Kodi Mumadziona Motani?
Kodi Mumadziona Motani?
ANALI munthu wonyada. Popeza anapatsidwa malo apamwamba m’boma, anakondetsa kutamandidwa ndi kupatsidwa ulemu. Koma mkulu wina anakana kum’patsa ulemu woterowo ndipo iye anawawidwa mtima. Pobwezera, mkulu wonyada ameneyu anakonza chiwembu chowononga anthu onse a mu ufumu umenewo omwe anali a fuko la munthu wolakwayo. Ndithudi anali ndi malingaliro opotoka zedi onyada!
Analinganiza chiwembuyo anali Hamani, mkulu wa boma m’khoti la Mfumu Ahaswero ya Perisiya. Nanga mdani wake anali yani? Myuda wotchedwa Moredekai. Ngakhale kuti chiwembu cha Hamani chofuna kupha fuko lonse chinali chonyanyira, chikusonyeza ngozi ndiponso zotsatira zoipa za kunyada. Mzimu wake wonyadawo sunangodzetsera ena mavuto basi komanso unam’chititsa manyazi pagulu ndipo potsirizira pake unam’dzetsera imfa.—Estere 3:1-9; 5:8-14; 6:4-10; 7:1-10.
Alambiri Oona Sali Otetezereka ku Kunyada
Yehova amafuna kuti ‘tiyende modzichepetsa ndi Mulungu wathu.’ (Mika 6:8) M’Baibulo muli nkhani zosiyanasiyana za anthu amene analephera kudziona moyenera. Zoterezi zinawabweretsera mavuto ndi chisoni. Kupenda zina mwa zitsanzo zimenezi kungatithandize kuona kupanda nzeru ndi kuipa kwa kusalingalira bwino.
Malingaliro a mneneri wa Mulungu Yona sanali oyenera kotero kuti anathaŵa pamene Mulungu anamuuza kuchenjeza anthu oipa a ku Nineve za chiweruzo cha Yehova. (Yona 1:1-3) Pambuyo pake, pamene ntchito yake yolalikira inapita patsogolo ndiponso a Nineve atalapa, Yona anapsa mtima. Ankangosamala za mbiri yake monga mneneri, mwakuti miyoyo ya anthu ambiri a ku Nineve sinali kum’detsa nkhaŵa kapena analibe nayo ntchito. (Yona 4:1-3) Ngati tisamala kwambiri za ife eni, kukakhala kovuta kukhala wopanda tsankho ndiponso kudziŵa bwinobwino malingaliro a anthu ndi zochitika m’dera lathu.
Lingaliraninso Uziya, amene anali mfumu yabwino ya Yuda. Pamene anayamba kusalingalira bwino, anayesa kulanda maudindo ena aunsembe modzikuza. Zochita zake zosayenera ndi zosasamala enazo, zinawonongetsa thanzi lake ndi kum’tayitsa chiyanjo cha Mulungu.—2 Mbiri 26:3, 16-21.
Kusalingalira bwino kunangotsala pang’ono kutchera msampha atumwi a Yesu. Anayamba kusamala kwambiri ulemerero ndi ukulu wa iwo eni. Pamene nthaŵi ya chiyeso chachikulu inafika, anam’thaŵa Yesu. (Mateyu 18:1; 20:20-28; 26:56; Marko 9:33, 34; Luka 22:24) Kusalingalira kwawo bwino ndiponso kudzitukumula kwawo pang’onon’gono zikanawaiwalitsa chifuno cha Yehova ndi malo awo mogwirizana ndi chifuno chake.
Kuipa Kodziona Ngati Wofunika Mopambanitsa
Kudziona ngati wofunika mopambanitsa kumapweteketsa ndiponso kumawononga unansi wathu ndi ena. Mwachitsanzo, tingakhale m’chipinda ndikuona banja likunong’onezana n’kumaseka. Ngati ndife odzikonda, tidzaganiza kuti akuseka ifeyo chifukwa chakuti akulankhulana monong’ona. Maganizo athu sadzatiuza zifukwa zina zimene akuchitira zimenezo. Tingati, ‘angakhalenso akukamba za ndani’? Tingakwiye nazo mwinanso kunena kuti sitidzalilankhulanso banja limeneli. Mwanjira imeneyi kudziona ngati wofunika mopambanitsa kudzapangitsa kusagwirizana komanso kuwononga unansi wathu ndi abwenzi, a m’banja, ndi ena.
