Mmene Yesu Kristu Angatithandizire
Mmene Yesu Kristu Angatithandizire
ZOMWE Yesu Kristu anachita kuthandiza anthu pamene anali padziko lapansi zinali zodabwitsa. Zimenezi zinalidi zoona kwakuti mboni ina yomwe inaona zonsezo, itatsiriza kulongosola zinthu zosiyanasiyana zomwe zinachitika m’moyo wa Yesu, inati: “Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anazichita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikanakhala nawo malo a mabuku amene akadalembedwa.” (Yohane 21:25) Popeza kuti Yesu anachita zambiri zotere padziko lapansi, tingafunse kuti: ‘Angakhale bwanji nkhoswe yathu kumwamba? Kodi tingapindule ndi chifundo chachikulu cha Yesu lerolino?’
Yankho lake n’losangalatsa ndiponso lolimbikitsa kwambiri. Baibulo limatiuza kuti Kristu analoŵa “m’mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.” (Ahebri 9:24) Kodi ife anatichitira chiyani? Mtumwi Paulo akufotokoza kuti: ‘Kristu analoŵa kamodzi kokha m’malo Opatulika Kopambana [m’mwamba momwe], sanaloŵemo ndi magazi a atonde a ana a ng’ombe amphongo ayi. Koma analoŵamo ndi magazi akeake, natikonzera chipulumutso chosatha.’—Ahebri 9:12, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono; 1 Yohane 2:2.
N’nkhanitu yabwino zedi imeneyo! M’malo motchinjiriza Yesu kuchitira anthu ntchito yake yabwinoyo, kukwera kwake kumwamba kunam’theketsa kuchitira mtundu wa anthu zowonjezereka. Chimenechi chili chifukwa chakuti Mulungu, m’chisomo chake chachikulucho, anaika Yesu kuti akhale “mtumiki,” mkulu wa ansembe, ‘ku dzanja lamanja la mpando wachifumu Waukulu kumwamba.’—Ahebri 8:1, 2.
“Mtumiki”
Chotero kumwambako, Yesu anakakhala mtumiki wa mtundu wonse wa anthu. Anakachita ntchito yofanana ndi yomwe mkulu wa ansembe wa Israyeli ankaichita m’malo mwa olambira a Mulungu m’nthaŵi zakalezo. Koma kodi ntchito imeneyo inali yotani? Paulo akufotokoza kuti: “Mkulu wa ansembe aliyense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero n’kofunika kuti ameneyo [Yesu Kristu yemwe anakwera kumwambayo] akhale nako kanthunso kakupereka.”—Ahebri 8:3.
Yesu anali nako kanthu kakupereka komwenso kanali kapamwamba kwambiri poyerekeza ndi zomwe mkulu wa ansembe kalero ankapereka. “Ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo” ukanatha kudzetsa chiyero chauzimu ku Israyeli wakale pamlingo winawake, “koposa kotani nanga mwazi wa Kristu . . . udzayeretsa chikumbumtima cha[thu] kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?”—Ahebri 9:13, 14.
Yesu alinso mtumiki wa onse wodalirika zedi chifukwa chakuti iye wapatsidwa moyo wosakhoza kufa. M’Israyeli wakale, “ambiri anakhala ansembe [motsatizana, NW], popeza imfa idawaletsa asakhalebe.” Koma bwanji ponena za Yesu? Paulo analemba kuti: “Iye . . . ali nawo unsembe wosasinthika, kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Ahebri 7:23-25; Aroma 6:9) Inde, kudzanja lamanja la Mulungu kumwambako, tilinayetu mtumiki yemwe ‘ali nawo moyo wake chikhalire kutipembedzera.’ Tangolingalirani zomwe chimenecho chikutanthauza kwa ife lerolino!
Iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.” (Pamene Yesu anali padziko lapansi, anthu ankakhamukira kwa iye kuti akathandizidwe naye, ndipo iwo nthaŵi zina ankayenda maulendo ataliatali kuti akapindule ndi thandizo lakelo. (Mateyu 4:24, 25) Kumwambako, Yesu n’ngwofikirika mosavuta ndi anthu amitundu yonse. M’malo ake apamwamba kumwambako, iye nthaŵi zonse n’ngwopezeka monga mtumiki.
