Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudzivomereza Nokha kwa Ena?

Kodi Mukudzivomereza Nokha kwa Ena?

Kodi Mukudzivomereza Nokha kwa Ena?

‘Sindisamala zimene anthu ena amaganiza!’ Panthaŵi imene mwapsa mtima kapena kukhumudwa, mwinamwake munanenapo mawu odzilimbitsa mtima ameneŵa. Komabe mungayambe kuda nkhaŵa pamene mkwiyo woopsa umenewo waphwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ambirife timasamaladi zimene ena amatiganizira.

NDITHUDI, tiyenera kukhala osamala za malingaliro a anthu ena. Makamaka ifeyo monga Akristu, atumiki oikidwa a Yehova Mulungu, tiyenera kuda nkhaŵa kwambiri ponena za momwe ena amationera. Ndi iko komwe, ndife “choonetsedwa ku dziko lapansi.” (1 Akorinto 4:9) Pa 2 Akorinto 6:3, 4, timapezapo uphungu wabwino kwambiri wa mtumwi Paulo wakuti: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira [“tidzivomereza,” NW] ife tokha monga atumiki a Mulungu.”

Komano, kodi kudzivomereza tokha kwa ena kumatanthauzanji? Kodi kumatanthauza kudzikweza tokha kapena kudzitama ife eni ndi maluso athu? Ayi. Koma kumafuna kugwiritsa ntchito mawu a pa 1 Petro 2:12 akuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti . . . akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino.” Akristu amadzivomereza okha mwa kulola makhalidwe awo kuwachitira umboni! Ndithudi, zimenezi zimadzetsa chitamando, osati kwa ife, koma kwa Mulungu. Komabe, kudzivomereza kwathu kwa ena kungadzetse mapindu enanso kwa ife eni. Tiyeni tione mbali zitatu za momwe zimenezi zingakhalire choncho kwa inu.

Monga Woyembekezera Ukwati

Mwachitsanzo, tiyeni titenge nkhani ya ukwati. Ukwati ndi mphatso yochokera kwa Yehova Mulungu, iye “amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina.” (Aefeso 3:15) Mwinamwake mukulakalaka kuti mudzakwatire kapena kukwatiwa tsiku linalake. Ngati ndi choncho, kodi ndi motani momwe mukudzivomerezera nokha monga woyembekezera ukwati? Inde, kodi mwadzipangira mbiri yotani monga mwamuna wachikristu wosakwatira kapena mkazi wachikristu wosakwatiwa?

M’madera ena zimenezi n’zodetsa nkhaŵa kwambiri ku mabanja. Mwachitsanzo, ku Ghana pamene anthu aŵiri akufuna kukwatirana, mwamwambo aŵiriwo adziŵitse makolo awo. Kenako, makolowo amadziŵitsa anthu ena a m’banjamo. Ndiyeno banja la mwamunayo limayamba kufufuza mbiri ya mkaziyo kwa anthu oyandikana nawo. Pamene makolowo akhutitsidwa kuti mkaziyo ndi woyenerera, iwo amakadziŵitsa banja la mkaziyo za malingaliro a mwana wawo wamwamuna kuti akufuna kukwatira mwana wawo wamkazi. Tsopano banja la mkaziyo limafufuza mbiri ya mwamunayo asanavomereze za ukwati. Pachifukwa chimenechi mwambi wina wa ku Ghana umati, “Funsirani kwa amene akum’dziŵa bwino kwambiri musanaloŵe mu ukwati.”

