Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Yehova ndi Mtima Wokonzekera

Kufunafuna Yehova ndi Mtima Wokonzekera

Kufunafuna Yehova ndi Mtima Wokonzekera

EZARA wansembe m’Israyeli anali kufufuza Chilamulo mwakhama. Analinso katswiri, mlembi komanso mphunzitsi wa Chilamulocho. Ali chitsanzo chabwino kwa Akristu lerolino monga munthu wodzipereka ndi mtima wake wonse pa utumiki wake. Motani? Chifukwa anasungabe kudzipereka kwake kwaumulungu ngakhale pamene anali ku Babulo, mzinda wodzala ndi milungu yonyenga komanso kulambira ziwanda.

Kudzipereka kwaumulungu kumene Ezara anali nako sikunachitike mwamwayi. Anachitirapo khama. Inde, akutiuza kuti ‘adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita.’​—Ezara 7:10.

Mofanana ndi Ezara, anthu a Yehova lerolino amafuna kuchita zonse zomwe Yehova amafuna kwa iwo pamene akukhala m’dziko limene limatsutsa kulambira koona. Tsopano tiyeni tipende zina mwa njira zimene ifenso tingakonzekeretse mitima yathu, munthu wam’kati​—kuphatikizapo maganizo athu, mzimu wathu, zokhumba zathu, komanso zolinga zathu​—kuti ‘tifune chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita.’

Kukonzekeretsa Mtima Wathu

Liwulo “adaikiratu” likutanthauza “kukonzekera pasanakhale muli ndi cholinga: kulinganiza chinthu kaamba ka ntchito inayake, kuti chigwiritsidwe ntchito, kapena kuchikonzekeretsa. Zoona, ngati mwapeza chidziwitso cholongosoka chonena za Mawu a Mulungu ndipo mwapatulira moyo wanu kwa Yehova, ndiye kuti mtima wanu wakhaladi wokonzekeretsedwa ndipo ungafanizidwe ndi “nthaka yabwino” imene Yesu ananena m’fanizo la wofesa.​—Mateyu 13:18-23.

Ngakhale zili choncho, mtima wathu umafuna kuusamalira ndiponso kuukonza nthaŵi zonse. N’chifukwa chiyani? Pali zifukwa ziŵiri. Choyamba, zizoloŵezi zoipa, ngati namsongole m’munda, zingamere mwamsanga, makamaka “masiku otsiriza” ano pamene “mlengalenga” wa dongosolo la Satana wangodzala mbewu zoipa zokhazokha za maganizo athupi. (2 Timoteo 3:1-5; Aefeso 2:2) Chifukwa chachiŵiri chikukhudza nthaka yeniyeniyo. Ngati nthakayo sisamalidwa ingakhale youma, yolimba, komanso yosabala. Mwina anthu ambiri posasamala angamaponde mundawo mpaka nthakayo n’kulimba. Nthaka yophiphiritsa ya mtima wathu ndi yofanana. Ingakhale yopanda chonde ngati sisamalidwa kapena ngati ipondedwa ndi anthu amene alibe nawo chidwi umoyo wathu wauzimu.

Ndiye tonsefe tifunika kugwiritsa ntchito langizo la Baibulo lakuti: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”​—Miyambo 4:23.

Zinthu Zowonjeza Chonde mu “Nthaka” ya Mtima Wathu

Tiyeni tipende zinthu zina, kapena mikhalidwe, yomwe imawonjeza chonde mu “nthaka” ya mtima wathu kuti ulole mbewu kukula bwino. Inde, pali zinthu zambiri zomwe zingathandize mtima wathu, koma pano tipenda zisanu ndi chimodzi: kuzindikira zosoŵa zathu zauzimu, kudzichepetsa, kuona mtima, mantha aumulungu, chikhulupiriro, ndiponso chikondi.

“Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu,” Yesu anatero. (Mateyu 5:3, NW) Mofanana ndi njala ya chakudya imene imatikumbutsa kuti tidye, kuzindikira kusoŵa kwathu kwauzimu kumatimvetsa njala ya chakudya chauzimu. Mwachibadwa, anthu ali ndi njala ya chakudya chimenechi chifukwa chimachititsa moyo kukhala ndi tanthauzo ndiponso cholinga. Zovuta za m’dongosolo la Satana la zinthu kapena kungogwa ulesi woŵerenga zingachepetse mphamvu yathu yozindikira chosoŵa chimenechi. Ngakhale zili choncho, Yesu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.”​—Mateyu 4:4.

