Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muli ndi “Mtima Wa Kristu”?

Kodi Muli ndi “Mtima Wa Kristu”?

Kodi Muli ndi “Mtima Wa Kristu”?

“Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi . . . monga mwa Kristu Yesu.”​—AROMA 15:5.

1. Kodi Yesu amasonyezedwa kukhala munthu wotani m’zithunzi zambiri za Matchalitchi Achikristu, ndipo n’chifukwa chiyani kumeneko si kum’sonyeza bwino Yesu?

“PALIBE munthu anamuonapo akuseka.” Ndi mmene buku linalake limene monyenga limanena kuti linalembedwa kalekale ndi mkulu wina wa boma la Roma, linam’fotokozera Yesu. Buku limeneli, limene ladziŵika monga momwe lilili lerolino chiyambire zaka za zana la 11, akuti lakhudza akatswiri ambiri ojambula zithunzi. * Pazithunzi zambiri, Yesu amaoneka kukhala munthu wachisoni amene nthaŵi zambiri sanali kumwetulira, ngati anali kumwetulira n’komwe. Koma kumeneko si kum’sonyeza bwino Yesu, amene Mauthenga Abwino amam’sonyeza kukhala munthu wosangalala, wokoma mtima ndi wachifundo kwambiri.

2. Kodi tingakulitse motani ‘mtima umodzi monga mwa Kristu Yesu,’ ndipo zimenezi zidzatikonzekeretsa kuchita chiyani?

2 Ndithudi, kuti tim’dziwedi Yesu, tiyenera kudzaza malingaliro athu ndi mitima yathu ndi chidziŵitso cholongosoka ponena za mtundu wa munthu amene Yesu analidi pamene anali padziko lapansi. Chotero tiyeni tisanthule nkhani zina za m’Mauthenga Abwino zimene zimatipatsa chidziŵitso ponena za “mtima wa Kristu,” kutanthauza, mmene ankamvera mumtima, nzeru zake, maganizo ake, ndi zifukwa zake zochitira zinthu m’njira imeneyo. (1 Akorinto 2:16) Pamene tikutero, tiyeni tizilingalira mmene tingakulitsire “mtima umodzi . . . monga mwa Kristu Yesu.” (Aroma 15:5) Chotero, tingakhale okonzeka bwino m’moyo wathu komanso pochita zinthu ndi ena kuti titsatire chitsanzo chimene anatipatsa.​—Yohane 13:15.

Wofikirika

3, 4. (a) Kodi nkhani yolembedwa pa Marko 10:13-16 inali pachochitika chotani? (b) Kodi Yesu anatani pamene ophunzira ake anayesa kuletsa tiana kuti tisafike kwa iye?

3 Anthu ankakopeka naye Yesu. Panthaŵi zosiyanasiyana, anthu amisinkhu yosiyanasiyana komanso ochokera uku ndi uku anali kum’fikira mosavuta. Talingalirani za chochitikachi chomwe chinalembedwa pa Marko 10:13-16. Chinachitika chakumapeto kwa utumiki wake pamene anali kupita ku Yerusalemu nthaŵi yomaliza, kukafa imfa yopweteka zedi.​—Marko 10:32-34.

4 Tayerekezani chochitikacho. Anthu akuyamba kubweretsa ana, ngakhalenso makanda, kuti Yesu awadalitse anawo. * Komano ophunzira akuyesa kutsekereza kuti tianato tisafike kwa Yesu. Mwinamwake ophunzirawo akuganiza kuti Yesu sangalolere ana kumam’sokoneza m’milungu yovutitsitsa ngati imeneyi. Koma ophunzirawo alakwitsa. Yesu ataona zimene ophunzira akuchita, sakusangalala. Yesu akuitana tianato kwa iye, nati: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse.” (Marko 10:14) Kenako akuchita kanthu kena komwe kakusonyeza mtima wake wachifundo ndi wachikondi zedi. Nkhaniyo imasimba kuti: “Iye anatiyangata [tianato], natidalitsa.” (Marko 10:16) Mosakayikira tianato tikusangalala pamene Yesu akutiyangata mosamala.

5. Kodi nkhani ya pa Marko 10:13-16 imatiuzanji ponena za mtundu wa munthu amene Yesu anali?

5 Nkhani imeneyo ikutiuza zinthu zambiri ponena za mtundu wa munthu amene Yesu anali. Mutha kuona kuti anali wofikirika. Ngakhale kuti anali pamalo apamwamba kumwamba, iye sanali woopsa kapena wopeputsa anthu opanda ungwiro. (Yohane 17:5) Kodi sizochititsanso chidwi kuti ngakhale ana anali omasuka kukhala pafupi naye? Ndithudi sakanakopeka ndi munthu wamsunamo, wosasangalala amene sanali kumwetulira kapena kuseka! Anthu amisinkhu yonse anali omasuka naye Yesu chifukwa anaona kuti iye anali munthu wachifundo, wosamala za ena, ndipo ankadziŵa bwino lomwe kuti sadzawanyalanyaza.

