Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wozunza Aona Kuunika Kwakukulu

Wozunza Aona Kuunika Kwakukulu

Wozunza Aona Kuunika Kwakukulu

SAULO anaipidwa kwambiri ndi otsatira a Yesu. Posakhutira ndi chizunzo chimene anali atawachitira kale m’Yerusalemu, kuphatikizapo kuponya miyala Stephano, tsopano anafuna zokulitsa chitsutsocho. “Wosaleka kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuwopsa ndi kupha, [Saulo] anamka kwa mkulu wa ansembe, napempha kwa iye akalata akumka nawo ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nawo omangidwa ku Yerusalemu.”​—Machitidwe 9:1, 2.

Pamene Saulo anali kupita ku Damasiko, ayenera kuti anali kulingalira za mmene adzachitira zofuna zakezo bwinobwino. Ufulu umene mkulu wa ansembe anam’patsa mosakayikira unapangitsa kuti agwirizane ndi olamulira dera lalikulu lachiyuda mu mzinda umenewo. Amene Saulo anafuna kuti am’thandize.

Kuyenera kuti Saulo anali wosangalala kwambiri pamene anali kuyandikira kumene anali kupita. Ulendo wochokera ku Yerusalemu kupita ku Damasiko unali wotopetsa kwambiri, wamakilomita pafupifupi 220 ndipo unali woyenda masiku asanu ndi aŵiri kapena asanu ndi atatu. Mwadzidzidzi chakumasana, kuunika kwakukulu koposa kwa dzuŵa kunaŵala mom’zungulira Saulo, ndipo anagwa pansi. Ndipo anamva mawu akunena kwa iye m’chilankhulo cha Chihebri akuti: “Saulo, Saulo, undilondalonderanji ine? N’kukuvuta kutsalima pachothwikira.” “Ndinu yani Mbuye?,” anafunsa motero Saulo. Ndipo anamuyankha kuti: “Ine ndine Yesu amene iwe um’londalonda. Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo iwe; ndi kukulanditsa kwa anthu, ndi kwa amitundu, amene ine ndikutuma kwa iwo.” “Ndidzachita chiyani, Ambuye?” anafunsa motero Saulo. “Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite.”​—Machitidwe 9:3-6; 22:6-10; 26:13-17.

Amene Saulo anali nawo paulendo anamva mawuwo, koma sanamuone yemwe anali kulankhula kapenanso kuzindikira zimene anali kunena. Chifukwa cha kuunika kwakukulu, Saulo atadzuka sanathe kuona ndipo anachita kum’gwira padzanja. “Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.”​—Machitidwe 9:7-9; 22:11.

Masiku Atatu Oti Alingalire

Yudasi amene anali kukhala ku khwalala lotchedwa Lolunjika anachereza Saulo. * (Machitidwe 9:11) Khwalala limeneli m’chiarabiki limatchedwa Darb al-Mustaqim mpaka pano lidakali dzina la msewu waukulu ku Damasiko. Tangolingalirani zimene Saulo anali kuganiza pamene anali kunyumba ya Yudasi. Chochitika chimenechi chinapangitsa Saulo kukhala wakhungu ndiponso wodabwa. Tsopano inali nthaŵi yoti alingalire tanthauzo lake.

Wozunzayo anakumana ndi zimene ankati zopanda pake. Ambuye Yesu Kristu yemwe anapachikidwa, amene akuluakulu achiyuda anamuona kukhala wolakwa komanso amene ‘ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu’ anali wamoyo. Inde, anaima movomerezeka padzanja lamanja la Mulungu “m’kuunika kosakhozeka kufikako”! Yesu anali Mesiya. Stefano ndi anthu ena anali kunena zoona. (Yesaya 53:3; Machitidwe 7:56; 1 Timoteo 6:16) Saulo anali kulakwa kwambiri, popeza Yesu anazidziŵikitsa yekha komanso amene Saulo anali kuwazunza ananena za iye! Popeza anaona umboni, m’motani mmene Saulo anali “kutsalima pachothwikira”? Ngakhale bulu wovuta amapita kumene mwini wa bulu afuna kuti apite. Choncho mwakukana kumvera zimene Yesu anali kufuna, Saulo akanadzipweteka yekha.

Monga Mesiya, Yesu sakanalangidwa ndi Mulungu. Koma, Yehova analola kuti afe imfa yochititsa manyazi komanso kulandira chilango cha Chilamulo chimene chimati: “Wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu.” (Deuteronomo 21:23) Yesu anafera pamtengo wozunzirapo. Anatembereredwa, osati chifukwa cha machimo ake, popeza analibe tchimo, koma chifukwa cha machimo a mtundu wa anthu. Kenako Saulo anafotokoza kuti: “Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, wotembereredwa aliyense wosakhala m’zonse zolembedwa m’buku la chilamulo, kuzichita izi. Ndipo chidziŵikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu . . . Kristu anatiwombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m’malo mwathu; pakuti kwalembedwa, wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.”​—Agalatiya 3:10-13.

Nsembe ya Yesu inali ndi mphamvu yowombola. Mwakulandira nsembe imeneyo, mophiphiritsa Yehova anakhomera Chilamulo ndi temberero pamtengo. Pakumva mfundo imeneyi, Saulo anaona monga “nzeru ya Mulungu” mtengo wozunzirapo umene “kwa Ayudatu [unali] chokhumudwitsa.” (1 Akorinto 1:18-25; Akolose 2:14) Choncho, ngati chipulumutso chikhala chopanda ntchito za chilamulo koma mwa chisomo cha Mulungu kwa ochimwa monga Saulo, ndiye kuti chinaperekedwa kwa amene sanali m’Chilamulo. Ndipo kunali kwa Akunja kumene Yesu anatuma Saulo.​—Aefeso 3:3-7.

