‘Mulungu, Tumizani Kuunika Kwanu’
‘Mulungu, Tumizani Kuunika Kwanu’
“Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere.”—SALMO 43:3.
1. Kodi Yehova amavumbula motani zifuno zake?
YEHOVA amasamala kwambiri za njira yomwe amadziŵitsira atumiki ake zifuno zake. M’malo mongovumbula choonadi chonse panthaŵi imodzi m’kuwalima kumodzi kothobwetsa m’maso kwa kuunika, amatiunikira pang’onopang’ono. Ulendo wathuwu m’njira yopita ku moyo tingauyerekeze ndi ulendo wautali wa munthu amene akuyenda pansi. Munthuyo amanyamuka
m’maŵa kwambiri kudakali kamdima ndithu. Pamene dzuŵa liyamba kutuluka pang’onopang’ono, iye amatha kuona zinthu zingapo mumsewumo. Zinazo zimaoneka chimbuuzi. Koma pamene dzuŵalo likwerabe, iye amatha kuona patali mowonjezereka. N’chimodzimodzinso ndi kuunika kwauzimu kumene Mulungu amapereka. Amatilola kuzindikira zinthu zingapo zokha panthaŵi imodzi. Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anapereka kuunika kwauzimu m’njira imodzimodziyo. Tiyeni tisanthule mmene Yehova anaunikira anthu ake m’nthaŵi zakale komanso mmene amawaunikira lerolino.2. Kodi Yehova anapereka motani kuunika m’nthaŵi zakale kusanakhale Chikristu?
2 Zikuoneka kuti omwe analemba Salmo la 43 anali ana a Kora. Pokhala Alevi, anali ndi mwayi wophunzitsa anthu Chilamulo cha Mulungu. (Malaki 2:7) Zoonadi, Yehova ndiye anali Mlangizi wawo Wamkulu, ndipo anayang’ana kwa iye monga Gwero la nzeru zonse. (Yesaya 30:20, NW) Wamasalimoyo anapemphera kuti: “Mulungu, . . . tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere.” (Salmo 43:1, 3) Malinga ngati Aisrayeliwo anakhalabe okhulupirika kwa iye, Yehova anawaphunzitsa njira zake. Patapita zaka mazana angapo, Yehova anawasonyeza chiyanjo mwa kuwapatsa kuunika ndi choonadi chapadera koposa. Mulungu anachita zimenezi pamene anatumiza Mwana wake padziko lapansi.
3. Kodi Ayuda anayesedwa motani ndi chiphunzitso cha Yesu?
3 Monga mwamuna Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu anali “kuunika kwa dziko lapansi.” (Yohane 8:12) Anaphunzitsa anthu “zinthu zambiri m’mafanizo,” zinthu zachilendo. (Marko 4:2) Iye anauza Pontiyo Pilato kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.” (Yohane 18:36) Imeneyo inali mfundo yachilendo kwa Mroma komansotu kwa Ayuda autunduwo, popeza ankalingalira kuti Mesiya adzagonjetsa Ufumu wa Roma ndi kubwezera Israyeli ulemerero wake woyambirira. Yesu anali kusonyeza kuunika kwa Yehova, koma mawu ake sanasangalatse olamulira achiyuda, amene “anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.” (Yohane 12:42, 43) Anthu ambiri anasankha kumamatira miyambo yawo yopangidwa ndi anthu m’malo molandira kuunika kwauzimu ndi choonadi zochokera kwa Mulungu.—Salmo 43:3; Mateyu 13:15.
4. Tikudziŵa motani kuti ophunzira a Yesu anayenera kupitirizabe kukula m’chidziŵitso?
4 Komabe, amuna ndi akazi angapo oona mtima analandira mosangalala choonadi chimene Yesu anaphunzitsa. Iwo anapita patsogolo m’kumvetsa kwawo zifuno za Mulungu. Komabe, pamene moyo wapadziko lapansi wa Mphunzitsi wawo unali pafupi kutha, panali padakali zambiri zoti iwo aphunzire. Yesu anawauza kuti: “Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.” (Yohane 16:12) Inde, ophunzirawo anayenera kukulitsabe kamvedwe kawo ka choonadi cha Mulungu.
