Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zinthu “Zofunika” Zikudzaza Nyumba ya Yehova

Zinthu “Zofunika” Zikudzaza Nyumba ya Yehova

Zinthu “Zofunika” Zikudzaza Nyumba ya Yehova

“Ineyo [Yehova] ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.”​—HAGAI 2:7.

1. Pakachitika ngozi, n’chifukwa chiyani timayamba kuganiza za okondedwa athu kaye?

KODI nyumba yanu ndi yodzaza ndi zinthu zotani zofunika? Kodi muli ndi mipando yochititsa kaso, kompyuta mbambande, galimoto latsopano m’garaja? Ngakhale kuti muli ndi zinthu zonsezi, kodi simungavomereze kuti zinthu zofunika koposa m’nyumba mwanu ndizo anthu, anthu a m’banja lanu? Tayerekezani kuti usiku wina mwagalamuka chifukwa cha kununkha kwa utsi. Nyumba yanu ikuyaka, ndipo mufunikira kuthaŵamo mwamsanga! Kodi mudzayamba kuganiza za chiyani kaye? Mipando yanu? Kompyuta yanu? Galimoto lanu? Kodi simudzaganizira za okondedwa anu kaye? Inde mudzatero, pakuti anthu n’ngofunika kwambiri kuposa zinthu.

2. Kodi zolengedwa za Yehova zikuphatikizapo chiyani, ndipo n’chiyani mwa zolengedwazo chimene Yesu anasangalatsidwa nacho kwambiri?

2 Tsopano talingalirani za Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu. Yehova ndiye “wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili mmenemo.” (Machitidwe 4:24) Mwana wakeyo, “mmisiri,” ndi amene Yehova anagwiritsa ntchito popanga zinthu zonse. (Miyambo 8:30, 31; Yohane 1:3; Akolose 1:15-17) Ndithudi onse aŵiri Yehova ndi Yesu amakonda zinthu zimene zinalengedwa. (Yerekezani ndi Genesis 1:31.) Koma kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimene amachikonda kwambiri pazolengedwa zonse? Zinthu kapena anthu? Poyankhula monga nzeru yomwe yakhala munthu, Yesu anati: “[Ndinali] kusekerera ndi ana a anthu,” kapena monga momwe Baibulo lotembenuzidwa ndi William F. Beck limanenera, Yesu “anasangalatsidwa ndi anthu.”

3. Kodi Yehova anapereka ulosi wotani kudzera mwa Hagai?

3 Mosakayikira, Yehova amaona anthu kukhala a mtengo wapatali. Imodzi mwa mfundo zimene zimatisonyeza zimenezi ikupezeka m’mawu aulosi amene iye ananena m’chaka cha 520 B.C.E. kudzera mwa mneneri Hagai. Yehova anati: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero. . . . Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo.”​—Hagai 2:7, 9.

4, 5. (a) N’chifukwa chiyani sizingakhale zomveka kunena kuti mawu akuti zinthu “zofunika” akunena zinthu zamtengo wapatali? (b) Kodi tanthauzo la zinthu “zofunika” mungalifotokoze motani, ndipo chifukwa chiyani?

4 Kodi ndi zinthu “zofunika” ziti zimene zinali kudzadzaza nyumba ya Yehova ndi kuidzetsera ulemerero woposa nyumba yoyambayo? Katundu wa mtengo wapamwamba ndi zokongoletsa zambambande? Golide, siliva, ndi miyala yamtengo wapatali? Zimenezi zikanakhala zovuta kumvetsa. Kumbukirani kuti kachisi woyamba uja, amene anaperekedwa zaka mazana asanu kumbuyoko, anali nyumba ya ndalama mabiliyoni, mabiliyoni! * Ndithudi, Yehova sakanayembekezera kachisi womangidwa ndi kagulu kakang’ono ka Ayuda omwe abwerera kuchokera kuukapolo kukhala womangidwa ndi zinthu zamtengo wapatali kuposa kachisi wa Solomo!