Kudya chakudya chabwino cha magulu onse nthaŵi zonse kumapatsa thanzi, komanso kumasonkhezera thupi kukhalanso ndi njala ya chakudya chinanso nthaŵi yake ikakwana. Zilinso choncho ndi chauzimu. Mungaganize kuti sindinu munthu wokonda kuŵerenga, koma ngati muli ndi chizoloŵezi choŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku ndiponso zofalitsa zozikidwa m’Baibulo mokhazikika, mudzaona kuti njala yanu ikukula. Ndipotu, mudzayembekeza mwachidwi nthaŵi yotsatira yophunzira Baibulo. Ndiyetu musagonje wambawamba, chitani khama kuti mukulitse njala yabwino yauzimu.

Kudzichepetsa Kumafeŵetsa Mtima

Kudzichepetsa n’kofunika kwambiri kuti tikonzekeretse mtima wathu chifukwa kumatithandiza kukhala ophunzitsika ndiponso kulandira uphungu ndi chilangizo mwamsanga. Talingalirani chitsanzo chabwino cha Mfumu Yosiya. Nthaŵi imene anali kulamulira, mpukutu wokhala ndi Chilamulo cha Mulungu choperekedwa kudzera kwa Mose unapezeka. Pamene Yosiya anamva mawu a Chilamulo ndi kuzindikira mmene makolo ake anapatukira pa kulambira koyera, anang’amba zovala zake ndi kulira pamaso pa Yehova. Kodi n’chifukwa chiyani Mawu a Mulungu anagwira mtima wa Mfumuyo? Nkhaniyo imati anali ndi mtima ‘wowolowa,’ kotero kuti anadzichepetsa pamene anamva mawu a Yehova. Yehova anaona kuti Yosiya anali ndi mtima wodzichepetsa komanso womvera ndipo pachifukwa chimenecho anam’dalitsa.​—2 Mafumu 22:11, 18-20.

Kudzichepetsa kunatheketsa ophunzira a Yesu “osaphunzira ndi opulukira” kumvetsa komanso kugwiritsa ntchito choonadi chauzimu chomwe sanazindikire anthu “anzeru ndi ozindikira” koma “monga mwa thupi.” (Machitidwe 4:13; Luka 10:21; 1 Akorinto 1:26) Ameneŵa sanali okonzekera kulandira mawu a Yehova chifukwa mitima yawo inali itauma ndi kunyada. Kodi n’zodabwitsa kuti Yehova amadana ndi kunyada?​—Miyambo 8:13; Danieli 5:20.

Kuona Mtima ndi Mantha Aumulungu

Mneneri Yeremiya analemba kuti “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziŵa?” (Yeremiya 17:9) Kunyenga kwa mtima kumeneku kumaonekera m’njira zosiyanasiyana, monga ngati pamene tidzikhululukira tokha titachimwa. Kumaonekanso pamene tipeputsa mbali zolakwika za umunthu wathu. Koma kuona mtima kudzatithandiza kugonjetsa mtima wathu wonyenga potithandiza kuvomereza zolakwa zathu kotero kuti tiziwongole. Wamasalmo anasonyeza kuona mtima kumeneku pamene anapemphera kuti: “Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.” Inde, wamasalmo anali atakonzekeretsa mtima wake kuti Yehova auyeretse ndi kuuyesa, ngakhale kuti zimenezi zingakhale zitafuna kuti iye avomereze kuti anali ndi mikhalidwe yoipa yonga zitoto yofunikira kuigonjetsa.​—Salmo 17:3; 26:2.

Mantha aumulungu, omwe amaphatikizapo “kuda zoipa,” ndi chida chothandiza kwambiri pa kuyeretsa kumeneku. (Miyambo 8:13) Pamene kuli kwakuti munthu amene amaopadi Yehova amayamikira kukoma mtima kwake ndi ubwino wake, amazindikiranso kuti Yehova ali ndi mphamvu yopereka chilango, ngakhale imfa, kwa iwo osamvera iye. Yehova anasonyeza kuti awo amene amamuopa ayeneranso kumumvera pamene ananena za Israyeli kuti: “Ha! mwenzi akadakhala nawo mtima wotere wa kundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana awo nthaŵi zonse!”​—Deuteronomo 5:29.

Mwachionekere, cholinga cha mantha aumulungu sichakuti tizigonjera mwamantha, koma kutisonkhezera kumvera Atate wathu wachikondi, amene tikum’dziŵa kuti amatifunira zabwino. Indetu, mantha aumulungu otere ndi abwino ndiponso opatsa chimwemwe, chimene chinasonyezedwa ndi Yesu Kristu.​—Yesaya 11:3; Luka 12:5.

