Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufalitsa Uthenga Wotonthoza ku Italy

Kufalitsa Uthenga Wotonthoza ku Italy

Ndife a Iwo Omwe Ali Ndi Chikhulupiriro

Kufalitsa Uthenga Wotonthoza ku Italy

YEHOVA ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse.” Mwa kuphunzira kum’tsanzira, atumiki ake ‘akutha kutonthoza iwo okhala m’nsautso iliyonse.’ (2 Akorinto 1:3, 4; Aefeso 5:1) Ichi ndi chimodzi cha zolinga zikuluzikulu za ntchito yolalikira imene Mboni za Yehova zikuchita.

Kuthandiza Mayi Wosauka

Makamaka m’zaka zaposachedwapa umphaŵi, nkhondo, ndi chikhumbo chofuna moyo wabwino zapangitsa ambiri kusamukira m’mayiko olemera kwambiri. Komabe sikwapafupi kuzoloŵera malo atsopano. Manjola ankakhala ndi a Albania anzake ku Borgomanero. Popeza anali kukhala ku Italy popanda chilolezo cha boma, ankaopa kulankhula ndi Wanda, amene ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Komabe, Wanda anakonza zokacheza ndi Manjola. Mofulumira anasonyeza chidwi zedi m’kuphunzira Mawu a Mulungu, ngakhale kuti kusadziŵa chinenero kunapangitsa zimenezi kukhala zovuta. Komabe, atapitako maulendo angapo, Wanda sankapezanso aliyense kumene Manjola ankakhalako. Chinachitika n’chiyani? Wanda anamva kuti onse panyumba imeneyo anathaŵa chifukwa mmodzi mwa iwo amene anali chibwenzi cha Manjola ankam’funafuna kuti am’mange chifukwa chopha munthu!

Pambuyo pa miyezi inayi, Wanda anakumananso ndi Manjola. “Ali wofooka ndiponso woonda, anaonekadi kuti anali kuvutika kwambiri,” akutero Wanda. Manjola anafotokoza kuti chibwenzi chake chakale chija chinali kundende ndiponso anzake amene amawapempha thandizo anamukhumudwitsa kwambiri. Mothedwa nzeru, anapemphera kwa Mulungu kuti am’thandize. Ndiyeno anakumbukira Wanda, amene anakamba za Baibulo. Si mmene Manjola anasangalalira pokumana nayenso!

Anayambanso kuphunzira Baibulo, mofulumira Manjola anayamba kumapezeka pamisonkhano yachikristu. Anapeza chilolezo cha boma choti akhoza kukhalabe mu Italy. Patatha chaka chimodzi, Manjola anakhala Mboni yobatizidwa. Motonthozedwa ndi malonjezo a Mulungu, anabwerera ku Albania kukauza anthu akwawo uthenga wotonthoza wa Baibulo.

Kuchitira Umboni Kumsasa wa Anthu Othaŵa Kwawo

Mipingo yambiri ku Italy inakonzapo zokachitira umboni anthu othaŵa kwawo monga Manjola. Mwachitsanzo, mpingo wa ku Florence unakonza zomapita kaŵirikaŵiri kumsasa wa anthu othaŵa kwawo. Anthu a kumsasako, ambiri ndi ochokera Kum’mawa kwa Ulaya, Makedoniya, ndi Kosovo omwe anali kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Ena anali ndi mavuto amankhwala osokoneza bongo kapena moŵa. Ambiri anali kudzithandiza okha mwa kuba.

Kulalikira m’dera limeneli kunali kovuta. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, mlaliki wanthaŵi zonse wotchedwa Paola analankhula ndi mayi wina wa ku Makedoniya wotchedwa Jaklina. Atalankhula naye kwa maulendo angapo, Jaklina analimbikitsa mnzake Susanna kusanthula Baibulo. Kenako, Susanna anauza abale ake ena. Mosakhalitsa, anthu asanu a m’banjamo anali kuphunzira Baibulo mokhazikika, kupezeka pamisonkhano, ndi kugwiritsa ntchito zimene anali kuphunzira. Mosasamala kanthu za mavuto amene anali kukumana nawo, anapeza chitonthozo kwa Yehova ndi Mawu ake.

Mviligo Apeza Chitonthozo kwa Yehova

M’tauni ya Formia, mlaliki wanthaŵi zonse wotchedwa Assunta analankhula ndi mayi wina amene anali kuyenda movutikira. Mayiyo anali mviligo m’gulu lina lachipembedzo limene limathandiza odwala ndi ofooka m’zipatala ndi m’nyumba zawo.

Assunta anati kwa mviligoyo: “Inunso mukuvutika, sichoncho kodi? N’zachisoni kuti tonse timakumana ndi mavuto.” Atatero mviligoyo analira ndipo anafotokoza kuti anali kudwala kwambiri. Assunta anamulimbikitsa mwa kumuuza kuti Mulungu wa Baibulo angam’tonthoze. Mviligoyo analandira magazini ofotokoza za Baibulo amene Assunta anam’patsa.

Pakukambirana kwawo kwachiŵiri, mviligoyo amene dzina lake linali Palmira, anavomereza kuti anali kudwaladi kwambiri. Anali atakhala kwa nthaŵi yaitali m’bungwe loyendetsedwa ndi aviligo. Atachoka kwa nthaŵi yochepa chifukwa cha kudwala, sanaloledwenso kubwererako. Mosasamala kanthu za zimenezo Palmira ankadziona kukhala ndi liwongo kwa Mulungu chifukwa cha malonjezo amene anapanga monga mviligo. Anapita kuti akalandire “machiritso” koma anali opsinjika maganizo chifukwa cha zimene zinam’chitikirazo. Palmira anavomera kuphunzira Baibulo, ndipo anapezeka pa misonkhano yachikristu kwa chaka chimodzi. Ndiyeno anasamukira kwina, ndipo Assunta sanathenso kukumana naye. Panapita zaka ziŵiri Assunta asanakumane nayenso. A m’banja lake komanso atsogoleri achipembedzo anali kum’tsutsa zedi Palmira. Komabe, anapitiriza kuphunzira Baibulo, ndipo anapita patsogolo mwauzimu, kenaka anabatizidwa monga m’modzi wa Mboni za Yehova.

Zoona, ambiri amalimbikitsidwa ndi uthenga wa ‘Mulungu wa chitonthozo.’ (Aroma 15:4, 5) N’chifukwa chake, Mboni za Yehova ku Italy zili zotsimikiza mtima kupitiriza kutsanzira Mulungu mwa kufalitsa uthenga wake wabwino kwambiri wa chitonthozo kwa ena.