Chipambano Chifukwa cha Khama
Chipambano Chifukwa cha Khama
KHAMA lakhala chinthu chosowa kwambiri m’nthaŵi ya makono ino. Anthu ambiri amakhulupirira kuti chipambano chimadalira pa kukhala pamalo oyenera ndi panthaŵi yoyenera kusiyana ndi mmene zimakhalira mwa kuchita khama. Kodi ndani angawatsutse? Zofalitsira nkhani zambiri n’zodzala ndi mawu otsatsira malonda amene mwamtseri amapereka lingaliro lakuti pafupifupi chinthu chilichonse chomwe mukufuna chingapezedwe mwa kungoyesa pang’ono ndiponso mwa kungowonjezera ndalama zochepa basi. Nyuzipepala kaŵirikaŵiri zimafalitsa nkhani zambiri zokhudza anthu omwe apeza chipambano kamodzin’kamodzi ndiponso za achinyamata aluso kwambiri amalonda omwe akupanga ndalama mamiliyoni atangomaliza maphunziro awo.
Wolemba nkhani m’nyuzipepala ina Leonard Pitts anadandaula kuti: “M’chitaganya chodera nkhaŵa kwambiri za kuganiza mwamsanga, kupambana kumaoneka ngati kosavuta. . . . Kumaoneka ngati chinthu chinachake chimene aliyense angachite ngati wadziŵa chinsinsi chake, ali ndi nzeru, kapena ngati wathandizidwa ndi Mulungu.”
Kodi Khama N’chiyani?
Kuchita khama kumatanthauza ‘kugwiritsitsa motsimikiza mtima ku cholinga chinachake, mkhalidwe winawake, kapena ntchito inayake mosasamala kanthu za zopinga kapena zododometsa.’ Liwu limeneli limapereka lingaliro la kupitiriza motsimikiza ngakhale pamavuto, kukhala wosatopa, wosafooka. Baibulo limasonyeza kufunika kwa mkhalidwe umenewu. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu,” Mateyu 6:33; Luka 11:9; Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:21.
“gogodani [mosaleka, NW] ndipo adzakutsegulirani,” “limbikani chilimbikire m’kupemphera,” ndiponso “sungani [“sungitsani,” NW] chokomacho.”—Mbali yofunika kwambiri pa kuchita khama ndiyo kulimbana ndi zododometsa zosapeŵeka. Miyambo 24:16 imati: ‘Wolungama amagwa kasanu ndi kaŵiri, nanyamukanso.’ M’malo ‘mosiya’ pamene akukumana ndi vuto linalake kapena pamene walephera, munthu wakhama ‘amanyamukanso,’ ‘osaleka,’ n’kuyeseranso.
Komabe, ambiri sakonzekera mavuto omwe angakumane nawo kapena kulephera komwe angakumane nako. Amasiya mwamsanga popeza kuti sakulitsa malingaliro ochita khama. “Anthu ambiri amaona kulephera m’njira yodzivulaza iwo eni,” akutero wolemba nkhani Morley Callaghan. “Amadzimvera chisoni, amaloza chala aliyense, amakhala okwiya ndiponso . . . amagwa mphwayi.”
Zimenezo n’zomvetsa chisoni. “Timaiŵala,” anatero Pitts, “kuti pali chifukwa choyesedwera, muli chinthu china chofunika mu nsautso.” Kodi n’chiyani chomwe chili chofunika mu nsautso? Iye anamaliza ndi kuti: “[Munthu] amaphunzira kuti kulephera sikufa kapenanso kugonja si kwamuyaya. Munthu amapeza chidziŵitso. Amakonzekera.” Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti: “M’ntchito zonse [zovuta, NW] muli phindu.”—Miyambo 14:23.
Inde, kupezanso mphamvu pambuyo pa chododometsa n’chinthu chovuta nthaŵi zambiri. Nthaŵi zina timakumana ndi zovuta zomwe zingaoneke kuti sizitha ngakhale titayesetsa motani. M’malo moziyandikira, zolinga zathu zingaoneke kuti zikuzimiririka pang’onopang’ono. Tingalefuke, n’kudziona ngati olephera, ndiponso tingataye mtima, ngakhalenso kupsinjika maganizo. (Miyambo 24:10) Komabe, Baibulo limatilimbikitsa kuti: ‘Tisaleme pakuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.’—Agalatiya 6:9.
