Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwasangalala kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, onani ngati mungayankhe mafunso otsatiraŵa:

N’chiyani chinafeŵetsa zinthu kuti khirisimasi ilandiridwe mosavuta ku Korea?

Munali chikhulupiriro chakalekale m’Korea ndi m’mayiko enanso chakuti panali mulungu wa m’khichini yemwe amati amaloŵera pa chumuni ndi kubweretsa mphatso mu December. Komanso, nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatha, asilikali a ku America anagaŵa mphatso ndi kupereka zithandizo m’matchalitchi akomweko.​—12/15, masamba 4, 5.

Pokwaniritsa Yesaya 21:8, kodi Mulungu ali ndi “mlonda” wotani m’nthaŵi yathu ino?

Akristu odzozedwa ndi mzimu, amene akutumikira monga gulu la mlonda, adziŵitsa anthu za tanthauzo la zochitika m’dzikoli zomwe zakwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. Iwo athandizanso ophunzira Baibulo kuzindikira ndi kupeŵa ziphunzitso ndi kuchita zinthu zosemphana ndi malemba.​—1/1, masamba 8, 9.

Kodi “Abale a ku Poland” anali yani?

Iwo anali kagulu kakang’ono ka chipembedzo m’zaka za m’mazana a 16 ndi 17 ku Poland omwe ankalimbikitsa kumamatira kwambiri ku Baibulo ndipo chifukwa cha chimenecho ankakana ziphunzitso zofala za matchalitchi, monga Utatu, ubatizo wa makanda, ndi moto wa helo. M’kupita kwa nthaŵi, anazunzidwa kwadzaoneni ndi kuwabalalitsira m’mayiko ena.​—1/1, masamba 21-3.

N’chifukwa chiyani maulosi a m’Baibulo ali oyenera kuwakhulupirira m’malo mwa zolosera za anthu ofufuza zinthu zodzachitika m’tsogolo kapena okhulupirira nyenyezi?

Anthu odziyesa aneneri aonekera kukhala osadalirika m’pang’ono pomwe chifukwa chakuti amanyalanyaza Yehova ndi Baibulo. Maulosi a m’Baibulo okha ndiwo angakuthandizeni kudziŵa momwe zochitika zikugwirizanira ndi chifuno cha Mulungu, kupindulitsa inuyo ndi banja lanu kosatha.​—1/15, tsamba 3.

Kodi ndi maumboni ena ati otsimikizira kuti tikukhala m’masiku otsiriza?

Tingaone zotsatira za kupitikitsidwa kwa Satana kumwamba. (Chivumbulutso 12:9) Tikukhala m’nthaŵi ya “mfumu” yotsiriza yotchulidwa pa Chivumbulutso 17:9-11. Chiŵerengero cha Akristu odzozedwadi chikuchepa, komabe zikuoneka kuti ena mwa ameneŵa adzakhala adakali padziko lapansi pompano mmene chisautso chachikulu chizidzayamba.​—1/15, masamba 12, 13.

Kodi buku la Habakuku linalembedwa liti, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi pa bukulo?

Buku la m’Baibulo limeneli linalembedwa cha m’ma 628 B.C.E. Muli ziweruzo za Yehova zoperekedwa pa Yuda wakale ndi pa Babulo. Limanenanso za chiweruzo cha Mulungu chomwe posachedwapa chidzaperekedwa pa dongosolo loipa lamakonoli.​—2/1, tsamba 9.

Kodi ndi pati m’Baibulo pamene tingapeze uphungu wanzeru wa amayi kwa mkazi waluso?

Chaputala chotsirizira cha buku la Miyambo, chaputala 31, ndilo gwero labwino koposa la uphungu woterowo.​—2/1, masamba 30, 31.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala othokoza kuti Yehova wativumbulira “mtima wa Kristu”? (1 Akorinto 2:16)

Mwa Mauthenga Abwino, Yehova watiphunzitsa zolingalira za Yesu, za mumtima, zochita, ndi zimene amaziika patsogolo. Zimenezi zingatithandize kukhala ofanana naye Yesu, makamaka pa khama lomwe timakhala nalo pa ntchito yolalikira yopulumutsa moyo.​—2/15, tsamba 25.

Kodi Mulungu amayankha mapemphero lerolino?

Inde. Ngakhale kuti Baibulo likusonyeza kuti Mulungu sayankha mapemphero onse, zochitika m’nthaŵi ino yamakono zasonyeza kuti mobwerezabwereza iye wayankha anthu omwe apempherera chitonthozo ndi chithandizo pa nkhani monga kuthetsa mavuto a m’banja.​—3/1, masamba 3-7.

Kodi tingachitenji kuti tipeze nyonga ya Mulungu?

Tingaipeze mwa pemphero, kuŵerenga Baibulo kuti tilimbe mwauzimu, ndi kulimbitsidwa m’mayanjano achikristu.​—3/1, masamba 15, 16.

Kodi makolo angathandize motani ana awo kuti apindule kwambiri ndi misonkhano yachikristu?

Angathandize ana awo kuti akhalebe ogalamuka, mwinamwake angakonze kuti azigoneratu asanapite kumsonkhanoko. Ana angalimbikitsidwe kumalemba “mfundo” papepala nthaŵi iliyonse pamene mawu kapena mayina ozoloŵereka atchulidwa.​—3/15, masamba 17, 18.

Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe tingaphunzire pa chitsanzo cha Yobu?

Yobu anaika unansi wake ndi Mulungu patsogolo, sanali wokondera pochita zinthu ndi anthu anzake, anayesetsa molimbika kukhalabe wokhulupirika kwa mkazi wake, anasonyeza kudera nkhaŵa mkhalidwe wauzimu wa banja lake, ndipo anapirira mokhulupirika m’mayesero.​—3/15, masamba 25-7.

Kodi Baibulo lili ndi zizindikiro zina zachinsinsi zomwe zimavumbula mauthenga ena obisika?

Ayi. Nkhambakamwa zakuti pali mauthenga obisika zinganenedwe chimodzimodzi pa buku lina lililonse. Mauthenga omwe akuti alipo m’Baibulowo angakhale opanda tanthauzo chifukwa chakuti kalembedwe ka mawu m’zolembedwa pamanja za chihebri n’kosiyanasiyana.​—4/1 masamba 30, 31.