Kuunika Kukupitirizabe Kuwala
5. Kodi panadzakhala funso lotani m’zaka za zana loyamba, ndipo ndani anali ndi udindo wolithetsa?
5 Yesu atamwalira ndi kuukitsidwa, kuunika kochokera kwa Mulungu kunawala kwambiri kuposa kalelonse. M’masomphenya omwe Petro anapatsidwa, Yehova anavumbula mfundo yakuti Akunja osadulidwa angathe kukhala otsatira a Kristu kuyambira panthaŵi imeneyo. (Machitidwe 10:9-17) Limenelo linali vumbulutso! Komabe, pambuyo pake panadzakhala funso lakuti: Kodi Yehova anafuna kuti Akunja oterowo akakhala Akristu azidulidwa? Funso limenelo silinayankhidwe m’masomphenyawo, ndipo nkhaniyo inayambitsa mkangano wovuta pakati pa Akristu. Inayenera kuthetsedwa, apo ayi umodzi wawo wamtengo wapataliwo ukanawonongeka. Chotero, ku Yerusalemu “anasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo.”—Machitidwe 15:1, 2, 6.
6. Kodi atumwi ndi akulu anatsatira njira yotani kuti ayankhe funso la mdulidwe?
6 Kodi awo amene anali pamsonkhanowo akanadziŵa motani chifuniro cha Mulungu chokhudza Akunja okhulupirira? Yehova sanatumize mngelo kuti akatsogolere makambiranowo, komanso sanapatse okambiranawo masomphenya. Ngakhale zinali motero, atumwi ndi akulu sanasiyidwe opandiratu chitsogozo. Iwo anapenda maumboni ochokera kwa Akristu ena achiyuda amene anaona zimene Mulungu anayamba kuchita ndi anthu amitundu, kutsanulira mzimu wake woyera pa Akunja osadulidwa. Anasanthulanso Machitidwe 15:12-29; 16:4.
Malemba kuti apeze chitsogozo. Chotero, wophunzira Yakobo anapereka lingaliro lozikidwa pa lemba lounikira. Pamene anali kusanthula maumboniwo, chifuno cha Mulungu chinaonekera. Amitundu sanayenere kudulidwa kuti apeze chiyanjo cha Yehova. Mwamsanga, atumwi ndi akulu analemba chosankhacho kuti chitsogoze Akristu anzawo.—7. Kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba anali opita patsogolo m’njira yotani?
7 Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda, amene anamamatira miyambo ya makolo awo, Ayuda ochuluka achikristu anasangalala pamene analandira kamvedwe katsopano kapadera ka chifuno cha Mulungu chokhudza anthu amitundu, ngakhale kuti kukalandira kunafuna kuti asinthe kaonedwe kawo ka Akunja onse. Yehova anadalitsa mzimu wawo wodzichepetsa, ndipo “mipingoyo inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiŵerengo chawo tsiku ndi tsiku.”—Machitidwe 15:31; 16:5.
8. (a) Kodi tikudziŵa bwanji kuti zaka za zana loyamba zitatha kuunika kunali kudzawonjezereka? (b) Kodi tidzakambirana mafunso ofunika ati?
8 Kuunika kwauzimu kunapitirizabe kuwala m’zaka zonse za zana loyamba. Koma Yehova sanavumbule mbali iliyonse ya chifuno chake kwa Akristu oyambirira. Mtumwi Paulo anauza okhulupirira a m’zaka za zana loyamba kuti: “Tsopano tipenya m’kalirole, ngati chimbuuzi.” (1 Akorinto 13:12) Kalirole woteroyo sanali kuoneka mowala kwambiri. Chotero, kuunika kwauzimu sikunali kowala mokwanira poyamba. Atumwi atamwalira, kuunikako kunathima kwakanthaŵi, koma m’nthaŵi zino chidziŵitso cha Malemba chachuluka. (Danieli 12:4) Kodi Yehova amawaunikira motani anthu ake lerolino? Ndipo kodi tiyenera kumva bwanji akawonjezera kamvedwe kathu ka Malemba?
Kuunika Kumkabe Kuwala Mowonjezeka
9. Kodi njira yachilendo ndiponso yothandiza yophunzirira Baibulo imene Ophunzira Baibulo oyambirira anaigwiritsa ntchito ndi yotani?
