Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chinsinsi cha Chipambano N’chiyani?

Kodi Chinsinsi cha Chipambano N’chiyani?

Kodi Chinsinsi cha Chipambano N’chiyani?

ANYAMATA aŵiri akhama lawo anali kukonzekeretsa mosamala makina odabwitsa kwabasi kaamba ka mayeso ofunika kwambiri. Mwadzidzidzi, mphepo yamkuntho inanyamula chiŵiya chosalimbachi, n’kuchipititsa m’mwamba, ndipo mokhumudwitsa mphepoyo inachigwetsera pansi ndi kuchiphwasula. Atakhumudwa, anyamatawo anangoti chilili. Ntchito yawo yaluso ndi yotopetsayo inangounjikana m’kamulu ka matabwa ndi zitsulo zopotokapotoka.

Kwa Orville ndi Wilbur Wright, zimene zinachitika patsiku limenelo la mu October mu 1900 sichinali chinthu choyamba kuwakhumudwitsa pakuyesayesa kwawo kupanga makina ouluka olemera kuposa mphepo. Anali atatherapo kale zaka zingapo ndiponso ndalama zambiri akuyesayesa.

Komabe, pomaliza pake khama lawolo linapindula. Pa December 17, 1903 m’tauni yaing’ono ya Kitty Hawk, North Carolina, U.S.A., Orville ndi Wilbur Wright anatha kuulutsa ndege yoyamba yokhala ndi injini yomwe inauluka kwa masekondi 12, nthaŵi yaifupi kwambiri poyerekeza ndi mmene ndege zimaulukira masiku ano, koma yokwanira kusintha dziko mpaka ku nthaŵi yosatha!

M’zochitika zambiri, chipambano chimadalira pa khama loleza mtima. Kaya ndi kuphunzira chinenero chatsopano, kuphunzira ntchito, ngakhalenso kukulitsa ubwenzi, zinthu zambiri zamtengo wapamwamba zimapezedwa kokha mwa kuyesayesa kosalekeza. “Nthaŵi zisanu ndi zinayi pa nthaŵi khumi,” akutero wolemba Charles Templeton, “chipambano chimagwirizanitsidwa mwachindunji ndi chinthu chimodzi: ntchito yolimba.” Wolemba nkhani m’nyuzipepala ina Leonard Pitts, Jr., akuti: “Timayankhula za luso, timavomereza kuti ndi mwayi, koma kaŵirikaŵiri timanyalanyaza zinthu zofunika kwambiri. Ntchito yolimba ndiponso kulephera kwambirimbiri. Kufika msanga pantchito ndi kuŵeruka mochedwa.”

Zimenezi zikutsimikizira zomwe Baibulo linanena kalekale kuti: “Dzanja la akhama lidzalamulira.” (Miyambo 12:24) Khama limasonyeza kuti tikulimbikira pa zoyesayesa zathu. Zimenezi n’zofunika ngati tikufuna kuti tikwaniritse zimene tikufuna kuchita. Kodi khama n’chiyani? Kodi tingalimbikire motani pantchito zomwe talingalira kuti tichite, ndipo kodi ndi pazinthu zotani zimene tiyenera kulimbikira? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Chithunzi cha U.S. National Archives