6. Kodi akulu angadzipangitse motani kukhala ofikirika kwambiri?

6 Poganizira nkhani imeneyi, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndili ndi mtima wa Kristu? Kodi ndine wofikirika?’ M’nthaŵi zovutazi, nkhosa za Mulungu zimafuna abusa ofikirika, amuna amene ali ngati “pobisalira mphepo.” (Yesaya 32:1, 2; 2 Timoteo 3:1) Akulu, ngati mukulitsa chidwi chenicheni, chochokera pansi pa mtima, pa abale anu ndipo ndinu wofunitsitsa kudzipereka m’malo mwawo, iwo adzaona kuti mumawadera nkhaŵa. Adzaona zimenezo mwa kaonekedwe ka nkhope yanu, kamvekedwe ka mawu anu, ndiponso mwa kukoma mtima kwanu. Chifundo ndiponso nkhaŵa yeniyeni imeneyi zingayambitse unansi wokhulupirirana umene ungapangitse ena, kuphatikizapo ana, kukufikirani momasuka. Mkazi wina wachikristu anafotokoza chifukwa chimene anayankhulira momasuka ndi mkulu wina: “Anandiyankhula mokoma mtima, mosonyeza chifundo. Mwina sindikanatchula liwu ndi limodzi lomwe. Anandipangitsa kusaopa kalikonse.”

Woganizira Ena

7. (a) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kuganizira ena? (b) Kodi Yesu ayenera kuti anachiritsa munthu wakhungu pang’onopang’ono pachifukwa chiti?

7 Yesu anali woganizira ena. Anali kusamala za mmene ena akumvera mumtima. Kungoona anthu ovutika kunkam’mvetsa chisoni kwambiri moti anali kusonkhezereka kuwathetsera mavuto awo. (Mateyu 14:14) Anali kuganiziranso ena pa zofooka zawo kapena zosoŵa zawo. (Yohane 16:12) Panthaŵi inayake, anthu anabwera ndi munthu wakhungu ndi kupempha Yesu kuti am’chiritse. Yesu anam’chiritsadi, koma anam’chiritsa pang’onopang’ono. Poyamba, munthuyo anayamba kungoona anthu mwachimbuuzi​—“ayendayenda ngati mitengo.” Kenako Yesu anam’chiritsiratu ndipo anaona bwino. N’chifukwa chiyani anachiritsa munthuyo pang’onopang’ono? Ayenera kuti anachita zimenezi pofuna kuthandiza munthu amene anazoloŵera kungoona mdima kuti azoloŵere kuona dziko lowala ndi dzuŵa ndiponso lokhala ndi zinthu zambiri.​—Marko 8:22-26.

8, 9. (a) N’chiyani chinachitika Yesu ndi ophunzira ake atangoloŵa m’dera la Dekapoli? (b) Longosolani mmene Yesu anachiritsira munthu wogontha.

8 Lingaliraninso za chinachake chimene chinachitika pambuyo pa Paskha wa 32 C.E. Yesu ndi ophunzira ake anali ataloŵa m’dera la Dekapoli, kum’maŵa kwa Nyanja ya Galileya. Posapita nthaŵi, chinamtindi cha anthu chinawapeza kumeneko ndipo anthuwo anabweretsera Yesu anthu ambiri odwala ndi opuwala, ndipo anawachiritsa onsewo. (Mateyu 15:29, 30) Koma chochititsa chidwi n’chakuti, Yesu anapatulapo munthu mmodzi kuti amuone mwapadera. Wolemba Uthenga Wabwino Marko, yekhayo amene analemba za chochitikachi, akusimba zimene zinachitika.​—Marko 7:31-35.

