Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuuza Ena za Chiyembekezo Chachikristu ku Senegal

Kuuza Ena za Chiyembekezo Chachikristu ku Senegal

Ndife a Iwo Omwe Ali Ndi Chikhulupiriro

Kuuza Ena za Chiyembekezo Chachikristu ku Senegal

NSOMBA zakhala chakudya chodalirika kuyambira nthaŵi zakale. Kwa zaka zikwi zambiri, anthu akhala akusodza m’nyanja zikuluzikulu ndi zing’onozing’ono zomwe komanso m’mitsinje. Ena mwa atumwi a Yesu Kristu anali asodzi ku Nyanja ya Galileya. Koma iwowa Yesu anawaphunzitsa kusodza kwa mtundu wina. Ndiko kusodza kwauzimu kumene kukanapindulitsa asodzi komanso nsombazo.

Za nkhani imeneyi, Yesu anauza Petro msodziyo kuti: “Kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.” (Luka 5:10) Usodzi wa mtundu uwu ukuchitika masiku ano m’mayiko opitirira 230, kuphatikizapo ku Senegal. (Mateyu 24:14) Kumeneku “asodzi a anthu” ameneŵa molimba mtima akuuza ena chiyembekezo chawo chachikristu.​—Mateyu 4:19.

Dziko la Senegal limapezeka kumadzulo kwenikweni kwa Afirika. Limayambira kudera lachipululu cha mchenga kumalire ndi Sahara kumpoto mpaka kudera la Casamance la nkhalango yalowe kumwera. Dziko la Senegal limaombedwa ndi mphepo yotentha yochokera ku chipululu komanso mphepo yozizira, yayeziyezi ya ku nyanja ya Atlantic. M’dziko limeneli muli anthu opitirira mamiliyoni asanu ndi anayi. Anthu a ku Senegal amadziŵika chifukwa cha kuchereza kwawo alendo. Anthu ambiri amati si Akristu. Ambiri ndi abusa a nkhosa, ndipo ena ndi a ng’ombe, ngamila ndi mbuzi. Kulinso alimi, amene amalima mtedza, thonje ndi mpunga. Inde, kulinso asodzi, amene amapha nsomba zambiri m’nyanja ya Atlantic ndi m’mitsinje ikuluikulu imene imadutsa dzikoli. Usodzi umathandiza kwambiri pa chuma cha Senegal. Kwenikweni chakudya chotchuka m’dzikoli ndi ceebu jën, chakudya chabwino cha mpunga, nsomba ndi ndiwo za masamba.

Asodzi a Anthu”

M’dzikoli la Senegal muli alaliki okangalika a Ufumu wa Mulungu okwanira 863. Usodzi wauzimu unayamba kumayambiriro a chaka cha 1950. Ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society inatsegulidwa ku Dakar, likulu la dzikolo, m’chaka cha 1965. “Asodzi” achimishonale anayamba kufika kuchokera ku mayiko ambiri akutali. Ntchito “yosodza” inayambika, ndipo kuuza ena za chiyembekezo chachikristu ku Senegal kunapita patsogolo ndithu. M’kupita kwa nthaŵi, nthambi yatsopano inamangidwa ku Almadies, kunja kwa mzinda wa Dakar, ndipo anaipatulira kwa Yehova mu June, 1999. Idalitu nthaŵi ya chisangalalo!

Vuto Lovomereza Choonadi

Anthu a mikhalidwe yosiyanasiyana akufikiridwa nthaŵi zambiri, ndipo ena alandira uthenga wopatsa chiyembekezo wopezeka m’Mawu a Mulungu. Ngakhale kuti ambiri salidziŵa Baibulo, amasangalala kuphunzira kuti zimene Yehova Mulungu analonjeza aneneri akale okhulupirika zidzakwaniritsidwa posachedwapa.

Kaŵirikaŵiri munthu afunikira kulimba mtima kuti atsate mfundo zachikristu, makamaka pamene nkhaniyo ikukhudza miyambo ya makolo ndi chikhalidwe cha anthu. Mwachitsanzo, ambiri ku Senegal amakwatira mitala. Talingalirani nkhani ya bambo wina amene anali ndi akazi aŵiri pamene anayamba kuphunzira Baibulo. Kodi akanalimbadi mtima kulandira choonadi chachikristu ndi kutsata zimene Malemba amafuna kuti akhale mwamuna wa mkazi mmodzi? (1 Timoteo 3:2) Ndiponso kodi akanatenga mkazi wa ubwana wake amene anam’kwatira poyamba? N’zimene anachita kumene, ndipo tsopano ndi mkulu wokangalika pa umodzi wa mipingo yaikulu mu Dakar. Mkazi wake woyambayo nayenso analandira choonadi komanso ana ake onse 12, ana 10 mwa mkazi wake woyamba ndipo ana 2 mwa mkazi yemwe anali wachiŵiriyo.

