Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mzimu wa Mulungu Umagwira Ntchito Motani Lerolino?

Kodi Mzimu wa Mulungu Umagwira Ntchito Motani Lerolino?

Kodi Mzimu wa Mulungu Umagwira Ntchito Motani Lerolino?

IYE ndi wopuwala miyendo. Masiku onse, anali kukhala pakhomo la kachisi lotchedwa Lokongola kuti apemphe mphatso zachifundo kwa iwo akuloŵa m’kachisi. Komabe, nthaŵi inayake, wopemphapempha wopuwalayu analandira mphatso yomwe inali yapamwamba zedi kuposa ndalama zing’onozing’ono zasiliva zoŵerengeka chabe. Anachiritsidwa!​—Machitidwe 3:2-8.

Ngakhale kuti atumwiwo Petro ndi Yohane n’ngomwe ‘anam’nyamutsa’ kotero kuti ‘mapazi ake . . . analimbikitsidwa,’ iwo sanadzikweze kaamba ka machiritsowo. Chifukwa chiyani sanatero? Petro mwiniyo anafotokoza kuti: “Amuna inu a Israyeli, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamuyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?” Ndithudi onse aŵiriŵa, Petro ndi Yohane anadziŵa kuti sikunali mwa mphamvu yawo, kuti chinthu choterocho chingachitike, koma mwa mzimu woyera wa Mulungu.​—Machitidwe 3:7-16; 4:29-31.

Panthaŵi imeneyo, “mphamvu” zoterozo, zinkaperekedwa pofuna kusonyeza kuti mpingo wachikristu watsopanowo unali kuchirikizidwa ndi Mulungu. (Ahebri 2:4) Koma ntchito zamphamvuzi zitakwaniritsa cholinga chake, izo ‘zinakhala chabe,’ anatero mtumwi Paulo. * (1 Akorinto 13:8) Chifukwa cha chimenecho, sitiona m’mipingo yachikristu choona lerolino mukuchitika machiritso ena alionse, mauthenga aulosi, kapena kutulutsa ziŵanda kulikonse kopatsidwa ndi Mulungu.

Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti mzimu woyera wa Mulungu sukugwiranso ntchito? Ndithudi ayi! Tiyeni tipende njira zina m’zomwe mzimu wa Mulungu unkagwirira ntchito m’zaka za zana loyamba ndi mmene ukugwirira ntchito m’tsiku lathuli.

“Mzimu wa Choonadi”

Imodzi mwa ntchito za mzimu woyera wa Mulungu ndiyo kudziŵitsa, kuzindikiritsa, kuvumbula choonadi. Kutangotsala nthaŵi pang’ono kuti afe, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino. Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m’choonadi chonse.”​—Yohane 16:12, 13.

“Mzimu wa choonadi” unaperekedwa pa Pentekoste mu 33 C.E. pamene ophunzira pafupifupi 120 omwe anasonkhana m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu anabatizidwa ndi mzimu woyera. (Machitidwe 2:1-4) Mtumwi Petro anali mmodzi mwa awo omwe analipo pa madyerero apachaka amenewo. Atadzazidwa ndi mzimu woyera, Petro “anaimirira” nakweza mawu ake, kapena kuti kumveketsa bwino zina za zoona zake za Yesu. Mwachitsanzo, iye analongosolanso mmene “Yesu Mnazarayo” ‘anakwezedwera ku dzanja lamanja la Mulungu.’ (Machitidwe 2:14, 22, 33) Mzimu wa Mulungu unasonkhezeranso Petro kulengeza molimba mtima kwa omvetsera ake achiyuda kuti: “Lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munam’pachika.” (Machitidwe 2:36) Chifukwa cha uthenga wa Petro wouziridwa ndi mzimuwo, anthu pafupifupi mazana atatu “analandira mawu ake” ndipo anabatizidwa. Mwa njira imeneyi, mzimu woyera wa Mulungu unathandiza kuwatsogolera ku choonadi.​—Machitidwe 2:37-41.

Mzimu woyera wa Mulungu unagwiranso ntchito monga mphunzitsi ndi wokumbutsa. Yesu anati: “Nkhosweyo, Mzimu woyera, amene Atate adzam’tuma m’dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.”​—Yohane 14:26.

