse, komanso sanafunikire kulongosolera akapolo ake chifukwa chimene wafikira panthaŵi yooneka ngati yochedwa imeneyo.
^ ndime 13 Ngati mukufuna mafotokozedwe atsatanetsatane a ulosiwu, onani mutu 11 m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
^ ndime 14 Kuti mumve zambiri, onani masamba 180-6 m’buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
^ ndime 15 Onani Revelation—Its Grand Climax At Hand!, masamba 251-4.
^ ndime 16 Onani mutu 4 m’buku lakuti Pay Attention to Daniel’s Prophecy!, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
^ ndime 18 M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Mwana wa munthu akufika muulemerero wake panthaŵi ya chisautso chachikulu nakhala pansi kuti apereke chiweruzo. Akuweruza anthu pamaziko akuti kaya anachirikiza abale a Kristu odzozedwa kapena ayi. Maziko oweruzirapo anthu ameneŵa angakhale opanda pake zitakhala kuti podzafika nthaŵi yachiweruzoyo, abale onse a Kristu adzakhala kuti anachokapo kalekale padziko lapansi.—Mateyu 25:31-46.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi ndi zitsanzo za m’Malemba ziti zimene zingatithandize kudikira?
• Kodi Yesu anasonyeza motani kufunika kwa kudikira?
• Kodi ndi maumboni asanu ndi umodzi ati amene amasonyeza kuti tilidi m’masiku otsiriza?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 9]
A. H. Macmillan anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka pafupifupi makumi asanu ndi limodzi
[Chithunzi patsamba 10]
Yesu anayerekeza ophunzira ake ndi akapolo amene akudikira