Nanga bwanji ponena za m’mayiko a Kumadzulo, kumene anthu kaŵirikaŵiri amaloledwa kudzisankhira munthu wodzakwatirana naye? Ngakhale kumadera amenewonso, Mkristu wokhwima m’nzeru, kaya wamwamuna kapena wamkazi, angachite bwino kufunsira chivomerezo choona kwa anthu amene akum’dziŵa bwino kwambiri munthu amene akuyembekezera kukwatirana nayeyo, monga ngati makolo kapena mabwenzi okhwima m’nzeru. Malinga ndi buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, mtsikana angadzifunse kuti: “‘Kodi mwamunayu ali ndi mbiri yotani? Kodi mabwenzi ake ndani? Kodi amasonyeza kudziletsa? Kodi amachita motani ndi okalamba? Kodi amachokera ku banja lotani? Kodi amachita motani ndi banja lake? Kodi ndalama amaziona motani? Kodi amamwetsa moŵa? Kodi ali wamtima wapachala, ndipo mwina wachiwawa? Kodi ali ndi mathayo otani mumpingo, ndipo amawachita motani? Kodi ndikhoza kum’patsa ulemu waukulu?’​—Levitiko 19:32; Miyambo 22:29; 31:23; Aefeso 5:3-5, 33; 1 Timoteo 5:8; 6:10; Tito 2:6, 7.” *

Chimodzimodzinso mwamuna angafunikire kufufuza mbiri ya mkazi wachikristu wina aliyense amene akulingalira kumukwatira. Malinga ndi Baibulo, Boazi anachita zimenezo kwa Rute, mkazi amene anadzam’kwatira pambuyo pake. Pamene Rute anafunsa kuti: “Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?” Boazi anayankha kuti: ‘Anandifotokozera bwino zonse unachita.’ (Rute 2:10-12) Inde, si Boazi yekha amene anaona kuti Rute anali mkazi wokhulupirika, wodzipereka, ndiponso wogwira ntchito zolimba koma analandiranso ndemanga zabwino kuchokera kwa anthu ena.

Mofananamo, khalidwe lanu lidzakhudza nkhani ya momwe ena amakuonerani monga wokwatirana naye woyenera. Mwa ichi, kodi mukudzivomereza nokha motani kwa ena?

Monga Wolembedwa Ntchito

Malo a ntchito ndi kwinanso kumene kukhala ndi makhalidwe abwino kungakupindulitseni. Pangakhale mpikisano waukulu kwambiri wolimbirana ntchito. Kaŵirikaŵiri, antchito amene amadziŵika kuti ndi amwano, a chizoloŵezi chochedwa, ndi opanda chilungamo kaŵirikaŵiri amachotsedwa ntchito. Makampani angapumitsenso antchito amene ndi odziŵa bwino ntchito n’cholinga choti achepetseko ndalama zomwe amawononga. Pamene anthu omwe ali paulova akufunsiranso ntchito, angaone kuti makampani amene akufunsirako ntchitowo akufunsa kwa makampani amene anagwirako ntchito kale n’cholinga choti adziŵe za momwe amagwirira ntchito, mzimu wawo pa ntchito, ndiponso momwe amadziŵira ntchitoyo. Akristu ambiri adzivomereza okha mwachipambano kwa owalemba ntchito mwa makhalidwe awo aulemu, mavalidwe odekha, kukhala pamtendere ndi ena, ndiponso mikhalidwe yabwino yachikristu.

Mkhalidwe umenewo ndiwo kuchita chilungamo​—mkhalidwe umene umalingaliridwa kwambiri ndi anthu olemba ntchito. Monga mtumwi Paulo, tikufuna “kukhala nawo makhalidwe abwino.” (Ahebri 13:18) Pakampani ina yamigodi ku Ghana, panatchuka ndi nkhani yakuba. Woyang’anira fakitale yoyenga, yemwe ndi Mboni, anapitirizabe kugwira ntchito yake pamene ena anachotsedwa ntchito. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti akuluakulu a kampaniyo anaona kuona mtima kwake kwa zaka zambiri. Anadziŵanso bwino kwambiri za kulimbikira kwake pantchito ndi kuchitira ulemu akuluakulu. Inde, makhalidwe ake abwino anateteza ntchito yake!

Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe Mkristu angachite kuti adzivomereze yekha pamsika wantchito? Phunzirani kukhala waluso pantchito iliyonse imene mwapatsidwa. (Miyambo 22:29) Gwirani ntchitoyo mwakhama ndiponso mosamala kwambiri. (Miyambo 10:4; 13:4) Chitirani ulemu okulembani ntchito ndiponso okuyang’anirani pantchitopo. (Aefeso 6:5) Kusunga nthaŵi, kuchita chilungamo, kugwira ntchito molongosoka, ndiponso mwakhama ndiyo mikhalidwe imene anthu olemba ntchito amafuna, ndipo mikhalidwe imeneyi ingakuthandizeni kupeza ntchito ngakhale panthaŵi yomwe ntchito zikusoŵa.

Maudindo a Mumpingo

Tsopano lino kuposa ndi kale lonse, amuna okhwima m’nzeru akufunika kuti atsogolere mpingo wachikristu. Chifukwa chake n’chiyani? Yesaya analosera kuti: “Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iŵe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.” (Yesaya 54:2) M’kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu, mpingo wa Yehova padziko lonse lapansi ukukulirakulira.

Choncho ngati ndinu mwamuna wachikristu, kodi ndi motani momwe mungadzivomerezere nokha monga munthu woyenerera kutumikira paudindo womwe mwapatsidwa? Talingalirani chitsanzo cha wachinyamatayo Timoteo. Luka anasimba kuti Timoteo “anam’chitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.” Inde, mwa makhalidwe ake abwino, mnyamata ameneyu anadzivomereza yekha kwa anthu a m’mizinda iŵiri. Chotero Paulo anaitana Timoteo kuti azikhala naye m’ntchito yoyendayenda, kulalikira ndi kuphunzitsa m’mpingo.​—Machitidwe 16:1-4.

Kodi ndi motani momwe munthu ‘angakhumbire udindo wa woyang’anira’ m’njira yoyenera ndi yaumulungu lerolino? Ndithudi osati mwa kukopa anthu kuti am’sankhe koma mwa kukhala ndi mikhalidwe ya mzimu yomwe ndi yofunika kaamba ka udindo umenewo. (1 Timoteo 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Angasonyezenso kuti “aifuna ntchito yabwino” mwa kutenga nawo mbali mokwanira bwino m’ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Anthu amene amadzivomereza okha monga amuna achikristu amaudindo amakhala oda nkhaŵa ponena za ubwino wa abale awo auzimu. Amatsatira uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Patsani zosoŵa oyera mtima; cherezani aulendo.” (Aroma 12:13) Mwakuchita zinthu zimenezi, ndithudi mwamuna wachikristu ‘angadzivomereze yekha monga mtumiki wa Mulungu.’

Nthaŵi Zonse

Kudzivomereza tokha kwa anthu ena sikutanthauza kuvala mkhalidwe wonyengezera kapena kukhala “okondweretsa anthu.” (Aefeso 6:6) Kwenikweni, kumatanthauza kudzivomereza tokha kwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu, mwa kutsata malamulo ndiponso mfundo zake zachikhalidwe mosonkhezeredwa ndi chikumbumtima. Ngati mukulitsa mkhalidwe wanu wauzimu ndi kulimbitsa unansi wanu ndi Yehova Mulungu, anthu ena adzazindikira kusintha m’njira imene mumachitira zinthu ndi anthu a m’banja lanu, ogwira nawo ntchito, ndi Akristu anzanu. Adzaonanso kukhazikika ndi kusamala kwanu, kusankha bwino zochita zanu, luso lanu la kusamalira udindo, ndiponso kudzichepetsa kwanu. Zimenezi zidzapangitsa kuti iwo azikukondani ndiponso kukulemekezani ndipo, chofunika kwambiri, zidzapangitsa kuti Yehova Mulungu akondwere nanu chifukwa chakuti mukudzivomereza nokha kwa ena!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 19]

Mwanzeru makolo ambiri amafunsira za mbiri ya munthu amene mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi akufuna kukwatirana naye

[Chithunzi patsamba 20]

Mbale amadzivomereza yekha pa maudindo a utumiki mwa kudera nkhaŵa anthu ena