Chikhulupiriro Chawo Chinafupidwa
Olengeza Ufumu Akusimba
Chikhulupiriro Chawo Chinafupidwa
MTUMWI Paulo anali mwamuna wa chikhulupiriro cholimba, ndipo analimbikitsa okhulupirira anzake kukhala ndi chikhulupiriro chofananacho. Anati: “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Nkhani zotsatirazi zochokera ku Mozambique zikusonyeza mmene Yehova amafupira chikhulupiriro cholimba ndi mapemphero ochokera pansi pa mtima.
• Mlongo wamasiye wa kudera la kumpoto la Niassa, anali ndi nkhaŵa kuti iye ndi ana ake asanu ndi mmodzi apita bwanji ku Msonkhano Wachigawo wa “Njira ya Moyo ya Mulungu.” Njira yokha imene amapezera ndalama inali kugulitsa katundu pamsika. Koma pamene tsiku la msonkhano linayandikira, ndalama zokha zomwe anali nazo zinali zokwanira kulipirira ulendo wawo wa pasitima ya pamtunda popita pokha basi. Ngakhale zinali choncho, anadalira Yehova kuti awathandiza ndipo sanasinthe maganizo ake okapezeka kumsonkhano wachigawo.
Anakwera sitima pamodzi ndi ana ake asanu ndi mmodziwo. Ali paulendowo kondakitala anafika kuti am’dulire tikiti. Ataona baji lomwe anavala, anafuna kudziŵa kuti linali kusonyeza chiyani. Mlongoyu anamuuza kuti linali chizindikiro chakuti anali mmodzi wa okapezeka nawo pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. “Kodi msonkhano umenewu ukachitikira kuti?” kondakitalayo anafunsa. Atazindikira kuti msonkhanowo ukachitikira kudera loyandikira la Nampula, pafupifupi makilomita 300, mosayembekezeka anam’lipitsa theka la mtengo wa tikiti! Komanso anapatsa mlongoyo ndi banja lake matikiti obwerera patheka la ndalama zotsala zija. Anasangalala kwambiri poika chidaliro chake mwa Yehova!—Salmo 121:1, 2.
• Kwa zaka pafupifupi 25, mayi wina wopembedza ankapemphera kwa Mulungu kuti amuonetse njira yolondola yomulambirira. Tchalitchi chomwe amapitako chinali kuphatikiza miyambo yachipembedzo ndi yachikunja, ndipo anakayikira ngati kulambira kotere kumasangalatsa Mulungu.
Akufotokoza kuti: “Nthaŵi zonse ndimakumbukira mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 7:7 akuti: ‘Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.’ Ndikakumbukira lemba limeneli, ndimapemphera kaŵirikaŵiri kwa Mulungu kuti andisonyeze choonadi. Tsiku lina abusa a mpingo wathu anapempha tonse amene timagwira ntchito mumsika kuti tiwapatse ndalama pamodzi ndi akatundu kuti azidalitse. Ndinaganiza kuti zimene amapemphazo sizikugwirizana ndi malemba ayi, ndiye sindinapereke kena kalikonse. Pamene mbusa anaona kuti sindinapereke ‘choperekacho,’ anayamba kundinyoza pamaso pa gulu lonse la tchalitchi. Tsiku lomwelo ndinazindikira kuti imeneyi si njira imene Mulungu amafuna kum’lambiriramo, choncho ndinachoka m’tchalitchicho. Komano, ndinalimbikira kupemphera kuti ndipeze choonadi.
“Pomalizira pake, n’talimba mtima ndinapita kwa wachibale amene anali wa Mboni za Yehova. Anandipatsa thirakiti, ndipo nditaŵerenga ndinadziŵa nthaŵi yomweyo kuti Mulungu akuyankha mapemphero anga. M’kupita kwa nthaŵi, chibwenzi changa chinayamba kuyamikira choonadi cha Baibulo, ndipo tinakalembetsa ukwati wathu. Ndiye pambuyo pake, mwamuna wanga anayamba kudwala kodetsa nkhaŵa. Koma kufikira imfa yake, anandilimbikitsa kusasiya njira ya choonadi kuti tikaonanenso m’Paradaiso.
“Ndimayamika Yehova nthaŵi zonse chifukwa chondiyankha mapemphero anga komanso kundionetsa njira yolondola yom’lambirira. Mapemphero anga ayankhidwanso chifukwa chakuti ndaona ana anga asanu ndi atatu onse akukhala atumiki odzipatulira a Yehova.”