Mmene Yehova Akutitsogolera
Mmene Yehova Akutitsogolera
“Munditsogolere pa njira yachidikha [“yowongoka,” NW].”—SALMO 27:11.
1, 2. (a) Kodi Yehova akuwatsogolera motani anthu ake lerolino? (b) Kodi kupindula mokwanira ndi misonkhano kumaphatikizapo kuchita chiyani?
YEHOVA ndiye Gwero la kuunika ndi choonadi, monga momwe tinaphunzirira m’nkhani yoyambayo. Mawu ake amatiunikira pamene tikuyenda m’njira yowongoka. Yehova amatitsogolera mwa kutilangiza za njira yake. (Salmo 119:105) Monga wamasalimo wakaleyo, timatsatira chitsogozo cha Mulungu moyamikira ndipo timapemphera kuti: “Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere pa njira yachidikha [“yowongoka,” NW].”—Salmo 27:11.
2 Njira imodzi imene Yehova amaperekera malangizo ndiyo kudzera m’misonkhano yachikristu. Kodi timapindula mokwanira ndi chogaŵira chachikondi chimenechi mwa (1) kupezekapo nthaŵi zonse, (2) kumvetsera nkhani zonse mwatcheru, ndiponso (3) kutengamo mbali momasuka m’nkhani zofuna kuti omvetsera ayankhepo? Komanso, kodi tikalandira malingaliro amene adzatithandiza kukhalabe “pa njira yowongoka” timawatsatira moyamikira?
Kodi Mumapezeka Pamisonkhano Nthaŵi Zonse?
3. Kodi mtumiki wina wanthaŵi zonse anakhala motani ndi chizoloŵezi chabwino chopezeka pamisonkhano mokhazikika?
3 Ofalitsa ena a Ufumu akhala akupezeka pamisonkhano mokhazikika kuyambira adakali ana. “Pamene ineyo ndi abale anga tinali ana m’ma 1930,” anakumbukira motero mtumiki wina wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova, “sitinali kuchita kufunsa makolo anthu ngati tipita kumsonkhano. Tinali kudziŵa kuti tipita pokhapokha titadwala. Banja lathu silinali kuphonya misonkhano.” Mofanana ndi mneneri wamkazi Anna, mlongo ameneyu ‘sachoka’ pa malo a Yehova olambirirapo.—Luka 2:36, 37.
4-6. (a) N’chifukwa chiyani olengeza Ufumu ena amaphonya misonkhano? (b) N’chifukwa chiyani kupezeka pamisonkhano kuli kofunika koposa?
4 Kodi ndinu mmodzi mwa anthu amene amapezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse, kapena kodi mwakhala wodumphadumpha pankhani imeneyi? Akristu ena amene ankadziona kuti akuchita bwino pankhani imeneyi anafuna kutsimikizira ngati akuterodi. Kwa milungu ingapo, ankati akapezeka pamsonkhano uliwonse ankalemba penapake. Atabwerera m’zolemba zawo pambuyo pa nthaŵi imene anaikayo, anadabwa poona chiŵerengero cha misonkhano yomwe anaphonya.
5 ‘Komatu paja anthu amakumana ndi zovuta zambiri masiku ano moti n’zosatheka kuti azipezeka pamisonkhano mokhazikika,’ wina angatero. N’zoonadi kuti tikukhala m’nthaŵi zovuta. Ndiponso mulimonse mmene zingakhalire, mavutoŵa adzawonjezeka. (2 Timoteo 3:13) Koma kodi si pamene kusonkhana mokhazikika kukukhala kofunika koposa? Popanda chakudya chauzimu cha nthaŵi zonse chotilimbitsa, sitingayembekezere kupirira mavuto amene dongosolo lino limatidzetsera. Ndithudi, popanda mayanjano a nthaŵi zonse tingakhale pachiyeso chofuna kungosiyiratu “mayendedwe a olungama.” (Miyambo 4:18) Inde, tikafika panyumba pambuyo pogwira ntchito yotopetsa, nthaŵi zina tingakayikire zokapezeka pamsonkhano. Koma ngati tapezekapobe, mosasamala kanthu kuti ndife otopa kwambiri, timadzipindulitsa tokha, ndipo timalimbikitsa Akristu anzathu pa Nyumba ya Ufumu.