9 Mwamunayo anali wogontha komanso wosatha kuyankhula. Yesu ayenera kuti anazindikira kuti munthuyo akuchita mantha kapena manyazi. Kenako Yesu anachita kanthu kena kachilendo ndithu. Anam’tengera pambali mwamuna ameneyu, kutali ndi gulu, poduka mphepo. Ndiyeno Yesu anapanga zizindikiro zina pofuna kusonyeza mwamunayo zimene anali pafupi kuchita. “[A]nalonga zala zake m’makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake.” (Marko 7:33) Kenako, Yesu anayang’ana kumwamba ndi kupemphera mousa moyo. Zizindikiro zimenezi zinali kuuza mwamunayo kuti, ‘Zimene nditi ndikuchitire zidzachitika mwamphamvu ya Mulungu.’ Pomalizira pake, Yesu anati: “Tatseguka.” (Marko 7:34) Pomwepo, makutu a mwamunayo anatseguka, ndipo anayambanso kuyankhula bwino.

10, 11. Kodi tingasonyeze motani kuganizira malingaliro a ena mumpingo? m’banja?

10 N’kuganiziratu ena kwakukulu komwe Yesu anasonyeza! Anali wosamala za mmene iwo akumvera mumtima, ndipo kuwaganizira mwachifundo kumeneku kunam’pangitsa kuchita zinthu m’njira imene sinawakhumudwitse kapena kuwachititsa manyazi. Monga Akristu, timachita bwino kukulitsa ndi kusonyeza mtima wa Kristu pankhani imeneyi. Baibulo limatilangiza kuti: “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.” (1 Petro 3:8) Ndithudi, zimenezi zimafuna kuti tizilankhula ndi kuchita zinthu moganizira malingaliro a anthu ena.

11 Mumpingo, tingasonyeze kuganizira malingaliro a ena mwa kuwalemekeza, kuwachitira mmene timafunira kuti azitichitira. (Mateyu 7:12) Zimenezo zingaphatikizepo kusamala zimene tikunena komanso mmene tikuzinenera. (Akolose 4:6) Kumbukirani kuti ‘kulankhula mwansontho kungapyoze ngati lupanga.’ (Miyambo 12:18) Nanga bwanji m’banja? Mwamuna ndi mkazi wake amene amakondanadi amasamala kwambiri za malingaliro a wina ndi mnzake. (Aefeso 5:33) Amapeŵa mawu aukali, kusuliza kopitirira muyeso, ndi mawu onyoza, zonse zimene zingapute nsautso ya mumtima yovuta kwambiri kuithetsa. Ananso nawo ali ndi malingaliro, ndipo makolo achikondi amasamala za mmene anawo amamvera mumtima. Ngati m’pofunika kuwawongolera, makolo otero amawawongolera mowalemekeza anawo ndi kusawachititsa manyazi. * (Akolose 3:21) Tikamaganizira ena motero, timasonyeza kuti tili ndi mtima wa Kristu.

Wokonzeka Kukhulupirira Ena

12. Kodi Yesu anali ndi kaonedwe kabwino komanso koyenera kotani ka ophunzira ake?

12 Yesu anali ndi kaonedwe kabwino ndiponso koyenera ka ophunzira ake. Anali kudziŵa bwino lomwe kuti ndi opanda ungwiro. Komansotu paja amatha kudziŵa za mumtima wa munthu. (Yohane 2:24, 25) Ngakhale zinali motero, sanali kuyang’ana zophophonya zawo koma mikhalidwe yawo yabwino. Iye anaonanso kuti amuna amene Yehova anawakoka ameneŵa angathe kuchita zabwino. (Yohane 6:44) Kaonedwe kabwino ka Yesu ka ophunzira ake kanaonekera m’njira imene anali kukhalira nawo ndi mmene anali kuwatengera. Chinthu chimodzi n’chakuti, anasonyeza kuti ndi wokonzeka kuwakhulupirira.

13. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti amakhulupirira ophunzira ake?

13 Kodi Yesu anasonyeza motani kuti amawakukhulupirira? Atachoka padziko lapansi, anapatsa ophunzira ake odzozedwawo udindo waukulu. Anawasiyira ntchito yosamalira zinthu za Ufumu wake zapadziko lonse. (Mateyu 25:14, 15; Luka 12:42-44) Panthaŵi ya utumiki wake, anasonyeza kuti amawakhulupirira, ngakhale pa zinthu zazing’ono zosanunkha kanthu. Pamene anachulukitsa chakudya mozizwitsa kuti adyetse makamu, anapatsa ophunzira ake udindo wogaŵa chakudyacho.​—Mateyu 14:15-21; 15:32-37.