Mtima Wokonzekera Uli ndi Chikhulupiriro Chachikulu

Mtima wa chikhulupiriro cholimba umadziŵa kuti zilizonse zimene Yehova amafuna kapena kutilamula kuchita kudzera m’Mawu ake n’zabwino nthaŵi zonse ndiponso zopindulitsa. (Yesaya 48:17, 18) Munthu amene ali ndi mtima wotere amakhutira komanso amasangalala kugwiritsa ntchito langizo lopezeka pa Miyambo 3:5, 6 lakuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” Komabe, mtima wosoŵa chikhulupiriro sufuna kukhulupirira Yehova, makamaka ngati kuteroko kukufuna kudzimana, monga kukhala ndi moyo wosafuna zambiri kuti munthu aike mtima pa zinthu za Ufumu. (Mateyu 6:33) Ndiye chifukwa chake Yehova amaona mtima wosakhulupirira kukhala “woipa.”​—Ahebri 3:12.

Timasonyeza kukhulupirira kwathu Yehova m’njira zambiri, kuphatikizapo zinthu zimene timachita kunyumba tili tokhatokha. Mwachitsanzo, titatenga mfundo yachikhalidwe ya pa Agalatiya 6:7 imene imati: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” Timasonyeza kuti mfundo imeneyi timaikhulupirira mwa zinthu zonga mafilimu amene timaonera, mabuku amene timaŵerenga, nthaŵi imene timathera kuphunzira Baibulo komanso m’mapemphero athu. Inde, tifunikira chikhulupiriro cholimba chimene chimatisonkhezera kufesera “kwa Mzimu” kuti tikhale ndi mtima wokonzekera kuvomereza Mawu a Yehova ndiponso kuwamvera.​—Agalatiya 6:8.

Chikondi​—Mkhalidwe Waukulu

Kupambana mikhalidwe ina yonse, chikondi chimapangitsa nthaka ya mtima wathu kumvera Mawu a Yehova. N’chifukwa chake, pochiyerekeza ndi chikhulupiriro ndi chiyembekezo, mtumwi Paulo anafotokoza chikondi kukhala “chachikulu cha izi.” (1 Akorinto 13:13) Mtima umene umakonda Mulungu kwambiri umakhutira zedi komanso umasangalala kumvera iye; sudandaula ndi zofuna za Mulungu. Mtumwi Yohane anati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Mofananamo Yesu anati: “Ngati wina akonda Ine, adzasunga mawu anga; ndipo Atate wanga adzam’konda.” (Yohane 14:23) Zindikirani kuti mtundu umenewu wa chikondi ndi uja woti wina akakukonda iwenso um’konde. Inde, Yehova amakondadi awo amene amam’yandikira chifukwa chom’konda.

Yehova amadziŵa kuti ndife opanda ungwiro ndi kuti nthaŵi ndi nthaŵi timachimwa. Ngakhale zili choncho, satalikirana nafe. Chomwe Yehova amafuna mwa atumiki ake ndi “mtima wangwiro” umene umatisonkhezera kum’tumikira mofunitsitsa ndi “moyo waufulu.” (1 Mbiri 28:9) Inde, Yehova amadziŵa kuti zimatenga nthaŵi komanso zimafuna khama kuti mtima wathu ukhale ndi mikhalidwe yabwino ndiyeno kubala zipatso za mzimu. (Agalatiya 5:22, 23) N’chifukwa chake amaleza mtima nafe “popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Pokhala ndi maganizo omwewo, Yesu sanadzudzule ophunzira ake mopitirira muyezo chifukwa cha zolakwa zawo koma anawathandiza ndi kuwalimbikitsa moleza mtima. Kodi chikondi chotere, chifundo, ndi kuleza mtima kwa Yehova ndi Yesu sizikukusonkhezerani kuwakonda kwambiri?​—Luka 7:47; 2 Petro 3:9.

Ngati nthaŵi zina mumavutika kuzula zizoloŵezi zolimba ngati namsongole kapena kusiya khalidwe lovuta, musagwe ulesi kapena kutaya mtima. M’malo mwake, limbikirani kuwongolera pamene ‘mulimbika chilimbikire m’kupemphera,’ kuphatikizapo kupembedzera Yehova mobwerezabwereza kuti akupatseni mzimu wake. (Aroma 12:12) Pokhala ali wofunitsitsa kukuthandizani, mofanana ndi Ezara, mudzakhala ndi mtima wokonzekera bwino “kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita.”

[Chithunzi patsamba 31]

Ezara anakhalabe wodzipereka kwa Mulungu ngakhale ali ku Babulo

[Mawu a Chithunzi patsamba 29]

Garo Nalbandian