6 Ahebri 10:25 amasonyezanso chifukwa china chimene tiyenera kupezekera pamisonkhano nthaŵi zonse. Pamenepo mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti adzisonkhana pamodzi ‘ndiko koposa monga momwe aona tsiku lilikuyandika.’ Inde, sitiyenera kuiŵala choonadi chakuti “tsiku la Mulungu” lili pafupi. (2 Petro 3:12) Tikamaganiza kuti mapeto a dongosolo lino adakali kutali, tingayambe kulola zokhumba zaumwini kuloŵa m’malo mwa zochita zofunika zauzimu, monga kupezeka pamisonkhano. Ndiyeno, monga momwe Yesu anachenjezera, ‘tsiku ilo lingadzafikire ife modzidzimutsa ngati msampha.’—Luka 21:34.
Khalani Womvetsera Wabwino
7. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti ana adzitchera khutu pamisonkhano?
7 Kungopezeka pamisonkhano sikokwanira. Tiyenera kumvetseranso mwatcheru, kutchera khutu ku zimene zikunenedwa pamisonkhanopo. (Miyambo 7:24) Zimenezi zikuphatikizapo ana athu. Mwana akamapita kusukulu, amayenera kumvetsera aphunzitsi, ngakhale ngati phunziro limene akuphunziralo silim’sangalatsa kapenanso sakulimvetsa. Mphunzitsi amadziŵa kuti ngati mwanayo ayesa kutchera khutu, adzapezamobe phindu linalake m’phunziro limenelo. Chotero, kodi si zomveka kuti ana a msinkhu wopita kusukulu adzitchera khutu ku malangizo operekedwa pamisonkhano yampingo m’malo mowalola kugona msonkhano ukangoyamba? Zoonadi, pakati pa choonadi chamtengo wapatali chopezeka m’Malemba pali “zina zovuta kuzizindikira.” (2 Petro 3:16) Koma sitiyenera kuganiza kuti ana amavutika kwambiri kuphunzira. Mulungu sawaganizira motero. M’nthaŵi za m’Baibulo, analamula atumiki ake aang’ono kuti ‘amve ndi kuphunzira kuopa Yehova ndi kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo ichi,’ mosakayikira amene ena mwa iwo anali ovuta kuti ana awamvetsetse. (Deuteronomo 31:12; yerekezani ndi Levitiko 18:1-30.) Kodi Yehova amafuna zochepera pa zimenezo kwa ana lerolino?
8. Kodi makolo ena amachita chiyani pofuna kuthandiza ana awo kuti adzikamvetsera pamisonkhano?
8 Makolo achikristu amadziŵa kuti zina mwa zosoŵa zauzimu za ana awo zimakhutiritsidwa ndi zimene amaphunzira pamisonkhano. Chotero, makolo ena amalinganiza kuti ana awo azigoneratu asanapite kumisonkhano kuti akafike pa Nyumba ya Ufumu ali ogalamuka komanso okonzeka kuphunzira. Makolo ena, pamasiku amisonkhano, amaikira ana awo malire pa kuonerera wailesi yakanema mwinanso ngakhale kuwaletseratu mwanzeru kuti asaionerere pamasikuwo. (Aefeso 5:15, 16) Ndipo makolo ameneŵa amachotsapo zojejemetsa zonse, kulimbikitsa ana awo kuti azimvetsera ndi kuphunzira, malinga ndi msinkhu wawo ndi nzeru zawo.—Miyambo 8:32.
9. Kodi n’chiyani chingatithandize kuphunzira luso la kumvetsera?
9 Yesu anali kuyankhula ndi anthu aakulu msinkhu pamene anati: “Yang’anirani mamvedwe anu.” (Luka 8:18) Masiku ano, mawu amenewo nthaŵi zambiri amangokhala nkhambakamwa. Zoonadi, kumvetsera mwatcheru ndi ntchito yovuta, koma munthu angaphunzire luso la kumvetsera. Pamene mukumvetsera nkhani ya Baibulo kapena mbali inayake ya pamisonkhano, yesani kupeza mfundo zake zazikulu. Yesani kuganizira mawu otsatira a wokamba nkhani. Funafunani mfundo zimene mungagwiritse ntchito mu utumiki wanu kapena zimene mungagwiritse ntchito m’moyo wanu. Mumtima mwanu bwerezani mfundozo pamene zikulongosoledwa. Lembani mfundo zachidule.
