Omenyana Ndi Mulungu Sadzapambana!
Omenyana Ndi Mulungu Sadzapambana!
“Adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa.”—YEREMIYA 1:19.
1. Kodi Yeremiya anapatsidwa ntchito yotani, ndipo anachita ntchito yakeyo kwautali wotani?
YEHOVA anapatsa Yeremiya wachinyamatayo ntchito yokakhala mneneri wa mitundu ya anthu. (Yeremiya 1:5) Zimenezi zinachitika mu ulamuliro wa mfumu ya Yuda yabwinoyo, Yosiya. Utumiki wamaulosi wa Yeremiya unapitirizabe mpaka m’nthaŵi yovutayo Yerusalemu asanagonjetsedwe ndi Babulo mpaka pamene anthu a Mulungu anatengedwa kuukapolo.—Yeremiya 1:1-3.
2. Kodi Yehova anam’limbikitsa motani Yeremiya, ndipo kumenyana ndi mneneriyo kunatanthauza kumenyana ndi ndani?
2 Mauthenga achiweruzo amene Yeremiya anayenera kulengeza anali kudzatsutsidwa ndi anthu. Chotero, Mulungu anam’limbikitsa kaamba ka zimene anali kudzakumana nazo. (Yeremiya 1:8-10) Mwachitsanzo, mtima wa mneneriyo unalimbikitsidwa ndi mawu akuti: “Adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.” (Yeremiya 1:19) Pomenyana ndi Yeremiya anthuwo akanakhala ngati kuti akumenyana ndi Mulungu. Lerolino, Yehova ali ndi gulu longa mneneri la atumiki amene ntchito yawo ndi yofanana ndi ija ya Yeremiya. Mofanana naye, iwo amalengeza mawu aulosi a Mulungu molimba mtima. Ndipo uthenga umenewu ukukhudza anthu onse ndi mitundu m’njira yabwino kapena m’njira yoipa malinga ndi mmene anthuwo akuuonera. Monga m’nthaŵi ya Yeremiya, pali awo amene akumenyana ndi Mulungu mwa kutsutsa atumiki ake ndi ntchito zawo zopatsidwa ndi Mulungu.
Atumiki a Yehova Aukiridwa
3. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova akhala akuukiridwa?
3 Anthu a Yehova akhala akuukiridwa kuyambira 1 Petro 5:8) “Nthaŵi zawo za anthu akunja” zitatha mu 1914, Mulungu analonga Mwana wake kukhala Mfumu yatsopano ya dziko lapansi, ndi kum’lamula kuti: “Chitani ufumu pakati pa adani anu.” (Luka 21:24; Salmo 110:2) Posonyeza mphamvu zake, Kristu anachotsa Satana kumwamba ndi kum’tsekera kudziko lapansi. Podziŵa kuti nthaŵi yam’thera, Mdyerekezi akulusira Akristu odzozedwa ndi mabwenzi awo. (Chivumbulutso 12:9, 17) Kodi kuukira kobwerezabwereza kwa olimbana ndi Mulungu ameneŵa kwakhala ndi zotsatira zotani?
kuchiyambi cha zaka za zana la 20. M’mayiko ambiri, anthu oipa mtima akhala akuyesa kusokoneza, inde, kuthetsa kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Asonkhezeredwa ndi Mdani wathu wamkulu, Mdyerekezi, amene “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwire.” (4. Kodi anthu a Yehova anakumana ndi ziyeso zotani m’nthaŵi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, koma kodi n’chiyani chinachitika mu 1919 ndi mu 1922?
