Kusodza Anthu ku Nyanja ya Aegean
Kusodza Anthu ku Nyanja ya Aegean
NYANJA ya Aegean imatenga chigawo chachikulu cha kum’maŵa kwa nyanja ya Mediterranean. Kumpoto kwake komanso kumadzulo kuli dziko la Greece. Kumwera kuli chilumba cha Krete ndipo kum’maŵa dziko la Turkey. Monga malo amene kunayambira chitukuko chopambana chamakedzana, nyanja ya Aegean ili ndi zilumba zokulirapo komanso zilumba zazing’ono zobalalikana. Maonekedwe a mapiri a zilumbazi, omwe pali tinyumba toŵerengeka toyera komanso toŵala chifukwa cha dzuŵa, anasonkhezera wolemba ndakatulo kuzifanizira ndi “akavalo amiyala okhala ndi manyenje ochuluka.”
Ndiyetu m’posadabwitsa kuti zilumbazi zakhala zimodzi mwa zilumba zotchuka kwambiri pokopa alendo padziko lonse lapansi! Chimene chimawonjezanso kukongola kwake ndi mikhalidwe yosiririka ya amuna ndi akazi amene amakhala komanso kugwira ntchito kumeneko. Pokhala anthu ake ameneŵa ali odzichepetsa ndi ochereza alendo komanso aufulu, malo ameneŵa ali apaderadera zedi.
Ambiri mwa anthu okhala pachilumbachi amadalira kusodza m’nyanja ya Aegean. Komanso, pali mtundu wina wa “usodzi” wofunika kwambiri umene ukubala zipatso zochuluka m’deralo. “Asodzi a anthu,” alaliki a uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, akuzungulira pazilumba za Aegean, kupanga ophunzira achikristu.—Mateyu 4:18, 19; Luka 5:10.
Pafupifupi zaka mazana 19 zapitazo, alaliki achikristu anakafika pazilumba za Aegean. M’chaka cha 56 C.E, mtumwi Paulo, pobwerera paulendo wake wachitatu waumishonale, anaima pazilumba za Lésvos, Kiyo, Samo, Ko ndi Rode. Pokhala mlaliki wokangalika nthaŵi zonse, Paulo ayenera kuti analalikira kwa ena okhala pa chilumbachi. (Machitidwe 20:14, 15, 24; 21:1, 2) Atatuluka m’ndende imene anakhala zaka ziŵiri ku Roma, mosakayikira anapita ku Krete ndi kuchita ntchito yachikristu kumeneko. Kumapeto kwa zaka za zana loyamba, mtumwi Yohane anali wandende pachilumba cha Patmo “chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 1:9) Kodi alaliki a uthenga wabwino m’nthaŵi zamakono akuchita zotani m’zilumbazi?
Ndawala Yopindulitsa Yolalikira
Kulalikira m’zilumba zimenezi n’kovuta. Kumafuna khama ndi kudzipereka, chifukwa zilumba zina ndi zotalikirana. Kwa ena umangokhala mwayi kuyenda panyanja kapena pandege komanso ena alibiretu mwayi umenewo, makamaka m’nyengo ya chisanu. Nyanja imakwiya, makamaka pamene meltemia—mphepo yakumpoto yamphamvu—iomba. Komanso, midzi ya pazilumba zambiri ndi yotalikirana ndiponso yovuta kufikako chifukwa misewu yambiri n’njafumbi, ndipo nthaŵi zambiri imakhala yosadutsika. Midzi ina ingafikiridwe pogwiritsa ntchito timabwato tating’ono.
