Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi M’madziŵanji Pankhani ya Ufiti?

Kodi M’madziŵanji Pankhani ya Ufiti?

Kodi M’madziŵanji Pankhani ya Ufiti?

UFITI! Kodi liwu limenelo limakupatsani malingaliro otani?

Kwa anthu ambiri, langokhala nkhani ya kuopa zikhulupiriro zina komanso malingaliro ongoyerekezera, zosafunika kuziganizira kwenikweni. Kwa iwo, ufiti umangokhala m’maganizo chabe. Amaganiza za mfiti zokalamba zimene zavala chophimba kunkhope zomwe zikuponya mapiko a mleme mu kamkhate kotokota, kusandutsa anthu kukhala achule, ndi kukwera tsache n’kumauluka usiku kwinaku zikumaseka mwanjiru.

Kwa ena, ufiti sinkhani yamaseŵera. Ofufuza ena amati kuposa theka la anthu padziko lonse amakhulupirira kuti mfiti zilikodi ndikuti zingasokoneze miyoyo ya ena. Miyandamiyanda ya anthu amakhulupirira kuti ufiti n’ngwoipa, woopsa, ndipo uyenera kuopedwa kwambiri. Mwachitsanzo, buku lina lonena za chipembedzo cha mu Africa linati: “Chikhulupiriro cha kugwira ntchito ndi kuopsa kwa matsenga oipa, nyanga ndi ufiti n’zozikika mwamphamvu m’chikhalidwe cha mu Africa . . . Mfiti limodzi ndi anyanga ndi anthu odedwa kwambiri m’midzi yawo. Ngakhale lerolino kuli malo ena kumene nthaŵi zina amamenyedwa ndi kuphedwa ndi anthu ena a m’mudzi omwewo.”

Komabe, m’mayiko a Kumadzulo, ufiti wavala maonekedwe ena atsopano olemekezeka. Mabuku, wailesi yakanema, ndi mafilimu zachita zochuluka pochepetsa kuopa ufiti. Wopenda za zosangalatsa, David Davis anati: “Mosayembekezereka, mfiti n’zachinyamata ndiponso zokongola kwambiri, zokongoladi kwambiri. Opanga mafilimu ku America amachitapo kanthu mofulumira akazindikira nkhani zomwe zikufala. . . . Mwa kuonetsa mfiti kukhala zokongola ndi zokondeka, angakope oonerera ambiri, kuphatikizapo amayi ndi ana ang’onoang’ono.” Opanga mafilimuwo amadziŵa bwino mmene angakonzere nkhani ina iliyonse yofala kukhala malonda opindulitsa.

Ena amanena kuti ufiti ndi limodzi mwa magulu auzimu omwe akukula mofulumira kwambiri mu United States. M’mayiko onse otukuka, chiŵerengero chowonjezereka cha anthu, mwa kusonkhezeredwa ndi magulu ofuna ufulu wa akazi omwe anyengedwa ndi zipembedzo zikuluzikulu zamakono, amafuna kukhutiritsidwa kwauzimu m’njira zosiyanasiyana za ufiti. Kunena zoona, yachulukadi mitundu ya ufiti mwakuti anthu sakugwirizananso chimodzi ponena za tanthauzo lake lenileni la mawu akuti “mfiti.” Komabe, odzinenera kukhala mfiti amati kaŵirikaŵiri amatsatira zochitika za Wicca, liwu lomasuliridwa m’buku lina lopereka matanthauzo a mawu kuti “chipembedzo chachikunja cholambira zinthu zachilengedwe chomwe chinayambira kumadzulo kwa Ulaya Chikristu chisanayambe ndi kukonzedwanso m’zaka za zana la 20.” * Chifukwa cha chimenecho, ambiri nawonso amadzitcha kukhala akunja kapena kuti akunja amakono.

M’mbiri yonse, mfiti zakhala zikudedwa, kuzunzidwa, kukwapulidwa, ngakhale kuphedwa kumene. N’zosadabwitsa kuti omwe amachita ufiti lerolino n’ngofunitsitsa kukonzanso malingaliro a anthu pa iwo. M’kafukufuku wina, mfiti zambirimbiri zinafunsidwa kuti ndi uthenga wotani umene zimafunitsitsa zitapereka kwa anthu. Yankho lawo, lomwe linalongosoledwa mwachidule ndi wofufuza wina Margot Adler, linali lakuti: “Sindife oipa. Sitilambira Mdyerekezi. Sitivulaza kapena kunyenga anthu. Sindife oopsa. Ndife anthu monga inu nomwe. Tili ndi mabanja, ntchito, ziyembekezo, ndi zokhumba. Sindife ampatuko. Sindife ochita zamalodza. . . . Simuyenera kutiopa. . . . Ndife ofanana zedi ndi inuyo kuposa momwe mumaganizira.”

Mokulira, uthenga umenewo walandiridwa. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe chifukwa chokhalira wodera nkhaŵa ponena za ufiti? Tiyeni tikambirane funso limenelo m’nkhani yotsatirayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Liwu Lachingelezi lakuti witchcraft [ufiti] linatengedwa mu Chingelezi Chakale chakuti wicca kutanthauza mfiti yaikazi ndi wicce, kuimira mfiti yaimuna.