N’chifukwa Chiyani Kuli Ziphuphu Zochuluka Chotere?
N’chifukwa Chiyani Kuli Ziphuphu Zochuluka Chotere?
“Musamalandira chiphuphu pakuti chiphuphu chichititsa khungu anthu openya, ndipo chingakhotetse mawu a anthu olungama.”—Eksodo 23:8, NW.
ZAKA zikwi zitatu ndi mazana asanu zapitazo, Malamulo a Mose analetsa kupereka ndi kulandira ziphuphu. Kwa zaka mazana ambiri kuchokera nthaŵi imeneyo, malamulo oletsa ziphuphu afala moŵirikiza. Komabe, malamulo alephera kuthetsa ziphuphu. Ziphuphu mamiliyoni ambiri zikuperekedwa ndi kulandiridwa tsiku ndi tsiku, ndipo anthu mabiliyoni ambiri akuvutika kwambiri chifukwa cha ziphuphuzo.
Ziphuphu zafala ponseponse ndipo zapita patsogolo kwambiri mwakuti zikuopseza chikhalidwe cha anthu. M’mayiko ena palibe chinthu chomwe chimachitika pokhapokha winawake atapatsidwa chiphuphu. Kupereka chiphuphu kwa munthu woyenera kumatheketsa munthu kukhoza mayeso, kupeza laisensi ya woyendetsa galimoto, kupeza ntchito, kapena kupambana pa mlandu m’khoti. “Ziphuphu zili ngati kuipitsidwa kwa dziko kosaneneka komwe kumadetsa nkhaŵa ndi kutayitsa mtima anthu,” anatero Arnaud Montebourg, wothandiza anthu pa milandu wa ku Paris.
Kupereka ndi kulandira ziphuphu kwapita patsogolo moŵirikiza makamaka m’nkhani za malonda. Makampani ena amaika padera gawo lachitatu la phindu lawo lonse kuti apereke ziphuphu kwa ogwira ntchito achinyengo m’boma. Malinga n’kunena kwa magazini ya ku Britain ya The Economist, pa ndalama zokwana madola 25 biliyoni zowonongedwa chaka chilichonse pa malonda a zida zankhondo a pakati pa mayiko, pafupifupi 10 peresenti ya ndalamazo zimagwiritsidwa ntchito popereka ziphuphu kwa makasitomala odalirika. Pamene kuli kwakuti ziphuphu zoterezi zawonjezereka kwambiri, zotsatira zake zikukhala zoopsa zedi. M’zaka khumi zapitazo, malonda a “pachiŵeniŵeni”—kuchita malonda mwachinyengo komwe kumakomera achuma oŵerengeka chabe omwe amagwirizana nawo—akuti n’zomwe zawononga kayendedwe ka chuma m’mayiko ambiri.
Mosapeŵeka, amene amavutika kwambiri chifukwa cha ziphuphu ndi kuloŵa pansi kwa chuma kochititsidwa ndi ziphuphuzo ndi anthu osauka—omwe sangathe n’komwe kupereka chiphuphu kwa wina aliyense. Monga momwe magazini ya The Economist ikunenera mosapita mbali, “ziphuphu ndi mtundu winanso wa kupondereza.” Kodi kuponderezana kwamtundu umenewu kungathetsedwe, kapena kodi ziphuphu n’zosapeŵeka? Kuti tiyankhe funso limenelo, choyamba tiyenera kudziŵa zinthu zikuluzikulu zomwe zimayambitsa ziphuphu.
Kodi N’chiyani Chomwe Chimayambitsa Ziphuphu?
N’chifuwa chiyani anthu amasankha kuchita ziphuphu m’malo mokhala oona mtima? Kwa ena, kulandira ziphuphu kungakhale njira yachidule kapenanso njira yokhayo yopezera zomwe akufuna. Nthaŵi zina, chiphuphu chingapereke njira yachidule yopeŵera chilango. Ambiri omwe amaona andale, apolisi, ndi oweruza milandu akusonyeza kusalabadira nkhani za ziphuphu ngakhalenso kuzichita kumene, iwo amangotsatira chitsanzo chawocho.
Pamene ziphuphu ziwonjezereka mofulumira Mlaliki 8:11.
kwambiri, zimachitidwa popanda choletsa chilichonse, ndipo pambuyo pake chimangokhala chizoloŵezi. Anthu omwe amalandira malipiro ochepa kwambiri kuntchito amaona kuti sangachitire mwina. Amaona kuti chomwe angachite kuti akhale ndi moyo wabwinopo ndicho kulandira ziphuphu basi. Ndipo pamene olandira kapena opereka ziphuphu ndi cholinga chofuna kupeza zabwino mwachinyengo sakulandira chilango, n’ngochepa omwe amadzipereka kuthetsa ziphuphuzo. “Popeza sam’bwezera choipa chake posachedwa atam’tsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa,” anatero Mfumu Solomo.—Mikhalidwe iŵiri yamphamvu kwambiri ikusonkhezera ziphuphu: dyera ndi umbombo. Chifukwa cha dyera, anthu a ziphuphu salabadira mavuto omwe ziphuphu zawozo zikudzetsa kwa ena, ndipo amaona ngati kuchita ziphuphu sikulakwa kokha chifukwa chakuti iwowo akupindula nazo. Akapeza chuma chochuluka chakuthupi, umbombo wa anthu a ziphuphuwa umakulirakulira. “Wokonda siliva sadzakhuta siliva,” anatero Solomo, “ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.” (Mlaliki 5:10) Kunena zoona, umbombo ungathe kukhala wabwino popanga ndalama, koma nthaŵi zonse umachititsa ziphuphu ndi kuswedwa kwa malamulo kusaonekera.
Chochititsa chinanso chomwe sichiyenera kunyalanyazidwa ndicho ntchito za wolamulira wadziko lino wosaonekayo, yemwe Baibulo likum’tchula kuti Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9) Satana akulimbikitsa ziphuphu mwakhama. Chiphuphu chachikulu zedi chodziŵika bwino ndi chimene Satana anafuna kupereka kwa Kristu. ‘Ndikupatsani Inu maufumu onse adziko lapansi ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.’—Mateyu 4:8, 9.
Koma Yesu sanali wolandira ziphuphu, chotero anaphunzitsa om’tsatira ake kukhalanso otero. Kodi ziphunzitso za Kristu zingakhale chida champhamvu chothetsera ziphuphu lerolino? Nkhani yotsatira idzayankha bwino lomwe funso limeneli.