Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Matupi Aang’ono, Mitima Yabwino

Matupi Aang’ono, Mitima Yabwino

Matupi Aang’ono, Mitima Yabwino

KODI mungamve bwanji pamene mukulankhula ndi anthu achilendo nkhani ya Ufumu wa Mulungu ngati mutakhala wotalika masentimita 76 okha? Laura angakuuzeni bwino. Ali ndi zaka 33 ndipo kumeneku ndiko kutalika kwake, masentimita 76 basi. Iye pamodzi ndi mng’ono wake, María, amene ali ndi zaka 24 zakubadwa ndipo ndi wamtali masentimita 86, amakhala ku Quito, ku Ecuador. Talekani afotokoze zovuta zomwe amakumana nazo mu utumiki wawo wachikristu.

“Kuti tipite ku gawo lathu lolalikirako komanso ku misonkhano yachikristu, timayenda pafupifupi theka la kilomita kuti tikakwere basi. Kuchokera pamene timatsikira, timayenda mtunda wina wokwananso theka la kilomita kuti tikakwere basi yachiŵiri. Mwatsoka, m’njira imeneyi muli agalu asanu olusa. Ifeyo agalu amatiopsa chifukwa amaoneka aakulu ngati akavalo. Kuti tiwathamangitse ngati kuli kofunika, timatenga kandodo kamene timakabisa penapake tisanakwere basi kuti tidzagwiritsenso ntchito pobwerera.

“Kukwera basi ndi chinthu chinanso chovuta kwambiri kwa ife. Kuti tikwere mosavutikira timaima pa chiundo chadothi pamalo pamene pamaima basi. Madalaivala ena amaima pafupi ndi chiundocho, koma ena satero. Ngati sanatiimire pabwino ndiye kuti wamtali amathandiza wamfupi kukwera. Kuti tikwere basi yachiŵiri timafunikiranso kudutsa msewu mmene mumayenda magalimoto ambiri​—chinthu chovuta ndi miyendo yathu yaifupiyi. Chifukwa cha kufupika kwathu, chikwama cha mabuku cholemera chimatipatsa vuto lina lapadera. Kuti chikwamacho chipepukeko, timagwiritsa ntchito Baibulo lamthumba komanso timatenga mabuku ochepa.

“Tonse aŵiri sitikonda kulankhulalankhula kuyambira pa ubwana wathu. Anansi athu amadziŵa kuti nthaŵi zonse timachita manyazi kulankhula ndi alendo. Kotero kuti amadabwa ndi kuchita chidwi kutiona tikugogoda pazitseko zawo, ndipo kaŵirikaŵiri amamvetsera. Koma kumene sitili odziŵika, anthu amangotiona kuti ndife amwandionerapati; kotero kuti si nthaŵi zonse pamene amatimvetsera mwachidwi chimene uthenga wathu umafuna. Komabe ngakhale zili choncho, kudziŵa chikondi cha Yehova kumatipatsa chilimbikitso kuti tipitirize ntchito yolalikira. Kusinkhasinkha pa mawu a pa Miyambo 3:5, 6 kumatipatsanso chilimbikitso.”

Ngati momwe Laura ndi María akusonyezera, kupirira mosasamala kanthu za zovuta zakuthupi kungathe kulemekeza Mulungu. Mtumwi Paulo anapemphera kuti “munga m’thupi” mwake, mwinamwake vuto lakuthupi, uchotsedwe kwa iye. Koma Mulungu anamuuza kuti: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m’ufoko.” Indetu, zovuta zathu zakuthupi siziyenera kuchotsedwa kuti tithe kutumikira Mulungu. Kuika chidaliro chathu chonse pa Mulungu kungatithandize kuchita zomwe tingathe mu mkhalidwe wathu. Chifukwa chakuti Paulo anaona “munga m’thupi” mwake mwanjirayi, anafikira kunena kuti: “Pamene ndifoka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:7, 9, 10) Patapita zaka zina Paulo analemba kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:13.

M’nthaŵi zamakono, Mulungu akukwaniritsa ntchito yaikulu kudzera mwa amuna, akazi, komanso ana amene ali odzipereka kotheratu kwa iye. Ena a iwo ndi olemala mu njira zina. Ngakhale kuti onseŵa amayembekeza kuchiritsidwa ndi Mulungu mu Ufumu wake, sakudikira kudzayamba kumutumikira Mulungu pamene wawamasula ku zovuta zawo.

Kodi mukuvutika ndi zovuta zina zakuthupi? Limbani mtima! Kupyolera mwa chikhulupiriro chanu mungakhale mmodzi wa anthu ofanana ndi Paulo, Laura ndi María. Kwa iwo tinganene kuti, ngati momwe zinalili ndi amuna ndi akazi achikhulupiriro akale: “Analimbikitsidwa pokhala ofoka.”​—Ahebri 11:34.

[Chithunzi patsamba 8]

María

Laura

[Chithunzi patsamba 9]

María amathandiza Laura kukwera basi

[Zithunzi patsamba 9]

“Ifeyo agalu amatiopsa chifukwa amaoneka aakulu ngati akavalo”

Pamunsi: Laura ndi María limodzi ndi amene amaphunzira nawo Baibulo