5 Nangano zinthu “zofunika” zomwe zinayenera kudzaza nyumba ya Yehova ndizo chiyani? N’zoonekeratu kuti ayenera kukhala anthu. Pajatu chimene chimakondweretsa mtima wa Yehova si siliva kapena golide koma anthu om’tumikira chifukwa chakuti amam’konda. (Miyambo 27:11; 1 Akorinto 10:26) Inde, Yehova amawakonda kwambiri onse amuna, akazi, ndi ana amene amam’lambira m’njira yovomerezeka. (Yohane 4:23, 24) Ameneŵa ndiwo zinthu “zofunika,” ndipo n’ngamtengo wapatali kwambiri kwa Yehova kuposa zokongoletsa zonse zamtengo wake zomwe zinali m’kachisi wa Solomo.

6. Kodi kachisi wakale wa Mulungu anali wantchito yanji?

6 Ngakhale kuti panali chitsutso chosatha, kachisiyo anamalizidwa mu 515 B.C.E. Mpaka pamene Yesu anaperekedwa nsembe, kachisi wa m’Yerusalemu ndiye anali malo a kulambira koyera kwa zinthu “zofunika” zochuluka, zomwe zinaphatikizapo Ayuda ndi Akunja otembenuka. Koma kachisiyo anaimira chinachake chaulemerero waukulu koposa, monga momwe tidzaonera.

Kukwaniritsidwa M’zaka za Zana Loyamba

7. (a) Kodi kachisi wakale wa Mulungu ku Yerusalemu anali chithunzi cha chiyani? (b) Longosolani zochita za mkulu wa ansembe pa Tsiku la Chitetezo.

7 Kachisi wa m’Yerusalemu anali chithunzi cha makonzedwe ena ake aakulu a kulambira. Makonzedwewo ndiwo a kachisi wauzimu wa Mulungu, amene Yehova anakhazikitsa mu 29 C.E. naika Yesu monga Mkulu wa Ansembe m’kachisiyo (Ahebri 5:4-10; 9:11, 12) Talingalirani kufanana kwa zochita za mkulu wa ansembe mu Israyeli ndi zochita za Yesu. Chaka chilichonse pa Tsiku la Chitetezo, mkulu wa ansembe ankapita kuguwa la nsembe m’bwalo la kachisi ndi kupereka ng’ombe monga chotetezera cha machimo a ansembe. Pambuyo pake, ankaloŵa m’kachisi ndi mwazi wa ng’ombe, kudutsa pazitseko zomwe zinasiyanitsa bwalo ndi Malo Opatulika ndi kudutsanso pachinsalu chosiyanitsa Malo Opatulika ndi Malo Opatulikitsa. Ataloŵa m’Malo Opatulikitsa, mkulu wa ansembe ankawaza mwaziwo patsogolo pa likasa la chipangano. Ndiyeno, potsatira mwambo umodzimodziwo, ankapereka mbuzi monga choteteza cha machimo a mafuko 12 a Israyeli osakhala a ansembe. (Levitiko 16:5-15) Kodi mwambo umenewo ukugwirizana motani ndi kachisi wauzimu wa Mulungu?

8. (a) Kodi Yesu anaperekedwa m’lingaliro lotani kuyambira mu 29 C.E.? (b) Kodi Yesu anali paunansi wapadera wotani ndi Yehova muutumiki wake wonse wapadziko lapansi?

8 Kwenikweni, Yesu anaperekedwa pa guwa la chifuniro cha Mulungu pomwe iye anabatizidwa ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu mu 29 C.E. (Luka 3:21, 22) Zoonadi, chochitika chimenechi ndicho chinali chiyambi cha moyo wodzipereka wa Yesu umene unatha zaka zitatu ndi theka. (Ahebri 10:5-10) Panthaŵi imeneyo, unansi umene Yesu anali nawo ndi Mulungu unali wobadwa ndi mzimu. Unansi wapadera umenewu umene Yesu anali nawo ndi Atate wake wakumwamba sunali kumvetsetsedwa bwino ndi anthu ena. Zinali ngati kuti nsalu inayake inali kutchinga maso awo a kuzindikira, monga momwe nsalu inkatchingira Malo Opatulika kuti asaonekere kwa amene akhala m’bwalo la chihema chosonkhanako.​—Eksodo 40:28.