Kodi Yesu Ndi Mkulu wa Ansembe Wamtundu Wanji?
Chithunzi cha Yesu Kristu chomwe Mauthenga Abwino akupereka sichimatikayikitsa kuti iye n’ngwothandiza ndi wachisomo chachikulu. Iye analitu wodzimana kwabasi! Nthaŵi zambirimbiri, ankalephera kukhala malo ayekhayekha pamene iyeyo ndi ophunzira ake amayesa kupeza nthaŵi yoti apume mokwanira. M’malo modzimva kuti akutaya nthaŵi yamtengo wapatali ya mtendere ndi bata, “[a]nagwidwa chifundo” ndi anthu omwe ankafuna chithandizo chake. Ngakhale pamene Yesu anali wotopa, wanjala, ndi waludzu, “iye anawalandira” ndipo anali wofunitsitsa kusadya ngati akanati athandize ochimwa oona mtima.—Marko 6:31-34; Luka 9:11-17; Yohane 4:4-6, 31-34.
Pogwidwa ndi chifundo, Yesu anachitapo kanthu kuti akhutiritse zosoŵa zakuthupi, zamaganizo, ndi zauzimu za anthuwo. (Mateyu 9:35-38; Marko 6:35-44) Komanso, anawaphunzitsa kupeza mpumulo ndi chitonthozo chosatha. (Yohane 4:7-30, 39-42) Mwachitsanzo, n’chokopatu chiitano chakecho chakuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.”—Mateyu 11:28, 29.
Chikondi cha Yesu pa anthu chinali chachikulu kwabasi mwakuti iye pamapeto pake anapereka moyo wake kaamba ka mtundu wa anthu wochimwawu. (Aroma 5:6-8) Pankhani imeneyi mtumwi Paulo anati: “Iye [Yehova Mulungu] amene sanatimana Mwana wake wa iye yekha, koma anam’pereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye? . . . Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.”—Aroma 8:32-34.
Mkulu wa Ansembe Yemwe Angatichitire Chifundo
Monga munthu, Yesu ankamva njala, ludzu, ankatopa, ankalefuka, ankamva ululu, ndipo anafa. Kupsinjika maganizo ndi kupanikizika zomwe anapirira zinam’konzekeretsa m’njira yapadera kwambiri kukatumikira monga Mkulu wa Ansembe wa mtundu wa anthu wakumva zoŵaŵawu. Paulo analemba kuti: “Kudamuyenera [Yesu] kufanizidwa ndi abale m’zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu. Pakuti popeza adamva zoŵaŵa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.”—Ahebri 2:17, 18; 13:8.
Yesu anasonyeza kuti ali woyeneretsedwa ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu kuyandikira kwa Mulungu. Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti iyeyo amanyengerera Mulungu wouma mtima ndi wopanda chifundo amene sakufuna kukhululukira? Ndithudi ayi, chifukwa chakuti Baibulo limatitsimikizira kuti “Ambuye [ndiye] wabwino, ndi wokhululukira.” Ilo limanenanso kuti: “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera Salmo 86:5; 1 Yohane 1:9) Ndithudi, mawu a Yesu achikondi ndi zochita zake zinasonyeza chisomo, chifundo, ndi chikondi chenicheni cha Atate wake.—Yohane 5:19; 8:28; 14:9, 10.
chosalungama chilichonse.” (Kodi Yesu amadzetsa motani mpumulo kwa ochimwa olapa? Mwa kuŵathandiza kupeza chimwemwe ndi chikhutiro m’kuyesayesa kwawo moona mtima kukondweretsa Mulungu. Polembera Akristu anzake odzozedwa, Paulo analongosola mkhalidwewo mwachidule mwakunena kuti: “Popeza tsono tili naye mkulu wa nsembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu. Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa.”—Ahebri 4:14-16.
