Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Latsopano—Kodi Mudzakhalamo?

Dziko Latsopano—Kodi Mudzakhalamo?

Dziko Latsopano​—Kodi Mudzakhalamo?

“Iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”​—MLALIKI 3:12, 13.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidaliro ponena za m’tsogolo?

ANTHU ambiri amaganiza kuti Mulungu Wamphamvuyonse ndi wokhwimitsa zinthu ndi wankhanza. Komabe, mawu ali pamwambaŵa ndi choonadi cha m’Mawu ake ouziridwa. Mawu ameneŵa amagwirizana ndi kukhala kwake “Mulungu wachimwemwe” ndi kuika kwake makolo athu oyambirira m’paradaiso wapadziko lapansi. (1 Timoteo 1:11, NW; Genesis 2:7-9) Pamene tikuyesetsa kuzindikira za tsogolo limene Mulungu walonjeza anthu ake, sitiyenera kudabwa potulukira mikhalidwe imene idzatipatsa chisangalalo chokhalitsa.

2. Ndi zinthu zina ziti zimene mukulakalaka kudzaziona?

2 M’nkhani yapitayo, tinafotokoza malo atatu pamene Baibulo limaneneratu za “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” (Yesaya 65:17) Limodzi la maulosi odalirika amenewo lalembedwa pa Chivumbulutso 21:1. Mavesi otsatira akunena za nthaŵi pamene Mulungu Wamphamvuyonse adzasinthe mikhalidwe padziko lapansi kuti idzakhale yabwino kwambiri. Adzachotsa misozi yonse ya chisoni. Anthu sadzafanso ndi ukalamba, matenda, kapena ngozi. Maliro, kulira, ndi zopweteka zidzapita. Ha, kusangalatsa kwake chiyembekezo chimenecho! Koma kodi tingatsimikize kuti chidzakwaniritsidwadi, ndipo chiyembekezo chimenecho chiyenera kutikhudza motani panopo?

Zifukwa Zokhalira ndi Chidaliro

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malonjezo a Baibulo onena za m’tsogolo?

3 Taonani mmene lemba la Chivumbulutso 21:5 likupitirizira. Limagwira mawu Mulungu, atakhala pampando wake wachifumu wakumwamba, akulengeza kuti: “Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.” Lonjezo laumulungu limenelo limaposa chilengezo cha dziko chilichonse kaya cha ufulu wa dziko wodzilamulira, kapena cha malamulo amakono alionse a za ufulu wachibadwidwe, kapenanso cha chiyembekezo cha anthu chilichonse kaamba ka m’tsogolo. Chimenecho ndi chilengezo chodalirika kotheratu choperekedwa ndi Uyo amene Baibulo limamutcha “wosanama.” (Tito 1:2) Inde, mukhoza kunena kuti basi tiimire pomwepa, zatikwanira kudziŵa za chiyembekezo chosangalatsachi ndi kukhulupirira Mulungu. Koma ayi, tisaimire panopa. Padakali zambiri zoti tiphunzire ponena za m’tsogolo.

4, 5. Kodi ndi maulosi otani a Baibulo omwe tawapenda amene angalimbikitse chidaliro chathu cha zimene zili m’tsogolo?

4 Sinkhasinkhani zimene nkhani yapitayo yakhazikitsa monga malonjezo a Baibulo ponena za miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Yesaya ananeneratu za dongosolo latsopano loterolo, ndipo ulosi wake unakwaniritsidwa pamene Ayudawo anabwerera kudziko lakwawo ndi kukakhazikitsanso kulambira koona. (Ezara 1:1-3; 2:1, 2; 3:12, 13) Komabe, kodi ndi zokhazo zimene ulosi wa Yesaya unalozako? Ayi sizokhazo! Zimene analoserazo zinali kudzakwaniritsidwa m’njira yokulirapo kwambiri m’tsogolo. Kodi tikutero kaamba ka chiyani? Kaamba ka zimene timaŵerenga pa 2 Petro 3:13 ndi Chivumbulutso 21:1-5. Malemba ameneŵa amakamba za miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene zidzapindulitsa Akristu onse padziko lapansi.

5 Monga taonera kale, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano’ kanayi. Tapenda atatu okha a mawu ameneŵa ndipo taona matanthauzo ake olimbikitsa kwambiri. Baibulo limaneneratu mosabisa mawu kuti Mulungu adzachotsa zoipa zonse ndi zinthu zina zochititsa mavuto ndi kuti adzadalitsanso anthu m’dziko lake latsopano limene walilonjezalo.

