Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudzichepetsa—Mkhalidwe Umene Umalimbikitsa Mtendere

Kudzichepetsa—Mkhalidwe Umene Umalimbikitsa Mtendere

Kudzichepetsa​—Mkhalidwe Umene Umalimbikitsa Mtendere

Dzikotu likanakhala losangalatsa kwabasi chikhala kuti aliyense akusonyeza kudzichepetsa. Anthu sakanakhala oumirira zinthu kwambiri, sibwenzi anthu akukanganakangana m’mabanja mwawo, sibwenzi makampani akulimbana kwambiri pochita malonda, ndiponso mitundu sikanakhala yokonda nkhondo. Kodi mungakonde kukhala m’dziko ngati limenelo?

ATUMIKI oona a Yehova Mulungu akukonzekera dziko lapansi latsopano limene iye analonjeza, mmene anthu onse azidzaona kudzichepetsa, osati monga kufooka, koma monga nyonga komanso khalidwe labwino. (2 Petro 3:13) Ndipotu akuphunzira mkhalidwe wa kudzichepetsa ngakhale tsopano. Chifukwa chiyani? Makamaka chifukwa chakuti n’zimene Yehova akufuna kwa iwo. Mneneri wake Mika analemba kuti: “Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”​—Mika 6:8.

Kudzichepetsa kungatanthauze zinthu zingapo, monga kusadziona ngati woposa ena, kapena kusadzitukumula, ndiponso kusafuna kudzitama chifukwa cha maluso ako, zomwe wakwaniritsa, ndiponso chuma chako. Malinga n’kunena kwa buku lina lamaumboni, kudzichepetsa kumatanthauzanso “kusapitirira malire.” Munthu wodzichepetsa sapitirira malire a khalidwe labwino. Amadziŵanso kuti zinthu zimene ayenera kuchita ndiponso zimene amatha kuchita zili ndi malire ake. Amadziŵa kuti pali zinthu zimene alibe ulamuliro wozichita. Timakopekadi ndi anthu odzichepetsa. “Palibe chinthu chosiririka ngati kudzichepetsa kwenikweni,” analemba motero wandakatulo wina wachingelezi Joseph Addison.

Kudzichepetsa si mkhalidwe wachibadwa mwa anthu opanda ungwiro. Tiyenera kuyesetsa zolimba kuti tikhale ndi mkhalidwe umenewu. Pofuna kutilimbikitsa, Mawu a Mulungu amasimba zochitika zingapo zosonyeza kudzichepetsa kosiyanasiyana.

Mafumu Aŵiri Odzichepetsa

Mmodzi mwa atumiki a Yehova okhulupirika kwambiri anali Davide, amene anali mnyamata pomwe amadzozedwa kukhala mfumu yam’tsogolo ya Israyeli. Kuyambira pamenepo, Mfumu Sauli yemwe anali kulamulira anavutitsa Davide kwambiri poyesayesa kumupha ndi kum’kakamiza kukhala moyo wothaŵathaŵa.​—1 Samueli 16:1, 11-13; 19:9, 10; 26:2, 3.

Ngakhale m’mikhalidwe yovuta ngati imeneyo, Davide anadziŵa kuti zimene angachite pofuna kuteteza moyo wake zili ndi malire ake. Panthaŵi ina ali m’chipululu, Davide anakana kulola Abisai kuti aphe Mfumu Sauli yemwe anali m’tulo, nati: “Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.” (1 Samueli 26:8-11) Davide anadziŵa kuti kuchotsa Sauli pa mpando waufumu ndiko kupitirira malire ake. Chotero Davide anasonyeza kudzichepetsa pachochitika chimenechi mwa kusapitirira malire a khalidwe labwino. Momwemonso, atumiki amakono a Mulungu akudziŵa kuti ‘Yehova amawaletsa’ kuchita zinthu zina, ngakhale moyo wa munthu utakhala pangozi.​—Machitidwe 15:28, 29; 21:25.

Solomo, mwana wa Mfumu Davide, anasonyezanso kudzichepetsa pamene anali mnyamata, ngakhale kuti anatero m’njira yosiyanako. Pamene Solomo analongedwa ufumu, anadziona kukhala wosakwanira woti n’kunyamula udindo wolemerawo wa ufumu. Anapemphera kuti: “Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m’malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziŵa kutuluka kapena kuloŵa.” Ndithudi, Solomo anali kudziŵa kuti sangathe kuchita udindowo komanso analibe chidziŵitso. Chotero anali wodzichepetsa, sanadzione ngati wodziŵa zinthu, kapenanso sanadzitame. Solomo anapempha Yehova kuti am’patse kuzindikira, ndipo anam’yankhadi pempho lake.​—1 Mafumu 3:4-12.