Mwachitsanzo, titenge chilumba cha Icaria. Olalikira uthenga wabwino wa Ufumu 11 mumpingo waung’ono kumeneko sangathe kulalikira midzi yonse pachilumba chimenecho ndi tizilumba tina toyandikira. Chotero, abale ndi alongo ochokera ku Samo amabwera kudzathandiza kulalikira kwa anthu a ku Icaria, ngakhalenso kwa okhala pachilumba cha
Phournoi, Patmo ndi Lipsos. Posachedwapa, nthaŵi ya ndawala ya masiku aŵiri, Mboni zinagaŵira magazini 650, mabulosha 99 ndi mabuku 25 a nkhani za Baibulo! Mboni zinadabwa kukumana ndi anthu amene sanali kudziŵa kuti Yehova ndani, anthu amene anawapempha kuti asapitenso kwawo koma kuti akhale ndi kuwaphunzitsa zambiri kuchokera m’Baibulo. Mkazi wina anauza Mboni kuti: “Taonani tsopano mukupita. Koma ndili ndi mafunso ambiri okhudza Baibulo. Adzandithandiza ndani?” Mlongo wachikristu ameneyo analonjeza kuti adzapitiriza kucheza naye patelefoni, ndipo anayambitsa phunziro la Baibulo mwanjira imeneyi.Pamene woyang’anira woyendayenda anakacheza ku Icaria, anakonza kuti alalikire chilumba chonse mapeto a mlungu umodzi. Anapempha ofalitsa Ufumu okwana pafupifupi 30 a ku Samo kuti am’thandize. Abale alendowo analipira ndalama ku hotela zogonera masiku aŵiri komanso zobwerekera galimoto wamba ndi galimoto zina zamphamvu zotha kudutsa pamatope. Kunali chimvula champhamvu masiku aŵiri ndipo odziŵa za nyengo anati mapeto a mlungu umenewo sakhala bwino. Koma abalewo sanalole kuti nyengo iwalepheretse chifukwa chokumbukira mawu a Mlaliki 11:4: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.” M’kupita kwa nthaŵi, nyengo inakhalako bwino pang’ono, ndipo atalalikira chilumba chonsecho ndi uthenga wofunikawo, abalewo anabwerera kumudzi ali osangalala ndi okhutira.
Ofalitsa 16 amene amakhala pachilumba cha Andros anachita khama kuti alalikire chilumba chonsecho. Pamene abale aŵiri anakafika kumudzi wakutali, anafunitsitsa kulalikira kwa onse okhala kumeneko. Analankhula ndi athu panyumba zawo, m’misewu ndi m’minda. Komanso anakafika ku siteshoni yapolisi ndi kugawira mabuku kumeneko. Atatsimikizira kuti anali atalalikira aliyense m’mudziwo, anayamba kunyamuka. Pamene amachoka pamalo apakati, anaona wansembe wa Greek Orthodox akufika. Atazindikira kuti sanam’lalikire, anam’patsa chofalitsa chaching’ono, chimene analandira mwansangala. Tsopano anakhulupirira kuti palibenso amene watsala wosalalikidwa!
Gavdos (kapena Kauda)—kachilumba kakang’ono m’munsi mwa Krete kokhala ndi anthu 38—kamaganizidwa kukhala kumwera kwenikweni kwa Ulaya. (Machitidwe 27:16) Woyang’anira woyendayenda ndi mkazi wake, pamodzi ndi banja lina, anathera masiku atatu akulalikira kumeneku. Kuti asunge ndalama, ankagona m’matenti. Anthu onse okhala kumeneko anafikiridwa ndi uthenga wabwino, komanso abalewo anali osangalala chifukwa anthu ake analibe tsankhu. Anali asanamve kena kalikonse—kabwino kapena koipa—kokhudza Mboni za Yehova. Anthu onse, kuphatikiza wansembe, analandira mabuku 19 ndi mabulosha 13. Pamene Mbonizo zimabwerera ku Krete pabwato laling’ono, nyanja inayamba kuwinduka, zimenezi zinaika miyoyo yawo pangozi. Koma iwo anati: “Tinayamikira Yehova kuti tinafika kumudzi amoyo, ndiponso tinam’tamanda chifukwa chotilola kulemekeza dzina lake kumwera kwenikweni kwa Ulaya.”