9. N’chifukwa chiyani Yesu sakanatha kuloŵa kumwamba ali munthu, nanga n’chiyani chinachitika kuti aloŵe?

9 Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu wodzozedwa ndi mzimu, munthuyo Yesu sakanaloŵa kumwamba. Kulekeranji? Chifukwa chakuti thupi ndi mwazi sizingathe kuloŵa mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (1 Akorinto 15:44, 50) Popeza kuti thupi laumunthu la Yesu linali chotchinga, linaphiphiritsidwa bwino ndi chinsalu chomwe chinasiyanitsa Malo Opatulika ndi Malo Opatulikitsa a m’kachisi wakale wa Mulungu. (Ahebri 10:20) Koma masiku atatu pambuyo pa imfa yake, Yesu anaukitsidwa ndi Mulungu ali mzimu. (1 Petro 3:18) Ndiyetu pamenepo akanatha kuloŵa m’Malo Opatulikitsa a m’kachisi wauzimu wa Mulungu kumwamba kwenikweniko. Ndipo n’zimenedi zinachitika. Paulo analemba kuti: “Kristu sanaloŵa m’malo opatulika [mwachionekere kutanthauza Malo Opatulikitsa] omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m’Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.”​—Ahebri 9:24.

10. Kodi Yesu anachitanji atabwerera kumwamba?

10 Kumwambako, Yesu ‘anawaza mwazi’ wa nsembe yake mwa kupereka kwa Yehova mtengo wa dipo la mwazi wake wopatsa moyowo. Komanso, Yesu anachitanso zina. Imfa yake itatsala pang’ono, anali atauza otsatira ake kuti: “Ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.” (Yohane 14:2, 3) Chotero mwa kuloŵa m’Malo Opatulikitsa, kapena kuti kumwamba, Yesu anatsegulira njira enanso kuti atsatire. (Ahebri 6:19, 20) Anthu ameneŵa, omwe anali kudzakwanira 144,000, anali kukatumikira monga ansembe aang’ono m’makonzedwe a Mulungu a kachisi wauzimu. (Chivumbulutso 7:4; 14:1; 20:6) Monga momwe mkulu wa ansembe m’Israyeli choyamba ankatenga mwazi wa ng’ombe kuloŵa nawo m’Malo Opatulikitsa monga choteteza cha machimo a ansembe, mtengo wa mwazi wokhetsedwa wa Yesu unagwira ntchito choyamba pa ansembe aang’ono 144,000 ameneŵa. *

Zinthu “Zofunika” Zamakono

11. Kodi mkulu wa ansembe wa mu Israyeli ankapereka mbuzi kaamba ka yani, ndipo zimenezi zinali chithunzi cha chiyani?

11 Zikuoneka kuti podzafika chaka cha 1935, kusonkhanitsa kwakukulu kwa odzozedwa kunatha. * Koma sikuti Yehova anamaliza kudzaza nyumba yake ndi ulemerero. Inde, zinthu “zofunika” zinali kudzaloŵabe m’nyumbayo. Kumbukirani kuti mkulu wa ansembe m’Israyeli ankapereka nyama ziŵiri, ng’ombe ya machimo a ansembe ndi mbuzi ya machimo a mafuko osakhala a ansembe. Popeza kuti ansembewo anali chithunzi cha anthu odzozedwa amene anali kukakhala ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba, kodi mafuko osakhala a ansembe ankaimira yani? Yankho likupezeka m’mawu a Yesu olembedwa pa Yohane 10:16 akuti: “Nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” Chotero, mwazi wokhetsedwa wa Yesu ukupindulitsa magulu aŵiri a anthu, gulu loyamba, Akristu amene akuyembekeza kukalamulira ndi Yesu kumwamba ndipo gulu lachiŵiri, awo amene akuyembekeza kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Umboni ukusonyeza kuti ndi gulu lachiŵiri limeneli limene zinthu “zofunika” za mu ulosi wa Hagai zikuchitira chithunzi.​—Mika 4:1, 2; 1 Yohane 2:1, 2.

