Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Imvani Chimene Mzimu Unena

Imvani Chimene Mzimu Unena

Imvani Chimene Mzimu Unena

“Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.”​—YESAYA 30:21.

1, 2. Kodi Yehova wayankhula motani ndi anthu m’mbiri yonseyi?

PACHILUMBA cha Puerto Rico pali chimbale champhamvu kwambiri padziko lonse lapansi cholandirira mauthenga akuthambo. Kwa zaka zambiri ndithu, asayansi akhala akuyembekeza kulandira mauthenga ochokera kwa zamoyo zina zakuthambo, pogwiritsa ntchito chipangizo chachikulu chimenechi. Koma sanalandirepo mauthenga ngati amenewo. Zodabwitsa n’zakuti pali mauthenga ochokera kunja kwa dziko la anthu ndipo aliyense wa ife angawalandire panthaŵi ina iliyonse​—popanda makina ambambande. Mauthengawa amachokera ku Gwero lina lapamwamba kwambiri loposa zolengedwa zakuthambo zilizonse zomwe anthu amaganiza kuti ziliko. Kodi Gwero la mauthenga amenewo ndani, ndipo ndani amawalandira? Kodi mauthengawo amati chiyani?

2 Baibulo lili ndi nkhani zingapo zosimba za nthaŵi pamene mauthenga ochokera kwa Mulungu anamveka m’makutu a anthu. Nthaŵi zina mauthenga ameneŵa anali kuperekedwa ndi zolengedwa zauzimu zotumikira monga amithenga a Mulungu. (Genesis 22:11, 15; Zekariya 4:4, 5; Luka 1:26-28) Katatu konse, mawu a Yehova weniweniyo anamveka. (Mateyu 3:17; 17:5; Yohane 12:28, 29) Mulungu anayankhulanso kudzera mwa anthu omwe anali aneneri, ochuluka mwa ameneŵa analemba zimene anawauzira kuti anene. Lerolino, tili ndi Baibulo, limene lili ndi nkhani zolembedwa zokhudza ambiri mwa mauthenga ameneŵa, limodzinso ndi ziphunzitso za Yesu ndi ophunzira ake. (Ahebri 1:1, 2) Yehova wakhaladi akupereka mauthenga kwa zolengedwa zake zaumunthu.

3. Kodi cholinga cha mauthenga a Mulungu n’chiyani, ndipo ifeyo tiyenera kuchitanji?

3 Mauthenga onse ouziridwa ndi Mulunguŵa safotokoza zambiri ponena za thambo lenilenili. Kwenikweni, amanena za nkhani zofunika koposa, zimene zimakhudza moyo wathu tsopano ndi m’tsogolo. (Salmo 19:7-11; 1 Timoteo 4:8) Mwa mauthenga amenewo, Yehova amatiuza za chifuniro chake ndi kutipatsa chitsogozo chake. Uku n’kukwaniritsidwa kwina kwa mawu a mneneri Yesaya akuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:21) Yehova satikakamiza kumvetsera “mawu” ake. Zili ndi ife kutsatira chitsogozo cha Mulungu ndi kuyenda m’njira yake. Pachifukwa chimenecho Malemba amatilangiza kumvetsera mauthenga ochokera kwa Yehova. M’buku la Chivumbulutso, chilimbikitso chakuti ‘timve chimene mzimu unena’ chilimo nthaŵi zisanu ndi ziŵiri.​—Chivumbulutso 2:7, 11, 17, 29; 3:6, 13, 22.

4. Kodi m’tsiku lathu lino tingayembekezere Mulungu kutiyankhula mwachindunji ali kumwamba?

4 Lerolino, Yehova sayankhula nafe mwachindunji ali kumwamba. Ngakhale m’nthaŵi za m’Baibulo, mauthenga odza mozizwitsa chotero anali akamodzikamodzi, mwinanso operekedwa kamodzi pazaka mazana ambiri. M’mbiri yonseyi, kaŵirikaŵiri Yehova wakhala akuyankhula ndi anthu ake m’njira zina. Ndi mmene zilili lerolino. Tiyeni tikambirane njira zitatu mmene Yehova amatiyankhulira lerolino.

“Lemba Lililonse Adaliuzira”

5. Kodi chiŵiya chachikulu cha Yehova choperekera mauthenga lerolino n’chiyani, ndipo tingapindule nacho motani?

5 Chiŵiya chachikulu chimene Mulungu amagwiritsa ntchito poyankhula ndi anthu ndicho Baibulo. Linauziridwa ndi Mulungu, ndipo mawu ake onse angatipindulitse. (2 Timoteo 3:16) Baibulo lili ndi zitsanzo zambirimbiri za anthu amene anagwiritsa ntchito ufulu wawo wa kusankha kumvera mawu a Yehova kapena ayi. Zitsanzo zimenezo zimatikumbutsa chifukwa chake kumvera zimene mzimu wa Mulungu unena kuli kofunika. (1 Akorinto 10:11) Baibulo lilinso ndi nzeru yeniyeni, yotilangiza tikafunikira kusankha zochita pankhani zina m’moyo. Zili ngati kuti Mulungu ali kumbuyo kwathu, kutiyankhulira m’makutu kuti: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.”

6. N’chifukwa chiyani Baibulo limaposa zolembedwa zina zonse?

6 Kuti timve zimene mzimu unena kudzera m’Baibulo, tiyenera kuliŵerenga nthaŵi zonse. Baibulo si buku wamba longolembedwa bwino ndi lotchuka, limodzi mwa enanso ambiri amene amapezeka lerolino. Baibulo linauziridwa ndi mzimu ndipo lili ndi malingaliro a Mulungu. Ahebri 4:12 amati: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” Pamene tiŵerenga Baibulo, mawu ake amapyoza kuloŵa m’katikati mwa malingaliro athu ndi zolinga zathu ngati lupanga, kuvumbula mmene moyo wathu umatsatirira chifuniro cha Mulungu.

7. N’chifukwa chiyani kuŵerenga Baibulo kuli kofunika, ndipo tikulimbikitsidwa kuliŵerenga kangati?

7 “Zolingirira ndi zitsimikizo za mtima” zingasinthe malinga ndi kupita kwa nthaŵi ndiponso pamene tikukhudzidwa ndi zokumana nazo zathu m’moyo​—zosangalatsa ndi zovuta zomwe. Ngati sitiphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, zolingalira zathu, kaonedwe kathu ka zinthu, ndi mtima wathu sizidzakhalanso mogwirizana ndi mfundo zachikhalidwe zaumulungu. Ndiye chifukwa chake Baibulo limatilangiza kuti: ‘Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha.’ (2 Akorinto 13:5) Kuti tipitirizebe kumva zimene mzimu unena, tiyenera kulabadira uphungu wonena kuti tiziŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku.​—Salmo 1:2.

8. Kodi ndi mawu a mtumwi Paulo ati amene amatithandiza kudzipenda tokha pankhani ya kuŵerenga Baibulo?

8 Nayi mfundo yofunika yomwe oŵerenga Baibulo ayenera kukumbukira: Khalani ndi nthaŵi yokwanira yoti musinkhesinkhe zimene mwaŵerenga! Pofuna kutsatira uphungu wonena kuti tiziŵerenga Baibulo masiku onse, sitingafune kungoŵerenga machaputala angapo mofulumira popanda kumvetsetsa zimene tikuŵerengazo. Pamenedi kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse n’kofunika, sitiyenera kutero kungoti titsatire ndandanda; tiyenera kukhala ndi chikhumbo chochokera pansi pa mtima chofuna kuphunzira za Yehova ndi zifuno zake. Chotero, tingagwiritse ntchito mawu aŵa a mtumwi Paulo podzipenda. Polembera Akristu anzake, iye anati: “Ndipinda mawondo anga kwa Atate, . . . kuti Kristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m’mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m’chikondi, mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama n’chiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Kristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.”​—Aefeso 3:14, 16-19.

9. Kodi tingakhale motani ndi chikhumbo chofuna kuphunzira kwa Yehova ndipo tingachikulitse motani?

9 Zoonadi, enafe mwachibadwa sitikonda zoŵerengaŵerenga, pamene ena n’ngakhama pakuŵerenga. Komabe, mosasamala kanthu kuti ndife otani tingakhale ndi chikhumbo cha kuphunzira kwa Yehova ndi kuchikulitsa. Mtumwi Petro analongosola kuti tiyenera kulakalaka kuphunzira Baibulo, ndipo anasonyeza kuti munthu angadziyambitse kukhala ndi chilakolako chimenecho. Analemba kuti: “Monga makanda obadwa chatsopano, khalani ndi chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu, kuti kupyolera mwa iwo mukafikire chipulumutso.” (1 Petro 2:2, NW) Kudzilanga n’kofunika ngati tikufuna ‘kukhala ndi chilakolako’ cha phunziro la Baibulo. Monga momwe tingayambire kukonda chakudya chatsopano titachilaŵa nthaŵi zingapo, mtima wathu ungasinthe n’kukhala wofunitsitsa kuŵerenga ndi kuphunzira ngati tidzilanga kuti titsatire ndondomeko ya nthaŵi zonse.

“Zakudya Panthaŵi Yake”

10. Kodi ndani amapanga gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo kodi Yehova akuwagwiritsa ntchito motani lerolino?

10 Njira inanso imene Yehova amagwiritsa ntchito poyankhula nafe lerolino inatchulidwa ndi Yesu pa Mateyu 24:45-47. Palembalo ananenapo za mpingo wachikristu wodzozedwa ndi mzimu, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” amene wasankhidwa kupereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.” Munthu aliyense m’gulu limeneli ndi wa ‘m’banja’ la Yesu. Ameneŵa, limodzinso ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” amalandira chilimbikitso ndi chitsogozo. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Chochuluka mwa chakudya cha panthaŵi yake chimenechi chimadza ngati zofalitsa zosindikizidwa, monga Nsanja ya Olonda, Galamukani!, ndi zofalitsa zina. Chakudya chinanso chimaperekedwa monga nkhani ndi zitsanzo za pamisonkhano yachigawo, yadera, yapadera ndi pamisonkhano yampingo.

11. Kodi timasonyeza motani kuti tikumvera zimene mzimu unena kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

11 Chidziŵitso choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” chimakonzedwa kuti chilimbitse chikhulupiriro chathu ndi kuzoloŵeretsa mphamvu zathu za kuzindikira. (Ahebri 5:14) Uphungu umenewu ungakhale wosakhudza chochitika chenicheni kuti aliyense augwiritse ntchito payekha. Nthaŵi ndi nthaŵi, timalandiranso uphungu wokhudza mbali zakutizakuti za khalidwe lathu. Kodi tiyenera kuuona motani ngati tikumvetseradi zimene mzimu unena kudzera mwa gulu la kapolo? Mtumwi Paulo anayankha kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere.” (Ahebri 13:17) N’zoona kuti atsogoleri onsewo ndi anthu opanda ungwiro. Ngakhale zili choncho, Yehova amasangalala kugwiritsa ntchito atumiki ake aumunthu, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro, kuti atitsogolere m’nthaŵi zino zachimaliziro.

Kutsogozedwa ndi Chikumbumtima Chathu

12, 13. (a) Kodi Yehova watipatsanso chiyani chotitsogolera? (b) Kodi chikumbumtima chingapangitse ngakhale anthu osadziŵa Mawu a Mulungu molondola kuchita zinthu zabwino zotani?

12 Yehova watipatsa chinthu chinanso chotitsogolera​—chikumbumtima chathu. Analenga munthu ndi nzeru yamumtima yom’zindikiritsa chabwino ndi choipa. N’chibadwa chathu chimenecho. M’kalata imene analembera Aroma, mtumwi Paulo analongosola kuti: “Pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.”​—Aroma 2:14, 15.

13 M’malingaliro awo ndi m’zochita zawo, anthu ambiri osam’dziŵa bwino Yehova amatha kutsatira mfundo zina za Mulungu zachikhalidwe zokhudza chabwino ndi choipa. Zili ngati kuti amamva liwu lam’munsi kwambiri mumtima mwawo lowatsogolera m’njira yoyenera. Ngati zimatere ndi anthu osadziŵa Mawu a Mulungu molondola, bwanji kwa Akristu oona? Liwu lamumtima limenelo liyenera kuyankhulatu kwambiri! Ndithudi, chikumbumtima chachikristu chophunzitsidwa Mawu a Mulungu molondola komanso chogwira ntchito mogwirizana ndi mzimu woyera wa Yehova chingatitsogolere modalirika kwabasi.​—Aroma 9:1.

14. Kodi chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo chingatithandize motani kutsatira chitsogozo cha mzimu wa Yehova?

14 Chikumbumtima chabwino, chophunzitsidwa Baibulo, chingatikumbutse njira imene mzimu ukufuna kuti tiyendemo. Pangakhale nthaŵi pamene Malemba kapena zofalitsa zolongosola Baibulo sizikutchula mkhalidwe weniweniwo umene tilimo. Ngakhale ndi tero, chikumbumtima chathu chingatichenjeze kuti tisayende m’njira yomwe ingativulaze. Zikatero, kunyalanyaza mawu a chikumbumtima chathu kungakhale, kwenikweni, kunyalanyaza zimene mzimu wa Yehova ukunena. Komano, mwa kuphunzira kudalira chikumbumtima chathu chophunzitsidwa bwino chachikristu, tingasankhe bwino ngakhale patakhala kuti palibe chitsogozo chenicheni cholembedwa. Komabe, m’pofunika kukumbukira kuti ngati palibe mfundo yachikhalidwe, langizo, kapena lamulo loperekedwa ndi Mulungu, kukakamiza Akristu anzathu kuti atsatire zofuna za chikumbumtima chathu pankhani zaumwini n’kulakwa.​—Aroma 14:1-4; Agalatiya 6:5.

15, 16. Kodi n’chiyani chingapangitse chikumbumtima chathu kuphonyaphonya, ndipo tingachitenji kuti tipeŵe zimenezo?

15 Chikumbumtima choyera, chophunzitsidwa Baibulo ndi mphatso yabwino yochokera kwa Mulungu. (Yakobo 1:17) Koma tiyenera kuteteza mphatso imeneyi ku zisonkhezero zoipa ngati tikufuna kuti izigwira ntchito bwino monga chiŵiya chotisonyeza khalidwe labwino. Kutsatira chikhalidwe, miyambo, ndi zizolowezi zakwathu zotsutsana ndi miyezo ya Mulungu kungapangitse chikumbumtima chathu kuphonyaphonya ndi kulephera kutisonyeza njira yoyenera. Tingalephere kugamula bwino pankhani zina ndipo tingadzinyengenso n’kuona khalidwe loipa ngati labwino.​—Yerekezani ndi Yohane 16:2.

16 Ngati tipitiriza kunyalanyaza machenjezo a chikumbumtima chathu, mawu ake adzayamba kufooka mpaka tidzakhala opanda khalidwe kapena osazindikira khalidwe labwino. Wamasalimo ankanena anthu oterowo pamene anati: “Mtima wawo unona [“sumva kalikonse,” NW] ngati mafuta.” (Salmo 119:70) Ena amene amanyalanyaza chikumbumtima chawo amasiya kuganiza bwino. Sakutsogozedwanso ndi mfundo za Mulungu zachikhalidwe ndipo amalephera kusankha bwino zochita. Kuti tipeŵe mkhalidwe umenewu, tiyenera kumvera mwamsanga chitsogozo cha chikumbumtima chathu chachikristu ngakhale ngati nkhani zakezo zikuoneka kukhala zazing’ono.​—Luka 16:10.

Achimwemwe ndi Amene Amamvetsera ndi Kulabadira

17. Pamene timvetsera ‘mawu kumbuyo kwathu’ ndi kulabadira chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo, kodi tidzadalitsidwa motani?

17 Pamene tizoloŵera kumvetsera ‘mawu kumbuyo kwathu’​—monga momwe aperekedwera kudzera mwa Malemba ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru​—ndiponso pamene tilabadira zikumbutso za chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo, Yehova adzatidalitsa ndi mzimu wake. Mzimu woyera, kenako, udzakulitsa nzeru zathu zolandira ndi kumvetsa zimene Yehova akutiuza.

18, 19. Kodi chitsogozo cha Yehova chingatipindulitse motani muutumiki ndi m’moyo wathu womwe?

18 Mzimu wa Yehova udzatilimbitsanso kupirira mikhalidwe yovuta mwanzeru ndi molimba mtima. Monga momwe zinalili ndi atumwi, mzimu wa Mulungu ungawonjeze mphamvu ya malingaliro athu ndi kutithandiza nthaŵi zonse kuchita zinthu ndi kuyankhula mogwirizana ndi mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo. (Mateyu 10:18-20; Yohane 14:26; Machitidwe 4:5-8, 13, 31; 15:28) Mzimu wa Yehova limodzi ndi kuyesayesa kwathu zidzatipatsa chipambano pamene tisankha zochita zikuluzikulu m’moyo, kutilimbitsa mtima kuti tikwaniritsedi zochita zimenezo. Mwachitsanzo, mungafune kusintha moyo wanu kuti mukhale ndi nthaŵi yochuluka yochita zinthu zauzimu. Kapena mungafunikire kusankha zochita pankhani zikuluzikulu zosintha moyo, monga kusankha wokwatirana naye, kupenda ntchito imene mwapemphedwa kuloŵa, kapena kugula nyumba. M’malo molola mtima wathu waumunthuwu kutisonkhezera kwambiri pazosankha zathu, tiyenera kumvera zimene mzimu unena ndipo titsatire chitsogozo chake.

19 Timathokozadi zikumbutso ndi uphungu wachikondi umene timalandira kwa Akristu anzathu, kuphatikizapo akulu. Komabe, sitiyenera kudikira nthaŵi zonse kuti ena achite kutiuza. Ngati tikudziŵa njira yabwino yoti tiitsatire ndiponso mbali zimene tiyenera kuwongolera m’maganizo athu ndi khalidwe lathu kuti tikondweretse Mulungu, tiyeni tichitepo kanthu. Yesu anati: “Ngati mudziŵa izi, odala inu ngati muzichita.”​—Yohane 13:17.

20. Kodi awo amene akumvetsera ‘mawu kumbuyo kwawo’ akulandira dalitso lotani?

20 Mwachionekere, kuti Akristu adziŵe kukondweretsa Mulungu, safunikira kuchita kumva liwu lenileni lochokera kumwamba, kapena kuchita kuchezeredwa ndi mngelo. Iwo ndi odala pokhala ndi Mawu olembedwa a Mulungu ndi kutsogozedwa mwachikondi kudzera mwa gulu la anthu ake odzozedwa padziko lapansi. Ngati alabadira mosamala ‘mawu kumbuyo kwawo’ ameneŵa ndi kutsatira chitsogozo cha chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo, adzachitadi chifuniro cha Mulungu. Ndiyeno adzaonadi lonjezo la mtumwi Yohane likukwaniritsidwa. Ilo limati: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.”​—1 Yohane 2:17.

Kubwereza Kwachidule

• N’chifukwa chiyani Yehova amayankhula ndi zolengedwa zake zaumunthu?

• Kodi pulogalamu yoŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ingatipindulitse motani?

• Kodi chitsogozo chochokera kwa gulu la kapolo tiyenera kutani nacho?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza mawu a chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Munthu sachita kufuna ziwiya zambambande kuti alandire mauthenga ochokera kwa Mulungu

[Mawu a Chithunzi]

Ndi chilolezo cha Arecibo Observatory/​David Parker/​Science Photo Library

[Chithunzi patsamba 15]

Yehova amayankhula nafe kudzera m’Baibulo ndi pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”