4 Atumiki odzozedwa a Yehova anakumana ndi ziyeso zambiri za chikhulupiriro chawo m’nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Ananyozedwa ndi kunenezedwa, kuthamangitsidwa ndi magulu a anthu aukali, komanso kukwapulidwa. Monga momwe Yesu anali ataloserera, ‘anthu a mitundu yonse anadana nawo.’ (Mateyu 24:9) Pakati pa chipwirikiti cha nkhondo, adani a Ufumu wa Mulungu anagwiritsa ntchito machenjera amene ena anagwiritsa ntchito polimbana ndi Yesu Kristu. Iwo ananamizira anthu a Yehova kuti ndi oukira boma, ndipo anakantha pamtima penipeni pa gulu la Mulungu looneka. M’May 1918, boma linapereka chilolezo chomanga pulezidenti wa Watch Tower Society, J. F. Rutherford, ndi ogwira naye ntchito oyandikana naye kwambiri asanu ndi aŵiri. Amuna asanu ndi atatu ameneŵa anaweruzidwa kukhala m’ndende kwa nthaŵi zazitali ndipo anatumizidwa kundende ya ku Atlanta, Georgia, U.S.A. Patapita miyezi isanu ndi inayi iwo anamasulidwa. M’May 1919 bwalo loyendayenda la apilo linagamula kuti oimbidwa mlanduwo anazengedwa mlandu wawo mwatsankhu, chotero chigamulocho chinafafanizidwa. Panaperekedwa chigamulo chakuti mlanduwo uzengedwenso, koma kenako boma linangolekeratu kuzenga mlanduwo, ndipo mlandu wa Mbale Rutherford ndi anzakewo unafafanizidwiratu. Iwo anayambiranso ntchito zawo, ndipo misonkhano ikuluikulu imene inachitika ku Cedar Point, Ohio, mu 1919 ndi mu 1922 inadzutsa changu chatsopano cha ntchito yolalikira.
5. Kodi Mboni za Yehova zinakumana ndi zinthu zotani m’Germany wolamulidwa ndi Anazi?
5 Cha m’ma 1930, kunabadwa maulamuliro opondereza anthu, ndipo Germany, Italy, ndi Japan anagwirizana kupanga gulu limodzi lankhondo. Kuchiyambi kwa zaka zimenezo, anthu a Mulungu anayamba kuzunzidwa koopsa, makamaka ku Germany wolamulidwa ndi Anazi. Panaikidwa ziletso. Nyumba zinkafufuzidwa, ndipo okhalamo ake anamangidwa. Zikwi zambiri anaponyedwa m’ndende chifukwa chakuti anakana kusiya chikhulupiriro chawo. Cholinga cha kumenyana ndi Mulungu ndi anthu ake kumeneku chinali chakuti afafanize Mboni za Yehova m’dziko lolamulidwa moponderezedwa limenelo. * Pamene Mboni ku Germany zinapita kumakhoti kuti zikamenyere ufulu wawo, a Unduna wa Zachilungamo m’boma ladzikolo anakonza chikalata chachitali cholongosola malingaliro awo pofuna kuonetsetsa kuti Mbonizo zisapambane. Icho chinati: “Makhoti sayenera kulephera pachifukwa chokhacho chofuna kutsatira chilungamo; koma ayenera kufunafuna ndi kupeza njira yokwaniritsira ntchito yawo yapamwamba ngakhale kuti kupondereza chilungamo n’kovuta.” Zimenezi zinatanthauza kuti sanali kudzachita chilungamo. Anazi ankanena kuti ntchito za Mboni za Yehova n’zodanitsa anthu, kapena kuti zowonongetsa khalidwe la anthu, ndipo ‘zinasokoneza chitukuko cha dziko chimene chipani cha National Socialistic chinali kuchita.’
6. Kodi panali kuyesayesa kotani kuti aletse ntchito yathu m’nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse ndi pambuyo pake?
6 M’nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse, ziletso zinaikidwa pa anthu a Mulungu ku Australia, Canada, ndi m’mayiko ena a m’chigwirizano cha Britain mu Afirika, ku Asia, ndi m’zilumba za m’nyanja za Caribbean ndi Pacific. Ku United States, adani okhala ndi maudindo apamwamba komanso anthu ena omwe ananamizidwa anadzetsa ‘mavuto pogwiritsa ntchito malamulo.’ (Salmo 94:20) Koma nkhani za kuchitira mbendera sawatcha ndi malamulo a m’madera ena oletsa kulalikira kukhomo ndi khomo zinakambidwa m’makhoti, ndipo, ku United States, zigamulo zabwino zinamanga khoma lochirikizira ufulu wa kulambira. Chifukwa cha thandizo la Yehova, zoyesayesa za adani sizinapambane. Pamene nkhondo inatha ku Ulaya, ziletso zinachotsedwa. Zikwizikwi za Mboni zomwe zinali m’ndende zachibalo zinamasulidwa, koma kulimbanako kunali kusanathe. Nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse itangotha, Nkhondo ya Mawu inayamba. Mayiko a kum’maŵa kwa Ulaya anapondereza anthu a Yehova mowonjezeka. Maboma anachitapo kanthu pofuna kusokoneza ndi kuimitsa ntchito zathu zochitira umboni, kutsekereza zofalitsa za Baibulo kuti zisaloŵe m’mayikomo, ndi kuletseratu misonkhano yathu ikuluikulu yapoyera. Ambiri anamangidwa kapena kutumizidwa kundende zachibalo.