10, 11. Kodi makolo ena athandiza motani ana awo kukhala omvetsera abwino, ndipo inuyo mwapeza njira zotani zothandiza?
10 Kumvetsera mwaluso kumaphunziridwa bwino kwambiri paubwana. Ngakhale pamene asanaphunzirebe kuŵerenga ndi kulemba, ana ena amene sanayambebe kupita kusukulu amalimbikitsidwa ndi makolo awo kuti adzilemba “mfundo” pamisonkhano. Amalemba chizindikiro papepala ngati patchulidwa mawu ozoloŵereka monga “Yehova,” “Yesu,” kapena “Ufumu.” Mwa njira imeneyi, ana angaphunzire kumvetsera zimene zikunenedwa papulatifomu.
11 Nthaŵi zina ngakhale ana aakulupo amafunikabe kuwalimbikitsa kuti adzimvetsera. Atazindikira kuti maganizo a mwana wake wamwamuna wazaka 11 ali kwina pamsonkhano waukulu wachikristu, mutu wina wa banja anapatsa mwanayo Baibulo ndi kumuuza kuti adzitsegula ndi kuŵerenga malemba amene akutchulidwa ndi okamba nkhani. Atatewo, amenenso anali kulemba mfundo, anali kumuyang’ana mwanayo atagwira Baibulo m’manja mwake. Kenako, mnyamatayo anatsatira nkhani za pamsonkhanopo mwakhama kwambiri.
Mveketsani Mawu Anu
12, 13. N’chifukwa chiyani kuimba nyimbo pamodzi ndi mpingo kuli kofunika?
12 Mfumu Davide anaimba kuti: “Ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova: kuti ndimveketse mawu a chiyamiko.” (Salmo 26:6, 7) Misonkhano ya Mboni za Yehova imapereka mpata wabwino zedi woti timveketse chikhulupiriro chathu mokweza. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndiyo mwa kuimba nyimbo limodzi ndi mpingo. Imeneyi ndi mbali yofunika ya kulambira kwathu, koma itha kunyalanyazidwa mosavuta.
13 Ana ena amene sathabe kuŵerenga amaloŵeza pamtima mawu a nyimbo za Ufumu zomwe zidzaimbidwa pamisonkhano mlungu uliwonse. Amasangalala kwabasi kuimbira pamodzi ndi akuluakulu. Koma ana akamakula, chidwi chawo choimba nyimbo za Ufumu pamodzi ndi ena chimayamba kutha. Anthu enanso akuluakulu amachita manyazi kwambiri kuimba nyimbo pamisonkhano. Koma kuimba ndi mbali ya kulambira kwathu, Aefeso 5:19) Timayesetsa kwambiri kutamanda Yehova mu utumiki wakumunda. Kodi sitingam’lemekezenso mwa kukweza mawu athu, kaya akhale osalala kapena ayi, poimba nyimbo zachitamando mochokera pansi pa mtima?—Ahebri 13:15.
monga momwenso utumiki wakumunda ulili mbali ya kulambira kwathu. (14. N’chifukwa chiyani nkhani zimene timaphunzira pamisonkhano yampingo zimafunikira kukonzekereratu bwino?
14 Timatamandanso Mulungu pamene tipereka ndemanga zolimbikitsa ena pankhani za pamisonkhano yathu zomwe zimafuna kuti omvetsera ayankhulepo. Zimenezi zimafuna kukonzekera. Kusinkhasinkha pa zinthu zakuya za m’Mawu a Mulungu kumatenga nthaŵi. Mtumwi Paulo, wophunzira Malemba wakhama, anazindikira zimenezi. Analemba kuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu!” (Aroma 11:33) Mitu ya mabanja, n’kofunika kuti mudzithandiza wina aliyense wa m’banja mwanu kuti afufuze m’nzeru za Mulungu, zomwe zavumbulidwa m’Malemba. Patulani nthaŵi pa phunziro la banja la Baibulo kuti mulongosole mfundo zovuta kumva ndi kuthandiza banja lanu kukonzekera misonkhano.
15. Kodi ndi malingaliro ati amene angathandize munthu kuyankhapo pamisonkhano?
15 Ngati mukufuna kuti mudziyankhapo kwambiri pamisonkhano, bwanji osakonzekereratu zimene mukufuna kukanena? Simufunikira kufotokoza zambiri. Lemba loyenerera la m’Baibulo loŵerengedwa ndi mtima wonse kapena mawu angapo osankhidwa bwino otchulidwa mochokera pansi pa mtima adzayamikiridwa. Ofalitsa ena amapempha wochititsa phunzirolo kuti awasungire mpata wa ndemanga yoyambirira pandime yakutiyakuti, kuti asaphonye mpata wosonyeza chikhulupiriro chawo.