Chinanso cholepheretsa anthu kulandira chiyembekezo chachikristu chingakhale kusadziŵa kuŵerenga. Kodi izi zikutanthauza kuti munthu wosadziŵa kuŵerenga sangalandire choonadi ndi kuchitsatira? Iyayi sizitanthauza zimenezo. Talingalirani chitsanzo cha Marie, mayi wolimbikira ntchito amenenso ali ndi ana asanu ndi atatu aang’ono. Anazindikira mofulumira kufunika kwa kukambirana malemba a Baibulo ndi ana ake tsiku lililonse asanapite kusukulu komanso iye asanapite kuntchito. Koma kodi akanachita bwanji zimenezi popeza sanali kudziŵa kuŵerenga? Tsiku lililonse m’mamaŵa, ankatenga kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku ndi kuima panjira yamchenga kutsogolo kwa nyumba yake. Pamene anthu amadutsa, amawafunsa ngati amadziŵa kuŵerenga. Akapeza wina wodziŵa kuŵerenga, amam’patsa kabukuko nam’chonderera kuti “Sindingathe kuŵerenga, ndiye chonde mungandiŵerengere chigawo ichi lero?” Amamvetsera mwachidwi pamene munthuyo amam’ŵerengera. Kenako amayamikira munthu wodutsayo, basi mofulumira amaloŵa m’nyumba mwake kukakambirana ndi ana ake asanapite kusukulu!

Anthu Amtundu Uliwonse Amvetsera

Ku Senegal, anthu amapezeka m’misewu akugulitsa nsomba, ndiwo zamasamba, kapena zipatso pamsika kapenanso atakhala pansi pa mtengo waukulu wa mlambe akumwa ataya, tiyi wobiriŵira koma woŵaŵa. Popeza anali ndi cholinga chouza aliyense amene amakumana naye za choonadi, abale aŵiri analakhula ndi munthu wolemala amene amapemphapempha mu msewu. Atam’patsa moni, anati: “Anthu ambiri amangokupatsani ndalama koma saima kuti acheze nanu. Ife tabwera kuti ticheze nanu nkhani ina yofunika kwambiri yokhudza moyo wanu wa m’tsogolo.” Wopemphapemphayo anadabwa. “Tikufuna tikufunseni,” abalewo anapitirira. “Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani pali kuvutika kwambiri padziko lapansi?” “Ndi cholinga cha Mulungu,” anayankha wopemphapemphayo.

Kenako abalewo anakambirana naye za m’Malemba ndi kum’fokozera Chivumbulutso 21:4. Wopemphapemphayo anakhudzidwa kwambiri ndi uthenga umenewu wopatsa chiyembekezo komanso ndi mfundo yakuti winawake anachita naye chidwi kwambiri mpaka kumuimira ndi kukambirana naye za Baibulo. Misozi inalengeza m’maso mwake. M’malo mopempha ndalama, anachonderera abale aja kuti atenge ndalama zonse zomwe anali nazo m’mbale yake yopempheramo ndalama! Anachita khama moti zinadabwitsa ndi kukopa chidwi cha aliyense amene amadutsa. Movutikira abale aja anam’nyengerera kuti asunge ndalamazo. Pomalizira anavomera koma anawauza kuti asadzalephere kum’chezeranso.

Yunivesite yaikulu ya ku Dakar ikuwonjezera nsomba mu ukonde wosodzera wauzimu. Kumeneko munthu wina wophunzira ntchito ya udokotala dzina lake Jean-Louis anayamba kuphunzira Baibulo. Analandira choonadi mofulumira, n’kupatulira moyo wake kwa Yehova kenako n’kubatizidwa. Cholinga chake chinali kutumikira Mulungu monga mpainiya wokhazikika. Komabe, amakondanso maphunziro ake a udokotala. Chifukwa cha pangano lake ndi dziko lakwawo, anakakamizika kupitiriza ndi maphunziro ake kuti awamalize. Komatu, anayamba kutumikira monga mpainiya wothandiza panthaŵi imodzimodziyo. Mosakhalitsa atalandira dipuloma yake yomuyeneretsa udokotala, anaitanidwa kukatumikira pa nyumba yaikulu ya Beteli mu Afirika ngati dokotala wa banjalo. Mnyamata winanso amene anafikiridwa ali pa Yunivesite ya Dakar akutumikira pabanja la Beteli m’dziko lakwawo.

Inde usodzi wauzimu ku Senegal n’ngwosangalatsa. Ambiri amakonda kwambiri mabuku ophunzirira Baibulo a Mboni za Yehova ndipo tsopano akufalitsidwa m’chinenero cha Chiwolofu. Kumva uthenga wabwino m’chilankhulo chawo kwalimbikitsa ambiri oona mtima kuulandira. Chifukwa cha dalitso la Yehova, mosakayikira nsomba zambiri zophiphiritsa zidzagwidwa pamene “asodzi [akhama] a anthu” a ku Senegal apitiriza kuuza ena mokhulupirika komanso molimba mtima za chiyembekezo chachikristu.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 31]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

SENEGAL

[Chithunzi]

Kuuza ena za chiyembekezo chachikristu ku Senegal

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.