9 M’nthaŵi zamakono, kuunika kwenikweni koyamba koma kosawala kwambiri kunayamba kuonekera chakumapeto kwa zaka za zana la 19 pamene gulu la amuna ndi akazi achikristu linayamba kuphunzira Malemba mwakhama. Iwo anapeza njira yothandiza yophunzirira Baibulo. Wina ankadzutsa funso; kenako gululo linali kusanthula Malemba ena ofanana ndi nkhaniyo. Pamene vesi limodzi la m’Baibulo linaoneka kuti likutsutsana ndi lina, Akristu oona mtima ameneŵa anayesetsa kugwirizanitsa malemba aŵiriwo. Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo a m’masikuwo, Ophunzira Baibulo (dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo)
anali otsimikiza mtima kulola Malemba Opatulika, osati miyambo ya anthu kapena ziphunzitso za anthu, kuwatsogolera. Atasanthula umboni wonse wa m’Malemba womwe unalipo, ankalemba zimene apeza. Mwanjira imeneyo anawongolera kamvedwe kawo ka ziphunzitso zambiri zoyambirira za m’Baibulo.10. Kodi Charles Taze Russell analemba mabuku otani othandiza kuphunzira Baibulo?
10 Munthu wapadera pakati pa Ophunzira Baibulo anali Charles Taze Russell. Analemba mabuku othandiza kuphunzira Baibulo asanu ndi limodzi otsatizanatsatizana otchedwa kuti Studies in the Scriptures (Kuphunzira Malemba). Mbale Russell ankafuna kulemba voliyumu yachisanu ndi chiŵiri, yomwe ikanalongosola mabuku a m’Baibulo a Ezekieli ndi Chivumbulutso. “Ndikangopeza mayankho ake,” iye anatero, “ndidzalemba Voliyumu ya Chisanu ndi Chiŵiri.” Komabe, anatinso: “Ngati Ambuye apereka mayankhowo kwa winawake, iyeyo adzailemba.”
11. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa nthaŵi ndi kumvetsa kwathu zifuno za Mulungu?
11 Mawu amenewo a C.T. Russell akusonyeza chinthu chofunika kwambiri pa kumvetsa kwathu zigawo zina za m’Baibulo—nthaŵi. Mbale Russell ankadziŵa kuti sangakakamize kuunika kuti kuwalire pa buku la Chivumbulutso monga momwe woyenda ulendo wapansi yemwe akufunitsitsa kutayera sangakakamizire dzuŵa kuti lituluke mwamsanga nthaŵi yake isanakwane.
Zivumbulutsidwa—Koma Panthaŵi Yake ya Mulungu
12. (a) Kodi maulosi a m’Baibulo amamvetsetseka panthaŵi yotani? (b) Ndi chitsanzo chiti chomwe chikusonyeza kuti kumvetsa kwathu maulosi a m’Baibulo kumadalira pa nthaŵi ya Mulungu? (Onani mawu a m’munsi.)
12 Monga momwe atumwi anamvetsetsera maulosi ambiri okhudza Mesiya Yesu atamwalira ndi kuukitsidwa, Akristu lerolino amamvetsa bwino kwambiri maulosi a m’Baibulo pokhapo atakwaniritsidwa. (Luka 24:15, 27; Machitidwe 1:15-21; 4:26, 27) Chivumbulutso ndi buku lamaulosi, choncho tiyenera kuyembekezera kulimvetsa bwino kwambiri pamene zinthu zimene limalongosola zikuchitika. Mwachitsanzo, C. T. Russell sakanamvetsa bwino lomwe tanthauzo la chilombo chofiiritsa chophiphiritsa chotchulidwa pa Chivumbulutso 17:9-11, popeza kuti mabungwe amene chilombocho chimaimira, amene ali bungwe la League of Nations ndi la United Nations, kunalibeko mpaka pambuyo pa imfa yake. *
13. Kodi n’chiyani chimachitika nthaŵi zina pamene kuunika kwawalira pankhani inayake ya m’Baibulo?
13 Akristu oyambirira atamva kuti Akunja osadulidwa atha kukhala okhulupirira anzawo, zimenezo zinadzutsa funso latsopano lokhudzana ndi kufunika kwa anthu amitundu kuti azidulidwa. Zimenezi zinapangitsa atumwi ndi akulu kuti aifufuzenso nkhani yonseyo ya mdulidwe. Leronso zimachitika mofananamo. Kuunika kukawalira pankhani imodzi ya m’Baibulo nthaŵi zina kumapangitsa atumiki odzozedwa a Mulungu, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kusanthulanso nkhani zina zogwirizana ndi nkhaniyo, monga momwe chitsanzo chotsatira chaposachedwapa chikusonyezera.—Mateyu 24:45.