6. Kodi ulosi wachinayi wotchula “m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano” umaneneratu za chiyani?

6 Tsopano tiyeni tipende malo otsalawo pamene pakutchulidwanso “m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” pa Yesaya 66:22-24: “Monga m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu. Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira ku linzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova. Ndipo iwo adzatuluka ndi kuyang’ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mbozi yawo sidzafa, pena moto wawo sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.”

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganiza kuti Yesaya 66:22-24 adzakwaniritsidwa m’masiku alin’kudza?

7 Ulosi umenewu unakwaniritsidwa pa Ayuda aja okhazikitsidwanso m’dziko lakwawo, koma panalinso kukwaniritsidwa kwina. Kumeneko kunali m’zaka zam’tsogolo kuchokera pa kulembedwa kwa kalata yachiŵiri ya Petro ndi buku la Chivumbulutso, chifukwa ananena za “m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Tiyenera kuyembekezera mwachidwi kukwaniritsidwa kwakukulu komanso kwathunthu kumeneko m’dongosolo latsopano. Taonani ina mwa mikhalidwe imene tingaiyembekezere kudzasangalala nayo panthaŵiyo.

8, 9. (a) Kodi anthu a Mulungu ‘adzakhalapobe’ m’ganizo lotani? (b) Kodi tanthauzo lake n’lotani la ulosi wakuti atumiki a Yehova adzalambira “kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira ku linzake”?

8 Lemba la Chivumbulutso 21:4 linasonyeza kuti imfa sidzakhalakonso. Mawu a pa Yesaya chaputala 66 amavomereza zimenezo. Tikhoza kuona pa vesi 22 kuti Yehova amadziŵa kuti miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano sizidzakhala zakanthaŵi, zosakhalitsa ayi. Ndiponso, anthu ake ‘adzakhalabe’ pamaso pake. Zimene Mulungu wachitira kale anthu ake osankhika zimatipatsa chifukwa chokhalira ndi chidaliro. Akristu oona akumana ndi mazunzo ankhalwe, ngakhale chiwawa cha anthu a changu chopulukira omwe ayesetsa kuti awafafanize kotheratu. (Yohane 16:2; Machitidwe 8:1) Komabe, ngakhale olamulira amphamvu kwambiri odana ndi anthu a Mulungu, monga Nero, Mfumu Yaikulu ya Roma komanso Adolf Hitler, sanathe kufafaniza okhulupirika a Mulungu, amene avala dzina lake. Yehova wateteza mpingo wa anthu ake, ndipo tili ndi chitsimikizo chonse chakuti adzaulola kukhalabe mpaka kalekale.

9 Mofananamo, okhulupirikawo kwa Mulungu monga mbali ya dziko lapansi latsopano, olambira oona m’dziko latsopano, adzakhalapobe aliyense payekha chifukwa azilambira Mlengi wa zinthu zonse m’njira yoyera. Kulambira kumeneko sikudzakhala kwa kamodzikamodzi kapena kochitika mwachisawawa. Chilamulo cha Mulungu, choperekedwa kwa Israyeli kudzera mwa Mose, chinalamula zochitika zina za kulambira mwezi uliwonse, pakukhala kwa mwezi watsopano, komanso mlungu ndi mlungu, patsiku la Sabata. (Levitiko 24:5-9; Numeri 10:10; 28:9, 10; 2 Mbiri 2:4) Choncho Yesaya 66:23 akunena za kulambira Mulungu kokhazikika, kopitirira, mlungu ndi mlungu komanso mwezi ndi mwezi. Panthaŵiyo sikudzakhalanso chikhulupiriro chokana Mulungu ndi chipembedzo chonyenga. “Anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa” Yehova.

10. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi chidaliro chakuti dziko latsopano lidzakhala lopanda anthu oipa amene angaliipitse kunthaŵi zonse?

10 Yesaya 66:24 amatitsimikizira kuti sikudzakhalanso chiopsezo chilichonse pa mtendere ndi chilungamo cha dziko lapansi latsopano. Kudzakhala kulibe anthu oipa amene angadzaliwononge. Kumbukirani kuti 2 Petro 3:7 amanena kuti kutsogolo kwathuku kuli “tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” Ati adzawonongedwewo ndi anthu osapembedza. Opanda chifukwa sadzakhudzidwa, kusiyana ndi zimene zimachitika kaŵirikaŵiri pankhondo za anthu, pamene anthu wamba ovulala ndi ophedwa ndiwo amachuluka kuposa asilikali. Woweruza Wamkulu akutitsimikizira kuti tsiku limenelo lidzakhala tsiku la chiwonongeko cha anthu osapembedza.