12. Kodi zinthu “zofunika” zambiri zikubwera motani ku nyumba ya Mulungu lerolino?

12 Zinthu “zofunika” zimenezi zikudzazabe nyumba ya Yehova. M’zaka zino, ziletso zachotsedwa ku Eastern Europe, m’mbali zina za mu Africa, ndi m’mayiko ena, zimene zapangitsa kuti uthenga wabwino wa Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu ufalikire m’magawo amene mpaka nthaŵiyo anali osakhudzidwabe. Pamene anthu ofunikawo akuloŵa m’makonzedwe a kachisi a Mulungu, iwo amayesetsa kupanganso ophunzira ena, momvera lamulo la Yesu. (Mateyu 28:19, 20) Pochita zimenezo, amakumana ndi anthu ambiri, ang’onoang’ono ndi akuluakulu omwe, amene amathanso kukhala zinthu “zofunika” zomwe zidzadzetsera nyumba ya Yehova ulemerero. Nazi zitsanzo zochepa zosonyeza mmene zimenezi zikuchitikira.

13. Kodi mtsikana wina wamng’ono ku Bolivia wasonyeza motani changu chake chofalitsa uthenga wa Ufumu?

13 Ku Bolivia, mtsikana wina wa zaka zisanu zakubadwa amene akuleredwa ndi makolo a Mboni anapempha chilolezo cha mphunzitsi wake kuti asabwere kusukulu pamlungu wa kucheza kwa woyang’anira dera. Chifukwa chiyani? Anali kufuna kuti akatengemo mbali muutumiki pamlungu wonsewu wazochita zapadera. Zimenezi zinadabwitsa makolo ake, koma iwo anakondwera kuti iye anali ndi mzimu wabwino chotero. Mtsikana wamng’ono ameneyu tsopano akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba asanu, ndipo ena mwa ophunzira ameneŵa amafika pamisonkhano yachikristu. Iye wabweranso ngakhale ndi mphunzitsi wake uja ku Nyumba ya Ufumu. Mwina m’kupita kwa nthaŵi, ena mwa ophunzira Baibulo ake adzadzisonyeza kukhala zinthu “zofunika” zimene zidzadzetsa ulemerero m’nyumba ya Yehova.

14. Ku Korea, kodi kulimbikira kwa mlongo poyankhula ndi munthu wooneka ngati wopanda chidwi kunafupidwa motani?

14 Podikira sitima ya pamtunda pamalo okwerera, mkazi wachikristu ku Korea anafikira mwana wasukulu amene anali kumvetsera nyimbo m’mahedifoni. “Kodi muli ndi chipembedzo?” iye anafunsa motero. “Sindikufuna chipembedzo china chilichonse,” mwana wasukuluyo anayankha motero. Mlongoyo sanagwe ulesi. “M’kupita kwa nthaŵi,” mlongoyo anapitiriza motere, “munthu amadzafuna kusankha chipembedzo. Koma ngati sakudziŵa kalikonse ponena za chipembedzo, angasankhe cholakwika.” Nkhope ya mwana wasukuluyo inasintha, ndipo anayamba kumvetsera mwachidwi zimene mlongo wathu anali kunena. Mlongoyo anam’gaŵira buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? ndi kumuuza kuti buku limeneli lidzam’thandiza kwambiri ikadzakhala nthaŵi yoti asankhe chipembedzo. Analandira bukulo mofunitsitsa. Mlungu wotsatira, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo tsopano amafika pamisonkhano yonse yampingo.

15. Kodi mtsikana wina wamng’ono ku Japan amayambitsa motani maphunziro a Baibulo, ndipo kodi kuyesayesa kwake kwafupidwa motani?

15 Ku Japan, Megumi wazaka 12 amaona sukulu yake monga munda wachonde wolalikiramo ndi kuphunzitsa. Iye wathanso kuyambitsa maphunziro ambiri a Baibulo. Kodi Megumi amatha bwanji kuchita zimenezo? Popeza kuti amaŵerenga Baibulo kapena kukonzekera misonkhano panthaŵi ya chakudya chamasana, anzake a m’kalasi nthaŵi zambiri amam’funsa zimene akuchita. Ena amafunsa Megumi chifukwa chimene iye sachita nawo zochita zina zapasukulupo. Megumi amayankha mafunso awo ndi kuwauza kuti Mulungu ali ndi dzina. Nthaŵi zambiri, zimenezi zimadzutsa chidwi mwa omvetsera ake. Kenako iye amawafunsa ngati angakonde kuphunzira Baibulo. Megumi akuchititsa maphunziro 20 tsopano, ndipo 18 mwa amenewo ndi anzake a m’kalasi.