Kodi mzimu woyera unagwira bwanji ntchito monga mphunzitsi? Mzimu wa Mulungu unatsegula malingaliro a ophunzirawo kuŵakumbutsa zinthu zimene anali atamva kale kuchokera kwa Yesu koma zomwe anali asanamvetsetse. Mwachitsanzo, atumwiwo ankadziŵa kuti m’kati mwa mayesero ake, Yesu anauza kazembe wachiroma wa ku Yudeya, Pontiyo Pilato kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.” Komabe, panthaŵi yomwe Yesu amakwera kumwamba pambuyo pa masiku 40, atumwiwo anali adakali ndi malingaliro olakwika akuti Ufumu udzakhazikitsidwa pano padziko lapansi. (Yohane 18: 36; Machitidwe 1:6) Mwachionekere, atumwiwo sanali kumvetsetsa bwino lomwe tanthauzo la mawu a Yesu mpakana kudzafika pamene mzimu woyera wa Mulungu unatsanulidwa pa iwo pa Pentecoste mu 33 C.E.

Mzimu wa Mulungu unkagwiranso ntchito monga wokumbutsa mwa kubweretsanso m’malingaliro ziphunzitso zosiyanasiyana za Yesu. Mwachitsanzo, maulosi onena za imfa ya Kristu ndi kuuka kwake, analandira tanthauzo latsopano mothandizidwa ndi mzimu woyera. (Mateyu 16:21; Yohane 12:16) Kukumbukira ziphunzitso za Yesu kunathandiza atumwiwo kuteteza udindo wawo molimba mtima pamaso pa mafumu, oweruza, ndi atsogoleri achipembedzo.​—Marko 13:9-11; Machitidwe 4:5-20.

Komanso, mzimu woyera wa Mulungu unathandiza kutsogolera Akristu oyambirira kugawo lobala zipatso muutumikiwo. (Machitidwe 16:6-10) Mzimu wa Mulungu unasonkhezeranso Akristu oyambirirawo kutenga nawo mbali m’kulemba Mawu a Mulungu, Baibulo, kuti lipindulitse mtundu wonse wa anthu. (2 Timoteo 3:16) Ndiyeno n’zoonekeratu kuti mzimu woyera unali kugwira ntchito m’njira zosiyanasiyana m’zaka za zana loyamba. Sunali kuperekedwa kokha kuti uchite zozizwitsa ayi.

Mzimu Woyera M’tsiku Lathu

Mzimu woyera wakhalanso ukugwira ntchito mofananamo kuthandiza Akristu oona m’tsiku lathu. Zimenezi zinachitiridwa umboni pa kagulu kakang’ono ka Ophunzira Baibulo mu Allegheny, Pennsylvania, U.S.A., m’theka lotsiriza la zaka za zana la 19. Ophunzira Baibulo akhama ameneŵa analidi ofunitsitsa kudziŵa “choonadi.”​—Yohane 8:32; 16:13.

Mmodzi wa gulu limeneli, Charles Taze Russell, anati ponena za kufunafuna kwake choonadi cha m’Malemba: “Ndinapemphera . . . kuti andipatse mphamvu kuti ndithe kuchotsa malingaliro olakwika ena alionse mumtima ndi m’malingaliro mwanga omwe angandilepheretse kumvetsa zinthu ndikuti anditsogoze ndi mzimu wake m’kumvetsetsa bwino lomwe.” Mulungu anadalitsa pemphero lodzichepetsali.

Pamene Russell ndi anzake ankafufuza m’Malemba mwakhama, zinthu zingapo anazimvetsetsa bwino. “Tinaona kuti kwa zaka mazana ambiri,” analongosola motero Russell, “mipatuko yosiyanasiyana ndi mabungwe anali atagaŵana ziphunzitso za Baibulo mwa iwo okha, ndi kuzisakaniza ndi zina zofananirako ndi zolingalira za anthu ndi ziphunzitso zawo zolakwa.” Zimenezi zinachititsa chomwe anachitcha kuti “kuika choonadi m’malo olakwika.” Ndithudi, choonadi cha m’Malemba chinali chitakwiriridwa ndi ziphuzitso zambirimbiri zachikunja zomwe zinali zitaloŵeratu m’Matchalitchi a Chikristu m’kupita kwa zaka mazana ambiri. Koma Russell anali wofunitsitsa kudziŵa ndi kufalitsa choonadi.