14. Kodi mungalongosole motani mwachidule nkhani yolembedwa pa Marko 4:35-41?

14 Lingaliraninso za nkhani yolembedwa pa Marko 4:35-41. Panthaŵi imeneyo Yesu ndi ophunzira ake anakwera ngalaŵa ndi kuloŵera cha kum’maŵa modutsa Nyanja ya Galileya. Atangoyenda pang’ono, Yesu anagona tulo kumchira kwa ngalaŵayo. Koma posapita nthaŵi, “panauka namondwe wamkulu wa mphepo.” Anamondwe ngati ameneŵa ankachitikachitika pa Nyanja ya Galileya. Popeza kuti nyanjayo ili potsika (mamita ngati 200 kuchokera pomwe pali nyanja zonse zikuluzikulu), mpweya ndi wotentha pamenepo kusiyana ndi mpweya wa pamtunda wozungulira nyanjayo, ndipo zimenezi zimapangitsa kusinthasintha kwa mphepo. Kuwonjezera apo, mphepo yamphamvu imawomba Chigwa cha Yordano kuchokera ku Phiri la Hermoni, limene lili chakumpoto. Mphindi ya bata ingasinthe mwadzidzidzi kukhala mphindi ya mkuntho. Talingalirani izi: Yesu mosakayikira ankadziŵa za anamondwe ameneŵa, popeza anakulira ku Galileya. Komabe, anagona tulo mtima uli m’malo, pokhulupirira maluso a ophunzira ake, amene ena mwa iwo anali asodzi.​—Mateyu 4:18, 19.

15. Kodi tingatsanzire motani kukhulupirira ophunzira ake kwa Yesu?

15 Kodi tingatsanzire kukhulupirira ophunzira ake kwa Yesu? Ena amavutika kugaŵira anthu ena maudindo. Nthaŵi zonse amafuna kuti ntchito aziichita okha. Angamaganize kuti, ‘Ngati ndikufuna kuti ntchitoyo ichitike bwino, ndiyenera kuichita ndekha!’ Koma tikamachita tokha ntchito zonse, ndiye kuti tili pangozi ya kudzitopetsa mwinanso kusapeza nthaŵi yocheza ndi banja lathu pamene tinayenera kucheza nalo. Komanso, ngati sitigaŵira ena ntchito zina ndi maudindo ena oti tingawagaŵire, tingakhale tikuwamana chidziŵitso ndi maphunziro ofunika. Kungakhale kwanzeru kuphunzira kukhulupirira ena, kuwagawira ntchito zina. Tingachite bwino kudzifunsa moona mtima kuti, ‘Kodi ndili ndi mtima wa Kristu pankhani imeneyi? Kodi ndimapatsa ena ntchito zina, ndichikhulupiriro chakuti adzazichita monga momwe angathere?’

Anasonyeza Kuti Ophunzira Ake Amawadalira

16, 17. Usiku womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi, kodi Yesu anawatsimikizira motani atumwi ake, ngakhale kuti ankadziŵa kuti iwo adzam’thaŵa?

16 Yesu anasonyeza kaonedwe kabwino ka ophunzira ake m’njira inanso yofunika kwambiri. Anawasonyeza kuti amawadalira. Zimenezi zinali zoonekeratu m’mawu owatsimikizira amene analankhulira atumwi ake usiku womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi. Taonani zimene zinachitika.

17 Madzulo amenewo Yesu anali ndi zochita zambiri. Anapatsa atumwi ake phunziro la chitsanzo mwa kuwasambitsa mapazi awo. Kenako, anayambitsa chakudya chamadzulo chomwe chinali kudzakhala chikumbutso cha imfa yake. Komano, atumwi ake anayambanso mkangano wadzaoneni wotsutsana za amene akuoneka kukhala wamkulu pakati pawo. Poleza mtima monga kale, Yesu sanawathire mphepo koma anayankhula nawo mwanzeru. Anawauza zimene zidzachitika: “Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.” (Mateyu 26:31; Zekariya 13:7) Anadziŵa kuti abwenzi ake apamtimawo adzam’thaŵa panthaŵi yomwe adzawafunitsitsa. Koma sanawadzudzule. M’malo mwake, anawauza kuti: “Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.” (Mateyu 26:32) Inde, anawatsimikizira kuti ngakhale kuti adzam’thaŵa, iye sadzawasiya. Nsautso imeneyi ikadzapita, iye adzakumananso nawo.

18. Ku Galileya, kodi Yesu anasiyira ophunzira ake ntchito yaikulu iti, ndipo atumwi anaichita motani ntchito imeneyo?

18 Yesu anasunga mawu ake. Pambuyo pake, m’Galileya, Yesu woukitsidwayo anaonekera kwa atumwi ake 11, amene mwachionekere anasonkhana ndi enanso ambiri. (Mateyu 28:16, 17; 1 Akorinto 15:6) Kumeneko, Yesu anawapatsa ntchito yaikulu: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Buku la Machitidwe limatipatsa umboni womveka wakuti atumwi anaichitadi ntchito imeneyo. Mokhulupirika, iwo anatsogolera ntchito yolalikira uthenga wabwino m’zaka za zana loyamba.​—Machitidwe 2:41, 42; 4:33; 5:27-32.