Kupitirizabe Ntchito Yolalikira!
7. Kodi Mboni za Yehova ku Poland, Russia, ndi m’mayiko ena zakumana ndi zinthu zotani m’zaka zaposachedwapa?
7 M’kupita kwa zaka, ntchito yolalikira Ufumu inayambiranso kuchitika poyera. Dziko la Poland, ngakhale kuti linali likadali mu ulamuliro wachikomyunizimu,
linalola kuti misonkhano yachigawo yatsiku limodzi ichitike mu 1982. Mu 1985, misonkhano ya mayiko inachitika kumeneko. Misonkhano yaikulu ya mayiko inatsatira mu 1989, ndipo anthu zikwizikwi ochokera ku Russia ndi Ukraine anasonkhana nawo kumeneko. M’chaka chimenecho, mayiko a Hungary ndi Poland analola Mboni za Yehova mwalamulo. Chakumapeto kwa chaka cha 1989, linga logaŵa mzinda wa Berlin linagwetsedwa. Patangopita miyezi yochepa, tinalandira chilolezo cha boma ku East Germany, ndipo posapita nthaŵi msonkhano wa mayiko unachitika mu Berlin. Ndiyeno kuchiyambi cha ma 1990, panali kuyesayesa kuti tionane ndi abale a ku Russia. Akuluakulu ena a boma anafikiridwa, ndipo mu 1991, Mboni za Yehova zinalembetsa mwalamulo m’kaundula wa boma. Kuyambira pamenepo ntchito yapita patsogolo kwambiri ku Russia ndi m’mayiko omwe kale anali mbali ya Soviet Union.8. Kodi n’chiyani chinachitikira anthu a Yehova m’zaka 45 zotsatira kutha kwa nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse?
8 Pamene kuli kwakuti chizunzo chinatha m’madera ena, chinawonjezeka m’malo enanso. M’zaka 45 zotsatira kutha kwa nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse, mayiko ambiri anakana kulola Mboni za Yehova mwalamulo. Komanso, ifeyo kapena ntchito yathu inaletsedwa m’mayiko 23 mu Afirika, 9 ku Asia, 8 ku Ulaya, 3 ku Latin America, ndiponso 4 m’zilumba zina zodzilamulira zokha.
9. Kodi atumiki a Yehova akumana ndi zotani ku Malaŵi?
9 Mboni za Yehova ku Malaŵi zinali pachizunzo choopsa kwambiri kuyambira mu 1967. Chifukwa cha kusaloŵerera kwawo m’nkhani zandale pokhala Akristu oona, okhulupirira anzathu kumeneko anakana kugula makhadi achipani. (Yohane 17:16) Pambuyo pa msonkhano wa Chipani cha Malaŵi Congress mu 1972, nkhanza zinayambiranso. Abale anathamangitsidwa panyumba zawo ndipo anachotsedwa ntchito. Zikwi zambiri anathaŵamo m’dzikolo kuti angaphedwe. Koma kodi omenyana ndi Mulungu ndi anthu ake anapambana? Ndithudi ayi! Zinthu zitasintha, chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa Ufumu 43,767 anachita lipoti m’Malaŵi mu 1999, ndiponso oposa 120,000 anafika pamisonkhano yachigawo kumeneko. Ofesi yanthambi yatsopano yamangidwa m’likulu la dzikolo.
Amafunafuna Chifukwa Chabodza
10. Mofanana ndi nkhani ya Danieli, kodi otsutsa amakono a anthu a Mulungu achitanji m’masiku ano?
10 Anthu ampatuko, atsogoleri achipembedzo, ndi ena akulephera kupirira uthenga wathu wa m’Mawu a Mulungu. Posonkhezeredwa ndi Gawo la Matchalitchi Achikristu, otsutsa amafunafuna njira yolimbanirana nafe imene iwowo amati ndi njira yalamulo. Kodi nthaŵi zina amagwiritsa ntchito machenjera ati? Eya, kodi anthu achiwembu anagwiritsa ntchito njira iti poukira mneneri Danieli? Pa Danieli 6:4, 5, timaŵerenga kuti: “Akuluŵa ndi akalonga anayesa kum’tola chifukwa Danieli, kunena za ufumuwo; koma sanakhoza kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo sanaona chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye. Pamenepo anthu aŵa anati, Sitidzam’tola chifukwa chilichonse Danieli amene, tikapanda kum’tola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.” Lerolinonso, otsutsa amafunafuna chifukwa chabodza. Amangosokosera za “magulu oopsa” ndipo amayesa kutcha Mboni za Yehova kuti ndi gulu loterolo. Mwa kutifotokoza molakwa, kutineneza, ndi kutinamizira, iwo amatsutsa kulambira kwathu ndi kumamatira kwathu ku mfundo zaumulungu zachikhalidwe.
11. Kodi ndi mfundo zabodza zotani zimene ena otsutsa Mboni za Yehova anena?
11 M’mayiko ena, magulu ena achipembedzo ndi andale amakana kuvomereza kuti timachita “mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu.” (Yakobo 1:27) Ngakhale kuti ntchito zathu zachikristu timazichita m’mayiko 234, otsutsawo amati sindife “chipembedzo chodziŵika.” Kutangotsala pang’ono kuti msonkhano wa mayiko uchitike mu 1998, nyuzipepala ya ku Athens inagwira mawu mtsogoleri wina wa chipembedzo cha Greek Orthodox akunena kuti “[Mboni za Yehova] si ‘chipembedzo chodziŵika,’” ngakhale kuti si zimene Khoti la Ulaya la Ufulu wa Anthu linagamula. Patangopita masiku angapo, nyuzipepala inanso m’mzinda womwewo inagwira mawu woyankhulira tchalitchi chinachake akunena kuti: “[Mboni za Yehova] sizingakhale ‘mpingo wachikristu,’ chifukwa chakuti sizigwirizana ndi chikhulupiriro chachikristu chilichonse chokhudzana ndi Yesu Kristu.” Izi n’zodabwitsa chifukwa chakuti palibe chipembedzo chinanso chimene chimalimbikitsa kwambiri kutsanzira Yesu monga momwe Mboni za Yehova zimachitira!
12. Pomenya nkhondo yathu yauzimu, kodi tiyenera kuchita chiyani?
12 Timayesetsa kutchinjiriza ndi kukhazikitsa uthenga wabwino mwalamulo. (Afilipi 1:7) Ndiponso, sitidzasiya kapena kuchepetsa kumamatira kwathu kwamphamvu ku miyezo ya Mulungu yachilungamo. (Tito 2:10, 12) Monga Yeremiya, ‘tikukwinda m’chuuno mwathu ndi kunena zonse zimene Yehova akutiuza,’ osalola kuti anthu olimbana ndi Mulungu atiopseze iyayi. (Yeremiya 1:17, 18) Mawu Opatulika a Yehova akusonyeza bwino lomwe njira yoyenera yoti tiyendemo. Sitikufuna kudalira “dzanja [lofooka] la thupi” kapena “kukhulupirira mthunzi wa Aigupto,” limene lili dziko lino lapansi. (2 Mbiri 32:8; Yesaya 30:3; 31:1-3) Pomenya nkhondo yauzimu, tiyenera kupitirizabe kukhulupirira mwa Yehova ndi mtima wathu wonse, kum’lola kutsogolera mapazi athu, ndiponso osachirikizika pa luntha lathu. (Miyambo 3:5-7) Ntchito yathu yonse itha kukhala ‘yachabe’ pokhapokha ngati tili ndi chichirikizo cha Yehova ndiponso ngati iye mwini akutisunga.—Salmo 127:1.
Ozunzidwa Koma Osaleka
13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chiukiro chausatana pa Yesu chinalephera?
13 Chitsanzo chachikulu cha kudzipereka kwa Yehova mosasunthika ndiye Yesu, amene ananamiziridwa kuti ndi woukira boma ndi woyambitsa chipwirikiti. Atapenda mlandu wa Yesu, Pilato ankafuna kum’masula. Koma khamulo, losonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo, linafuula kuti Yesu apachikidwe, ngakhale kuti analibe mlandu. Iwo anafuna kuti Baraba, mwamuna amene anaikidwa m’ndende chifukwa cha mlandu wa kuukira boma ndi mbanda, amasulidwe m’malo mwa Yesu! Pilato anayesanso kuletsa Luka 23:2, 5, 14, 18-25) Ngakhale kuti Yesu anafera pamtengo, kuukira Mwana wa Mulungu wopanda mlandu kwausatana ndiponso koipitsitsa kumeneko kunalephereratu, popeza kuti Yehova anaukitsa Yesu ndi kum’kweza kukhala ku dzanja Lake lamanja. Ndipo kudzera mwa Yesu waulemereroyo, mzimu woyera unatsanulidwa patsiku la Pentekoste mu 33 C.E., kukhazikitsa mpingo wachikristu—“wolengedwa watsopano.”—2 Akorinto 5:17; Machitidwe 2:1-4.
otsutsa opulukirawo, koma pomalizira pake anamvera zonena za gulu lopokoseralo. (14. Kodi n’chiyani chinachitika pamene gulu lachiyuda lachipembedzo linaukira otsatira a Yesu?