‘Thandizo Panthaŵi Yakusoŵa’
Tsono kodi tingachitenji pamene tayang’anizana ndi mavuto omwe tikuŵaona kuti n’ngaakulu mwakuti sitingathe kuŵathetsa, monga matenda akayakaya, kusweka mtima podzimva kukhala wamlandu, kufooketsedwa kwakukulu, ndi kupsinjika maganizo? Tingagwiritse ntchito makonzedwe enieniwo amene Yesu mwiniyo mobwerezabwereza anaŵagwiritsa ntchito, omwe ali mwayi wamtengo wapatali zedi wa pemphero. Mwachitsanzo, usiku uja asanapereke moyo wake kaamba ka ife, iye “anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.” (Luka 22:44) Inde, Yesu amadziŵa mmene munthu amamvera pamene akupemphera kwa Mulungu ali wokhudzika kwambiri. Nayenso “anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kum’pulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu.”—Ahebri 5:7.
Yesu amadziŵa mmene kulili kokoma kwa anthu ‘kumvedwa’ ndi kulimbikitsidwa. (Luka 22:43) Ndiponso iye analonjeza kuti: “Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa. . . . Pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.” (Yohane 16:23, 24) Choncho, tingapemphe Mulungu ndi chidaliro chakuti adzalola Mwana wake kuika umboni wake ndi mtengo wa nsembe yake ya dipo m’malo mwa ifeyo.—Mateyu 28:18.
Tingakhale otsimikizira kuti m’malo ake aulamulirowo kumwamba, Yesu adzapereka thandizo loyenerera panthaŵi yake. Mwachitsanzo, ngati tachita tchimo lomwe moona mtima tikumva nalo chisoni, tingapeze chitonthozo m’mawu otsimikizira akuti “nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama.” (1 Yohane 2:1, 2) Nkhoswe yathu ndi Wotonthoza wathu kumwamba adzachonderera m’malo mwa ife kotero kuti mapemphero athu operekedwa m’dzina lake ndinso mogwirizana ndi Malemba adzayankhidwa.—Yohane 14:13, 14; 1 Yohane 5:14, 15.
Kuyamikira Thandizo la Kristu
Pakufunika zambiri kuposa kungochonderera Mulungu kudzera mwa Mwana wake. Ndi mtengo wa nsembe yake ya dipo, “Kristu anatiwombola” titero kunena kwake, nakhala ‘Ambuye amene adagula’ mtundu wa anthu. (Agalatiya 3:13; 4:5; 2 Petro 2:1) Tingasonyeze kuyamikira kwathu pa zonse zimene Kristu amatichitira mwa kuvomereza kuti ndife ake ndi kuvomera chiitano chake mokondwa chakuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.” (Luka 9:23) ‘Kudzikana wekha’ si kungonena chabe kuti tsopano ndife ake ayi. Ndiiko komwe, Kristu “adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo.” (2 Akorinto 5:14, 15) Choncho, kuyamikira dipo kudzakhudza kwambiri ziyembekezo zathu, zolinga zathu, ndi moyo wathu. Kukhala kwathu a “Yesu Kristu; amene anadzipereka yekha m’malo mwa ife,” kutisonkhezeretu kuphunzira zambiri ponena za iyeyo ndi Atate ake achikondiwo, Yehova Mulungu. Tifunikiranso kukula m’chikhulupiriro, kukhala m’miyezo yopindulitsa ya Mulungu, ndikukhala “achangu pa ntchito zokoma.”—Tito 2:13, 14; Yohane 17:3.
Mpingo wachikristu ndi njira yomwe timalandirira chakudya chauzimu cha panthaŵi yake, chilimbikitso, ndi chitsogozo. (Mateyu 24:45-47; Ahebri 10:21-25) Mwachitsanzo, ngati ena akudwala mwauzimu, iwo “a[nga]dziitanire akulu a Mpingo.” Yakobo akuwonjezera chilimbikitso china akumati: “Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.”—Yakobo 5:13-15.