11. Kodi Yesaya akusonyeza kuti tsogolo lidzakhala lotani kwa aliyense amene apandukira Mulungu ndi kusam’lambira?

11 Olungama odzapulumukawo adzaona kuti mawu aulosi a Mulungu alidi oona. Vesi 24 limaneneratu kuti ‘mitembo ya anthu amene analakwira’ Yehova idzakhala umboni wa chiweruzo chake. Mawu amphamvuwo amene Yesaya anawagwiritsa ntchito angamveke ngati ochititsa kakasi kwambiri. Komabe, ndiwo mawu oyenerera zimene zinachitikadi. Kunja kwa linga la Yerusalemu wakale kunali dzala lotayako zinyalala, ndipo nthaŵi zina ankatayakonso mitembo ya apandu onyongedwa osayenerera kuikidwa mwa mwambo wa maliro. * Kudzalako, zinyalala ndi mitemboyo zinkafafanizika mofulumira chifukwa cha nyongolotsi ndi moto wonyeketsa. Mwachionekere, mawu a Yesayawo opereka chithunzi champhamvu motero, amaonetsa mmene chiweruzo cha Yehova chidzafafaniziratu anthu ochimwa.

Zimene Iye Walonjeza

12. Kodi Yesaya akufotokozanso zotani ponena za moyo wa m’dziko latsopano?

12 Lemba la Chivumbulutso 21:4 limatiuza za zinthu zina zimene sizidzakhalamo m’dongosolo latsopano likudzalo. Nanga zidzakhalemo ndi zinthu zotani? Kodi moyo udzakhala wotani? Kodi tingapeze chithunzi chodalirika chilichonse? Inde. Yesaya chaputala 65 mwaulosi amafotokoza mikhalidwe yabwino imene tidzakhalamo ngati Yehova ativomereza kukhala ndi moyo pamene iye, pomalizira pake, alenga miyamba yatsopano imeneyi ndi dziko lapansi latsopano. Ajawo amene adzapatsidwe malo achikhalire m’dziko lapansi latsopano limenelo sadzakalamba kapena kufa. Yesaya 65:20 amatitsimikizira kuti: “Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi [“pakuti munthu adzafa ngati mwana, ngakhale ali wa zaka zana limodzi,” NW]; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatembereredwa.”

13. Kodi Yesaya 65:20 akutitsimikizira motani kuti anthu a Mulungu adzakhala otetezeka?

13 Pamene ulosiwu choyamba unakwaniritsidwa pa anthu a mtundu wa Yesaya, zinatanthauza kuti makanda m’dzikomo anali otetezeka. Palibe adani amene anafika m’dzikomo, muja anachitira Ababulo, kudzatenga makanda ndi kupha amuna anyonga zawo. (2 Mbiri 36:17, 20) M’dziko latsopano likudzalo, anthu adzakhala osungika, otetezeka, okhoza kusangalala ndi moyo. Munthu akadzasankha kupandukira Mulungu, sadzaloledwa kukhalabe ndi moyo. Mulungu adzam’chotsa. Bwanji ngati wochimwa wopandukayo ali wa zaka zana limodzi? Adzafa “ngati mwana” poyerekeza ndi kukhala ndi moyo wosatha.​—1 Timoteo 1:19, 20; 2 Timoteo 2:16-19.

14, 15. Malinga n’kunena kwa Yesaya 65:21, 22, kodi mungayembekezere ndi chidwi ntchito zopindulitsa zotani?

14 M’malo molongosola zambiri mmene wochimwa dala angadzachotsedwere, Yesaya akufotokoza mikhalidwe ya moyo imene idzakhalapo m’dziko latsopanolo. Tayesani kudziika m’chithunzi cha mkhalidwewo. Zimene mungayambirire kuona ndi zinthu zimene zili pafupi ndi maganizo anu. Yesaya akufotokoza zimenezo m’mavesi 21 ndi 22 kuti: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhika anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.”