Opusa Akhala Anzeru
16, 17. Kodi ndi uphungu wotani umene mkulu wina anapatsa mtumiki wotumikira, nanganso n’chifukwa chiyani uphunguwo unagwira ntchito?
16 Pamisonkhano ya Mboni za Yehova, nthaŵi zambiri timakumbutsidwa kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku. Kuchita zimenezo n’kotsitsimula. Kumatithandizanso kusankha zinthu moyenera, kuwongolera umunthu wathu, kukana ziyeso, ndi kubwereranso panjira yauzimu yoyenera ngati tatenga njira yolakwika.—Salmo 19:7.
17 Akulu achidziŵitso mumpingo amakhala okonzeka kupereka uphungu wa m’Malemba woyenerana ndi zosoŵa zathu. Zomwe tingofunikira kuchita ndizo ‘kuutunga’ mwa kupempha uphungu wawo wa m’Baibulo. (Miyambo 20:5) Tsiku lina mtumiki wotumikira wachinyamata ndiponso wachangu anapempha mkulu wina kuti amuuzeko mmene angakhalire wothandiza kwambiri mumpingo. Mkuluyo, yemwe ankam’dziŵa bwino kwambiri mnyamatayo, anatsegula Baibulo lake pa 1 Timoteo 3:3, pomwe pamanena kuti amuna osankhidwa ayenera kukhala ‘ofatsa.’ Mokoma mtima analongosola njira zimene mnyamatayo angasonyezere kufatsa m’maunansi ake ndi anthu ena. Kodi mbale wachinyamatayo anakhumudwa ndi uphungu wosapita m’mbali umene anaulandira? Ayi ndithu! “Mkuluyo anagwiritsa ntchito Baibulo,” iye anatero, “chotero ndinazindikira kuti uphunguwo ukuchokera kwa Yehova.” Mtumiki wotumikirayo anatsatira uphunguwo moyamikira ndipo akupita patsogolo kwambiri.
18. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza Mkristu wina wachinyamata kukana ziyeso kusukulu? (b) Kodi ndi malemba a m’Baibulo ati amene mumakumbukira mukakumana ndi chiyeso?
18 Mawu a Mulungu angathandizenso achinyamata kuti ‘athaŵe zilakolako za unyamata.’ (2 Timoteo 2:22) Mboni ya Yehova yachinyamata imene yamaliza maphunziro ake akusekondale posachedwapa inatha kukana ziyeso pazaka zonse zomwe inakhala pasukulu mwa kusinkhasinkha pa malemba ena a m’Baibulo ndi kuwatsatira. Nthaŵi zambiri mtsikanayu anali kulingalira za uphungu wolembedwa pa Miyambo 13:20 wakuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.” Chotero, anali kuonetsetsa kuti akupalana ubwenzi ndi okhawo omwe anali kulemekeza kwambiri mfundo zachikhalidwe za m’Malemba. Anali kudziuza kuti: “Sindili wosiyana ndi ena. Ngati ndicheza ndi anthu olakwika, ndidzafuna kusangalatsa mabwenzi anga, ndipo zimenezo zidzandiloŵetsa m’mavuto.” Uphungu wa Paulo wolembedwa pa 2 Timoteo 1:8 unam’thandizanso. Paulo analemba kuti: “Usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, . . . komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino.” Mogwirizana ndi uphungu umenewo, iye molimba mtima anauzako anzake a m’kalasi za zikhulupiriro zake zozikidwa pa Baibulo panthaŵi ina iliyonse yabwino. Nthaŵi zonse akapatsidwa ntchito yolemba lipoti loti akaŵerengere kalasi lake, ankasankha nkhani imene inam’lola kupereka umboni wokhudza Ufumu wa Mulungu mochenjera.
19. N’chifukwa chiyani mnyamata wina sanathe kupirira ziyeso za dzikoli, koma kodi n’chiyani chinam’patsa nyonga yauzimu?
