Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mverani Chenjezo!

Mverani Chenjezo!

Mverani Chenjezo!

PHULII! Pa June 3, 1991, Phiri la Fugen ku Japan, linaphulika ndi mkokomo wa bingu lamphamvu, ndi kutulutsa mpweya ndi phulusa. Msanganizo wotentha kwambiri umenewo unayenderera kutsikira m’munsi mwa phirilo. Kuphulika kumeneko kunaphetsa anthu 43. Ambiri mwa omwe anapulumuka anali atapsa kodetsa nkhaŵa. “Madzi, madzi, chonde,” ena ankalira motero. Ozimitsa moto ndi apolisi anathamangira komweko mitima ili m’malere kuti akawathandize.

MILUNGU iŵiri zimenezi zisanachitike, anali ataona kale mulu wa matope pansonga pa phiri la Fugen, chotero akuluakulu a boma ndi anthu okhala kumeneko anali tcheru. Kwa nthaŵi yoposa mlungu umodzi tsokalo lisanachitike, chenjezo lakuti anthu ayenera kuchoka ku malo amenewo linali likuperekedwa. Kutangotsala tsiku limodzi lokha kuti phirilo liphulike, apolisi anapempha atolankhani kuti ayenera kupeŵa kupita kudera loletsedwalo. Komabe, anthu 43 omwe anafa madzulo oopsa amenewo, anali m’dera loopsalo.

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri ankapitabe kapena kukhalabe m’malo oopsawo? Alimi ena omwe anali atachoka m’nyumba zawo anabwereranso kukayendera katundu wawo ndi minda yawo. Akatswiri atatu ofufuza za kuphulika kwa mapiri ankayesa kufika pafupi ndithu ndi phirilo kuti akhutiritse chidwi chawo m’zamaphunziro. Atolankhani ena ndi ojambula zithunzi sanaope kudutsa malire oletsedwawo chifukwa chakuti ankafuna kufufuza nkhani yochititsa chidwi ya zochitika paphirilo. Madalaivala atatu omwe anachitidwa hayala kuti anyamule atolankhani analinso pamalo angoziwo. Apolisi ndi ozimitsa moto odzifunira anali pantchito zawo. Aliyense anali ndi chifukwa chake chopitira m’dera langozilo, ndipo chotsatira chake chinali chakuti anataya moyo wake.

Kodi Inuyo Muli M’dera Langozi?

Sikuti tonsefe tingakhale m’dera la phiri lomwe lingaphulike. Komabe, bwanji ngati tinali kuyang’anizana ndi tsoka loipitsitsa la dziko lonse, lomwe likanatiika tonsefe m’dera langozi, kuzingiratu dziko lonse? Buku lomwe lasonyeza kukhala maziko odalirika a uthenga wa ulosi limatichenjeza za kubwera kwa tsoka la dziko lonse ndipo limalongosola tsokalo motere: “Dzuŵa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka . . . mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa.” (Mateyu 24:29, 30) Panopa zochitika zodabwitsa za m’mlengalengazi padziko lonse lapansi zalongosoledwa kuti zidzakhudza “mitundu yonse ya padziko lapansi.” M’mawu ena, ulosi umenewu ukukamba za tsoka loipitsitsa lomwe lidzakhudza aliyense wa ife.

Buku la ulosi wodalirika limeneli ndilo Baibulo. Chochititsa chidwi n’chakuti mawu a lemba lomwe latchulidwa pamwambali akulongosola mwandondomeko zinthu zomwe zidzachitike tsoka ladziko lonse limenelo lisanayambe. Monga momwedi mulu wa matope osonyeza kuti phiri lidzaphulika ndi zinthu zina zosonyeza kuti phiri lili pafupi kuphulika zinaperekera zifukwa zabwino kwa akuluakulu a mzinda wa Shimabara zonenera kuti deralo ndi langozi, Baibulonso likutipatsa zifukwa zokhalira atcheru ndi kudzikonzekeretsa kuti tidzapulumuke. Tingatengerepo phunziro pa tsoka la pa Phiri la Fugen ndi kuzindikira kuopsa kokulira kwa zomwe zidzachitika m’tsogolo.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Yomiuri/​Orion Press/​Sipa Press

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Yomiuri/​Orion Press/​Sipa Press