Pogwiritsa ntchito magazini ya Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence (Nsanja ya Olonda ya Ziyoni ndi Yolengeza Kukhalapo kwa Kristu), Russell ndi anzake anatsutsa molimba mtima ziphunzitso zonyenga zachipembedzo zimene zinkapereka chithunzi cha Mulungu molakwika. Mosiyana ndi malingaliro ofala a zipembedzo, iwo anazindikira kuti, moyo umafa, kuti paimfa timapita kumanda, ndi kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona ndipo chifukwa cha chimenecho sali mbali ya Utatu.

Komabe, mungaone kuti kuvumbula ziphunzitso zonyenga kumeneko kunakwiyitsa atsogoleri achipembedzo a m’Gawo la Matchalitchi Achikristu. Pokakamira zolimba ku malo awo aulamulirowo, atsogoleri ambiri a Chikatolika ndi Chipulotesitanti anapanga ndaŵala zomwe cholinga chake chinali kunyoza Russell. Koma iye ndi anzake sanafooke. Motsimikiza mtima, anadalira chitsogozo cha mzimu wa Mulungu. “Zomwe Ambuye watitsimikizira,” anatero Russell, “n’zakuti . . . mzimu woyera wa Atate, wotumizidwa chifukwa cha kupempha kwa Yesu Momboli wathu, Mkhalapakati ndiponso Mutu, udzakhala mlangizi wathu.” Ndipotu mzimu woyerawo unaperekadi malangizo! Ophunzira Baibulo okhulupirika ameneŵa anapitirizabe kumwa madzi abwino a choonadi kuchokera m’Baibulo ndi kuŵalengeza dziko lonse.​—Chivumbulutso 22:17.

Gulu lamakono la Mboni za Yehova lakhala likutsatira mzimu woyera wa Mulungu mwakhama kwa pafupifupi zaka zoposa 100 tsopano. Pamene mzimu wa Yehova ukupitiriza kuunikira maso awo auzimu pang’onopang’ono, mofunitsitsa Mbonizo zimapanga masinthidwe oyenerera kuti zigwirizane ndi kamvedwe katsopano.​—Miyambo 4:18.

“Mudzakhala Mboni Zanga”

Yesu anasonyeza chizindikiro chinanso cha mzimu woyera wa Mulungu pamene anauza ophunzira ake kuti: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Lonjezo la Yesu lakuti adzapatsa ophunzira ake “mphamvu” ndi “Mzimu Woyera” kuti agwirebe ntchito yawo yopatsidwa ndi Mulungu likugwira ntchito ngakhalenso lerolino.

Monga gulu, Mboni za Yehova n’zodziŵika bwino kaamba ka ntchito yawo yolalikira. (Onani bokosi.) Ndithudi, Mboni za Yehova zikulankhula za uthenga wa choonadi m’mayiko oposa 230 ndi m’zisumbu. M’mikhalidwe yosiyanasiyana, kuphatikizapo kuika miyoyo yawo pangozi m’madera omwe muli nkhondo, izo molimba mtima zimakweza mawu awo pochirikiza Ufumu wa Mulungu. Khama lawo pa utumiki wachikristu limapereka umboni wamphamvu wakuti mzimu woyera ukugwiradi ntchito lerolino. Ndipo n’chachidziŵikire kuti Yehova Mulungu akudalitsa zoyesayesa zawo.

Mwachitsanzo, chaka chathachi maola opyola 1,000,000,000 anathera pa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndi zotsatira zotani? Anthu okwana 323,439 anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu pobatizidwa mwa kumizidwa m’madzi. Kuwonjezera pamenepo, maphunziro a Baibulo apanyumba okwana 4,433,884 anali kuchitidwa mlungu ndi mlungu ndi achatsopano. Zonse pamodzi, mabuku okwana 24,607,741, magazini 631,162,309, komanso mabulosha ndi timabuku zokwana 63,495,728 zinagaŵiridwa. Ndi umbonitu wamphamvu zedi wa kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu!

Mzimu wa Mulungu ndi Inu

Pamene munthu alabadira uthenga wabwino, agwirizanitsa moyo wake ndi miyezo ya Mulungu, ndi kusonyeza chikhulupiriro m’kuperekedwa kwa dipo, ndiye kuti ali ndi mpata wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kwa oterowo mtumwi Paulo anati: ‘Mulungu, wapatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.’​—1 Atesalonika 4:7, 8; 1 Akorinto 6:9-11.

