Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo wa Banja Wachisangalalo Umakopera Ena kwa Mulungu

Moyo wa Banja Wachisangalalo Umakopera Ena kwa Mulungu

Olengeza Ufumu Akusimba

Moyo wa Banja Wachisangalalo Umakopera Ena kwa Mulungu

YEHOVA anadalitsa Yosefe ndi nzeru zochuluka komanso kuzindikira. (Machitidwe 7:10) Ndiye, chotsatira chake cha kuzindikira kwa Yosefe “chinali chabwino m’maso mwa Farao, ndi m’maso mwa anyamata ake.”​—Genesis 41:37.

N’chimodzimodzinso lerolino, Yehova amapatsa anthu ake Kuzindikira ndi nzeru kudzera m’phunziro la Baibulo. (2 Timoteo 3:16, 17) Nzeru ndi kuzindikira kumeneku kumabala zipatso zabwino pamene uphungu wopezeka m’Baibulo ugwiritsidwa ntchito. Khalidwe lawo nthaŵi zonse ‘lakhala labwino m’maso mwa onse amene amawaona,’ ngati mmene chochitika chotsatirachi cha ku Zimbabwe chikusonyezera.

• Mayi wina anali ndi anansi ake a Mboni za Yehova. Ngakhale kuti sankakonda anansi ake a Mboniwo, ankasirira khalidwe lawo, makamaka moyo wapakhomo pawo. Anaona kuti mwamunayo ndi mkazi wake anali ogwirizana komanso kuti ana awo anali omvera. Makamaka, mkaziyu anaonanso kuti mwamunayo ankakonda mkazi wake kwambiri.

Zimene ambiri amakhulupirira m’madera ena mu Afirika n’zakuti, ngati mwamuna akonda mkazi wake kwambiri ndiye kuti mkaziyo anadyetsa mwamuna wake mankhwala kuti azim’konda. Choncho mayiyu anakafika kwa Mboni yachikazi ija ndi kufunsa kuti: “Kodi anzathu simungandipatseko mankhwala amene munadyetsa amuna anu kuti nanenso mwamuna wanga azindikonda ngati mmene amuna anu amakukonderani?” Mboniyo inati: “Chabwino, ndikubweretserani mankhwalawo maŵa masana.”

Tsiku lotsatira, mlongoyo anapita kwa mnansi wakeyo ndi “mankhwala” ake. Kodi anali mankhwala anji? Linali Baibulo, pamodzi ndi buku la Chidziwitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Atakambirana mfundo zopezeka m’buku la Chidziwitso pa mutu wakuti “Kumanga Banja Lolemekeza Mulungu,” anauza mayiyo kuti: “Awa ndiwo ‘mankhwala’ amene ine ndi mwamuna wanga timagwiritsa ntchito kuti tizikondana, moti n’chifukwa chake timakondana kwambiri.” Phunziro la Baibulo linayamba, ndipo mofulumira mayiyu anapita patsogolo mpaka kusonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova mwa kubatizidwa m’madzi.

• Apainiya apadera aŵiri a mpingo wina waung’ono kumpoto chakumwera kumalire kwa dziko la Zimbabwe ndi Mozambique, sanapite muulaliki wa kunyumba ndi nyumba kwa milungu iŵiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anthu anali kubwera kwa iwo kudzamvetsera zimene amanena. Mmodzi wa apainiyawo akusimba mmene izi zinachitikira kuti: “Tinkayenda makilomita 15 kukachititsa phunziro la Baibulo lapanyumba mlungu uliwonse kwa munthu wina wokondwerera. Sikunali kwapafupi kwa ife kukafika kuderalo. Tinkayenda m’matope, ndiponso kuwoloka mitsinje yodzaza, ya madzi oyesa m’khosi. Ndipo izi zinatanthauza kumanga zovala ndi nsapato zathu ndi kuzinyamula pamutu, n’kuyamba kusambira, n’kukavalanso tsidya lina la mtsinjewo.

Anansi a munthu wokondwererayo anachita chidwi ndi khama lathu. Pakati pa awo amene anachita chidwi nafe panali m’tsogoleri wachipembedzo. Amene anafunsa om’tsatira ake kuti: ‘Kodi simufuna kukhala akhama ngati anyamata aŵiri a Mboni za Yehova aja?’ Tsiku lotsatira, anthu ambiri om’tsatira anafika kunyumba kwathu kuti adzadziŵe chifukwa chimene timachitira khama. Kuwonjezera apo, milungu iŵiri yotsatira, tinalandira alendo ambiri moti tinalibe nthaŵi yoti n’kudziphikira chakudya!”

Mmodzi wa anthu amene anakacheza kwa apainiyawo nthaŵi imeneyi adali m’tsogoleri wachipembedzo uja. Apainiyawo analitu achimwemwe pamene m’tsogoleri wachipembedzoyo anavomera phunziro la Baibulo lapanyumba!