Mphamvu ya Pemphero
Mphamvu ya Pemphero
Dzuŵa likuloŵa litadutsa pamwamba pa mzinda wa Nahori ku Middle East. Msuriya wina yemwe dzina lake ndi Eliezere akufika ndi namtindi wa ngamila khumi pachitsime china kunja kwa mzindawo. Ngakhale kuti mosakayikira iye ali wotopa ndi waludzu, Eliezere akulingalirako zofuna za ena. Wachokera kudziko lina kudzafuna mkazi wa mwana wa mbuye wake. Komanso, ayenera kupeza mkazi ameneyu pakati pa abale a mbuye wake. Kodi akwanitsa motani ntchito yovutayi?
ELIEZERE amakhulupirira m’mphamvu ya pemphero. Ndi chikhulupiriro champhamvu chonga cha mwana, akupempha modzichepetsa kuti: “Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lerolino, mum’chitire ufulu mbuyanga Abrahamu. Taonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana aakazi a m’mudzi atuluka kudzatunga madzi; ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo chotero ndidzadziŵa kuti mwam’chitira mbuyanga ufulu.”—Genesis 24:12-14.
Chidaliro cha Eliezere m’mphamvu ya pemphero sichikupita pachabe. Inde, zikuchitikadi kuti mkazi woyambirira kudza pachitsimecho ndiyedi mdzukulu wamkazi wa mbale wake wa Abrahamu! Dzina lake ndi Rebeka, ndipo n’ngwosakwatiwa, wodzisunga, komanso wokongola. Chosangalatsa n’chakuti, iye sakupatsa Eliezere yekha madzi akumwa komanso mwachifundo akudzipereka kupha ludzu la ngamila zake zonse. Pambuyo pake, banja litatha kukambirana, Rebeka mofunitsitsa akuvomera kubwerera limodzi ndi Eliezere kudziko lakutali kukakhala mkazi wa Isake mwana wa Abrahamu. Linalitu yankho logwira mtima ndi loonekeratu la pemphero la Eliezere kalero panthaŵi yomwe Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi amaloŵerera mozizwitsa m’zochitika!
Tingaphunzire zambiri m’pemphero la Eliezerelo. Likusonyeza chikhulupiriro, kudzichepetsa, ndi kulabadira kwake zofuna za ena mopanda dyera. Pemphero la Eliezere linasonyezanso kugonjera kwake pa njira ya Yehova yochitira ndi mtundu wa anthu. Mwachionekere iye amadziŵa bwino za ubwenzi wapadera wa Mulungu ndi Abrahamu komanso lonjezo Lake lakuti madalitso a m’tsogolo adzagwera mtundu wonse wa anthu kupyolera mwa Abrahamu. (Genesis 12:3) N’chifukwa chaketu Eliezere anayamba pemphero lakelo ndi mawu akuti: “Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu.”
Yesu Kristu anali mbadwa ya Abrahamu yemwe anali njira yodalitsira mtundu wonse wa anthu omvera. (Genesis 22:18) Ngati tikufuna kuti mapemphero anthu ayankhidwe lerolino, tifunikira kusonyeza modzichepetsa kuzindikira njira zomwe Mulungu akuchitira ndi mtundu wa anthu kupyolera mwa Mwana wake. Yesu Kristu anati: “Ngati mukhala mwa Ine, ndi mawu anga akhala mwa inu, pemphani chimene chilichonse muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.”—Yohane 15:7.
Wotsatira wa Kristu yemwe anaona kuti mawu a Yesu ameneŵa analidi oona anali mtumwi Paulo. Chikhulupiriro chake m’pemphero mwachionekere sichinapite pachabe. Analimbikitsa Akristu anzake kupereka nkhaŵa zawo zonse kwa Mulungu m’pemphero ndi kuvomereza kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:6, 7, 13) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti zonse zimene Paulo anapempha kwa Mulungu zinapatsidwa kwa iye? Tiyeni tione.