15 Ngati mudakalibe luso la kumanga kapena ngati simunalimepo munda, ulosi wa Yesaya ukuonetsa kuti maphunziro akukuyembekezerani. Komabe, kodi mudzakonda kuphunzira mothandizidwa ndi alangizi aluso, mwina anansi oyandikana nawo amene adzakhala ofunitsitsa kukuthandizani? Yesaya sananene kaya ngati nyumba yanu idzakhala ya mawindo aakulu opanda magalasi ongokhala ndi tinsalu totchinga dzuŵa, kuti muzisangalala ndi kamphepo kayeziyezi, kapena mawindo otsekedwa ndi magalasi mmene mungaonere nyengo zomasintha panja. Kodi mudzamanga nyumba ya denga lotaya madzi ndi chipale chofeŵa? Kapena kodi nyengo ya malo amenewo idzafuna denga lafulati​—muja alili madenga a ku Middle East​—pamene mungakhale ndi banja lanu posangalala ndi chakudya chokoma ndi kucheza kwabwino?​—Deuteronomo 22:8; Nehemiya 8:16.

16. N’chifukwa chiyani mungayembekezere dziko latsopano kukhala lokhutiritsa mpaka kalekale?

16 Chofunika kwambiri koposa kungodziŵa chabe zinthu ngati zimenezo ndicho mfundo yakuti mudzakhala ndi nyumba yanuyanu. Idzakhaladi yanuyanu​—osati umu zilili masiku ano kuti pamene mwaivutikira nyumba kuimanga, akukapindula nayo ndi wina. Yesaya 65:21 akunenanso kuti mudzaoka ndi kudya zipatso zake. Mwachionekere, mawu amenewo akupereka chithunzi chonse. Mudzakhutira mokwanira ndi nyonga zanu, zipatso za ntchito zanu. Mudzatha kuchita zimenezo kwa moyo wanu wonse​—“monga masiku a mtengo.” Chithunzi chimenechi chikuyeneranadi ndi mawu akuti “zonse zikhale zatsopano”!​—Salmo 92:12-14.

17. Ndi lonjezo lotani limene makolo adzaliona kukhala lolimbikitsa kwambiri?

17 Ngati muli kholo, mawuŵa adzakukhudzani kwambiri: “Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo. Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.” (Yesaya 65:23, 24) Kodi munakumvapo kuŵaŵa kwake ‘kobalira tsoka’? Sitingachite kutchula mavuto ambirimbiri amene ana amakhala nawo omwe amadzetsa tsoka kwa makolo ndi ena. Limodzi ndi zimenezo, tonse taonanso mmene makolo ena amakhalira otanganidwa kwambiri ndi ntchito, zochita zawo, kapena ndi zosangalatsa zawo moti amakhala ndi nthaŵi yochepa kwambiri yokhala limodzi ndi ana awo. Kusiyana ndi zimenezo, Yehova watitsimikizira kuti iye adzamvetsera ndi kulabadira zosoŵa zathu, ngakhale kuziyembekezera.

18. N’chifukwa chiyani mungayembekezere kudzasangalala ndi nyama m’dziko latsopano?

18 Pamene mukuganizira zimene mungasangalale nazo m’dziko latsopano, taonani m’maganizo mwanu chithunzi cha mkhalidwe umene mawu aulosi a Mulungu akufotokoza: “Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng’ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m’phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.” (Yesaya 65:25) Akatswiri a zojambulajambula ayesa kujambula chithunzi cha zimenezo, koma pano sitikunena za chithunzi cha mkhalidwe wongoyerekeza m’maganizo. Zimene tikunenazi zidzachitikadi. Mtendere udzafalikira pakati pa anthu ndipo udzatsagananso ndi mtendere pakati pa anthu ndi nyama. Akatswiri a zamoyo ndi okonda nyama ambiri amathera zaka zawo zofunika kwambiri m’moyo akumaphunzira mitundu yoŵerengeka chabe ya nyama kapena mtundu umodzi wokha. Mosiyana ndi zimenezo, taganizirani zimene mudzatha kuphunzira pamene nyama zidzakhala zosaopanso anthu. Panthaŵiyo mudzatha kufikira ngakhale mbalame ndi tizilombo ting’onoting’ono timene timakhala m’thengo kapena m’nkhalango​—inde, mudzazionerera, kuphunzira kwa izo, ndi kusangalala nazo. (Yobu 12:7-9) Mudzatero bwinobwino, mosaopa munthu kapena nyama. Yehova akuti: “Sizidzapwetekana, kapena kusakazana m’phiri langa lonse lopatulika.” Kumeneko kudzakhala kusintha kodabwitsa, poyerekeza ndi zimene tikuona ndi kukumana nazo lero!