Mesiya ndi Kalambulebwalo Wake

Patapita zaka zoposa 1,000 kuchokera m’tsiku la Solomo, Yohane Mbatizi anachita ntchito yokonzekeretsa njira ya Mesiya. Monga kalambulebwalo wa Wodzozedwa, Yohane anali kukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. Akanadzitama ndi mwayi wakewo. Yohane akanayesanso kudzipezera ulemu chifukwa chakuti anali mbale wakuthupi wa Mesiya. Koma Yohane anauza ena kuti sanali woyenerera ngakhale kumasula lamba la nsapato za Yesu. Ndipo pamene Yesu anadzipereka kuti abatizidwe m’Mtsinje wa Yordano, Yohane anati: “Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?” Zimenezi zikusonyeza kuti Yohane sanali munthu wodzitamandira. Anali wodzichepetsa.​—Mateyu 3:14; Malaki 4:5, 6; Luka 1:13-17; Yohane 1:26, 27.

Yesu atabatizidwa, anayamba utumiki wanthaŵi zonse, kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ngakhale kuti Yesu anali munthu wangwiro, iye anati: “Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; . . . sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.” Ndiponso, Yesu sanafune ulemu wa anthu, koma analemekeza Yehova pa chilichonse chimene anachita. (Yohane 5:30, 41-44) Kudzichepetsatu kochititsa chidwi!

Chotero, m’posakayikitsa kuti atumiki okhulupirika a Yehova, monga Davide, Solomo, Yohane Mbatizi, ndiponso ngakhale munthu wangwiroyo Yesu Kristu, anasonyeza kudzichepetsa. Sanadzitamandire, sanali onyada, kapena odziona ngati odziŵa zonse, ndipo sanapitirire malire. Zitsanzo zawo n’zifukwa zokwanira bwino kuti atumiki amakono a Yehova akhale odzichepetsa ndiponso asonyeze kudzichepetsako. Komabe, palinso zifukwa zina zokhalira otero.

M’nyengo yodzaza mavuto ino m’zochitika za anthu, kudzichepetsa ndi mkhalidwe wofunika kwambiri kwa Akristu oona. Kumapangitsa munthu kukhala pamtendere ndi Yehova Mulungu, anthu anzake, ndi iye mwini.

Mtendere ndi Yehova Mulungu

Mtendere ndi Yehova ndi wotheka pokhapokha ngati sitipitirira malire a kulambira koona amene anaika. Makolo athu oyambawo, Adamu ndi Hava, anapitirira malire oikidwa ndi Mulungu, ndipo anakhala anthu oyamba kukhala osadzichepetsa. Anatayikidwa mbiri yawo yabwino ndi Yehova, limodzi ndi mudzi wawo, tsogolo lawo, ndi miyoyo yawo. (Genesis 3:1-5, 16-19) Anakumanatu ndi zotsatira zoopsa zedi!

Tiyeni titengepo phunziro pa cholakwa cha Adamu ndi Hava, popeza kuti kulambira koona kumatiikira malire a mmene tiyenera kuchitira zinthu. Mwachitsanzo, Baibulo limaneneratu kuti “adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Mwanzeru Yehova anaika malire ameneŵa kuti tipindule, ndipo ndi nzeru kwa ife kusawadumpha malirewo. (Yesaya 48:17, 18) Miyambo 11:2 imatiuza kuti: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.”

Nangano bwanji ngati chipembedzo chikutiuza kuti tingadumphe malirewo ndi kukhalabe pamtendere ndi Mulungu? Chipembedzo chimenecho chikufuna kutisocheretsa. M’malo mwake, kudzichepetsa kumatithandiza kukulitsa unansi wolimba ndi Yehova Mulungu.

Mtendere ndi Anthu Anzathu

Kudzichepetsa kumalimbikitsanso kukhala mwamtendere ndi ena. Mwachitsanzo, pamene makolo asonyeza chitsanzo cha kukhutira ndi zimene ali nazo ndi kuika zinthu zauzimu patsogolo, ana awo nthaŵi zambiri adzakhalanso ndi mzimwu wofananawo. Anawo adzakhutira mwamsanga ndi zimene ali nazo, ngakhale kuti nthaŵi zina sadzapeza zonse zimene akufuna. Zimenezi zidzawathandiza kukhala modzichepetsa, ndipo moyo wa banja udzakhala pamtendere waukulu.

Oyang’anira ayenera kuonetsetsa kwambiri kuti ndi odzichepetsa ndipo ulamuliro wawo sakuugwiritsa ntchito molakwa. Mwachitsanzo, Akristu amalangizidwa kuti: ‘Musapitirire zimene zalembedwa.’ (1 Akorinto 4:6) Akulu a mumpingo amadziŵa kuti sayenera kukakamiza ena kutsatira zimene iwo amakonda. M’malo mwake, amagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu monga maziko olimbikitsira njira yabwino ya khalidwe, kavalidwe, kudzikongoletsa, kapena zosangalatsa. (2 Timoteo 3:14-17) Pamene ena onse a mumpingo aona kuti akulu sakudutsa malire a m’Malemba, zimenezi zimawalimbikitsa kuti azilemekeza amuna ameneŵa ndipo zimalimbikitsanso mzimu waubwenzi, wachikondi, ndi mtendere mumpingo.