Kukhala ndi mzimu wa Mulungu kumadzetsa madalitso ambiri. Madalitso amtundu wanji? Choyamba, Mawu ouziridwa a Mulungu amati: “Chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, [komanso] chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Choncho, mzimu woyera wa Mulungu ndi nyonga yamphamvu yochita zabwino, yotheketsa aliyense kusonyeza mikhalidwe yaumulungu.

Komanso, ngati muŵerenga Baibulo ndi kuchita zimene mukuphunzira, mzimu wa Mulungu ungakuthandizeni kukula m’nzeru, chidziŵitso, kuzindikira, chilungamo, ndi luso la kulingalira. Mfumu Solomo analandira “nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziŵa za mitundumitundu” chifukwa chakuti anafunafuna kukondweretsa Mulungu osati anthu. (1 Mafumu 4:29) Popeza kuti Yehova anapereka mzimu woyera kwa Solomo, ndithudi sadzaleka kupereka mzimu wake woyera kwa omwe akufuna kum’kondweretsa lerolino.

Mzimu woyera wa Mulungu umathandizanso Akristu kulimbana ndi Satana ndi ziŵanda, dongosolo la zinthu loipali, komanso zizoloŵezi zauchimo za matupi awo ofookawo. Kodi zimenezo zingatheke motani? Mtumwi Paulo akuyankha kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Mzimu woyera sungachotse ziyeso; koma ungakuthandizeni kuzipirira. Mwa kudalira mzimu woyera wa Mulungu, tingalandire “ukulu woposa wamphamvu” kuti tithane ndi mavuto alionse kapena nkhaŵa.​—2 Akorinto 4:7; 1 Akorinto 10:13.

Mutalingalira umboni wonsewu, simudzakayikira kuti mzimu woyera wa Mulungu ukugwiradi ntchito lerolino. Mzimu wa Yehova umapatsa nyonga atumiki ake kuti achitire umboni zifuno zake zazikulu. Ukupitirizabe kuvumbula cheza cha kuwala kwauzimu, ndipo ukulimbitsa chikhulupiriro chathu, kutithandiza kukhalabe okhulupirika kwa Mlengi wathu. Tiyeneratu kuyamikira kwabasi kuti Mulungu wakwaniritsadi lonjezo lake mwa kutsanulira mzimu woyera pa atumiki ake okhulupirika lerolino!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani nkhani yakuti “Kodi N’chifukwa Ninji Mphatso Zozizwitsa za Mzimu Zaleka?” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1972, masamba 547-51.

[Bokosi patsamba 10]

Zimene Ena Amanena za Mboni za Yehova

“Pamene matchalitchi ena akugula alangizi kuti akope anthu kuti aloŵe m’matchalitchi mwawo kapena pamene matchalitchiwo akulimbana ndi nkhani zamakonozi monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi kuchotsa mimba, Mboni sizikugonjera dziko lomwe likusinthali. Iwo akulalikirabe mwadongosolo labwino zedi padziko lonse lapansi.”​—Nyuzipepala ya The Orange Register ya ku Orange County, California, U.S.A.

“Tikanena za kufalitsa chikhulupiriro, n’zipembedzo zochepa zomwe zimachita zimenezo mwachangu kwambiri monga momwe zimachitira Mboni za Yehova.”​—Nyuzipepala ya The Republic ya ku Columbus, Indiana, U.S.A.

“Ndi okhawo omwe amapita khomo ndi khomo ndi ‘uthenga wabwino,’ kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe chabwino za m’Baibulo.”​—Nyuzipepala ya Życie Literackie, ku Poland.

“M’ndaŵala ya ulaliki yaikulu koposa zonse, Mboni za Yehova zatenga uthenga wa Yehova padziko lonse.”​—Nyuzipepala ya News-Observer ku Tamaqua, Pennsylvania, U.S.A.

[Zithunzi patsamba 9]

Mzimu woyera wa Mulungu umatiunikira mwauzimu,

. . . kulimbikitsa mikhalidwe yabwino yachikristu,

. . . ndi kutithandiza pa ntchito yolalikira yapadziko lonse