16. Kodi mbale wina ku Cameroon anatha bwanji kuyambitsa maphunziro a Baibulo kwa ena omwe anali pagulu la onyoza?

16 Ku Cameroon, gulu la amuna limene linali kugwira ntchito pamalo ena ake linaitana mbale amene anali kugaŵira zofalitsa zolongosola Baibulo kwa winawake yemwe ankadutsa pamalopo. Pofuna kuti amunyoze mbaleyo, anamufunsa chifukwa chimene sakhulupirira Utatu, moto wa helo, kapenanso kusafa kwa mzimu. Pogwiritsa ntchito Baibulo, mbale wathuyo anawayankha mafunso awo. Chotsatira chake chinali chakuti atatu mwa amunawo anavomera kuphunzira Baibulo. Mmodzi mwa iwo, Daniel, anayamba kufika pamisonkhano ndiponso anawononga zinthu zake zonse zokhudzana ndi mizimu. (Chivumbulutso 21:8) Chaka chisanathe, iye anabatizidwa.

17. Kodi abale ena ku El Salvador anagwiritsa ntchito motani luso kuti alalikire kwa munthu amene poyamba sankafuna kumvetsera uthenga wa Ufumu?

17 Ku El Salvador, mwamuna wina ankati akaona Mboni za Yehova zikubwera, anali kumangirira galu wake wolusa pakhomo la nyumba. Munthuyo anali kuyembekeza kuti Mbonizo zidutse, ndiyeno ankamasula galuyo ndi kumuloŵetsanso m’nyumba. Abale sanathe kulankhula naye mwamuna ameneyu. Motero tsiku lina anayesa kugwiritsa ntchito njira ina. Podziŵa kuti mwamunayo adzamva zimene akunena, iwo anaganiza zolalikira kwa galuyo. Anafika panyumbayo nalonjera galuyo, ndi kunena kuti iwo anali okondwa kwambiri kukhala ndi mwayi wolankhula naye. Iwo anakamba za nthaŵi pamene padziko lapansi padzakhala paradaiso, pamene palibe munthu amene adzakhala waukali. Inde, pamene ngakhale nyama zidzakhala zamtendere. Ndiyeno anamutsanzika galuyo mwaulemu ndi kumapita ulendo wawo. Mowadabwitsa kwambiri, mwininyumbayo anatuluka m’nyumbamo ndi kupepesa posapatsa Mboni mwayi wolankhula naye. Anatenga magazini, ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Mwamuna ameneyu ndi mbale wathu tsopano​—mmodzi mwa zinthu “zofunika”!

“Musamawopa Inu”

18. Ndi mavuto ati amene Akristu ambiri ali nawo, koma kodi Yehova amawaona motani olambira ake?

18 Kodi mukutengamo mbali mokwanira m’ntchito yofunikayi yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira? Ngati mukutero, mulitu ndi mwayi waukulu. Indedi, zinthu “zofunika” zikubweretsedwa m’nyumba ya Yehova kudzera mwa ntchito imeneyi. (Yohane 6:44) Ndithudi, nthaŵi zina mungakhale wotopa kapena mungagwe ulesi. Nthaŵi zina, ena, ngakhale pakati pa atumiki okhulupirika a Yehova, amalimbana ndi malingaliro odziona ngati sali kanthu. Koma musataye mtima! Yehova amaona wolambira wake aliyense kukhala wofunika, ndipo akufunitsitsadi mutapulumuka.​—2 Petro 3:9.