19 Ngati zitachitika kuti tachoka pa “mayendedwe a olungama,” Mawu a Mulungu angatithandize kuwongolera mayendedwe athu. (Miyambo 4:18) Mnyamata wina wa mu Afirika anadzionera yekha zimenezi. Pamene mmodzi wa Mboni za Yehova anam’chezera, analola kuti azichita phunziro la Baibulo. Iye ankasangalala ndi zimene anali kuphunzira koma posapita nthaŵi anayamba kuyanjana ndi achinyamata a makhalidwe oipa kusukulu. M’kupita kwa nthaŵi, iye anayamba moyo wachiwerewere. “Chikumbumtima changa chinali kundizunza, chotero ndinaleka kusonkhana,” akuvomereza motero. Pambuyo pake, anayambiranso kusonkhana. Mnyamatayu ananena mawu osonyeza chifukwa chake chenicheni akuti: “Ndinazindikira kuti chochititsa chachikulu cha zonsezi chinali chakuti sindinali kudya mwauzimu. Sindinali kuchita phunziro laumwini. Ndiye chifukwa chaketu sindinapirire chiyeso chimenecho. Ndiyeno ndinayamba kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pang’onopang’ono, ndinapezanso nyonga yauzimu ndipo ndinayeretsa moyo wanga. Zimenezi zinapereka umboni wabwino kwa anthu amene anaona kuti ndasintha. Ndinabatizidwa, ndipo tsopano ndine wachimwemwe.” Kodi n’chiyani chinapatsa mnyamatayu nyonga yogonjetsera zoofoka zake zakuthupi? Anapezanso nyonga yake mwa phunziro laumwini la Baibulo lokhazikika.
20. Kodi wachinyamata angalimbane motani ndi mivi ya Satana?
20 Akristu achinyamata, muli pankhondo lerolino! Ngati mukufuna kulimbana ndi mivi ya Satana, muyenera kudya chakudya chauzimu nthaŵi zonse. Wamasalimo, mwachionekere yemwe anali wachinyamata iyeyo, anaimvetsa nkhani imeneyi. Anathokoza Yehova chifukwa chopereka Mawu ake, kuti ‘mnyamata ayeretse mayendedwe ake.’—Salmo 119:9.
Kulikonse Kumene Mulungu Akutitsogolera, Tidzam’tsatira
21, 22. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti njira ya choonadi n’njovuta kwambiri?
21 Yehova anatsogolera mtundu wa Israyeli potuluka m’Igupto kukaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Njira imene anasankha mwina inaoneka ngati yotopetsa popanda chifukwa chomveka malinga n’kaonedwe ka anthu. M’malo moyenda yomwe inaoneka ngati njira yosavuta, njira yachidule ya m’mbali mwa Nyanja ya Mediterranean, Yehova anayendetsa anthu ake m’njira yovuta ya m’chipululu. Koma, kwenikweni, kumeneku kunali kukoma mtima kwa Mulungu. Ngakhale kuti njira ya m’mbali mwa nyanja inali yaifupi, ikanalowetsa Aisrayeli m’dziko la Afilisti audaniwo. Posankha njira ina, Yehova anateteza anthu ake kuti asamenyane ndi Afilisti kumayambiriro kwa ulendo wawo.
22 Momwemonso, njira imene Yehova akutiyendetsamo lerolino ingaoneke ngati yovuta nthaŵi zina. Mlungu uliwonse, timakhala ndi zochita zambiri zachikristu, kuphatikizapo misonkhano ya mpingo, phunziro laumwini, ndi utumiki wakumunda. Njira zina zingaoneke ngati zapafupi. Koma ngati titsatira chitsogozo cha Mulungu tidzafika kumene tikupitako kumene tikukugwirira ntchito yolimba chotere. Chotero, tiyeni tipitirize kulandira malangizo ofunikawo ochokera kwa Yehova ndipo tikhalebe “panjira yowongoka” kosatha!—Salmo 27:11.
Kodi Mungalongosole?
• N’chifukwa chiyani tiyenera makamaka kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse?
• Kodi makolo angachitenji kuti athandize ana awo kutchera khutu pamisonkhano?
• Kodi kukhala womvetsera wabwino kumaphatikizapo chiyani?
• Kodi n’chiyani chingatithandize kuyankhapo pamisonkhano?
[Mafunso]
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Kupezeka pamisonkhano yachikristu kumatithandiza kukumbukirabe tsiku la Yehova
[Zithunzi pamasamba 18]
Pali njira zambiri zotamandira Yehova pamisonkhano yachikristu