19. Kodi zochita za Yesu pambuyo pa chiukiriro chake zikutiphunzitsa chiyani ponena za mtima wa Kristu?

19 Kodi nkhani yolongosola zonse imeneyi ikutiphunzitsanji ponena za mtima wa Kristu? Yesu anawaona atumwi ake ali panthaŵi yawo yovuta koposa, komabe “anawakonda kufikira chimaliziro.” (Yohane 13:1) Mosasamala kanthu za zophophonya zawo, anawasonyeza kuti amawadalira. Mutha kuona kuti chidaliro cha Yesu sichinali cholakwika. Chidaliro ndi chikhulupiriro zimene anawasonyeza mosakayikira zinawalimbitsa kuti akhale otsimikizira kwambiri kuchita ntchito imene anawalamula kuchita.

20, 21. Kodi tingasonyeze motani kuti okhulupirira anzathu timawaona bwino?

20 Kodi tingasonyeze motani mtima wa Kristu pankhaniyi? Musamakayikire okhulupirira anzanu. Ngati mumawakayikira, zolankhula zanu ndi zochita zanu zidzasonyeza zimenezo. (Luka 6:45) Komabe, Baibulo limatiuza kuti chikondi “chikhulupirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) Chikondi chimafunira ena zabwino, osati zoipa. Chimamangirira osati kugwetsa. Anthu amachitapo kanthu mofunitsitsa ngati asonyezedwa chikondi ndi kulimbikitsidwa osati ngati aopsezedwa. Tingamangirire ndi kulimbikitsa ena mwa kuwasonyeza kuti timawadalira. (1 Atesalonika 5:11) Ngati, monga Kristu, timawaona bwino abale athu, tidzawatenga m’njira zimene zidzawamangirira ndi kuwalimbikitsa kuchita zinthu zabwino kwambiri zimene angathe.

21 Kukulitsa ndi kusonyeza mtima wa Kristu kumafuna zambiri, osati kungoyerekeza kuchita zinthu zina zimene Yesu anachita. Monga momwe tatchulira kale m’nkhani yoyambayo, ngati tikufuna kuchitadi zinthu monga Yesu, choyamba tiyenera kuphunzira kuona zinthu monga momwe iye ankazionera. Mauthenga Abwino amatithandiza kuona mbali inanso ya umunthu wake, malingaliro ake ndi mmene ankamvera mumtima ponena za ntchito imene anapatsidwa, monga momwe nkhani yotsatira idzalongosolera.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 M’cholembedwa chachinyengo chimenecho, wolemba wakeyo akufotokoza amene akuti ndiwo anali maonekedwe a Yesu, kuphatikizapo maonekedwe a tsitsi lake, ndevu zake, ndi maso ake. Wotembenuza Baibulo Edgar J. Goodspeed anafotokoza kuti chinyengo chimenechi “chinakonzedwa kuti anthu avomereze mafotokozedwe opezeka m’mabuku a malangizo a ojambula zithunzi onena za maonekedwe a Yesu.”

^ ndime 4 Zikuoneka kuti anawo anali amisinkhu yosiyanasiyana. Panopo liwu lotembenuzidwa kuti “tiana” likugwiritsidwanso ntchito potchula mwana wamkazi wa Yairo wazaka 12 zakubadwa. (Marko 5:39, 42; 10:13) Koma posimba nkhani yofananayo ya ana, Luka akugwiritsa ntchito liwu lomwe limatanthauzanso makanda.​—Luka 1:41; 2:12; 18:15.

^ ndime 11 Onani nkhani yakuti “Kodi Mumawalemekeza?” m’kope la April 1, 1998, la Nsanja ya Olonda.

Kodi Mungalongosole?

• Kodi Yesu anatani pamene ophunzira ake anayesa kutsekereza ana kuti asafike kwa iye?

• Kodi Yesu anasonyeza kuganizira ena m’njira ziti?

• Kodi tingatsanzire motani kukhulupirira ophunzira ake kwa Yesu?

• Kodi tingatsanzire motani chidaliro chimene Yesu anasonyeza mwa atumwi ake?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Ana anali omasuka ndi Yesu

[Chithunzi patsamba 17]

Yesu ankachitira ena chifundo

[Chithunzi patsamba 18]

Akulu ofikirika ali dalitso