19. Kodi Yehova anapereka chilimbikitso chotani kudzera mwa Hagai, ndipo kodi mawu amenewo angatilimbitse motani ifeyo?

19 Pamene talefuka, kaya chifukwa cha kutsutsidwa kapena zochitika zina zosasangalatsa, mawu a Yehova kwa Ayuda omwe anabwerera kwawo angakhale olimbikitsa kwambiri. Pa Hagai 2:4-6, timaŵerenga kuti: “Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m’dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu; monga momwe ndinapangana nanu muja munatuluka m’Aigupto, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu. Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthaŵi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe.” Onanitu kuti Yehova sakutilimbikitsa chabe kukhala olimba komanso akutipatsa njira yopezera mphamvu. Motani? Taonani mawu olimbikitsawo akuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu.” N’zolimbitsa chikhulupiriro zedi kudziŵa kuti kaya tikumane ndi zopinga zotani, Yehova ali nafe!​—Aroma 8:31.

20. Kodi ulemerero waukulu kuposa wonse wakale ukudzadza motani nyumba ya Yehova tsopano?

20 Yehova wasonyezadi kuti ali ndi anthu ake. Inde, zilidi monga momwe ananenera kudzera mwa mneneri Hagai kuti: “Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo . . . ndipo m’malo muno ndidzapatsa mtendere.” (Hagai 2:9) Zoonadi, ulemerero waukulu koposa lerolino ukupezeka m’kachisi wauzimu wa Yehova. Inde, anthu zikwi mazana ambiri amayamba kulambira koyera chaka chilichonse. Ameneŵa akudyetsedwa bwino kwambiri mwauzimu, ndipo ngakhale m’dziko lazipolowe lino, ali ndi mtendere umene udzangoposedwa ndi wa m’dziko latsopano la Mulungu.​—Yesaya 9:6, 7; Luka 12:42.

21. Kodi tiyenera kuzitsimikizira chiyani?

21 Kugwedeza mitundu kwa Yehova pa Armagedo kuli pafupi. (Chivumbulutso 16:14, 16) Chotero tiyeni tigwiritse ntchito nthaŵi yotsala kuthandiza kupulumutsa miyoyo inanso. Tikhaletu olimba ndipo tikhulupirire Yehova kotheratu. Tidzitsimikizire mumtima kuti tidzapitirizabe kulambira pa kachisi wake wamkulu wauzimu, kum’dzazabe ndi zinthu “zofunika” zowonjezereka mpaka Yehova atanena kuti ntchito yathu yatha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Zinthu zimene zinaperekedwa pomanga kachisi wa Solomo zingalingane ndi ndalama zokwanira madola 40,000,000,000 pamitengo yamasiku ano. Zonse zimene sizinagwiritsidwe ntchito pantchito yomangayo zinaikidwa mosungiramo chuma m’kachisimo.​—1 Mafumu 7:51.

^ ndime 10 Mosiyana ndi mkulu wa ansembe wa m’Israyeli, Yesu analibe machimo kuti afune choteteza. Komabe, ansembe anzakewo anali ndi machimo chifukwa chakuti anagulidwa pakati pa anthu ochimwa.​—Chivumbulutso 5:9, 10.

^ ndime 11 Onani Nsanja ya Olonda, February 15, 1998, masamba 17-22.

Kodi Mukukumbukira?

Kwa Yehova, kodi chofunika kwambiri kuposa zinthu zakuthupi n’chiyani?

Mwazi wokhetsedwa wa Yesu umapindulitsa magulu aŵiri ati a anthu?

Kodi zinthu “zofunika” zomwe zikudzaza nyumba ya Yehova ndi ulemerero ndiwo ndani?

Kodi tili ndi umboni wotani wosonyeza kuti ulosi wa Hagai ukukwaniritsidwa lerolino?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kodi mukudziŵa tanthauzo lophiphiritsa la kachisi wakale wa Yehova?

Malo Opatulikitsa

Chinsalu chotchinga

Malo Opatulika

Khumbi

Guwa la nsembe

Bwalo

[Chithunzi patsamba 17]

Mkulu wa ansembe ankapereka ng’ombe kaamba ka machimo a Ansembe ndi mbuzi ya machimo a mafuko a Israyeli osakhala a ansembe

[Chithunzi patsamba 18]

Ntchito yapadziko lonse yolalikira Ufumu ikubweretsa makamu a anthu ku nyumba ya Yehova