Mwachitsanzo: Mwamuna wina yemwe ankagwira ukaidi ku South Africa analembera kalata mkulu wina wa mumpingo kuyamikira “Mboni zonse za Yehova zomwe zikugwira ntchito yabwino yomwe inayambitsidwa ndi Yesu Kristu yothandiza
anthu kuyesetsa kulondola Ufumu wa Mulungu.” Ndiyeno analemba kuti: “Ndinali ndi chimwemwe choposa nditalandira kalata yanu. Kudera nkhaŵa kwanu za kuwomboledwa kwanga mwauzimu kwandikhudza mtima kwambiri. N’chifukwa chokwanira kwa ine kuti ndiyambe kumvera chiitano cha Yehova Mulungu chakuti ndilape. Kwa zaka 27 ndakhala ndikupunthwa komanso kusokera mu mdima wa uchimo, chinyengo, mikhalidwe yoipa ndi yosaloleka, ndi zipembedzo zokayikitsa. Nditadziŵana ndi Mboni za Yehova, ndinadzimva kuti tsopano ndaipeza njira, inde njira yeniyeni! Zomwe ndiyenera kuchita ndizo kungoitsata.”Thandizo Lowonjezereka M’tsogolomu
Mikhalidwe yadziko lowonongekali ili umboni woonekeratu wakuti tikukhala m’nyengo ya nthaŵi zovuta zomwe zidzatsogolera kuyambika kwa “chisautso chachikulu.” Padakali pano, khamu lalikulu lochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe ‘akuchapa zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.’ (Chivumbulutso 7:9, 13, 14; 2 Timoteo 3:1-5) Mwa kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu, akulandira chikhululukiro cha machimo awo ndipo akuthandizidwa kukhala mu unansi wolimba ndi Mulungu, inde, kukhala mabwenzi ake.—Yakobo 2:23.
Mwanawankhosa ameneyu, Yesu Kristu, “adzawaŵeta [opulumuka chisautso chachikulu], nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pawo.” (Chivumbulutso 7:17) Ndiyeno Kristu adzagwira ntchito yake monga Mkulu wa Ansembe ndi kuitsiriza. Adzathandiza mabwenzi onse a Mulungu kupindula kotheratu ndi “akasupe a madzi a moyo”—mwauzimu, mwakuthupi, mwamaganizo, ndi mwamalingaliro. Zomwe Yesu adaziyamba mu 33 C.E. ndi zimene wazipitiriza kumwamba kuchokera panthaŵiyo zidzachitika mwangwiro.
Chotero tisaleme, pa kusonyeza kuyamikira kochokera pansi pa mtima zonse zimene Mulungu ndi Kristu atichitira, ndiponso zimene akutichitira. Mtumwi Paulo analimbikitsa kuti: “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse . . . Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:4, 6, 7.
Pali njira yofunika kwambiri ya momwe mungasonyezere kuyamikira kwanu Yesu Kristu, Nkhoswe yathu kumwamba. Dzuŵa litaloŵa Lachitatu pa April 19, 2000, Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zidzasonkhana pamodzi kuchita Chikumbutso cha imfa ya Kristu. (Luka 22:19) Umenewu udzakhala mwayi wanu woti muzamitse kuyamikira kwanu nsembe ya dipo ya Kristu. Mukuitanidwa mwachikondi kuti mudzakhalepo ndi kudzamva momwe makonzedwe ozizwitsa a Mulungu a chipulumutso kupyolera mwa Kristu angakupindulitsireni kosatha. Chonde funsani Mboni za Yehova zakwanuko kuti mudziŵe nthaŵi yeniyeni ndi malo kumene msonkhano wapaderawu udzachitikire.
[Chithunzi patsamba 7]
Yesu amadziŵa mmene munthu amamvera pamene akupemphera kwa Mulungu ali wokhudzika kwambiri
[Zithunzi patsamba 8]
Kristu adzatithandiza kugonjetsa mavuto aakulu omwe mwa ife tokha sitingathe kuŵathetsa
[Chithunzi patsamba 9]
Kristu amatithandiza kupyolera mwa akulu achikondi