Patmo ndi chilumba chimene mtumwi Yohane analemberako buku lomaliza la Baibulo la Chivumbulutso. Kufikira posachedwapa kwakhala kulibe Mboni za Yehova kuchilumbachi. Ndawala yolalikira pa chilumbachi inalinganizidwa bwino ndi abale ochokera ku Samo. Anadziŵa kuti mwina akatsutsidwa kwambiri chifukwa pa chilumbachi, tchalitchi cha Greek Orthodox ndicho champhamvu. Alongo aŵiri amene anali kulalikira uthenga wabwino kwa mkazi wina, anawaitanira m’nyumba mwake. Mwamuna wa mkaziyo analimbikira kufunsa alongowo kuti ndani anawauza kufika panyumba pawopo. Pamene anafotokoza kuti amayenda nyumba
ndi nyumba, anawafunsanso kuti: “Mukunena zoona kuti anzathu oyandikana nafe sanakuuzeni kufika pano?” Tsiku lina, mkazi wake amene anadziŵa Mboni za Yehova pamene anali ku Zaire, anafotokozera alongowo chomwe chinachitika tsiku loyamba lija m’maŵa. Anati: “Ndinali kupemphera kwa Yehova monga momwe ndimachitira masiku onse, kuti anditumizire Mboni ku chilumba chino. Koma mwamuna wanga anandiseka. Ndiye pamene tinakuonani pakhomo, ine ndi mwamuna wanga tinadabwa. N’chifukwa chake anafunsitsa kuti wakutumizani kunyumba yathu ndani.” Nthaŵi yomweyo anayamba phunziro la Baibulo ndi mkaziyu. Ankachitira phunzirolo patelefoni miyezi khumi, ngakhale kuti zinawadyera ndalama zambiri onse, mlongoyo komanso mayi wokondwererayo. Anabatizidwa ndipo tsopano ndi iye yekha amene ali Mboni pachilumba chimenecho, kumene mtumwi Yohane anali yekhayekha zaka 1,900 zapitazo.“Kusodza” M’madoko
Sitima zamaulendo okasangalala zimaima pa madoko osiyanasiyana a zilumba za Aegean chilimwe chilichonse, kubweretsa anthu ambiri odzachita tchuthi. Chotero Mboni za Yehova zili ndi mwayi waukulu wolalikira anthu amitundu yambiri ndi zinenero. Mipingo imasunga m’sitoko mabuku azinenero zambiri ofotokoza Baibulo, ndipo ofalitsa amagaŵira magazini zikwizikwi kwa alendo odzacheza. Sitima zina zimafika pamadoko amodzimodziwo mlungu uliwonse, zimene zimatheketsa abale kupanga maulendo obwereza ngakhalenso kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi ena ogwira ntchito m’sitimazo.
M’chilimwe cha 1996, mlongo amene ndi mlaliki wanthaŵi zonse ku Rode analalikira kwa mnyamata wina wa ku Jamaica amene amagwira ntchito m’sitima yamaulendo okasangalala imene imabwera kudokolo Lachisanu lililonse. Lachisanu mlungu wotsatira, mwamunayo anaitanidwa kuti akapezeke pamsonkhano wachigawo wochitikira pachilumbachi. Baibulo lachingelezi lili m’manja, mlongo mpainiyayo anathandiza mnyamatayu kuti amvetse mfundo zina za choonadi cha Baibulo zokambidwa pamsokhano umenewo. Mnyamata ameneyu anasangalala kwambiri ndi chikondi ndi ubwenzi umene Mboni zinasonyeza pamsonkhanowo. Kenako Lachisanu mlungu wotsatira, anaitanira apainiya aŵiri m’sitima. Apainiyawa anatenga mabuku achingelezi ndi achispanya. Mabukuwo anatha m’zikwama zawo lisanathe n’komwe ola limodzi! Mnyamata wa ku Jamaica ankaphunzira Baibulo Lachisanu mlungu uliwonse
mpaka chilimwe chitatha. Chilimwe chotsatira anabweranso, wokonzeka kupitiriza phunziro. Koma panthaŵiyi anasintha ntchito yake kuti apite patsogolo mwauzimu. Kenako anapitanso. Abale a ku Rode analitu achisangalalo pamene anamva kuti mnyamata amene uja anabatizidwa kuchiyambi kwa 1998!Kugwira “Nsomba” Zosamukasamuka
Nyanja ya Aegean imadziŵika chifukwa cha nsomba zochuluka zosamukasamuka, monga masadinya ndi swordfish, zomwe zimadutsa nyanjayi ndipo zimathera m’maukonde a asodzi aluso. Mofananamo, alengezi a Ufumu amapeza mitima yomvetsera mwa odzagwira ntchito amene anasamukira ku Greece kuchokera ku mayiko ambiri a Kum’mawa kwa Ulaya.