Zina Zimene Timapempha Siziperekedwa
Muutumiki wake wosadzikondawo, Paulo anavutika ndi chomwe anachilongosola kukhala “munga m’thupi.” (2 Akorinto 12:7) Zimenezi zikanatha kukhala kuvutika m’maganizo ndi mumtima chifukwa cha otsutsa ndi “abale onyenga.” (2 Akorinto 11:26; Agalatiya 2:4) Kapena kungathe kukhala kusamva bwino m’thupi kaamba ka vuto lalikulu la maso. (Agalatiya 4:15) Mulimonse momwe zinalili, ‘munga m’thupiwu’ unali wofoola kwa Paulo. Iye analemba kuti: “Ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine.” Komabe, zomwe Paulo anapempha sizinaperekedwe. Paulo anauzidwa kuti mapindu auzimu omwe anali atalandira kale kuchokera kwa Mulungu, monga mphamvu ya kupirira chiyeso, anali okwanira. Komanso, Mulungu anati: “Mphamvu yanga ithedwa [“ikhala yangwiro,” NW] m’ufooko.”—2 Akorinto 12:8, 9.
Kodi tikuphunziranji m’zitsanzo za Eliezere ndi Paulo? Ndithudi Yehova Mulungu amamvetsera mapemphero a awo amene modzichepetsa amafuna kum’tumikira. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti nthaŵi zonse amapereka zimene iwo apempha chifukwa Mulungu amaona zinthu zidakali patali. Amadziŵa bwino zimene zili m’malingaliro mwathu kuposa momwe ifeyo timadziŵira. Chofunika koposa, iye nthaŵi zonse amachita zinthu mogwirizana ndi chifuno chake chonenedwacho monga momwe chalembedwera m’Baibulo.
Nthaŵi ya Kuchiritsa Mwauzimu
Mulungu akulonjeza kudzachiza mtundu wa anthu ku nthenda zonse zakuthupi, za m’maganizo, ndi za mu mtima m’kati mwa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Mwana wake padziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 20:1-3; 21:3-5) Akristu okhulupirika akuyembekezera mwachidwi m’tsogolo molonjezedwa mmenemo, ndi chikhulupiriro chonse m’mphamvu ya Mulungu yotheketsa zimenezo. Pamene kuli kwakuti sakuyembekezera kuti kuchiritsa kozizwitsako kuchitidwa tsopano lino, amapempha chitonthozo ndi chilimbikitso kwa Mulungu kuti athe kupirira ziyeso. (Salmo 55:22) Pamene adwala, angapemphenso chitsogozo cha Mulungu kuti apeze thandizo labwino kwambiri lamankhwala mogwirizana ndi ndalama zimene angakhale nazo.
Zipembedzo zina lerolino zimalimbikitsa odwala kupemphera kuti achiritsidwe tsopano, akumalingalira za kuchiritsa kozizwitsa kumene Yesu ndi ophunzira ake anakuchita. Koma zozizwitsa zoterozo zinkachitika ndi cholinga chapadera. Zinagwira ntchito yosonyeza kuti Yesu Kristu analidi Mesiya weniweni ndi kusonyeza kuti Mulungu sanalinso kuyanja mtundu wa Ayuda koma mpingo waung’ono wachikristu. Kalelo, mphatso zozizwitsa zinafunikadi kuti zilimbitse chikhulupiriro cha mpingo wachikristu wongokhazikitsidwa chatsopanowo. Mpingo waung’onowo utakhazikika, ndikukhala wokhwima, mphatso zozizwitsa ‘zidakhala chabe.’—1 Akorinto 13:8, 11.
Panthaŵi yamapeto ino, Yehova Mulungu akutsogolera olambira ake ku ntchito yofunika kwambiri ya kuchiritsa mwauzimu. Popeza kuti nthaŵi adakali nayo, anthu afunikira kutsatira mwamsanga pempho lake lakuti: “Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzam’chitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.”—Yesaya 55:6, 7.
Kuchiritsidwa kwauzimu kumeneku kwa ochimwa olapa kukukwaniritsidwa kupyolera mu ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Mwa kupatsa mphamvu atumiki ake kuti agwire ntchito yopulumutsa moyo imeneyi, Yehova Mulungu akuthandiza anthu miyandamiyanda amitundu yonse kulapa machimo awo ndi kukhala naye paubwenzi wolimba mapeto a dongosolo loipali asanadze. Onse amene amapempha machiritso auzimu oterowo komanso onse amene amapempha thandizo kuti agwire ntchito yochiritsayo ndithudi, mapemphero awo akuyankhidwa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Eliezere ndi Rebeka/The Doré Bible Illustrations/Dover Publications