Awo amene amadziona ngati ofunika mopambanitsa angakhale a matama, nthaŵi zonse angamadzitame chifukwa cha maluso awo apamwamba, zochita zawo, kapena chuma chawo. Mwinanso amafuna kumangolankhula okha pazokambirana, nthaŵi zonse akumatchula china chake chokhudza iwowo. Malankhulidwe oterowo amasonyeza kupanda chikondi chenicheni ndiponso ndi oipa kwambiri. Choncho, nthaŵi zambiri odzikonda amadzipatula pakati pa anzawo.—Monga Mboni za Yehova, mu utumiki wathu wa poyera tinganyozedwe ndiponso kukanidwa. Tiyenera kukumbukira kuti chitsutso choterocho sakuchitira ife, koma Yehova, Mwini uthenga wathu. Komabe, malingaliro opotoka pa kufunika kwathu angakhale ndi zotsatira zoipa kwambiri. Zaka zapitazo, mbale wina yemwe analankhulidwa mosayenera ndi mwininyumba, analingalira kuti mwininyumbayo anali kunyoza iyeyo mwachindunji, ndipo mbaleyo anayankhanso zosayenera. (Aefeso 4:29) Kenaka, mbaleyo anasiyiratu kuloŵa muutumiki wa kunyumba ndi nyumba. Inde, kunyada kungatipangitse kupsa mtima pamene tikulalikira. Tiyeni tiyesetse kuti zimenezo zisachitike. M’malo mwake, tipemphe Yehova modzichepetsa kuti atithandize kupitiriza kuyamikira mwayi wochita utumiki wachikristu.—2 Akorinto 4:1, 7; 10:4, 5.
Kukhala ndi mtima wodzikuza kungatipangitse kukana uphungu wofunika kwambiri. Zaka zingapo zapitazo m’dziko la ku Central America, mnyamata wina anakamba nkhani m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase mu mpingo wachikristu. Pamene woyang’anira sukulu anam’patsa uphungu wachindunji, mnyamatayo mokwiya anaponya Baibulo lake pansi ndipo anatuluka m’Nyumba ya Ufumuyo msanga ndi cholinga chosadzabweranso. Koma patapita masiku angapo, analeka kunyadako, ndipo anakambirana ndi woyang’anira sukuluyo, ndiyeno analandira uphunguwo modzichepetsa. M’kupita kwa nthaŵi, mnyamata ameneyu anakula mwauzimu.
Kudzikuza ndi kudziona ngati wofunika mopambanitsa kungawononge unansi wathu ndi Mulungu. Miyambo 16:5 imachenjeza kuti: “Yense wonyada mtima anyansa Yehova; zoonadi sadzapulumuka chilango.”
Kudziona Moyenera
Ndithudi, sitiyenera kulingalira kuti ndife wofunika kwambiri. Komanso zimenezi sizikutanthauza kuti tisamalingalire zimene timachita ndiponso kunena. Baibulo limasonyeza kuti oyang’anira, atumiki otumikira, tingoti onse mumpingo ayenera kulingalira. (1 Timoteo 3:4, 8, 11; Tito 2:2) Choncho m’motani mmene Akristu angakulitsire ndi kupitiriza kukhala odzichepetsa, olingalira bwino ndi odziona moyenera?
Baibulo limapereka zitsanzo zolimbikitsa zambiri za anthu amene anadziona moyenera. Yesu Kristu n’chitsanzo chapadera cha kudzichepetsa. Kuti achite chifuno cha Atate ake ndi kupulumutsa mtundu wa anthu, Mwana wa Mulungu mofunitsitsa anasiya malo aulemerero kumwamba ndi kubwera pansi pano monga munthu wamba. Mosasamala kuti anachitiridwa mwano, chipongwe, ndi kufa imfa yochititsa manyazi, anakhalabe wodziletsa ndi waulemu. (Mateyu 20:28; Afilipi 2:5-8; 1 Petro 2:23, 24) Kodi Yesu anatha bwanji kuchita zimenezi? Anadalira kwambiri Yehova ndipo anali wotsimikiza mtima kuchita chifuniro cha Mulungu. Yesu anaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama, anapemphera ndi mtima wonse, ndipo anali wodzipereka kwambiri mu utumiki. (Mateyu 4:1-10; 26:36-44; Luka 8:1; Yohane 4:34; 8:28; Ahebri 5:7) Kutsatira chitsanzo cha Yesu kungatithandize kukulitsa ndi kupitiriza kukhala odziona moyenera.—1 Petro 2:21.