14 Pasanathe nthaŵi yaitali, gulu lachipembedzolo linaukira atumwi, koma otsatira a Kristu amenewo sanaleke kuyankhula za zinthu zimene anaziona ndi kumva. Ophunzira a Yesu anapemphera kuti: “Ambuye, penyani mawu awo akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.” (Machitidwe 4:29) Yehova anayankha pempho lawo mwa kuwadzaza ndi mzimu woyera ndi kuwalimbitsa kuti apitirize kulengeza kwawo mosaopa. Posapita nthaŵi, atumwiwo analamulidwanso kuti aleke kulalikira, koma Petro ndi atumwi ena anayankha nati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Kuopsezedwa, kumangidwa, ndi kukwapulidwa sizinawaletse kuwonjezera ntchito yawo ya Ufumu.
15. Kodi Gamaliyeli anali ndani, ndipo anapereka uphungu wotani kwa otsutsa achipembedzo a otsatira a Yesu?
15 Kodi olamulira achipembedzowo anachitanji? “Iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha [atumwiwo].” Komabe, mphunzitsi wina wa Chilamulo wotchedwa Gamaliyeli, Mfarisi, analipo, ndipo anali wolemekezedwa ndi anthu onse. Atalamula atumwiwo kuti akakhale panja kwa kanthaŵi kochepa, iye anauza otsutsa achipembedzo amenewo kuti: “Amuna inu a Israyeli, kadzichenjerani nokha za anthu aŵa, chimene muti muwachitire. . . . Ndinena ndi inu, Lekani anthu ameneŵa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka; koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.”—Machitidwe 5:33-39.
Palibe Chida Chosulidwira Ife Chidzapambana
16. M’mawu anuanu, kodi mungalongosole motani chitsimikiziro chimene Yehova akupatsa anthu ake?
16 Uphungu wa Gamaliyeli unali wabwino, ndipo timathokoza pamene ena atiyankhulira. Timazindikiranso kuti ufulu wa kulambira wachirikizidwa mwa zigamulo za makhoti zopangidwa ndi oweruza osakondera. Inde, kumamatira kwathu ku Mawu a Mulungu kumanyansa atsogoleri achipembedzo ndi atsogoleri ena a Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 18:1-3) Ngakhale kuti iwowo ndiponso anthu osonkhezeredwa ndi iwo amalimbana nafe, tili ndi chitsimikiziro ichi: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi choloŵa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chawo chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.”—Yesaya 54:17.
17. Ngakhale kuti otsutsa akulimbana nafe, n’chifukwa chiyani tikulimba mtima?
17 Adani athu akulimbana nafe popanda chifukwa, koma sitichita mantha. (Salmo 109:1-3) Sitidzalola awo amene amadana ndi uthenga wathu wa m’Baibulo kutiopseza kuti tisiye chikhulupiriro chathu. Ngakhale kuti tikudziŵa kuti nkhondo yathu yauzimuyi idzakula, tikudziŵa zotsatira zake. Monga Yeremiya, tidzaona kukwaniritsidwa kwa mawu aulosi akuti: “Adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.” (Yeremiya 1:19) Inde, tikudziŵa kuti omenyana ndi Mulungu sadzapambana!
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Onani nkhani yakuti “Okhulupirika ndi Opanda Mantha Poponderezedwa ndi Anazi” masamba 24-8.
Kodi Mungayankhe Motani?
• N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova akhala akuukiridwa?
• Kodi otsutsa amenyana ndi anthu a Yehova m’njira zotani?
• N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikizira kuti olimbana ndi Mulungu sadzapambana?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 17]
Yehova anatsimikizira Yeremiya kuti adzakhala naye
[Chithunzi patsamba 18]
Opulumuka m’ndende zachibalo
[Chithunzi patsamba 18]
Gulu likuchitira chiwawa Mboni za Yehova
[Chithunzi patsamba 18]
J. F. Rutherford ndi anzake
[Chithunzi patsamba 21]
Ponena za Yesu, omenyana ndi Mulungu sanapambane