Mtendere ndi Iwe Mwini

Anthu odzichepetsa amafupidwa ndi mtendere wamumtima. Munthu wodzichepetsa savutika maganizo chifukwa chosirira maudindo. Zimenezi sizikutanthauza kuti saika zolinga. Mwachitsanzo, atha kukhumba mwayi wowonjezereka wautumiki, koma amayembekeza kwa Mulungu, ndipo amatamanda Yehova pamwayi wachikristu uliwonse umene alandira. Samauona ngati kuti wabwera mwa nzeru zake. Zimenezi zimapangitsa wodzichepetsayo kuyandikira kwambiri kwa Yehova, “Mulungu wa mtendere.”​—Afilipi 4:9.

Tinene kuti nthaŵi zina timaona kuti anthu ena atinyalanyaza. Kodi sikwabwinopo kunyalanyazidwa chifukwa chakuti ndife odzichepetsa kusiyana n’kudzitchukitsa mosadzichepetsa? Anthu odzichepetsa sasirira maudindo monyanyira. Chotero, amakhala pamtendere, zimene zimapangitsa munthu kukhala pamtendere mumtima komanso kukhala wathanzi.

Kuphunzira Kudzichepetsa ndi Kukhalabe Wotero

Adamu ndi Hava anakhala osadzichepetsa, mkhalidwe umene anapatsira mbadwa zawo. Kodi n’chiyani chingatithandize kusabwereza cholakwa cha makolo athu oyambawo? Kodi tingakhale motani ndi mkhalidwe wabwino wa kudzichepetsa?

Choyamba, kudziŵa bwino lomwe amene tili poyerekeza ndi Yehova, Mlengi wa chilengedwe chonse, kudzatithandiza. Kodi n’zinthu zotani zomwe takwaniritsapo zomwe tingayerekeze ndi zimene Mulungu wakwaniritsa? Yehova anafunsa mtumiki wake wokhulupirikayo Yobu kuti: “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziŵa kuzindikira.” (Yobu 38:4) Yobu analibe yankho. Kodi ifenso sitili ochepa m’nzeru, mphamvu, ndi chidziŵitso mofananamo? Kodi sikopindulitsa kwa ife kumakumbukira kuti sitingathe kuchita zambiri?

Ndiponso, Baibulo limatiuza kuti: “Dziko lapansi n’la Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m’mwemo.” Zimenezi zikuphatikizapo “zamoyo zonse za kuthengo . . . ndi ng’ombe za pa mapiri zikwi.” Yehova amatha kunena kuti: “Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga.” (Salmo 24:1; 50:10; Hagai 2:8) Kodi ndi chuma chanji chimene tingakhale nacho chimene chingalingane ndi chuma cha Yehova? Inde, ngakhale munthu wolemera koposa padziko lonse lapansi alibe chifukwa chodzitamandira ndi zomwe ali nazo! Chotero, n’kwanzeru kutsatira uphungu wouziridwa wa mtumwi Paulo kwa Akristu a ku Roma. Uphunguwo umati: “Ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa.”​—Aroma 12:3.

Pokhala atumiki a Mulungu ofunitsitsa kukulitsa mkhalidwe wa kudzichepetsa, tiyenera kupempherera chipatso cha mzimu​—chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, kudziletsa. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti uliwonse wa mikhalidwe imeneyo udzatithandiza kwambiri kukhala odzichepetsa. Mwachitsanzo, chikondi chathu pa anthu anzathu chidzatithandiza kukana malingaliro ofuna kudzitama kapena kudziyesa woposa ena. Ndipo kudziletsa kudzatipangitsa kuima kaye ndi kuganiza tisanachite kanthu mosadzichepetsa.

Tiyeni tichenjere! Tikufunikira kukhala maso nthaŵi zonse kuti tisagwere m’mbuna ya kudzikuza. Aŵiri mwa mafumu aja otchulidwa poyamba sanakhale odzichepetsa nthaŵi zonse. Mfumu Davide anachita zinthu mwaphuma mwa kuŵerenga anthu m’Israyeli, chinthu chomwe chinasemphana ndi chifuno cha Yehova. Mfumu Solomo anakhala wosadzichepetsa mpaka anayamba kulambira konyenga.​—2 Samueli 24:1-10; 1 Mafumu 11:1-13.

Malinga ngati dongosolo losaopa Mulunguli lidakali pano, kukhala wodzichepetsa kumafuna kukhala maso nthaŵi zonse. Komabe, m’pakedi kuyesayesa motero. M’dziko latsopano la Mulungu, mudzangokhala anthu odzichepetsa basi. Adzaona kudzichepetsa monga nyonga, osati monga kufooka. Zidzakhala zabwino bwanji pamene anthu onse ndi mabanja onse adzadalitsidwa ndi mtendere womwe umadza ndi kudzichepetsa!

[Chithunzi patsamba 23]

Modzichepetsa, Yesu anathokoza Mulungu pazonse zimene anachita