19, 20. N’chifukwa chiyani anthu a Mulungu ali osiyana kwambiri ndi anthu ochuluka lerolino?

19 Monga tinatchulira kale, anthu satha kuneneratu molondola zam’tsogolo, ngakhale kuti pali maganizo ofala ponena za meleniyamu yatsopano. Zimenezo zimachititsa anthu ambiri kukhala okhumudwa, osokonezeka, kapena otaya mtima. Peter Emberley, mtsogoleri wa Yunivesite ku Canada, analemba kuti: “[Achikulire] ambiri m’kupita kwa nthaŵi amakumana ndi mafunso ofunika enieni onena za moyo. Kodi ndine ndani? Kodi cholinga changa makamaka n’chiyani? Kodi choloŵa chimene ndingasiyire mbadwo wotsatira n’chiyani? Iwo amalimbikira ali m’zaka zapakati za moyo wawo kuti apeze mtendere ndi cholinga cha miyoyo yawo.”

20 Inunso mutha kumvetsa chifukwa chake anthu ambiri amakhalanso ndi maganizo amenewo. Iwo angayesetse kuti asangalale ndi moyo kudzera m’mitundu yosiyanasiyana ya maseŵera amene angawakonde. Komabe, sadziŵa zimene zili m’tsogolo, choncho moyo ungakhale wopanda tanthauzo, wopanda dongosolo, kapena cholinga chenicheni. Tsopano siyanitsani maganizo amenewo ndi mmene inuyo mumauonera moyo, malinga ndi zimene tapenda. Inuyo mukudziŵa kuti m’miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene Yehova walonjeza, tidzatha kumwaza maso uku ndi uku ndi kunena mochokera pansi pa mtima kuti, ‘Zoonadi, Mulungu wachita zonse kukhala zatsopano’! Ha, mmene tidzasangalalire ndi zimenezo!

21. Kodi ndi mfundo yofanana iti imene timapeza pa Yesaya 65:25 ndi Yesaya 11:9?

21 Sikuyerekedwa ngati tidziyerekeza kuti tili m’dziko latsopano la Mulungu. Iye akutipempha, ngakhalenso kutilimbikitsa kuti tim’lambire m’choonadi tsopano kuti tidzayenerere moyo pamene ‘sizidzapwetekana, kapena kusakazana m’phiri lake lonse lopatulika.’ (Yesaya 65:25) Komabe, kodi munkadziŵa kuti Yesaya poyambirirapo ananena zofananazo, ndi kuti anaphatikizapo mfundo yofunika kwambiri kuti tikasangalaledi ndi dziko latsopanolo? Yesaya 11:9 amati: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”

22. Kodi kupenda kwathu maulosi anayi a m’Baibulo kuyenera kutilimbikitsa kuchitanji?

22 “Odziŵa Yehova.” Pamene Mulungu apanga zinthu zonse kukhala zatsopano, anthu a m’dziko lapansi adzakhala ndi chidziŵitso cholondola ponena za iye ndi chifuniro chake. Zimenezo zidzaphatikizapo kuphunziranso chinthu china kuwonjezera pa kuphunzira za chilengedwe cha zinyama. Zikuphatikizapo kuphunzira Mawu ake ouziridwa. Mwachitsanzo, taganizirani zimene taona mwa kupenda maulosi anayi okha otchula ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.’ (Yesaya 65:17; 66:22; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1) Muli ndi chifukwa chabwino choŵerengera Baibulo tsiku ndi tsiku. Kodi chimenechi ndi chizoloŵezi chanu m’moyo wanu? Ngati ayi, kodi mungachite kusintha kotani kuti tsiku ndi tsiku muziŵerenga zina mwa zimene Mulungu akunena? Mudzapeza kuti pambali pa kuyembekezera mwachidwi kudzasangalala ndi dziko latsopano, mudzapezanso chisangalalo choŵirikiza ngakhale pakali pano, monga zinakhalira kwa wamasalmo.​—Salmo 1:1, 2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 906, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesaya 66:22-24 akuneneratu zam’tsogolo?

• Kodi mukuyembekezera chiyani mwachidwi pa zimene zatchulidwa m’maulosi a pa Yesaya 66:22-24 ndi pa Yesaya 65:20-25?

• Kodi muli ndi zifukwa zotani zokhalira ndi chidaliro ponena za tsogolo lanu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 15]

Yesaya, Petro, ndi Yohane ananeneratu mbali zina za “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano”