Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chirikizani Chiphunzitso Chaumulungu Molimbika

Chirikizani Chiphunzitso Chaumulungu Molimbika

Chirikizani Chiphunzitso Chaumulungu Molimbika

“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”​—MIYAMBO 3:5, 6.

1. Kusiyana ndi kale lonse, kodi chidziŵitso cha anthu n’chofalikira m’njira yotani lerolino?

PAKALI pano, kuli mitundu ngati 9,000 ya nyuzipepala zimene zimalembedwa tsiku lililonse padziko lonse lapansi. Chaka chilichonse kumatulutsidwa mabuku atsopano okwanira ngati 200,000 m’dziko la United States mokha. Malinga ndi ziŵerengero zina, pofika m’March 1998, panali malo a pa Intaneti oonetserapo zinthu okwanira 275 miliyoni. Chiŵerengero chimenechi akuti chikukula pamene malo enanso oterowo okwanira 20 miliyoni akuwonjezedwa pa Intaneti mwezi uliwonse. Kusiyana ndi kale lonse, anthu amatha kudziŵa zinthu pafupifupi pankhani ina iliyonse. Pamene kuli kwakuti zinthu zikatere pamakhala mapindu ake, kuchuluka kwa chidziŵitso kumeneku kwayambitsa mavuto ena.

2. Kodi kupeza chidziŵitso chochuluka zedi kungayambitse mavuto otani?

2 Anthu ena akhala ongofuna kupeza chidziŵitso chatsopano, ndipo nthaŵi zonse amangofuna kukhutiritsa chilakolako chosalamulirika chofuna kudziŵa zinthu zatsopano uku akunyalanyaza zinthu zofunika koposa. Ena amangodziŵa zinthu zochepa kwambiri pankhani kapena pachidziŵitso chocholoŵana kwambiri koma n’kumadziona ngati akatswiri. Modalira chidziŵitso chosakwaniracho, pankhani zazikulu kwambirii iwo angasankhe kuchita zimene zingaike iwowo kapena anthu ena m’mavuto adzaoneni. Ndipo nthaŵi zonse pamakhala ngozi yopeza chidziŵitso chonyenga kapena chosalondola kwenikweni. Kaŵirikaŵiri sipakhala njira yodalirika yodziŵira kuti chidziŵitso chochulukitsitsacho n’cholondola ndi choyenerera.

3. Kodi Baibulo lili ndi machenjezo otani okhudza kufunafuna nzeru za anthu?

3 Kuyambira kalekale, chidwi chakhala msampha wa anthu. Kuopsa kwa kuwononga nthaŵi yochuluka pa kufunafuna chidziŵitso chopanda pake mwinanso ngakhale chovulazitsa kunali kodziŵika kalelo m’masiku a Mfumu Solomo. Iye anati: “Tachenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.” (Mlaliki 12:12) Patapita zaka mazana ambiri mtumwi Paulo analembera Timoteo kuti: “Dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama; chimene ena pochivomereza adalakwa ndi kutaya chikhulupiriro.” (1 Timoteo 6:20, 21) Inde, Akristu lerolino ayenera kupeŵa kutchera khutu ku malingaliro ovulazitsa.

4. Kodi njira imodzi imene tingasonyezere chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi ziphunzitso zake ndi iti?

4 Anthu a Yehova amachitanso bwino pomvetsera mawu a pa Miyambo 3:5, 6 akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” Kukhulupirira Yehova kumaphatikizapo kukana lingaliro lililonse losemphana ndi Mawu a Mulungu, kaya likhale lochokera mumtima mwathu kapena lochokera kwa munthu mnzathu. Kuti titeteze uzimu wathu, n’kofunika kwambiri kuphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikira kuti tizidziŵa chidziŵitso choopsa ndi kuchipewa. (Ahebri 5:14) Tiyeni tikambirane za magwero ena a chidziŵitso choterocho.

Dziko Lolamulidwa ndi Satana

5. Kodi gwero limodzi la malingaliro ovulazitsa ndi liti, ndipo ndani akuwachititsa?

5 Dziko losadziŵa Mulunguli ndi gwero lalikulu kwambiri la malingaliro ovulaza. (1 Akorinto 3:19) Yesu Kristu anapemphera kwa Mulungu ponena za ophunzira ake kuti: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.” (Yohane 17:15) Pempho la Yesu lakuti ophunzira ake atetezedwe kwa “woipayo” linasonyeza kuti Satana alidi ndi chisonkhezero m’dziko lapansi. Ngakhale ndife Akristu sizitanthauzabe kuti mosakayikira ndife otetezedwa ku zisonkhezero zoipa za dzikoli. Yohane analemba kuti: “Tidziŵa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Makamaka m’chigawo chomalizira chino cha masiku otsiriza, tiyenera kuyembekezera kuti Satana ndi ziŵanda zake adzadzaza dzikoli ndi nkhani zovulaza.

6. Kodi zosangalatsa zamitundumitundu zingam’pangitse motani munthu kusazindikira khalidwe loipa?

6 Tiyeneranso kuyembekezera kuti zina mwa nkhani zovulaza zimenezi zidzaoneka ngati zabwinobwino. (2 Akorinto 11:14) Mwachitsanzo, tiyeni titenge zosangalatsa zamitundumitundu kuphatikizapo nkhani za pa TV, mafilimu, nyimbo, ndi mabuku. Ambiri amavomereza kuti kaŵirikaŵiri, zosangalatsa zina ndi zina zimalimbikitsa khalidwe loipa, monga chiwerewere, chiwawa, ndi kumwa mankhwala osokoneza bongo. Anthu akaona kwa nthaŵi yoyamba zosangalatsa zosonyeza khalidwe loipitsitsa lomwe sanaonepo, iwo amadabwa. Koma kuziona mobwerezabwereza kumapangitsa munthu kusaonanso kuipa kwa zosangalatsazo. Tisayerekeze n’komwe kuona zosangalatsa zomwe zimalimbikitsa malingaliro oopsa ngati zabwinobwino kapena zosavulazitsa.​—Salmo 119:37.

7. Kodi ndi nzeru ziti za anthu zimene zingafooketse chidaliro chathu pa Baibulo?

7 Lingaliraninso za gwero lina la nkhani zomwe zingakhale zowononga kwambiri​—malingaliro ambirimbiri ofalitsidwa ndi asayansi ndi akatswiri ena amene amatsutsa ulamuliro wa Baibulo. (Yerekezani ndi Yakobo 3:15.) Kaŵirikaŵiri nkhani zimenezi zimalembedwa m’magazini ndi m’mabuku otchuka, ndipo zingafooketse chidaliro cha munthu pa Baibulo. Anthu ena amasangalala akamachititsa Mawu a Mulungu kukhala opanda mphamvu ndi mfundo zosaŵerengeka zongoyerekeza. Ngozi yofananayi inaliponso m’masiku a atumwi, monga momwe tikuonera bwino lomwe m’mawu a mtumwi Paulo akuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”​—Akolose 2:8.

Adani a Choonadi

8, 9. Kodi mpatuko ukuonekera motani lerolino?

8 Anthu ampatuko angaikenso uzimu wathu pangozi. Mtumwi Paulo ananeneratu kuti padzauka mpatuko pakati pa amene akudzitcha kuti Akristu. (Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:3) Pa kukwaniritsidwa kwa mawu akewo, atumwi onse atamwalira, mpatuko waukulu unabala Gawo la Matchalitchi Achikristu. Lerolino, palibe mpatuko waukulu pakati pa anthu a Mulungu. Komabe, anthu angapo achoka pakati pathu, ndipo ena akulimbikira kuneneza Mboni za Yehova mwa kufalitsa mabodza ndi nkhani zopotoka. Enanso angapo amagwirizana ndi magulu ena amene akupingapinga kulambira koyera. Pochita zimenezi, iwo akugwirizana ndi wampatuko woyambirirayo, Satana.

9 Ampatuko ena akugwiritsa ntchito kwambiri njira zosiyanasiyana zotumizira mauthenga kwa anthu ambiri, kuphatikizapo makompyuta, pofalitsa nkhani zonama zokhudza Mboni za Yehova. Chotero, pamene anthu oona mtima afufuza kuti adziŵe zikhulupiriro zathu, angathe kupeza nkhani zonama zimenezi za ampatuko. Ngakhale Mboni zina mosadziŵa zamvetsera nkhani zovulaza zimenezi. Ndiponso, ampatuko nthaŵi zina amayankhulapo pamapulogalamu a pawailesi yakanema ndi pawailesi. Kodi njira yanzeru yoti titsatire pamenepa ndi iti?

10. Kodi mwanzeru tiyenera kuchitanji ndi nkhani za ampatuko?

10 Mtumwi Yohane analangiza Akristu kuti asalandire ampatuko m’nyumba zawo. Analemba kuti: “Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musam’landire iye kunyumba, ndipo musam’lankhule. Pakuti iye wakum’lankhula ayanjana nazo ntchito zake zoipa.” (2 Yohane 10, 11) Kupeŵa kuyanjana kwa mtundu wina uliwonse ndi otsutsa ameneŵa kudzatiteteza kuti asaipitse malingaliro athu. Kumvetsera ziphunzitso za ampatuko kudzera m’njira zosiyanasiyana zotumizira mauthenga n’koopsa monga momwe kulandira wampatukoyo m’nyumba zathu kulili. Tisalole chidwi kutikokera m’njira yodzetsa tsoka imeneyo!​—Miyambo 22:3.

Mumpingo

11, 12. (a) Kodi gwero la malingaliro ovulaza linali liti mumpingo wa m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi Akristu ena analephera motani kuchirikiza ziphunzitso zaumulungu molimbika?

11 Lingaliraninso malo ena amene angakhale gwero la malingaliro owononga. Pamene kuli kwakuti alibe cholinga chophunzitsa chinyengo, Mkristu wodzipatulira angayambe chizoloŵezi cholankhula mopanda nzeru. (Miyambo 12:18) Popeza ndife anthu opanda ungwiro, tonsefe lilime lathu limatilakwitsa nthaŵi zina. (Miyambo 10:19; Yakobo 3:8) Zikuoneka kuti m’tsiku la mtumwi Paulo, panali ena mumpingo amene sanalamulire lilime lawo ndipo ankatsutsana pa zinthu zopanda pake zokhudza mawu. (1 Timoteo 2:8) Panalinso ena amene ankaumirira kwambiri pa malingaliro a iwo okha moti anatsutsanso ulamuliro wa Paulo. (2 Akorinto 10:10-12) Mzimu umenewo unawombanitsa abale popanda chifukwa.

12 Nthaŵi zina kusagwirizana kumeneku kunkakhala “makani opanda pake,” owonongetsa mtendere wa mpingo. (1 Timoteo 6:5; Agalatiya 5:15) Ponena za amene ankayambitsa mikangano imeneyo, Paulo analemba kuti: “Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nawo mawu a moyowo a Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo: iyeyo watukumuka, wosadziŵa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mawu, kumene zichokerako njiru, ndewu, zamwano, mayerekezo oipa.”​—1 Timoteo 6:3, 4.

13. Kodi Akristu ochuluka m’zaka za zana loyamba anachita motani?

13 Mwamwayi, Akristu ochuluka m’nthaŵi za atumwi anali okhulupirika ndipo analunjikabe maganizo awo pa ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Iwo anali otanganidwa ndi kusamalira “ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo,” ndipo anadzisungira ‘osachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi,’ osataya nthaŵi yawo pamikangano yosapindulitsa ya mawu. (Yakobo 1:27) Iwo anapewa “mayanjano oipa” ngakhale mumpingo wachikristu momwe kuti ateteze uzimu wawo.​—1 Akorinto 15:33; 2 Timoteo 2:20, 21.

14. Ngati sitisamala, kodi kucheza wamba kungayambitse motani mikangano yoipa?

14 Mofananamo, zochitika zomwe zatchulidwa m’ndime 11 sizionekaoneka m’mipingo ya Mboni za Yehova lerolino. Komabe, tichita bwino kuzindikira kuti mikangano yopanda pake ngati imeneyo ingabuke nthaŵi zina. Zoonadi, palibe vuto ndi kukambirana nkhani za m’Baibulo kapena kuganizira zinthu zina za m’dziko latsopano lolonjezedwalo zimene sizinavumbulidwebe. Ndiponso palibe vuto ndi kucheza pankhani za mmene mumaonera zinthu zina zaumwini, monga kavalidwe ndi kudzikongoletsa kapena zosangalatsa zomwe mumakonda. Komabe, ngati tingoumirira malingaliro athu ndi kuipidwa pamene ena sakuvomerezana nafe, mpingo ungagaŵanike pankhani zing’onong’ono. Zomwe zinayamba ngati nkhani wamba zingayambitse mavuto aakulu.

Kuteteza Zomwe Tasungitsidwa

15. Kodi “maphunziro a ziŵanda” angativulaze motani mwauzimu, nanga Malemba akupereka uphungu wotani?

15 Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda.” (1 Timoteo 4:1) Inde, malingaliro ovulaza ndi oopsadi. Ndiye chifukwa chaketu Paulo anachonderera bwenzi lake lokondedwalo Timoteo kuti: “Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama; chimene ena pochivomereza adalakwa ndi kutaya chikhulupiriro.”​—1 Timoteo 6:20, 21.

16, 17. Kodi Mulungu watisungitsa chiyani, ndipo tiyenera kuziteteza motani?

16 Kodi ifeyo lerolino tingapindule motani ndi mawu achikondi ochenjeza ameneŵa? Timoteo anasungitsidwa chinachake​—chinthu chofunika kwambiri choti achisamalire ndi kuchiteteza. Kodi chinali chiyani chimenecho? Paulo anafotokoza kuti: “Gwira chitsanzo cha mawu a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Kristu Yesu. Chosungitsa chokomacho udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.” (2 Timoteo 1:13, 14) Inde, zomwe Timoteo anasungitsidwa zinaphatikizapo “mawu a moyo,” “chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo.” (1 Timoteo 6:3) Mogwirizana ndi mawu ameneŵa, lerolino Akristu n’ngotsimikiza mtima kuteteza chikhulupiriro chawo ndi choonadi chonse chimene asungitsidwa.

17 Kuteteza chosungitsidwa chimenecho kumaphatikizapo kukulitsa zinthu monga chizolowezi chabwino cha phunziro la Baibulo ndi kulimbikira m’pemphero, pamene ‘tikuchitira onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10; Aroma 12:11-17) Paulo analangizanso kuti: ‘Utsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.’ (1 Timoteo 6:11, 12) Popeza Paulo anagwiritsa ntchito mawuwo akuti “limba nayo nkhondo yabwino,” ndi “gwira moyo wosatha” zikusonyezadi kuti mwachangu ndiponso motsimikiza mtima tiyenera kukana zinthu zovulaza mwauzimu.

Kufunika kwa Kuzindikira

18. Kodi tingasonyeze motani kusamala kwachikristu pa momwe timaonera chidziŵitso chadziko?

18 Inde, polimba nayo nkhondo yabwino yachikhulupiriro, kuzindikira n’kofunikira. (Miyambo 2:11; Afilipi 1:9) Mwachitsanzo, sikungakhale kwanzeru kukayikira chidziŵitso chonse chakudziko. (Afilipi 4:5; Yakobo 3:17) Si malingaliro onse a anthu amene amatsutsana ndi Mawu a Mulungu. Yesu anatchulapo za kufunikira koti anthu odwala adzikaonana ndi dokotola​—imene ili ntchito yakudziko. (Luka 5:31) Ngakhale kuti m’tsiku la Yesu zachipatala sizinali zotsogola monga masiku ano, iye anasonyezabe kuti thandizo la dokotala n’laphindube. Akristu lerolino amasonyeza kusamala pankhani ya chidziŵitso chakudziko, koma amakana kumvetsera chilichonse chimene chingawavulaze mwauzimu.

19, 20. (a) Kodi akulu amasonyeza motani kuzindikira pamene akuthandiza awo amene amayankhula mopanda nzeru? (b) Kodi mpingo umatani ndi anthu amene amalimbikira kuchirikiza ziphunzitso zonama?

19 Akulu nawonso amafunikira kuzindikira pamene apemphedwa kuthandiza awo amene amayankhula mopanda nzeru. (2 Timoteo 2:7) Nthaŵi zina, ena mumpingo angakoledwe m’mikangano yankhani zing’onong’ono ndiponso zopanda maziko. Pofuna kuteteza umodzi wa mpingo, akulu ayenera kusamalira mavuto ameneŵa mwamsanga. Panthaŵi imodzimodziyo, iwo amapeŵa kuona ngati kuti abale awo ali ndi zolinga zoipa ndipo sathamangira kuwaona ngati ampatuko.

20 Paulo analongosola mzimu umene iwo ayenera kukhala nawo popereka thandizo. Iye anati: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso.” (Agalatiya 6:1) Ponena kwenikweni za Akristu amene akulimbana ndi zikayiko, Yuda analemba kuti: “Ena osinkhasinkha muwachitire chifundo, koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto.” (Yuda 22, 23) Zoonadi, ngati pambuyo poti munthu walangizidwa mobwerezabwereza iye alimbikirabe kuchirikiza ziphunzitso zonama, akulu ayenera kuchitapo kanthu kuti ateteze mpingo.​—1 Timoteo 1:20; Tito 3:10, 11.

Kudzaza Maganizo Athu ndi Zinthu Zotamandika

21, 22. Kodi n’chiyani chimene tiyenera kusankha bwino kwambiri, ndipo kodi tiyenera kudzaza maganizo athu ndi chiyani?

21 Mpingo wachikristu umapeŵa mawu ovulaza amene ‘amanyeka ngati chilonda.’ (2 Timoteo 2:16, 17; Tito 3:9) Zimenezi zimatere kaya mawu amenewo akhale “chidziŵitso” chosokeretsa chakudziko, mabodza a ampatuko, kapena nkhani zopanda pake za mumpingo. Pamene kuli kwakuti chidwi chabwino chofuna kuphunzira zinthu zatsopano chingakhale chopindulitsa, chidwi chosalamulirika chingatipangitse kumvetsera malingaliro ovulaza. Sindife mbuli ponena za machenjera a Satana. (2 Akorinto 2:11) Tikudziŵa kuti iye akuyesetsa kutisokoneza kuti tifooke pautumiki wathu kwa Mulungu.

22 Monga atumiki abwino, tiyeni tichilikize chiphunzitso chaumulungu molimbika. (1 Timoteo 4:6) Tiyeni tigwiritse ntchito nthaŵi yathu mwanzeru mwa kusankha bwino chidziŵitso chimene tikufuna kukhala nacho. Chotero sitidzadodometsedwa wambawamba ndi nkhani zabodza zouziridwa ndi Satana. Inde, nthaŵi zonse tiyeni tiziganizira “zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china.” Ngati tidzaza maganizo athu ndi malingaliro athu ndi zinthu zoterozo, Mulungu wamtendere adzakhala nafe.​—Afilipi 4:8, 9.

Kodi Taphunziranji?

• Kodi nzeru zakudziko zingaike motani uzimu wathu pachiswe?

• Kodi tingachitenji kuti tidziteteze ku nkhani zovulaza za ampatuko?

• Kodi ndi mayankhulidwe otani amene tiyenera kupeŵa mumpingo?

• Kodi kusamala kwachikristu kumasonyezedwa motani pochita ndi kuchulukitsitsa kwa chidziŵitso kwamakono?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Magazini ndi mabuku ambiri otchuka amasemphana ndi mfundo zathu zachikristu

[Chithunzi patsamba 10]

Akristu angafotokozerane malingaliro awo popanda kukakamiza wina kuti awatsatire