Kodi N’chiyani Chimene Chingatithandize Kuti Tichite Khama?
Chinthu choyamba chofunika kuti tichite khama pa chochitika chinachake ndi kukhazikitsa zolinga zofunika ndiponso zomwe tingazikwaniritse. Mtumwi Paulo anamvetsetsa zimenezi. Anauza Akorinto kuti: “Ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga.” Paulo anadziŵa kuti ngati akufuna kuti zoyesayesa zake zikhale zopambana anafunikira zolinga zabwino, monga ngati wothamanga yemwe amathamanga atasumika malingaliro ake pa kumaliza kuthamanga kwakeko. “Kodi simudziŵa kuti iwo akuchita makani a liŵiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire,” iye anawalangiza motero. (1 Akorinto 9:24, 26) Kodi tingachite motani zimenezi?
“Wochenjera asamalira mayendedwe ake,” imatero Miyambo 14:15. N’kwanzeru kumapendanso njira zathu m’moyo nthaŵi ndi nthaŵi, n’kumadzifunsa kumene tikupita ndiponso ngati pakufunika kusintha. M’pofunika kudziŵa bwinobwino zinthu zomwe tikufuna kukwaniritsa ndiponso chifukwa chake. Ngati tisungitsa kwambiri m’malingaliro mwathu chithunzi cha zinthu zimene timalingalira kuchita, sitingafune kuzisiya. “Maso ako ayang’ane m’tsogolo,” umalimbikitsa motero mwambi wouziridwa, kotero kuti “njira zako zonse zikonzeke.”—Miyambo 4:25, 26.
Mutazindikira zolinga zanu, chinthu chachiŵiri ndicho kupenda momwe mungazikwanitsire. Yesu anafunsa kuti: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake.” (Luka 14:28) Mogwirizana ndi mfundo yachikhalidwe imeneyi katswiri wina wa za maganizo ananena kuti: “Chimodzi mwa zinthu zomwe ndaona ponena za anthu opambana n’chakuti amamvetsa bwinobwino kugwirizana kwa gwero la chinthu ndi zomwe gwerolo limachita m’moyo wawo. Anthu opambana amamvetsetsa kuti ngati akufuna kanthu kenakake, ayenera kuchita zinthu zonse zofunikira kuti akapeze.” Kumvetsa bwinobwino zinthu zonse zofunikira kuchita kuti tipeze zomwe tikufuna kudzatithandiza kuika malingaliro athu pa zimenezo. Kudzapangitsanso kukhala kosavuta kuti tipezenso mphamvu ngati takumana ndi chododometsa. Kupenda zinthu koteroko ndiko kunali chinsinsi cha chipambano cha Orville ndi Wilbur Wright.
Choncho, pakachitika zododometsa, yesetsani kuziona ndi malingaliro abwino ndiponso monga chokumana nacho chopatsa phunziro. Pendani mkhalidwewo, dziŵani pomwe munalakwa, ndipo kenako konzani polakwikapo kapena thetsani chofookacho. Kuyankhula ndi ena kumathandiza, Miyambo 20:18) Mwachibadwa, mwa kuyesayesa kulikonse, mumakulitsa luso lanu, ndithudi kumakuthandizani kuti mupambane.
chifukwa chakuti “uphungu utsimikiza zolingalira.” (Mbali yachitatu yofunika kwambiri pa kuchita khama ndiyo kuchita zinthu mokhazikika. Mtumwi Paulo akulangiza kuti: “Kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.” (Afilipi 3:16) Monga momwe ananenera mphunzitsi wina, “kuchita zinthu mosapambanitsa ndiponso mosasinthasintha kwanthaŵi yaitali kumabweretsa zotsatirapo zikuluzikulu.” Zimenezi zimasonyezedwa bwino kwambiri m’nthano yodziŵika kwambiri ya Aesop yonena za fulu ndi kalulu. Fulu anapambana mpikisano wothamangawo ngakhale kuti amathamanga pang’onopang’ono kusiyana ndi kalulu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti fulu anali ndi malingaliro okhazikika ndiponso odziletsa. Iye sanaleke koma anasankha liŵiro lomwe anapitirizabe nalo mosavuta ndiyeno analimbikira pa limenelo kufikira atalumpha mzera womaliza. Popeza kuti munthu wokonzekera ndiponso wosasinthasintha malingaliro amapitabe patsogolo, iye amakhala wosonkhezeredwabe maganizo ndiponso pachifukwa chimenechi nthaŵi zambiri saleka kapena kugonja pa mpikisano. Inde, “thamangani” kotero kuti mupeze cholinga chanu.
Kusankha Zolinga Zothandiza
Ndithudi, kuti khama likhale laphindu, tifunikira kukhala ndi zolinga zothandiza. Anthu ambiri amavutika ndi zinthu zomwe sizibweretsa chimwemwe. Koma Baibulo limati: “Iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, . . . adzakhala wodala m’kuchita kwake.” (Yakobo 1:25) Inde, kuphunzira kuti timvetsetse lamulo la Mulungu monga momwe kwasonyezedwera m’Baibulo n’cholinga chofunika kwambiri. Chifukwa chiyani? Kwakukulukulu chili chifukwa chakuti lamulo la Mulungu n’lozikidwa pa chiyero ndi chilungamo chake. Monga Mlengi, iye amadziŵa chinthu chimene chili chabwino kaamba ka zolengedwa zake. Choncho ngati tilimbikira kuphunzira malangizo a Mulungu ndi kuwagwiritsa ntchito pa moyo wathu, ndithudi kulimbikira koteroko kudzatidzetsera chimwemwe. “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, . . . ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako,” imalonjeza motero Miyambo 3:5, 6.
Ndiponso, kuloŵetsa chidziŵitso cha Mulungu ndi cha Yesu ndiwo “moyo wosatha,” akutero Yesu. (Yohane 17:3) Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo lino. (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3-13) Posachedwapa Ufumu wa Mulungu, boma lake lolungama, lidzakhazikitsa ulamuliro wake pa anthu okhala padziko lapansi. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Boma limeneli lidzadzetsa nyengo yosayerekezereka ya mtendere, ulemerero, ndiponso thanzi labwino kwa anthu omvera. (Salmo 37:10, 11; Chivumbulutso 21:4) “Mulungu alibe tsankhu,” akutero Machitidwe 10:34. Inde, aliyense akuitanidwa kudzasangalala ndi mapindu ameneŵa!
Baibulo ndi buku lakale lodzala ndi nzeru ndiponso thandizo. Kulimvetsetsa kumafuna nthaŵi ndi kuyesetsa. Koma ndi thandizo la Mulungu, ndiponso ngati tilimbikira kufunafuna chidziŵitso chake, lidzakhala buku lotseguka kwa ife. (Miyambo 2:4, 5; Yakobo 1:5) N’zoona kuti kugwiritsa ntchito zinthu zimene timaphunzira kungakhale kovuta. Tingafunikire kusintha m’kalingaliridwe kathu ndiponso m’makhalidwe. Mabwenzi kapena ena a m’banja otifuniradi zabwino angatsutse kuphunzira kwathu Baibulo. Choncho kulimbikira n’kofunika. Mtumwi Paulo akutikumbutsa kuti Mulungu adzapereka moyo wosatha kwa anthu omwe asonyeza “kupirira pa ntchito zabwino.” (Aroma 2:7) Mboni za Yehova zidzakhala zokondwera kukuthandizani kukwaniritsa cholinga chimenechi.
Dziŵani kuti mudzapeza chipambano ngati muchita khama pa kuphunzira za Mulungu ndi chifuno chake ndiponso ngati mulimbikira kugwiritsira ntchito zinthu zomwe mwaphunzira.—Salmo 1:1-3.
[Chithunzi patsamba 6]
Mudzapeza chipambano ngati muchita khama pa kuphunzira za Mulungu ndi chifuno chake
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
Culver Pictures