14-16. Kodi kuwongoleredwa kwa kamvedwe kathu ka kachisi wauzimu kunakhudza motani kamvedwe kathu ka Ezekieli machaputala 40 mpaka 48?
14 Mu 1971 malongosoledwe a ulosi wa Ezekieli anafalitsidwa m’buku lakuti “The Nations Shall Know That I Am Jehovah”—How? Mutu wina wa m’buku limenelo unalongosola mwachidule masomphenya a Ezekieli a kachisi. (Ezekieli, machaputala 40-48) Panthaŵi imeneyo, nkhani inagona pa mmene masomphenya a Ezekieli a kachisi adzakwanitsidwira m’dziko latsopano.—2 Petro 3:13.
15 Komabe, nkhani ziŵiri zofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1972, m’chingelezi, zinakhudza kamvedwe kathu ka masomphenya a Ezekieli. Nkhanizo zinalongosola kachisi wamkulu wauzimu yemwe anafotokozedwa ndi mtumwi Paulo mu Ahebri chaputala 10. Nsanja ya Olonda imeneyo inafotokoza kuti chipinda Chopatulika ndiponso bwalo lam’kati la kachisi wauzimu n’zokhudzana ndi mkhalidwe wa odzozedwa adakali padziko lapansi. Pamene Ezekieli machaputala 40 mpaka 48 anasanthulidwanso patapita zaka, anazindikira kuti monga momwe kachisi wauzimuyo akugwirira ntchito lerolino, kachisinso amene Ezekieli anaona m’masomphenya ayenera kuti akugwira ntchito lerolino. Motani?
16 M’masomphenya a Ezekieli, ansembe akuoneka kuti akuyendayenda m’mabwalo a kachisi pamene akutumikira mafuko osakhala aunsembe. Mosakayikira, ansembe ameneŵa amaimira “ansembe achifumu,” atumiki odzozedwa a Yehova. (1 Petro 2:9) Komabe, sadzakhala akutumikira m’bwalo la padziko lapansi la kachisiyo mu Ulamuliro wonse wa Zaka Chikwi wa Kristu, ayi. (Chivumbulutso 20:4) M’chigawo chachikulu cha nthaŵi imeneyo, ngatitu si kwanthaŵi yonseyo, odzozedwa adzakhala akutumikira Mulungu m’chipinda Chopatulikitsa cha kachisi wauzimu ameneyu, “m’Mwamba momwe.” (Ahebri 9:24) Popeza kuti ansembe akuonekera akuloŵa ndi kutuluka m’mabwalo a kachisi wa Ezekieli, masomphenya amenewo ayenera kuti akukwaniritsidwa lerolino, pamene ena mwa odzozedwa adakali padziko lapansi. Chotero, kope la March 1, 1999, la magazini inoyi linalongosola kamvedwe kowongoleredwa ka nkhani imeneyi. Chotero, mpaka kumapeto kwenikweniko kwa zaka za zana la 20, kuunika kwauzimu kunawalira pa ulosi wa Ezekieli.
Khalani Wokonzeka Kusintha Malingaliro Anu
17. Kodi mwasintha motani malingaliro anu kuchokera pamene munadziŵa choonadi, ndipo kodi kusinthako kwakupindulitsani motani?
17 Aliyense wofuna kuchidziŵa bwino choonadi ayenera kukhala wofunitsitsa “kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu.” (2 Akorinto 10:5) Zimenezo zimakhala zovuta nthaŵi zina, makamaka ngati malingaliro ena akhazikika kwambiri mumtima. Mwachitsanzo, musanaphunzire choonadi cha Mulungu, mwina munkasangalala kuchita mapwando ena achipembedzo ndi a m’banja mwanu. Mutayamba kuphunzira Baibulo, munadzazindikira kuti mapwando ameneŵa kwenikweni anachokera kuchikunja. Mwina poyamba munali kuzengereza kutsatira zimene munali kuphunzira. Komabe, pomalizira pake chikondi chanu cha Mulungu chinadzakula kwambiri kuposa kutengeka maganizo ndi zochitika zachipembedzo zimenezo, ndipo munasiya kuchita nawo mapwando osakondweretsa Mulungu. Kodi Yehova sanadalitse chosankha chanu?—Yerekezani ndi Ahebri 11:25.
