Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Anthu a Mitundu Yonse mu Netherlands

Kuthandiza Anthu a Mitundu Yonse mu Netherlands

Olengeza Ufumu Akusimba

Kuthandiza Anthu a Mitundu Yonse mu Netherlands

ABRAHAMU anali ndi chikhulupiriro chodabwitsa. “Poitanidwa,” anatero mtumwi Paulo, Abrahamu anamvera mawu a Mulungu ndipo “anatuluka wosadziŵa kumene akamukako.” Abrahamu atasamutsa banja lake lonse, “anakhala mlendo ku dziko la lonjezano” kwa zaka zana limodzi zotsatira m’moyo wake.​—Ahebri 11:8, 9.

Chimodzimodzinso lerolino, ambiri a Mboni za Yehova avomera kusamukira ku mayiko amene ali ndi kusowa kwakukulu n’cholinga choti akatumikire kumeneko. Ena aphunzira zinenero zina kuti achitire umboni kwa alendo odzakhala m’dziko mwawo. Monga momwe zikusonyezera zitsanzo zotsatirazi, mzimu wabwino umenewu watsegula “khomo lalikulu la kuntchito” m’dziko la Netherlands, kumene miliyoni imodzi mwa anthu 15 miliyoni ndi ochokera ku mayiko ena.​—1 Akorinto 16:9, NW.

□ Bahram, mlangizi wakale wa maluso omenyera a Kung Fu, anachokera ku dziko lina ku Middle East. Analandira Baibulo ndi zofalitsa zina za Watch Tower. M’mwezi umodzi, Bahram anazindikira kuti wapeza choonadi. Iyeyo ndi mkazi wake anayamba kuphunzira, koma panali vuto​—mphunzitsi wawo wa Baibulo sankayankhula chiyankhulo chawo. Amayankhulana ndi magesichala, kuyankhula ndi “manja ndi mapazi,” iwo anakumbukira motero. M’kupita kwa nthaŵi, Bahram ndi mkazi wake anapeza mpingo wa chiyankhulo chawo, ndipo pambuyo pake anapita patsogolo mofulumira. Bahram ndi Mboni yobatizidwa tsopano.

□ Mwamuna ndi mkazi wake achidatchi amene ali apainiya anafikira mwamuna wina wa ku Indonesia amene anaima kutsogolo kwa sitolo ina yaikulu. Iye anadabwa komanso anasangalala pamene aŵiriwo anamuyankhula m’chinenero chakwawo. Ndiye anapanga makonzedwe okamufikira kunyumba kwake. Iwo anapeza kuti mwamunayo anakhala ku Russia kwa zaka zoposa 20, ndipo ndi m’nthaŵi imeneyo pamene anakhala dokotala wa nthenda za akazi. Ankanena kuti ndi wosakhulupirira kuti kuli Mulungu, koma anavomereza kuti nthaŵi iliyonse pamene wathandizira mayi kubereka mwana, samalephera kudabwa kuti, “Komatu thupi la munthu ndi langwiro! N’zodabwitsa zedi!” Anavomera kuphunzira Baibulo, ndipo posakhalitsa anayamba kukhulupirira kuti pali Mlengi amene amasamala za mtundu wa anthu. (1 Petro 5:6, 7) Tsopano ndi mbale wobatizidwa ndipo akutumikira ndi mpingo wachiindoneziya ku Amsterdam.

□ Ku Rotterdam, limodzi mwa madoko akuluakulu kwambiri padziko lonse, gulu la apainiya lakhala laluso m’kulalikira kwa anthu oyankhula zinenero zosiyanasiyana ofika padokopo tsiku ndi tsiku. Zotsatirapo zake za ntchito yolalikira ya gulu lachangu limeneli n’zakuti, amalinyero angapo, kuphatikizapo mkulu wina wa chombo, msilikali wapamadzi, ndi mlonda wakale, alandira choonadi. Nawonso tsopano akufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kuzungulira dziko lonse.​—Mateyu 24:14.

Monganso m’madera ena onse adziko lapansi, Mboni za Yehova ku Netherlands zikuyesetsa kuchita mbali yawo pofalitsa uthenga wabwino wosatha ku mtundu uliwonse, fuko, manenedwe, ndi anthu.​—Chivumbulutso 14:6.