Onaninso chitsanzo chabwino cha Yonatani, mwana wa Mfumu Sauli. Chifukwa cha kusamvera kwa atate ake, Yonatani anataya mwayi wake wolowa ufumu m’malo mwa Sauli. (1 Samueli 15:10-29) Kodi Yonatani anapsa nazo mtima zimenezi? Kodi anamuchitira nsanje Davide, mnyamata amene anali kudzalamulira m’malo mwa iye? Ngakhale kuti Yonatani anali wokulirapo ndipo wodziŵa zambiri kuposa Davide, modzichepetsa anachita mogwirizana ndi makonzedwe a Yehova ndipo anam’chirikiza Davide mokhulupirika. (1 Samueli 23:16-18) Kudziŵa bwinobwino chifuno cha Mulungu ndiponso kufunitsitsa kuchigonjera kudzatithandiza ‘kusadziyesa koposa kumene tiyenera kudziyesa.’—Aroma 12:3.
Yesu anaphunzitsa kufunika kosonyeza kudzichepetsa. Anafanizira zimenezi mwa kunena kuti pamene ophunzira ake anali paphwando la ukwati, sanayenera ‘kuseyama pa mpando waulemu’ chifukwa mwina wina wolemekezeka kuposa iwo angabwere ndipo angadzachite manyazi pamene adzachokapo ndi kukhala pansi. Pomveketsa phunziro limeneli, Yesu anawonjezera kuti: “Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.” (Luka 14:7-11) Tidzachita bwino ngati timvera langizo la Yesu ndi ‘kuvala kudzichepetsa.’—Akolose 3:12; 1 Akorinto 1:31.
Madalitso Odziona Moyenera
Kukhala ndi mzimu wodzichepetsa kumapangitsa atumiki a Yehova kupeza chimwemwe chenicheni mu utumiki wawo. Akulu sakhala ovuta kulankhula nawo pamene modzichepetsa ‘asamalira nkhosa mwachifundo.’ (Machitidwe 20:28, 29, NW) Ndipo onse a mumpingo amaona kukhala kosavuta kulankhula nawo ndi kuwapempha thandizo. Mwanjira imeneyo mpingo umakhala wogwirizana kwambiri mu mzimu wachikondi, wachisangalalo, ndi wodalirana.
Kusadzitukumula kumatitheketsa kupanga abwenzi abwino. Kudzichepetsa kudzatipangitsa kupeŵa mzimu wopikisana ndi kudzionetsera kwa ena m’ntchito zakutizakuti kapena kudzionetsera pa zinthu zakuthupi. Mikhalidwe yaumulungu imeneyi idzatithandiza kuganizira kwambiri ena, chotero tidzakhala okhoza kutonthoza ndi kuchirikiza osoŵa. (Afilipi 2:3, 4) Pamene anthu akhudzidwa mtima ndi chikondi ndiponso kukoma mtima, nthaŵi zambiri amabwezera zabwino. Ndipo kodi si unansi wopanda dyera woterewu womwe uli maziko amene ubwenzi wolimba umamangidwapo? Ndi dalitsotu lalikulu zedi kusadzikweza!—Aroma 12:10.
Kudziona moyenera kumatipangitsanso kuvomereza cholakwa mosavuta pamene talakwira wina. (Mateyu 5:23, 24) Izi zimapangitsa kukhala ndi maunansi abwino, kuthetsa nkhani ndi kulemekezana. Ngati amene ali ndi maudindo oyang’anira, monga akulu achikristu ali odzichepetsa, angachitire ena zabwino. (Miyambo 3:27; Mateyu 11:29) Munthu wodzichepetsa adzaona kukhala kosavuta kukhululukira ena amene amulakwira. (Mateyu 6:12-15) Sadzachita mopambanitsa ndi zophophonya za ena, ndipo adzakhulupirira Yehova kuti ndiye adzakonza zinthu zimene sizingakonzeke mwa njira ina iliyonse.—Salmo 37:5; Miyambo 3:5, 6.
Madalitso aakulu amene amadza mwa kukhala wodzichepetsa ndi akuti timasangalala ndi chiyanjo komanso chikondi cha Yehova. “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Petro 5:5) Tisagweretu mu msampha woganiza kuti ndife ochita bwino kwambiri kuposa mmene tilili. M’malo mwake, modzichepetsa tizindikire malo anthu m’makonzedwe a zinthu a Yehova. Madalitso aakulu akudikira onse amene amakwanitsa ‘kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu.’
[Chithunzi patsamba 22]
Yonatani anathandiza Davide modzichepetsa