Chifukwa Chimene Mtundu wa Anthu Ukufunira Nkhoswe
Chifukwa Chimene Mtundu wa Anthu Ukufunira Nkhoswe
‘NDINALI wolondalonda wamwano,’ anavomereza motero yemwe kalero anali munthu wonyada ndi wachiwawa. Iye anali wolankhula mwachipongwe yemwe mwankhanza ankasautsa ndi kuzunza otsatira a Yesu Kristu oopa Mulungu. “Komatu anandichitira chifundo.” Iye anatero mothokoza. Ngakhale kuti zingaoneke ngati zovuta kuzikhulupirira, wozunza wankhwidzi ameneyu anadzakhala mtumwi wokhulupirika wachikristu, Paulo.—1 Timoteo 1:12-16; Machitidwe 9:1-19.
Sikuti aliyense wachitako zinthu zomwe Pauloyo anachita. Komabe, tonsefe timalephera kukwaniritsa miyezo ya Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Komanso, n’chapafupi kulefulidwa ndi nkhaŵa, mwinamwake kulingalira kuti ndife oipitsitsa mwakuti sitingalandire chifundo cha Mulungu. Posinkhasinkha za ziyambukiro zake zauchimo, Paulo mwiniyo anati: “Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?” Poyankha funso lake lomwe, iye analemba kuti: “Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.”—Aroma 7:24, 25.
M’motani momwe Mlengi wolungamayo angayanjire ochimwa? (Salmo 5:4) Onani kuti Paulo anati: ‘Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.’ Winanso yemwe analandira chifundo cha Mulungu anafotokoza kuti: “Akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.”—1 Yohane 2:1, 2.
N’chifukwa chiyani Yesu Kristu akutchedwa ‘Nkhoswe ya kwa Atate’? Ndipo kodi m’motani momwe Yesuyo alili “chiombolo” cha machimo?
Chifukwa Chake Nkhoswe Ikufunika
Yesu anadza kudziko lapansi “ku[dza]pereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Dipo ndi malipiro operekedwa kuwombola, kapena kuti winawake kapena chinachake chimasulidwe. Mneni wachihebri wotembenuzidwa kuti “dipo” amapereka lingaliro la kuphimba, kapena kulipirira, machimo. (Salmo 78:38) Liwu lachigiriki longa limene likupezeka pa Mateyu 20:28, analigwiritsa ntchito kwenikweni ponena za mtengo wolipiridwa kuwombola akaidi ankhondo kapena kumasula akapolo. Pofuna kukwaniritsa zofunika pa chilungamo, chinthu chimodzi chikuperekedwa posinthanitsa ndi china cholingana nacho mtengo.
Mtundu wa anthu unaloŵa mu ukapolo chifukwa chakuti munthu woyambayo anapandukira Mulungu. Monga momwe kwasonyezedwera pa Genesis chaputala 3, munthu wangwiro ameneyo, Adamu, anasankha kulondola njira ya kusamvera Yehova Mulungu. Mwa kuchita zimenezo, anadzigulitsa yekha ku ukapolo wa tchimo ndi imfa, limodzi ndi mbadwa zake zimene panthaŵiyi zinali zisanabadwe. Chotero Adamu anataya mphatso ya moyo wake waumunthu wangwiro ndi wa mbadwa zake zonse.—Aroma 5:12, 18, 19; 7:14.
Mu Israyeli wakale, Mulungu analinganiza kuti nsembe zanyama zidziperekedwa kulipirira kapena kuphimba machimo a anthu. (Levitiko 1:4; 4:20, 35) Chotero, moyo wa nyama yophedwera nsembe unkaperekedwa m’malo mwa munthu wochimwayo. (Levitiko 17:11) Choncho, “tsiku la chitetezero” ankalitchanso “tsiku la malipo.”—Levitiko 23:26-28.
Komabe, popeza kuti nyama n’zotsika poziyerekeza ndi munthu, “sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo [kotheratu].” (Ahebri 10:1-4) Kuti nsembe ikhale yamtengo woyenereradi kuwombola kapena kuchotseratu machimo onse, inayenera kukhala yolingana mtengo wake ndi womwe anataya Adamuwo. Muyeso wa chilungamo unafuna munthu wangwiro (Yesu Kristu) kuti apereke cholingana ndi chomwe munthu winanso wangwiro (Adamu) anataya. Moyo wa munthu wangwiro wokha ndiwo ukanalipirira mtengo wa dipo kuwombola mbewu za Adamu muukapolo umene atate wawo woyambayo anawagulitsa. “Moyo kulipa moyo” n’zomwe zinafunikira kuti chilungamo chenicheni chikwaniritsidwe.—Eksodo 21:23-25.
Adamu atachimwa ndipo ataweruzidwira ku imfa, mbadwa zake zomwe zinali zisanabadwe panthaŵiyo zinali zidakali m’chiuno mwake chotero zinafa naye limodzi. Munthu wangwiro Yesu, “Adamu wotsirizayo,” mofunitsitsa sanapange mbumba. (1 Akorinto 15:45) Anali ndi mbewu zosabadwa m’chiuno mwake pamene anafa monga nsembe ya munthu wangwiro. Chotero, kunganenedwe kuti mtundu wa anthu womwe udakatuluka m’chiuno mwake unafa naye limodzi. Yesu anatenga mbumba ya Adamu yochimwa ndi yomafayo kukhala ngati yakeyake. Sanafune kukhala ndi mbumba yakeyake. Mwa kupereka nsembe moyo wake wangwiro wa umunthuwo, Yesu anagulanso mtundu wonse wa anthu wochokera kwa Adamu kotero kuti ukhale fuko lake, kum’pangitsa iyeyo kukhala “Atate [wawo] Wosatha.”—Yesaya 9:6, 7.
Nsembe ya dipo ya Yesu inatsegulira njira mtundu wa anthu okhulupirika kuti akalandire chifundo cha Mulungu ndi kukapeza moyo wosatha. Ndiye chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Ndife osonkhezereka mtima kutamanda Yehova kaamba ka chikondi ndi chifundo zosonyezedwa mwa dipo, loperekedwa pamtengo waukulu zedi kwa iye mwiniyo ndi kwa Mwana wake wokondedwayo. (Yohane 3:16) Ndipotu Yesu anasonyezadi kukhala ‘Nkhoswe ya kwa Atate’ pamene anaukitsidwira ku moyo wakumwamba ndi kukapereka mtengo wa nsembe yake ya dipo kwa Mulungu kumwambako. * (Ahebri 9:11, 12, 24; 1 Petro 3:18) Komano kodi lerolino Yesu Kristu akusonyeza motani kukhala nkhoswe yathu kumwamba?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 Onani machaputala 4 ndi 7 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 4]
Moyo wangwiro wa munthuyo Yesu unakhala malipiro owombolera mbadwa za Adamu