Sitikudziŵa kuti Saulo anadziŵa zochuluka motani panthaŵi ya kulapa kwake. Yesu anali kudzalankhula nayenso kachiŵiri, mwinanso kuposerapo ponena za ntchito yake kwa amitundu. Komanso, zaka zambiri zinapitapo kuti Saulo alembe zonsezi mouziridwa ndi Mulungu. (Machitidwe 22:17-21; Agalatiya 1:15-18; 2:1, 2) Komabe, panapita masiku Saulo asanalandire malangizo ena kuchokera kwa Ambuye ake atsopano.

Kuchezeredwa ndi Hananiya

Ataonekera kwa Saulo, Yesu anaonekeranso kwa Hananiya, ndikumuuza kuti: “Pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m’nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera ndipo anaona mwamuna dzina lake Hananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.”​—Machitidwe 9:11, 12.

Popeza Hananiya ankamudziŵa Saulo, mpake kuwadabwa mawu a Yesu. Ndipo anati: “Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu m’Yerusalemu; ndi kuti pano ali nawo ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.” Koma Yesu anamuuza Hananiya kuti: “Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli.”​—Machitidwe 9:13-15.

Ndi mtima wonse, Hananiya anapita kumene Yesu anamuuza. Atam’peza Saulo ndi kum’pasa moni, Hananiya anaika manja ake pa iye. “Ndipo pomwepo” nkhaniyo imatero, “padagwa kuchoka m’maso mwake [mwa Saulo] ngati mamba, ndipo anapenyanso.” Tsopano Saulo anali wokonzeka kumvetsera. Mawu a Hananiya anatsimikizira zimene Saulo anamva m’mawu a Yesu akuti: “Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mawu otuluka mkamwa mwake. Ndipo udzam’khalira iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva. Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.” Chotsatira chake? Saulo “ananyamuka nabatizidwa; ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu.”​—Machitidwe 9:17-19; 22:12-16.

Atakwaniritsa ntchito yake, Hananiya wokhulupirikayo sanamvekenso m’nkhani za Baibulo, ndipo sitikuuzidwanso zambiri za iye. Koma Saulo anadabwitsa onse amene anamumva! Amene kale anali wozunza, amene anapita ku Damasiko kukagwira ophunzira a Yesu, anayamba kulalikira m’masunagoge ndi kumatsimikizira kuti Yesu anali Kristu.​—Machitidwe 9:20-22.

“Mtumwi wa Anthu Amitundu”

Zimene Saulo anakumana nazo panjira ya ku Damasiko zinam’siyitsa mchitidwe wake wozunza. Atam’dziŵa Mesiya, Saulo anagwiritsa ntchito malingaliro ndi maulosi ambiri a Malemba Achihebri pa Yesu. Kudziŵa kuti Yesu anamuonekera ndi ‘kum’gwira’ komanso kum’patsa ntchito monga “mtumwi wa anthu amitundu” kunasintha kwambiri moyo wa Saulo. (Afilipi 3:12; Aroma 11:13) Tsopano monga mtumwi Paulo, anali ndi mwayi komanso ntchito yosintha osati masiku otsala amoyo wake wapadziko lapansi okha komanso mbiri yachikristu.

Patapita zaka zingapo, pamene utumwi wake unakanidwa, Paulo anachirikiza umboni wake mwa kufotokoza zimene anaona panjira ya ku Damasiko. “Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaona Yesu Ambuye wathu?” anafunsa motero. Ndipo atauza ena za maonekedwe a Yesu woukitsidwayo, Saulo (Paulo) anati: “Potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.” (1 Akorinto 9:1; 15:8) Kunali ngati kuti Saulo, kuona kwake masomphenya aulemerero wakumwamba wa Yesu, anapatsidwa ulemu wobadwa, kapena kuukitsidwa, kumoyo wauzimu nthaŵi yake isanakwane.

Saulo analandira ntchito yake ndipo anayesetsa kuchita mogwirizana ndi zimene ntchitoyo imafuna. “Ine ndili wamng’ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu,” analemba motero. “Koma . . . chisomo [cha Mulungu] cha kwa ine sichinakhala chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya [atumwi ena onse].”​—1 Akorinto 15:9, 10.

Mwinamwake mofanana ndi Saulo mukukumbukira nthaŵi imene munadziŵa kuti mufunika kusintha malingaliro a chipembedzo amene mwakhala mukutsatira kwanthaŵi yaitali kuti mupeze chiyanjo cha Mulungu. Ndithudi munali wokondwa kwambiri kuti Yehova anakuthandizani kupeza choonadi. Pamene Saulo anaona kuunika ndikuzindikira zimene anafunikira kuchita, sanazengereze kuzichita. Ndipo anapitirizabe kuzichita mwachangu ndiponso anatsimikiza mtima kuzichita masiku amoyo wake wonse. Ndi chitsanzo chapadera zedi kwa onse amene akufuna kuyanjidwa ndi Yehova lerolino!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Katswiri wina wamaphunziro akuganiza kuti Yudasi ayenera kuti anali m’tsogoleri wa dera lachiyuda la kumeneko kapena mwini wa nyumba ya alendo yachiyuda.

[Chithunzi patsamba 27]

Khwalala lotchedwa Lolunjika m’Damasiko wamakono

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chojambulidwa ndi ROLOC Color Slides