18. Kodi tiyenera kumva bwanji pamene kamvedwe kathu ka choonadi cha m’Baibulo kawongoleredwa?
18 Nthaŵi zonse timapindula mwa kuchita zinthu m’njira ya Mulungu. (Yesaya 48:17, 18) Chotero pamene kamvedwe kathu ka chigawo china cha m’Baibulo kawongoleredwa, tiyeni tizikondwera kuti choonadi chikupita patsogolo! Ndithudi, kupitiriza kwathu kuunikiridwa kumatitsimikizira kuti tili panjira yabwino. Ndiwo “mayendedwe a olungama,” amene “akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.” (Miyambo 4:18) Zoonadi, mbali zina za chifuno cha Mulungu timaziona “ngati chimbuuzi” padakali pano. Koma nthaŵi ya Mulungu iyemwini ikadzafika, tidzaona kukongola konse kwa choonadi, malinga ngati mapazi athu ali okhazikika mu “mayendedwe” amenewo. Padakali pano, tiyeni tikondwere ndi choonadi chimene Yehova wachivumbula, tikudikira kuunikira kwa pa choonadi chinacho chimene sitikuchimvetsabe bwinobwino.
19. Kodi njira imodzi yosonyezera kuti timakonda choonadi ndi iti?
19 Kodi tingasonyeze m’njira yothandiza iti kuti timakonda kuunika? Njira imodzi ndiyo mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse—tsiku ndi tsiku ngati n’kotheka. Kodi muli ndi ndandanda yoŵerenga Baibulo nthaŵi zonse? Magazini
a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amatipatsanso chakudya chauzimu chabwino chochuluka choti tisangalale nacho. Talingaliraninso za mabuku, mabulosha, ndi zofalitsa zina zomwe zinakonzedwa kuti zitipindulitse. Nanganso bwanji za nkhani zolimbikitsa zokhudza ntchito yolalikira Ufumu zimene zimalembedwa m’buku la Yearbook of Jehovah’s Witnesses?20. Kodi kuunika ndi choonadi zochokera kwa Yehova n’zogwirizana motani ndi kupezeka kwathu pamisonkhano yachikristu?
20 Inde, Yehova wayankha pemphero lomwe lili pa Salmo 43:3 modabwitsa. Kumapeto kwa vesi limenelo, timaŵerenga kuti: “[Kuunika kwanu ndi choonadi chanu] zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.” Kodi mukukhumba kuti mudzalambire Yehova pamodzi ndi khamu la anthu enanso? Malangizo auzimu amene amaperekedwa pamisonkhano yathu ndiyo njira yofunika kwambiri imene Yehova amaperekera kuunika lerolino. Kodi tingachitenji kuti tikulitse chikondi chathu cha misonkhano yachikristu? Tikukupemphani kuti musanthule mfundo imeneyi mwapemphero m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 C. T. Russell atamwalira, buku lomwe linanenedwa kuti ndi voliyumu yachisanu ndi chiŵiri ya Studies in the Scriptures linalembedwa pofuna kuyesa kulongosola mabuku a Ezekieli ndi Chivumbulutso. Mfundo zina za m’bukulo zinazikidwa pa ndemanga za Russell zokhudza mabuku amenewo a m’Baibulo. Komabe, nthaŵi yovumbula tanthauzo la maulosi amenewo inali isanafike, ndipo kuyankhula mwachisawawa, mafotokozedwe operekedwa m’voliyumu imeneyo ya Studies in the Scriptures anali a chimbuuzi. M’zaka zotsatira, chisomo cha Yehova ndi zochitika padziko lapansi zapangitsa Akristu kuzindikira bwino lomwe tanthauzo la mabuku amaulosi amenewo.
Kodi Mungayankhe?
• Kodi n’chifukwa chiyani Yehova amavumbula zifuno zake pang’onopang’ono?
• Kodi atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anaithetsa motani nkhani ya mdulidwe?
• Kodi Ophunzira Baibulo oyambirira anagwiritsa ntchito njira iti yophunzirira Baibulo, nanga n’chifukwa chiyani njirayo inali yapadera?
• Perekani chitsanzo cha mmene kuunika kwauzimu kumavumbulidwira panthaŵi ya Mulungu iyemwini.
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 12]
Charles Taze Russell ankadziŵa kuti kuunika kudzawalira pa buku la Chivumbulutso panthaŵi ya Mulungu iyemwini