Rezi anali ndi zaka khumi pamene anaŵerenga koyamba zokhudza Yehova ndi zolinga zake m’masamba a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Nthaŵiyo anali ku Albania. Patapita zaka zitatu anasamuka ndi banja lonse kupita ku chilumba cha Rode. Tsiku lina, Rezi anapemphera kwa Yehova kuti am’thandize kupeza anthu ake kumudzi wake watsopano. Tsiku lotsatira abambo ake anabwera ndi magazini aja amene amawadziŵa, a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, zomwe zinam’sangalatsa Rezi kwambiri. Rezi anakumana ndi mlongo amene anagaŵira magazini kwa bambo ake, ndipo posapita nthaŵi anayamba kuphunzira buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Nthaŵi zina, ankapempha kuchita phunziro katatu tsiku limodzi! Patapita miyezi iŵiri anakhala wofalitsa wosabatizidwa, ndipo m’March 1998, anabatizidwa ali ndi zaka 14. Tsiku lomwelo anayamba upainiya wothandiza, ndipo patapita miyezi isanu ndi umodzi analembetsa kukhala mpainiya wokhazikika, kapena kuti mlaliki wanthaŵi zonse.
Mbale wapachilumba cha Ko ankachita phunziro ndi anthu ena a ku Russia. Atawafunsa ngati anali ndi mabwenzi amene angafune kuphunzira Baibulo, anam’tengera kwa banja la ku Armenia—Leonidas ndi mkazi wake Ophelia—kumudzi wokhala pamtunda wa makilomita 30. Abalewo sanadziŵe kuti akaona zodabwitsa. Banja la ku Armenia linatulutsa chikwama chodzaza ndi mabuku ofotokoza Baibulo achialameniya ndi achirasha osindikizidwa ndi Watch Tower Society! Anafotokoza kuti anaphunzirapo Baibulo ndi Mboni za Yehova kufikira pokhala ofalitsa osabatizidwa. Koma chifukwa cha kusokonezeka kwa zandale ndi mavuto azachuma, sakanachitira mwina kusiyapo kusamuka ku dziko lakwawo. Atangofika ku Ko, anayamba kuphunzira ndi amayi a Leonidas ndi mlongo wake, amene anali kale kumeneko. Mosayembekezeka, Mboniyo inakhala ndi maphunziro a Baibulo atatu atsopano—loyamba ndi Ophelia, lachiŵiri ndi Leonidas ndipo lachitatu ndi mayi ndi mlongo wake wa Leonidas. Zimenezi zinafuna kuti aziyenda panjinga yamoto mtunda wokwana makilomita 30 katatu pamlungu, kupita ndi kubwera. Leonidas ndi mkazi wake anabatizidwa pambuyo pake patapita miyezi yoŵerengeka. Abale ameneŵa okhala ndi mzimu wodzimana adalitsika kwambiri!
Yehova Amakulitsa
Madalitso a Yehova aonekera pakhama la anthu oposa 2,000 okangalika kulengeza Ufumu pazilumba za Aegean zimenezi. Tsopano kuli mipingo 44 ndi magulu 25 a Mboni za Yehova kumeneko. Mwa maguluŵa, 17 ndi oyankhula zinenero zakunja, chifukwa ndi chifuniro cha Yehova kuti “anthu onse [“amtundu uliwonse,” NW] apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Kuwonjezera apo, apainiya 13 apadera akuchita khama kufikira anthu ambiri m’magawo akutali amenewo.
Kwa zaka mazana ambiri, nyanja ya Aegean yakhala chimake cha chikhalidwe komanso msika wa malonda. M’zaka zaposachedwapa, nyanjayo yakhala malo okondeka kwa alendo zikwi mazana ambiri okaona malo. Koma kopambana zonse, monga “asodzi a anthu,” alengezi a Ufumu apeza anthu ambiri oona mtima pazilumba zimenezi ofunitsitsa kutamanda Yehova. Onse pamodzi, ayankha mwanjira yodabwitsa kwambiri chiitano chaulosi chakuti: “Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ake m’zisumbu.”—Yesaya 42:12.
[Mapu patsamba 22]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Nyanja ya Aegean
GREECE
Lésvos
Kiyo
Samo
Icaria
Fournoi
Patmo
Ko
Rode
Krete
TURKEY
[Chithunzi patsamba 23]
Chilumba cha Lésvos
[Chithunzi patsamba 24]
Chilumba cha Patmo
[Chithunzi patsamba 24]
Chilumba cha Krete